Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • pr gawo 8 tsamba 29-31
  • Khalani ndi Moyo Kosatha Padziko Lapansi Laparadaiso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani ndi Moyo Kosatha Padziko Lapansi Laparadaiso
  • Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Anthu Akukhala pa Mtendere Weniweni
  • Munthu Adzakhala pa Mtendere ndi Nyama
  • Thanzi Langwiro, Moyo Wosatha
  • Akufa Abwezeretsedwa ku Moyo
  • Dziko Lapansi, Paradaiso Wokhala ndi Zochuluka
  • Nyumba Zabwino kwa Onse
  • Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso
  • Dziko Latsopano Lokongola Koposa la Mulungu
    Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
  • Linaneneratu Zimene Zichitike Posachedwapa
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere
    Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere
  • Pambuyo pa Harmagedo, Dziko Lapansi Laparadaiso
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
pr gawo 8 tsamba 29-31

Mbali 8

Khalani ndi Moyo Kosatha Padziko Lapansi Laparadaiso

1 Kodi moyo udzakhala wotani Mulungu akadzachotsa kuipa ndi kuvutika padziko lapansi ndi kubweretsa dziko lake latsopano muulamuliro wachikondi wa Ufumu wake wakumwamba? Mulungu akulonjeza ‘kuoloŵetsa dzanja lake ndi kukwaniritsa zamoyo zonse chokhumba chawo.’​—⁠Salmo 145:⁠16.

2 Kodi zokhumba zanu zoyenera nzotani? Kodi sindizo moyo wachimwemwe, ntchito yopindulitsa, chuma chakuthupi chochuluka, malo okongola, mtendere pakati pa anthu onse, ndi ufulu ku chisalungamo, matenda, kuvutika, ndi imfa? Ndipo bwanji za moyo wauzimu wosangalatsa? Zinthu zonsezo zidzakwaniritsidwa posachedwapa muulamuliro wa Ufumu wa Mulungu. Tawonani zimene maulosi a Baibulo amanena za madalitso abwino koposa amene adzakhala m’dziko latsopanolo.

Anthu Akukhala pa Mtendere Weniweni

3 “ [Mulungu] aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magareta [ankhondo] ndi moto.”​—⁠Salmo 46:⁠9.

4 “Adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”​—⁠Yesaya 2:⁠4.

5 “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”​—⁠Salmo 37:⁠11.

6 “Dziko lonse lapuma, lili du; iwo ayamba kuimba nyimbo.”​—⁠Yesaya 14:⁠7.

Munthu Adzakhala pa Mtendere ndi Nyama

7 “Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choŵeta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera. Ndipo ng’ombe yaikazi ndi chilombo zidzadya pamodzi; ndipo ana awo aang’ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng’ombe. Ndipo mwana wakuyamwa adzaseŵera pa una wa mamba, ndi mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lake m’funkha la mphiri. Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga [madzi] adzaza nyanja.”​—⁠Yesaya 11:​6-9.

8 “Ndipo tsiku lomwelo ndidzawachitira pangano ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi . . . ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka.”​—⁠Hoseya 2:⁠18.

Thanzi Langwiro, Moyo Wosatha

9 “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba.”​—⁠Yesaya 35:​5, 6.

10 “ [Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.”​—⁠Chivumbulutso 21:⁠4.

11 “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”​—⁠Yesaya 33:⁠24.

12 “Mnofu wake udzakhala se, woposa wa mwana.”​—⁠Yobu 33:⁠25.

13 “Mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.”​—⁠Aroma 6:⁠23.

14 “Yense wakukhulupirira iye . . . [adzakhala] nawo moyo wosatha.”​—⁠Yohane 3:⁠16.

Akufa Abwezeretsedwa ku Moyo

15 “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”​—⁠Machitidwe 24:⁠15.

16 “Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda [chikumbukiro cha Mulungu] adzamva mawu ake, nadzatulukira.”​—⁠Yohane 5:​28, 29.

17 “Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade [manda] zinapereka akufawo anali m’menemo.”​—⁠Chivumbulutso 20:⁠13.

Dziko Lapansi, Paradaiso Wokhala ndi Zochuluka

18 “Padzakhala mivumbi ya madalitso. Ndi mitengo ya kuthengo idzapereka zobala zawo, ndi nthaka idzapereka zipatso zake, ndipo adzakhazikika m’dziko mwawo.”​—⁠Ezekieli 34:​26, 27.

