Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 3/8 tsamba 29-31
  • Kodi Umodzi Wachikristu Ngwothekera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Umodzi Wachikristu Ngwothekera?
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Tchalitchi cha Katolika ndi Umodzi
  • Kodi Nchoyeneretsedwa Kuchilikiza Umodzi?
  • World Council ndi Umodzi
  • Umodzi Weniweni Ngwothekera
  • Zoyesayesa za Kugwirizanitsa
    Galamukani!—1991
  • Kupanikizidwa kwa Tchalitchi cha Katolika
    Galamukani!—1991
  • Masiku Otchuka m’Gulu la Mgwirizano wa Matchalitchi
    Galamukani!—1991
  • Kodi Nchifukwa Ninji Pali Kugaŵanikana?
    Galamukani!—1990
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 3/8 tsamba 29-31

Kodi Umodzi Wachikristu Ngwothekera?

CHIKRISTU CHADZIKO ndinyumba yogaŵikana. Mamembala ake oyerekezedwa kukhala anthu mamiliyoni 1,500 ngogaŵikana m’Roma Katolika, Orthodox Yakum’mawa, Protestanti, ndi matchalitchi ndi mipatuko ina imene imati Njachikristu. Anthu ambiri owona mtima amadabwa kaya ngati umodzi Wachikristu udzafikiridwa konse.

Polongosola moipidwa ndi kusagwirizana kwachipembedzo, chikalata cha Msonkhano Wachiŵiri wa Vatican chinafotokoza kuti: “Onse amadzilengeza kukhala ophunzira a Ambuye, koma zikhutiro zawo zimaombana ndi njira yawo yotakata, ngati kuti Kristu Iyemwini anali wogaŵikana (yerekezerani 1 Akor. 1:13). Mosakaikira, kusamvana kumeneku kumasemphana kotheratu ndi chifuno cha Kristu, kumaika chophunthwitsa ku dziko, ndipo chimatseka njira yoyera yolengezera mbiri yabwino kwa cholengedwa chirichonse.”

Tchalitchi cha Katolika ndi Umodzi

Tchalitchi cha Katolika, chomwe chiri ndi pafupifupi theka la chiwonkhetso chonse cha mamembala a Chikristu Chadziko, chiri ndi lingaliro lakelake la umodzi Wachikristu. “Zigwirizano za pemphero” zosiyanasiyana zinapangidwa kuchiyambi kwa zaka za zana lino. Pakati pa ameneŵa pali pemphero la Zaufulu za kwa Dona Wathu Wachifundo Kaamba ka Kubwerera kwa Mangalande ku Chikhulupiriro Chachikatolika, Pemphero Logwirizanitsa Odzipereka kwa Dona Wathu Wachifundo Kaamba ka Kutembenuzidwa kwa Opanduka, ndi Mapemphero Azaufulu ndi Ntchito Zabwino Ogwirizanitsanso Mipatuko Yakum’mawa ndi Tchalitchi.

Mu 1908, moyambitsidwa ndi wansembe wa Angilikani amene anakhala Mkatolika, mlungu wamapemphero wachaka ndi chaka Wachikatolika (January 18-25) unalinganizidwa “kutembenuza ndi kubweza abale opatuka.” Pambuyo pake umenewu unadzakhala Mlungu wa Pemphero la Umodzi Wachikristu wachaka ndi chaka, womwe bungwe la WCC (World Council of Churches) lakhala logwirizanitsidwa nawo chiyambire kuchiyambi kwa m’ma 1950.

Bukhu Lachikatolika lakuti The Documents of Vatican II likufotokoza kuti: “Chaka chirichonse m’January, kwa zaka makumi ambiri, Aroma Katolika akhala akupereka masiku asanu ndi atatu kupereka pemphero la umodzi wa Tchalitchi. Kufikira 1959, lingaliro lachisawawa la masiku a pemphero amenewo, January 18-25, linali chiyembekezo chakuti Aprotestanti ‘akabwerera’ ku Tchalitchi chimodzi chowona, ndikuti mpatuko wa Orthodox ukatha.”

Kodi Vatican II inasinthadi lingaliro la Tchalitchi cha Katolika ponena za umodzi Wachikristu? Woloŵa mmalo wa Papa John, Paul VI, analengeza poyera Lamulo la Chiphunzitso Choikidwiratu cha Tchalitchi cha Vatican II, chimene chimati: “Ichi ndicho Tchalitchi chenicheni cha Kristu chimene m’Chikhulupiriro timanena kukhala chimodzi, choyera, chachikatolika ndi cha atumwi. . . . Tchalitchi chimenechi, cholamulidwa ndi kulinganizidwa monga chitaganya m’dziko liripoli, chimachilikizika pa Tchalitchi cha Katolika, chomwe chimalamulidwa ndi mloŵa mmalo wa Petro ndi abishopu limodzi naye.”

