Chithandizo kwa Omafawo m’Nyengo Yathu Yamakono
MKAZIYO, dokotala iyemwiniyo, anali atangochoka kumene m’chochitika chopweteka koposa. Iye adawona gogo wake wachikazi akufa m’chipinda cha m’chipatala cha odwala mosachiritsika pambuyo pa opaleshoni ya kansa imene “iwo sanaifune konse.”
“Misozi yanga pa maliro awo sinali chifukwa cha imfa yawo, pakuti gogo wanga wachikazi anali atakhala ndi moyo wautali, wokwanira,” dokotalayo analemba motero. “Ndinalira chifukwa cha ululu umene iwo anapirira, ndipo chifukwa cha kusakwaniritsidwa kwa zofuna zawo. Ndinalirira amayi ŵanga ndi ana awo, chifukwa cha lingaliro lawo la kutayikiridwa kwawo ndi kugwiritsidwa mwala.”
Komabe, inu mungafune kudziŵa, ponena za kuthekera kwa kuthandiza munthu wodwala mosachiritsika woteroyo. Dokotalayu akupitiriza kuti:
“Kwakukulukulu, ndinadzilirira: chifukwa cha liwongo lalikulu limene ndinamva pa kusakhoza kuwapulumutsa ku ululu ndi kuzunzika, ndi chifukwa cha kupereŵera kowopsa kumene ndinamva monga dokotala, wosakhoza kuchiritsa, wosakhoza kuchepetsa kuvutika. Pakuti palibe kulikonse m’maphunziro anga kumene ndinaphunzitsidwa kulandirika kwa imfa kapena kumwalira. Utenda unali mdani—woyenera kulimbana naye panthaŵi iriyonse, ndi mphamvu iriyonse yotsirizira. Imfa inali chigonjetso, kulephera; nthenda yalizunzo chikumbutso chosalekeza cha kusoŵa mphamvu kwa dokotala. Chithunzithunzi cha gogo wanga wachikazi wokondedwa chondiyang’ana ndi maso owopsedwa pamene anali pa makina opeperera mu ICU chimandifikirafikira kufikira lerolino.”
Mdzukulu wamkazi wachikondi ameneyu anayambitsa nkhani yocholoŵana yamakhalidwe, yazamankhwala ndi zalamulo imene tsopano ikukambitsiridwa m’makhoti ndi zipatala kuzungulira dziko lonse: Kodi nchiyani chimene chiri chabwino koposa kaamba ka odwala opanda chiyembekezo m’nyengo yathu yopita patsogolo mwaluso lazopangapanga?
Ena ali ndi lingaliro lakuti zirizonse zothekera mwazamankhwala ziyenera kuchitidwa kaamba ka munthu aliyense amene akudwala. Lingaliro limeneli likunenedwa ndi Association of American Physicians and Surgeons kuti: “Thayo la dokotala kwa wodwala wokomoka, wotsiruka, kapena chirema silimadalira pa chiyembekezo cha kuchira. Dokotalayo nthaŵi zonse ayenera kuchitapo kanthu mokomera ubwino wa wodwalayo.” Zimenezi zimatanthauza kupereka mankhwala onse kapena chithandizo chamankhwala chimene chingaperekedwe mothekera. Kodi mukulingalira kuti zimenezi nthaŵi zonse nzabwino koposa kwa munthu amene akudwala kwakukulu?
Kwa anthu ochuluka njirayo imamvekeradi kukhala yoyamikirika. Komabe, m’zaka makumi oŵerengeka apitawo, kuchita ndi mankhwala opititsidwa patsogolo ndi luso lazopangapanga kwadzutsa lingaliro latsopano ndi losiyana. Mu pepala la 1984 losonyeza posinthira lokhala ndi mutu wakuti “Thayo la Dokotala Kwa Odwala Opanda Chiyembekezo,” gulu la madokotala khumi odziŵa linati: “Kutsika m’kupatsidwa mankhwala kwamphamvu kwa wodwala wopanda chiyembekezo kuli koyenera pamene kupatsidwa mankhwala koteroko kukangotalikitsa njira ya kumwalira yovuta ndi yopweteka.” Zaka zisanu pambuyo pake madokotala amodzimodziwo anafalitsa nkhani ya mutu umodzimodziwo imene inatchedwa “Lingaliro Lachiŵiri.” Polingalira vuto limodzimodzilo, iwo ananena mawu omvekera bwino: “Madokotala ochuluka ndi akatswiri azamakhalidwe . . . chifukwa cha chimenecho, anena kuti kuli bwino kuleka kudyetsa ndi kuthirira [madzi] odwala omafa akutiakuti, odwala mosachiritsika, kapena okomoka mwachikhalire.”
Sitinganyalanyaze mawu oterowo kukhala kupeka chabe kapena kukhala nthanangula chabe zimene ziribe chochita ndi ife. Akristu ambiri ayang’anizana ndi zosankha zovuta m’nkhaniyi. Kodi wodwala mopanda chiyembekezo wokondedwayo ayenera kukhalitsidwa moyo ndi makina othandizira kupuma? Kodi kudyetsera m’mitsempha kapena njira zodyetsera zosakhala zachibadwa ziyenera kugwiritsiridwa ntchito kwa wodwala mosachiritsika? Pamene mkhalidwewo uli wopanda chiyembekezo, kodi ndalama zonse za wachibale, kapena za banja lonse, ziyenera kuwonongedwera kulipirira kupatsidwa mankhwala, mwinamwake kophatikizapo kupita kumalo akutali kukalandira chisamaliro chazamankhwala chopititsidwa patsogolo?
Mosakaikira inu mukuzindikira kuti mafunso oterowo sali osavuta kuyankha. Monga momwe mukafunira kuthandiza bwenzi lodwala kapena wokondedwa, ngati munafunikira kuyang’anizana ndi mafunso ameneŵa inu mungafune kudziŵa kuti: ‘Kodi Mkristu ali ndi chitsogozo chotani? Kodi ndimagwero otani amene alipo kaamba ka chithandizo? Chofunika koposa, kodi Malemba amanenanji pankhaniyo?’