Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingampangitse Motani Msungwanayo Kuleka Kundivuta?
YOSEFE anali mnyamata wotchuka. Wogwira ntchito, wodalirika, ndipo wokongola, anali kukondedwa ndi aliyense amene anagwira naye ntchito. Vuto linali lakuti, mkazi wa bwana wake anakopeka naye. Kuyang’ana kwake kotyasira kunayamba kukhala kolimba mtima; kulankhula kwake kotyasira koseleula kunayamba kukhala kotsimikiza.
Yosefe anayesa kunyalanyaza machitidwe a mkaziyo, koma tsiku lina ali pantchito, anadzipeza ali yekha ndi mkaziyo. Mkaziyo anali atalinganiza bwino lomwe; sipadzakhala munthu wina aliyense kwa maola angapo. Yosefe asanazindikire zimene zinali kuchitika, mkaziyo anasonyezeratu poyera chilakolako chake, namchonderera kuti agonane naye!—Genesis 39:7-12.
Nkhani yowona imeneyi inachitika zaka 3,500 zapitazo. Koma zochitika zofananazo zikuchitika tsiku lirilonse m’sukulu ndi pantchito. Ngakhale kuti ofalitsa nkhani amanena zambiri ponena za kuvutitsidwa kwa akazi—ndipo kuli bwino popeza kuti ndivuto lalikulu—kaŵirikaŵiri vuto lonyalanyazidwa liri la kuvutitsidwa mwakugonana kwa amuna achichepere.a Popeza kuti chitaganya chamakono chimagogomezera pa kugonana ndi kulingana kwa akazi, limodzi ndi kunyonyotsoka kwake kwa makhalidwe ndi miyezo yamayanjano, siziyenera kutidabwitsa kuti amuna achichepere ambiri amasimba kuti anali chandamale cha kusadziletsa kwachikondi kwa akazi.
Anyamata ena amalandira kusintha kwa zinthu kumeneku; iwo amakondweretsedwa ndi chisamaliro cha akazi. Komabe, achichepere Achikristu amamamatira ku miyezo ya Baibulo ya makhalidwe akugonana. Iwo samafuna kuvutidwa ndi akazi olimba mtima okhala ndi zolinga zachisembwere. Funso nlakuti, Kodi angapeŵe motani kuvutitsidwa koteroko?
Nchifukwa Ninji Ine?
Baibulo limati: “Kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu yawo.” (Miyambo 20:29, NW) Ulemerero wa uchichepere, limodzi ndi chiyero chamakhalidwe ndi mikhalidwe Yachikristu ya mwamuna wachichepere, zingakhale zokopa kwenikweni kwa mkazi. Ena angalingaliredi kuwonongedwa kwa chiyero cha Mkristu wachichepere kukhala chitokoso chosautsa.
Ndiyeno pali chisonkhezero cha chitaganya chamakono. Mabuku ndi nkhani zambirimbiri zalembedwa kuthandiza asungwana kukopa amuna. Magazini a azaka zapakati pa 13 ndi 19 amasonkhezera kwenikweni asungwana kutyasira popanda manyazi. Magazini a Seventeen analengeza kuti: “Kutyasira kuli njira yaikulu yodziŵitsira winawake kuti mwampeza kukhala . . . wokopa. . . . Kungatsogolere ku ubwenzi kapena chikondi.” Zinthu zomwe zimalingaliridwa kukhala zovomerezedwa ndi ofalitsa nkhani ndi makhalidwe zimathandizanso kuchepetsa nyonga ya anyamata. Wolemba nkhani Kathy McCoy anadziŵitsa kuti: “Mwachisawawa chitaganya ndi makolo ndipo makamaka ausinkhu wawo amakhala olekerera kwenikweni zochita za kugonana mwa anyamata. Akatswiri ena amakhulupirira kuti anyamata amalandira chilimbikitso chosaneneka . . . kuti akhale okangalika m’zakugonana.”
Komabe, Mawu a Mulungu amachenjeza achichepere kukhala oyera. ‘Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule ku dama.’ (1 Atesalonika 4:3) Simungalole zisonkhezero za dzikoli kukusokeretsani! Pamenepo, kodi muyenera kuchitanji ngati wina wake wosiyana naye chiŵalo abwera kwa inu ndi machitidwe ofuna kugonana?