Chotero lingaliro la Tchalitchi cha Katolika la umodzi Wachikristu silinasinthe kwenikweni. Lingaliro lolongosoledwa pa Vatican II kwenikweni, nlakuti zinthu zabwino zimene ziri kunja kwa Tchalitchi cha Katolika nzake, ndipo chotero, monga momwe Lamulo la Chiphunzitso Choikidwiratu cha Tchalitchi limanenera, “ziri mphamvu zosonkhezera kulinga ku umodzi wa Chikatolika.”

Kodi Nchoyeneretsedwa Kuchilikiza Umodzi?

Kodi tinganenenji za kunena kobwerezedwabwerezedwa kwa Tchalitchi cha Katolika kuti ndicho “chimodzi, choyera, chachikatolika, ndi cha atumwi”? Choyamba, mpatuko waposachedwapa wa Akatolika amwambo wotsogozedwa ndi Akibishopu Lefebvre, osatchulapo za kupanduka kwapoyera kwa akatswiri a maphunziro azaumulungu Achikatolika mazana ambiri, kumasonyeza kunena kumeneko kwa tchalitchi kukhala “chimodzi” kukhala kwabodza.a

Chachiŵiri, mbiri ya Tchalitchi cha Katolika, ndi kudana kwake ndi Ayuda, kuzunza kwake “opanduka,” kuchilikiza kwake “nkhondo zopatulika,” ndikudziloŵetsa kwake m’ndale zadziko ndi mbiri zoipa zakusakaza ndalama, zimavumbula kuti sichiri konse choyera.

Chachitatu, Tchalitchi cha Roma sichingalungamitse konse kunena kwake kwakuti “nchachikatolika,” kapena “chapadziko lonse,” popeza kuti chimapanga kokha theka la anthu omwe amati ndi Akristu, kapena pafupifupi 15 peresenti ya chiŵerengero cha dziko lonse.

Pomalizira, palibe mfundo za mbiri yakale, cholembera cha upapa, kapena chuma, chisembwere, kuloŵa m’ndale zadziko kwa atsogoleri ambiri Achikatolika, zimene zingalungamitse kunena kwa tchalitchi kuti “ncha atumwi.” Mwachiwonekere, Tchalitchi cha Katolika chilibe udindo wonenera kuti ndicho maziko a umodzi weniweni Wachikristu.

World Council ndi Umodzi

Bungwe la World Council of Churches limaphatikizapo matchalitchi a Chiprotestanti oposa 300 ndi a Orthodox Yakum’mawa omwe ali ndi mamembala oposa mamiliyoni 400 m’maiko oposa zana limodzi. Cholinga cha bungwelo ndicho “kulengeza umodzi wofunika wa Tchalitchi cha Kristu ndikudziŵikitsa mowonekera thayo la matchalitchi lakusonyeza umodzi umenewo ndi kufunika kofulumira kwa ntchito yolengeza.” Komabe, kodi bungwe la WCC limapereka chiyembekezo choposa cha umodzi wa Chikristu chowona kuposa mmene chimachitira Tchalitchi cha Roma Katolika?

Kodi bungwe la WCC likuyembekezera kugwirizanitsa Akristu pamaziko otani? Bukhu lanazonse likufotokoza kuti: “World Council of Churches. . . . Mwachisawawa mamembala amavomereza kuti kugaŵanikana pakati pa Akristu nkosemphana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo nchopinga chachikulu choletsa anthu osakhala Akristu kuvomereza Chikristu. . . . Chikhutiro chakuti umodzi uyenera kuzikidwa pa chowonadi chakula.” Chotero, pamenepo, kodi nchiyani chimene chimalingaliridwa kukhala chowonadi chenicheni ndi matchalitchi oposa 300 omwe ndi mamembala a bungwe la WCC?

Mu 1948 maziko oyambirira okhalira membala wa bungwe la WCC analingaliridwa ndi matchalitchi ena kukhala a Utatu. Chotero mu 1961 maziko okhalira membala anasinthidwa kuŵerenga motere: “Bungwe la World Council of Churches ndilo mgwirizano wa matchalitchi amene amati Ambuye Yesu Kristu ali Mulungu ndi Mpulumutsi mogwirizana ndi Malemba ndipo chotero amafuna kukwaniritsa pamodzi chiitano chawo chofanana ku ulemerero wa Mulungu mmodzi, Atate, Mwana ndi Mzimu Woyera.”—Kanyenye ngwathu.

