Bwanji Ponena za Mtsogolo?
Kodi nchifukwa ninji mtendere pakati pa anthu ndi chilombo uli wokoma motero? Nchifukwa chakuti anthu poyambirira analengedwa kuti akhale pamtendere ndi nyama, ngakhale zija zakuthengo.
Pamene Mulungu anapanga mwamuna ndi mkazi oyambirira, iye anawaika m’dera laparadaiso lapadziko lapansi kuti asangalale ndi moyo. Chinali chifuno chake kuti iwo akhale ndi ana ndi kufutukula malire a Paradaiso woyambirirayo kufikira atakuta dziko lonse lapansi. M’malo onsewo, anthu akakhala ndi nyama zowagonjera mwamtendere.
Cholembedwa cha Genesis chimati: ‘Alamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa ng’ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi. . . . Ndipo anaziwona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, tawonani, zinali zabwino ndithu.’—Genesis 1:26-31; 2:9.
Kugonjera kwa nyama kumeneku sikunayenera kukhala kwa nkhalwe. Anthu limodzi ndi nyama analinganizidwa kukhalira pamodzi mumtendere. Izi zingawonedwe ndi chenicheni chakuti pamene nyama zinadza kwa munthu kuti azitche maina, iye analibe zida. Ndipo sipakutchulidwa mantha osonyezedwa ndi munthu kapena chilombo.—Genesis 2:19, 20.
Chifuno Choyambirira Chidzakwaniritsidwa
Mosangalatsa, chifuno choyambirira cha Mulungu chimenecho chidzachitidwa posachedwapa, pamene maboma onse opangidwa ndi anthu adzalowedwa mmalo ndi Ufumu wa Mulungu, umene umalamulira kuchokera kumwamba. (Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10) Ulamuliro wa Mulungu utakhazikitsidwa kotheratu padziko lonse lapansi, chifuno choyambirira cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi ndi anthu ake limodzi ndi nyama zokhalamo chidzakwaniritsidwa.
Ziyambukiro zosanduliza za ulamuliro wolungama wa Mulungu zafotokozedwa bwino m’maulosi ambiri Abaibulo. Mwachitsanzo, tawonani zimene Yesaya analemba mouziridwa kumati: ‘Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wankhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choŵeta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera. Ndipo ng’ombe yaikazi ndi chilombo zidzadya pamodzi; ndipo ana awo aang’ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng’ombe. Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.’—Yesaya 11:6, 7, 9.
Maulosi ena nawonso amasonyeza mtendere waukulu womwe udzakhalako m’dziko latsopano la Mulungu. Ponena za ichi Mika ananeneratu kuti: ‘Ndipo iwo adzasula malupanga awo akhale makasu, ndi mikondo yawo ikhale mazenga, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo. Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa.’—Mika 4:3, 4.
Palibe nyama iriyonse yakuthengo imene idzadodometsa mtendere wa anthu, pakuti mawu aulosi a Mulungu amati: ‘Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m’dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m’chipululu. . . . Ndipo adzakhazikika m’dziko mwawo.’—Ezekieli 34:25, 27.
Chotero mtendere ndi chigwirizano kuzungulira Paradaiso wobwezeretsedwanso ameneyo udzakhala wokwana kotheratu. Ndicho chifukwa chake mikhalidwe mmenemo inafotokozedwa m’bukhu lomalizira la Baibulo mwanjira iyi: ‘[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita. Ndipo iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, Tawonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mawu aŵa ali okhulupirika ndi owona.’—Chibvumbulutso 21:4, 5.
Inde, ali okhulupirika ndi owona. Izi zitanthauza kuti tingadalire malonjezo a Mulungu, popeza kuti mosiyana ndi anthu opanda ungwiro, iye ali nazo mphamvu, nzeru, ndi kutsimikiza mtima kuchita zifuno zake. Monga momwe mmodzi wa atumiki okhulupirika a Mulungu akale ananenera kuti: ‘Pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasowapo mawu amodzi.’—Yoswa 23:14; onaninso Yesaya 55:11.
Tingakhale ndichidaliro chimodzimodzicho chakuti posachedwapa, m’dziko latsopano la Mulungu, chifuno chake choyambirira kaamba ka dziko lapansi, anthu, ndi nyama chidzakwaniritsidwa. Mtendere woperekedwa ndi Mulungu udzakhala weniweni padziko lonse lapansi. Sikuti mtendere woterowo udzangokhala pakati pa anthu pokha komanso udzasonyezedwa pakati pa nyama.