Chifukwa Chake Kuli Kovuta Kupeŵa
Pamene kuli kwakuti kaŵirikaŵiri amuna agonjetsa mwakuthupi akazi omwe anakana machitidwe awo ofuna kugonana, kaŵirikaŵiri akazi samagonjetsa amuna mwanjira imeneyo. Pamenepo, nchifukwa ninji kuli kovuta kwa mnyamata kupeŵa msungwana wosadziletsa?
Chifukwa chimodzi nchakuti ‘mtima uli wonyenga.’ (Yeremiya 17:9) Monga momwe Wayne wachichepere anavomerezera kuti: “Umatsala pang’ono kulakalaka kukhumbiridwa kotero. Kumakusangalatsa kudziŵa kuti winawake ali wokondweretsedwa nawe. Kuli mtundu wa kusyasyalika.” Ndithudi, kuli kwachibadwa kusangalala ndi kukondedwa ndi mkazi. Koma samalani! Mtima wanu wonyenga ungapangitse zilakolako zachibadwa zimenezi kugonjetsa zimene mudziŵa kukhala zolondola. (Yakobo 1:14, 15) Musanachizindikire, mungamatsogozedwe ‘monga ng’ombe yopita kukaphedwa’!—Miyambo 7:22.
Chotero Miyamboyo ikuchenjeza amuna achichepere kuchenjera ndi ‘lilime losyasyalika la mkazi wachiwerewere. Asakuchititse kaso m’mtima mwako, asakukole ndi zikope zake.’ (Miyambo 6:24, 25) Pamenepo, mfungulo ndiyo kulamulira mtima ndi zilakolako zanu. (1 Atesalonika 4:4-6) Kokha ngati mulidi otsimikiza kwenikweni kuti chisembwere chakugonana sichimapereka chirichonse koma “njira ya kumanda,” kapena imfa, mpamene mungapange chodzichinjiriza chokhutiritsa ndi chogwira mtima.—Miyambo 7:27.b
Kulaka Chitsenderezo
“Asungwana amaumirira; iwo amapitirizabe kubweranso,” anadandaula motero mnyamata wina. “Amakuthokoza kwambiri ndikugwiritsira ntchito mawu osyasyalika.” Kwanthaŵi yaitali mawu osyasyalika akhala chida cha mkazi wosadziletsa. Kodi mumakopeka nawo mopambanitsa? (Miyambo 26:28) ‘Nzeru iri ndi odzichepetsa,’ imatero Miyambo 11:2, ndipo ngati mumadzilingalira mosamalitsa, simudzakopeka kwenikweni ndi mawu osyasyalika opanda pake.
Koma kodi mumanenanji pamene msungwana ayamikira tsitsi lanu, kawonekedwe, kapena kumwetulira? Mwinamwake sipakuloŵetsedwa malingaliro oipa. Ndipo posafuna kuwoneka wachikale, achichepere ena amayamikira msungwanayo—ndikusintha nkhaniyo mofulumira. Komabe, chenjerani ndikupereka lingaliro lakuti mumasangalala ndi nkhani yotyasira.
Nthaŵi zina miyezo yokhwima imafunikira. Ena amachita ndi nkhaniyo mwachindunji mwamsanga monga momwe kungathekere. Mwanjirayi amapeŵa kupitiriza mkhalidwe wovuta womwe ulipo kale. Daniel wachichepere amayankha mwachindunji kuti: “Sindiri wokondweretsedwa kukhala ndi bwenzi lalikazi pakali pano.”
Kaŵirikaŵiri kwanenedwa kuti kuchinjiriza kwabwino ndiko kuukira kwabwino. Wofufuza wina anapereka uphungu uwu: “Kuti muthetseretu nkhaniyo, yambani kukambitsirana zachipembedzo.” Ndithudi, ngati mudziŵika kukhala munthu amene nthaŵi zonse amalankhula za zitsimikizo zake zachipembedzo, sikudzakhala kothekera kwenikweni kuti mungakhale chandamale poyamba penipeni. Ndipo ngati winawake alimba mtima kukufikirani, ndemanga yachindunji yonena za zikhulupiriro zanu zachipembedzo ingamuletseretu panthaŵi yomweyo.