Maziko enieni a umembala amenewo m’bungwe la WCC ngosemphana mawu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti chikhulupiriro mwa “Mulungu mmodzi, Atate, Mwana ndi Mzimu Woyera” sichiri ‘chogwirizana ndi Malemba.’ The Encyclopedia of Religion ikufotokoza kuti: “Akatswiri azaumulungu lerolino amavomerezana kuti Baibulo Lachihebri liribe chiphunzitso cha Utatu.” Kuwonjezerapo, The New International Dictionary of New Testament Theology ikulongosola kuti: “Chikristu choyambirira chinalibe chiphunzitso chenicheni cha Utatu.” Ndipo The New Encyclopædia Britannica ikulengeza kuti: “Ndiponso mawu akuti Utatu kapena chiphunzitso chenichenicho mulibe m’Chipangano Chatsopano, ndiponso Yesu ndi otsatira ake sanafune kutsutsa Shema m’Chipangano Chakale: ‘Imvani, Israyeli: Ambuye Mulungu wathu ali Ambuye mmodzi’ (Deut. 6:4).”

Ndiponso, bungwe la WCC lakhala lodziloŵetsa kotheratu m’kulimbana kwa ndale zadziko. Mwachitsanzo, lapereka ndalama zochilikiza magulu omenyera ufulu okhala ndi zida. The New Encyclopædia Britannica ikuvumbula kuti: “Kuloŵetsedwamo m’magulu omenyera ufulu kochitidwa ndi magulu ena a bungwe la WCC kwanthaŵi ndi nthaŵi kwapangitsa chisulizo chochokera kwa matchalitchi ena oimiridwa m’bungwelo.” Kudziloŵetsa m’ndale zadziko kosakhala Kwachikristu sikungabweretse umodzi wowona Wachikristu, monga momwe sangachitire maziko a chiphunzitso osazikidwa pa Baibulo.

Umodzi Weniweni Ngwothekera

Mosangalatsa, Encyclopædia Universalis (1989) Yachifrenchi ikulongosola kuti cholinga cha mgwirizano wa matchalitchi ndicho “kubwezera banja logaŵanikana Lachikristu umodzi weniweni ndipo wowonekera, mogwirizana ndi ziphunzitso za Yesu. . . . Powona mmene Akristu amakonderana, osakhala Akristu ayenera kukhala ndi chikhulupiriro ndikugwirizana ndi Tchalitchi, akumalingalira kuti dziko latsopano m’limene utumiki, chilungamo, ndi mtendere zidzakhala malamulo amakhalidwe abwino olamulira, monga momwe kunanenedweratu ndi kusonyezedwa ndi Kristu. . . . Nkoyenerera kuti . . . Kalata ya kwa Ahebri (II, 5) iyenera kulankhula za ‘oi·kou·meʹne [dziko lapansi lokhalidwa ndi anthu] likudzalo,’ mwakutero kugogomezera kuti chiyembekezo Chachikristu sichiri cha dziko lauzimu lopanda anthu anyama, koma dziko [lapansi] lokhalidwa ndi anthu limeneli loyanjanitsidwa ndi Mlengi wake.”

Mamembala owonjezerekawonjezereka a matchalitchi a Chikristu Chadziko akufikira pa kuzindikira kuti ziphunzitso za tchalitchi chawo sizogwirizana ndi ziphunzitso za Yesu. Iwo amawona mwamanyazi kuti mamembala a chipembedzo chawo samakondana. Komabe, ambiri a iwo apeza banja la Akristu amene ali ogwirizanadi, ndipo awona mmene iwo amakonderana. Inde, iwo apeza umodzi weniweni Wachikristu ndi chiyembekezo pakati pa banja lapadziko lonse la Mboni za Yehova.

Monga chotulukapo, mamiliyoni omwe kale anali mamembala a matchalitchi a Chikristu Chadziko afikira pakukhala ndi chiyembekezo mwa Mulungu cha kugwirizanitsa kwake dziko latsopano, mmene utumiki, chilungamo, ndi mtendere zidzakhala malamulo amakhalidwe abwino olamulira.

[Mawu a M’munsi]

a Kaamba ka tsatanetsatane, onani Galamukani! ya July 8, 1990, masamba 25-31.

[Mawu Otsindika patsamba 31]

Anthu ambiri apeza banja lapadziko lonse la Akristu omwe ngogwirizana kale

[Chithunzi patsamba 30]

Chifanizo chachikumbukiro ichi chimene chiri pamalikulu a bungwe la World Council of Churches, Geneva, Switzerland, chimaphiphiritsira mapemphero awo a umodzi wa tchalitchi, omwe sanayankhidwebe

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena