Masiku Otchuka m’Gulu la Mgwirizano wa Matchalitchi
1844: Kuyambika kwa gulu la zipembedzo zosiyanasiyana lomwe pambuyo pake linapanga magulu a Young Men’s ndi Young Women’s Christian Associations.
1846: Msonkhano woyamba wa mitundu yonse wa zipembedzo zonse wa Evangelical Alliance, wochitidwira mu London, Mangalande.
1908: Bungwe la Federal Council of the Churches of Christ mu Amereka linapangidwa. Mu 1950 ilo linakhala National Council of the Churches of Christ in the United States of America.
1910: Msonkhano woyamba wa World Missionary Conference unachitidwa mu Edinburgh, Scotland, “kumene gulu la mgwirizano wa matchalitchi lamakono linayambiradi.”—Encyclopædia Britannica.
1919: Papa Benedict XV anakana chiitano chakuti Tchalitchi cha Katolika chikhale ndi phande pamsonkhano ndi Tchalitchi Chachiprotestanti cha Episcopal wonena za chikhulupiriro ndi utumiki (kusiyana kwa matchalitchi m’chiphunzitso ndi uminisitala).
1921: Bungwe la International Missionary Council linapangidwa.
1925: Msonkhano woyamba wa mitunduyonse wa Universal Christian Council on Life and Work (wophunzira lamulo lofala la tchalitchi pankhani za chuma, ndale zadziko, ndi mayanjano), wochitidwira mu Stockholm, Sweden.
1927: Msonkhano woyamba wapadziko lonse wa matchalitchi onse wa gulu la “Faith and Order,” wochitidwira mu Lausanne, Switzerland.
1928: Papa Pius XI anapereka kalata yonka kwa mabishopu onse yotchedwa Mortalium animos, yoletsa Akatolika kupereka chilikizo lirilonse ku gulu la mgwirizano wa matchalitchi.
1937: Msonkhano wa “Life and Work” wochitidwira mu Oxford, Mangalande, ndi msonkhano wa “Faith and Order” wochitidwira mu Edinburgh, Scotland, unavomereza kupanga komiti yoyembekezera kukhazikitsa bungwe lapadziko lonse la matchalitchi. Ntchito imeneyi inalekezedwa chifukwa cha kuulika kwa Nkhondo Yadziko ya II.
1948: Bungwe la WCC (World Council of Churches) linapangidwa pamsonkhano wopanga malamulo wochitidwira mu Amsterdam, Netherlands. Mamembala ake anaphatikizapo pafupifupi matchalitchi 150 Achiprotestanti ndi ena a Orthodox Yakum’mawa. Chiyambire pamenepo bungwe la WCC lakhala likuchititsa misonkhano mokhazikika (1954: Evanston, Illinois, U.S.A.; 1961: New Delhi, India; 1968: Uppsala, Sweden; 1975: Nairobi, Kenya; 1983: Vancouver, Canada).
1960: Papa John XXIII anakhazikitsa Bungwe Lochilikiza Umodzi Wachikristu pa Vatican. Uku “kunali kuzindikira koyamba kwalamulo kochitidwa ndi Tchalitchi cha Roma Katolika kwa kukhalapo kwa gulu la mgwirizano wa matchalitchi.”—Encyclopædia Britannica.
1961: Bungwe la International Missionary Council linagwirizana ndi bungwe la WCC. Vatican inayamba kutumiza openyerera alamulo Achikatolika ku misonkhano ya bungwe la WCC.
1964: Papa Paul VI analengeza poyera “Lamulo la Mgwirizano wa Matchalitchi” pa Msonkhano Wachiŵiri wa Vatican, lomwe linalongosola malire a kukhalamo ndi phande kwa Katolika m’gulu la mgwirizano wa matchalitchi.
1965: Papa ndi akalambula bwalo a Orthodox anathetsa lamulo lochotsa munthu m’tchalitchi limene omwe analipo kalelo analengeza motsutsana mu 1054.
1968: Bungwe lotchedwa SODEPAX (Joint Committee on Society, Development, and Peace) linakhazikitsidwa ndi Vatican ndi bungwe la WCC.
1969: Papa Paul VI anakachezera malikulu adziko lonse a bungwe la WCC, mu Geneva, Switzerland. Komabe, iye anagogomezera kuti iye anali mloŵa mmalo wa mtumwi Petro ndikuti kukambitsirana kulikonse kwa kugwirizana kwa Tchalitchi cha Katolika ndi bungwe la WCC kunali kosayenera panthaŵiyo.
1980: Bungwe la SODEPAX linathetsedwa.
1986: Papa John Paul II analinganiza mgwirizano wa matchalitchi wa “Tsiku Lopempherera Mtendere Padziko Lonse” mu Assisi, Italy, kumene atsogoleri auzimu oimira zipembedzo zazikulu padziko anasonkhana kupempherera mtendere mogwirizana ndi miyambo yawo yosiyanasiyana.