Mwatsokalanji, nthaŵi zina achichepere Achikristu amalephera kugwiritsira ntchito chida chabwino koposa chimenechi. Tim wachichepere anati: “Ambirife sitinafune kunena kuti, ‘Wawonatu! Ndine Mkristu, ndipo sindikufuna kuchita zimenezi.’ Tinafuna kulingana ndi onse.” Kachiŵirinso, kokha ngati mulidi wokhutira kuti njira ya Yehova ndiyo yabwino koposa mpamene mudzakhala ndi kulimba mtima kofunikira kuthaŵa tsoka lachisembwere.
Kuthaŵa Msampha!
Komabe, bwanji ngati mosasamala kanthu za zoyesayesa zanu zabwino koposa, kusadziletsako kupitiriza? Eya, talingaliraninso chitsanzo cha mnyamata amene tinamfotokoza kuchiyambi—Yosefe. Genesis 39:6 amatiuza kuti “anali wokoma thupi ndi wokongola” ndipo anakopa mkazi wa mbuye wake, Potifara. Mkaziyo anachita zonse zomwe akanatha kuti amnyenge. Ndipo Baibulo silimasonyeza kuti mkaziyo anali wakawonekedwe koipa kapena kuti mwanjira inayake sanamkondweretse Yosefe. Komabe, iye anakana chikondi cha mkaziyo. Kodi anakhoza motani kuchita zimenezo?
Choyamba, Yosefe anali wochirimika m’zitsimikizo zake. Iye anati: ‘Ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?’ Ngakhale kuti panthaŵiyo kunalibe lamulo lachindunji lolembedwa loletsa kugonana kwa ukwati usanakhale, chikumbumtima chake chimamuuza kuti zimene mkazi wa Potifara anafuna kuchita zinali zoipa. Chikhalirechobe, mkaziyo anaumirira. Mothedwa nzeru, iye anagwira chovala cha mwamunayo namchonderera kuti: “Gona ndi ine.” Yosefe sanataye nthaŵi kuyesa kusintha mkhalidwewo ndi njerengo, ndiponso sanampatse nkhani yonena za makhalidwe. Panthaŵi yomweyo ‘anasiya chofunda chake m’dzanja lake nathaŵa.’—Genesis 39:9-12.
Yosefe anakhoza kuthaŵa mofulumira chifukwa chakuti sanafunikire kusankha chochita. Chosankha chake chinapangidwiratu. Iye anakoda kuvutika ndi zotulukapo za mkwiyo wamkaziyo m’malo mosakondweretsa Yehova. Ndipo zotulukapo zake zinali zowawa; Yosefe anaponyedwa m’ndende! Koma Yehova anadalitsa zoyesayesa zake zakukhala woyera. Pomalizira pake anakhala chiŵalo chotsogolera m’bwalo la Farao ndipo anagwirizanitsidwa ndi banja lake lomwe anasiyana nalo kwanthaŵi yaitali.
Zoyesayesa zanu zakukhala ‘osalakwa ndi owona . . . pakati pa mbadwo wokhotakhota’ zidzadalitsidwa ndi Yehova. (Afilipi 2:15) Mosasamala kanthu za mmene zinthu zingawonekere poyamba, njira yabwino nthaŵi zonse imatulukapo madalitso. Koma muyenera kutsimikiza mtima kukhala woyera monga momwe anachitira Yosefe. Muyenera kukhala woumirira ndi wokhazikika m’zoyesayesa zanu, kulola ‘Ayi wanu kukhala Ayi.’ (Mateyu 5:37) Muyenera kukhala wokonzeka ndi wofunitsitsa kugaŵana ndi ena zitsimikizo zanu zozikidwa pa Baibulo. Ngati muchita zimenezo, ngakhale asungwana olimba mtima kwenikweni adzamvetsetsa—ndipo mwinamwake kuleka kukuvutani!
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka chidziŵitso chonena za mmene asungwana angalakire mkhalidwe wosadziletsa wa anyamata, onani nkhani yakuti “Kodi Ndingampangitse Motani Kuleka Kundivuta?” m’kope la Galamukani! la June 8, 1991.
b Onani mitu 23 ndi 24 ya bukhu la Questions Young People Ask—Answers That Work, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 18]
Kodi mumachita motani ndi mikhalidwe yachikondi yachisembwere?