Njira Zosakhala Zabwino Koposa Zopangira Kusintha
PAMENE makhalidwe akhazikitsidwa, kodi mungawasinthe motani? Kodi mungatembenukire kwa yani, ndipo ndinjira zotani zimene zingagwiritsiridwe ntchito kupanga masinthidwe okhalitsa?
Tiyeni tipende njira zina zonkitsa zimene zikugwiritsiridwa ntchito lerolino.
Chipsinjo Chandale Zadziko
Anthu mamiliyoni ambiri lerolino akukhala ndimoyo pansi pa maulamuliro amene amafuna kulamulira miyezo ndi dongosolo la mayendedwe. Maboma oterowo amagwiritsira ntchito mphamvu zawo kukakamiza kusintha—ena mwamachenjera, ena mokakamiza. Ena amagwiritsira ntchito maluso okakamiza kutaya zikhulupiriro zakale, kaŵirikaŵiri ophatikizapo chiwopsezo, kuponyedwa m’ndende, ndi kuzunza. Mwakugwiritsira ntchito ulamuliro pa zoulutsira nkhani ndi madongosolo ena azamaphunziro, iwo amafuna kuloŵetsa m’malo malingaliro onse okhazikitsidwa kale ndi aja ofunidwa ndi bungwe lomwe likulamulira. Malingaliro osiyana onse amaponderezedwa. Aliyense amene amasonyeza kukhala wosafuna kuphunzitsidwanso angachitidwe nkhanza imene kaŵirikaŵiri imaswa mzimu wa munthuyo.
Opareshoni Yaubongo ndi Kuikidwa Magetsi
Mbali zinazake za ubongo zazindikiridwa kuti zimayambukira mkhalidwe wakutiwakuti wamaganizo ndi mitundu ina ya khalidwe la munthu. Opareshoni yaubongo imaphatikizapo kuchotsa kapena kuwononga minyewa m’mbali imeneyo ya ubongo. Pamene yachotsedwa, chigawo chimenecho cha ubongo wanu sichingagwirenso ntchito, ndipo khalidwe lirilonse limene chinasonkhezera lidzazimiririka.
Kumanenedwa kuti zikwi za maopareshoni oterowo akhala akuchitidwa, makamaka pa anthu okhala ndi khalidwe lakugonana loipitsitsa ndi lowopsa. Ena anaikidwa tizipangizo tolandira magetsi mkati mwa ubongo wawo, ndipo pamene magetsi amayatsidwa, kamayambitsa kapena kutsekereza ntchito ya ubongo m’malo amenewo. Amati chimenechi chimasintha mphamvu yoyambukira khalidwe lolamuliridwa ndi mbali imeneyo ya ubongo.
Mankhwala
Kugwiritsiridwa ntchito kwa mankhwala m’chipatala cha ochita misala nkotchuka ndipo kaŵirikaŵiri kumafunika. Pali mankhwala otonthoza, mankhwala ogoneka, mankhwala okangalitsa, ndi mankhwala owongolera kusalinganizika kwa machemical muubongo. Palinso mankhwala omwe agwiritsiridwa ntchito monga okhaulitsira m’ndende ndi m’ziungwe zina zolangira. Aŵiri a mankhwala oterowo ndiwo apomorphine ndi Anectine.
Apomorphine amagwiritsiridwa ntchito kwa akaidi amene khalidwe lawo linalingaliridwa kukhala loipitsitsa. Iwo amachititsa nseru yosautsa ndi kusanza. Mkaidiyo amauzidwa kuti ngati adzisungiranso moipa, adzapatsidwa apomorphine wowonjezereka. Ichi chimatchedwanso kuchiritsidwa ndi nkhanza. Anectine amachititsa kupuma nkhweza, kotsamwitsa mwa mkaidi wopulupudzayo. Iye amalingalira kuti adzafa. Ngati apulupudzanso, amapatsidwa Anectine wowonjezereka.
Kodi zimenezi ndizo njira zimene mukagwiritsira ntchito kusintha khalidwe lanu?
Njira zochuluka zotchulidwa pamwambapa zimapondereza ufulu wakudzisankhira. Izo zimaloŵetsamonso chisonkhezero cha anthu okhala ndi ulamuliro pa wina komabe sinthaŵi zonse kuti amakhala ndi ubwino wa winayo m’maganizo. Kodi mphamvu ya ndale zadziko imafuna ubwino wake kapena wa munthuyo? Pochita opareshoni yaubongo, kodi ndani amene amagwira lumo lotumbulira? Kodi ndani amene amayatsa ndi kuzima choyatsira pamene kuika magetsi muubongo kukugwiritsiridwa ntchito? Kodi kuchiritsidwa ndi nkhanza kumatenga utali wotani? Kodi wochiritsayo angadaliridwe?
Tiyeni tilingalire njira yolandirika kwenikweni.