19 “Dziko lapansi lapereka zipatso zake: Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.”​—⁠Salmo 67:⁠6.

20 “Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti se lidzasangalala ndi kuphuka ngati duwa.”​—⁠Yesaya 35:⁠1.

21 “Mapiri ndi zitunda, zidzaimba zolimba pamaso panu, ndi mitengo yonse ya m’thengo idzaomba m’manja mwawo. M’malo mwa mithethe mudzatuluka mtengo wamlombwa; ndi m’malo mwa lunguzi mudzamera mtengo wamchisu.”​—⁠Yesaya 55:​12, 13.

22 “Udzakhala ndine m’Paradaiso.”​—⁠Luka 23:⁠43.

Nyumba Zabwino kwa Onse

23 “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo . . . Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzaoka, ndi wina kudya; . . . osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo. Iwo sadzagwira ntchito mwachabe, pena kubalira tsoka.”​—⁠Yesaya 65:​21-23.

24 “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa.”​—⁠Mika 4:⁠4.

Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso

25 Ha, ndimtsogolo mwabwino koposa chotani nanga! Miyoyo yathu ingakhale ndi chifuno chenicheni chotani nanga tsopano itazikidwa pa chiyembekezo cholimba chakuti m’dziko latsopano la Mulungu mavuto onse alerolino adzakhala zinthu zakale! “Zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima.” (Yesaya 65:17) Ndipo nkotonthoza chotani nanga kudziŵa kuti panthaŵiyo moyo udzakhala wamuyaya: “ [Mulungu] wameza imfa ku nthaŵi yonse.”​—⁠Yesaya 25:⁠8.

26 Kodi mukufuna kudzakhala ndi moyo kosatha m’dziko latsopano Laparadaiso limene layandikiralo? Mungafunse kuti: ‘Kodi ndifunikira kuchita chiyani kuti ndidzakhale ndi chiyanjo cha Mulungu pamapeto a dzikoli ndi kuloŵa m’dziko lake latsopano? ’ Muyenera kuchita zimene Yesu anasonyeza m’pemphero lomka kwa Mulungu kuti: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”​—⁠Yohane 17:⁠3.

27 Chotero, pezani Baibulo, ndi kutsimikizira zimene mwaŵerenga m’broshali. Funafunani ena amene amaphunzira ndi kuphunzitsa zowonadi za m’Baibulo zimenezi. Wonjokani ku zipembedzo zonyenga zimene zimaphunzitsa ndi kuchita zinthu zosemphana ndi Baibulo. Phunzirani mmene inuyo, limodzi ndi mamiliyoni ena amene akuchita kale chifuniro cha Mulungu, mungakhalire ndi phande m’chifuno cha Mulungu chakuti anthu akhale ndi moyo kosatha padziko lapansi laparadaiso. Ndipo khulupirirani zimene Mawu ouziridwa a Mulungu amanena ponena za patsogolopa: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.”​—⁠1 Yohane 2:⁠17.

[Study Questions]

1, 2. Kodi moyo udzakhala wotani muulamuliro wa Ufumu wa Mulungu?

3-6. Kodi tili ndi chitsimikiziro chotani chakuti anthu adzakhala ndi mtendere m’dziko latsopano?

7, 8. Kodi padzakhala mtendere wotani pakati pa anthu ndi nyama?

9-14. Fotokozani mikhalidwe ya thanzi ya m’dziko latsopano.

15-17. Kodi pali chiyembekezo chotani kwa amene afa kale?

18-22. Kodi dziko lonse lapansi lidzasandulizidwa kukhala chiyani?

23, 24. Kodi tili ndi chitsimikiziro chotani chakuti padzakhala nyumba zokwanira kwa onse?

25. Kodi ndimtsogolo mwabwino motani mmene tili namo?

26. Kodi nchiyani chomwe chili mfungulo ya kukhala ndi moyo kosatha m’dziko latsopano la Mulungu?

27. Kodi muyenera kuchita chiyani kuti mukhale ndi phande m’chifuno cha Mulungu?

[Picture on page 31]

Chifuno cha Mulungu chakubwezeretsa paradaiso wapadziko lapansi chidzakwaniritsidwa posachedwapa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena