Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Nchifukwa Ninji Chiletso Chofika Usiku Panyumba Chiri Chopambanitsa pa Ine?
LEN anakonda kuyenda usiku kwambiri ndi mabwenzi ake. Koma mwamsanga atate ake anadziŵa kuti kuyenda usiku kwa Len sikunali kuseŵera wamba. “Nthaŵi ina ndinagwera m’mavuto aakulu,” akukumbukira tero Len, “kotero kuti sindinaloledwe kutuluka m’chipinda changa kwa milungu iŵiri—kupatulapo nthaŵi yakudya ndi yopita kusukulu. Ndinaletsedwa ngakhale kuyang’ana kunja pazenera! Pamene chilangocho chinatha, ndinapita kokayenda ndi mabwenzi anga mpaka pakati pa usiku. Poloŵa pamsewu wopita panyumba ndi galimoto, ndinawona atate alikhale m’khonde akundiyembekezera . . . ”
Achichepere ambiri samafuna makolo kumawaikira nthaŵi yakufika ndi kuchoka panyumba. Msungwana wina anati: “Pamene ndinasinkhuka, makolo anga anayamba kuika ziletso za mtundu uliwonse pa ine, monga ngati kufika panyumba kusanade kwambiri. Sindinafune zimenezo.” Pamene achichepere otero asonyeza kuipidwa kwawo mwakupanduka, kaŵirikaŵiri zotulukapo zimakhala, osati ufulu wowonjezereka, koma ziletso zokhwimirapo ndi zochulukirapo.
Pamene zolakwa ziri zazing’ono chilango chingangokhala kufika panyumba nthaŵi ikadalipo. Koma ngati zolakwa nzazikulu, wachichepere angamanidwe maubwino akutiakuti, kapena angabindikiritsidwe panyumba kwakanthaŵi, titero kunena kwake. “Utafika usiku kwambiri panyumba Loweruka,” anafotokoza motero msungwana wina, “mwina sungakhozenso kupita kokayenda Loweruka lotsatira.” Ndiyeno pamakhala ‘kubindikiritsidwa’ kwina: suyenera kulandira alendo, foni, ndipo suyenera kuwonerera wailesi yakanema. Koma kwa achichepere ena, chilango choŵaŵa kwambiri ndicho kudzudzulidwa. “Chimakhala chochitika chomvetsa liŵongo chotani nanga!” anadzuma motero mnyamata wina. “Amayamba kufotokoza mmene analiri odera nkhaŵa kwambiri ponena za iweyo. Umadzimva waliŵongo koposa.”
Komabe, kodi sizowona kuti makolo anu amakukondani ndipo ali ndi kuyenera kwakukuuzani kufika panyumba panthaŵi yoyenera? Ndipo pamene simutero, ayenera kukhala otekeseka, odera nkhaŵa, mwina ngakhale kusatuwona tulo. Ndithudi wachichepere yemwe amawakondadi makolo ake ndi wosamala sangafune kuwadetsa nkhaŵa mosayenera chotero. Kodi sikukasonyeza dyera lopambanitsa?
Komabe, achichepere ambiri amaganiza kuti makolo awo awaikira ziletso zosayenera ndi zopambanitsa. “Amapambanitsa, kumandiyesa ngati wazaka khumi ndi zisanu,” anadandaula motero Fred wazaka zakubadwa 18. “Nditangokana zimene amandiuza, pamenepo ndimaloŵa m’vuto ndi atate.” Koma pali njira zabwinopo zochita ndi makolo anu mmalo mwakuwapandukira.
Kodi Nzoyenera Kapena Nzosayenera?
Choyamba, kodi kwenikweni ndimotani mmene ziletso zimenezo ziliri zosayenera? Monga momwe nkhani yapapitapo inasonyezera, mwina makolo anu ali ndi zifukwa zabwino zodera nkhaŵa za chisungiko chanu ndi ubwino.a Kodi Akristu achichepere ena salinso pansi pa ziletso zofanana? Ngati nditero, kodi muli ndi zifukwa zabwino zotani zokaikirira zosankha za makolo anu?
Len wachichepere, wotchulidwa poyamba, sanazindikire kuti atate ake amadera nkhaŵa za ubwino wake. Mukukumbukira kuti anaswa lamulo lakufika msanga panyumba, ndiyeno anapeza atate ake akumuyembekezera m’khonde la nyumba. Kodi njira ya Len yothetsera vutolo inali yotani? Kukulitsa kusamvera kwake. “Pamene galimoto linaloŵa mumsewu wopita panyumba, ndinabisala m’galimotomo kotero kuti Atate asandiwone, ndiyeno ndinauza bwenzi langa kuti tibwerere. Ndinasankha kuchoka panyumba.” Ndipo Len anachokadi panyumba nayamba kuyanjana ndi gulu lopulupudza limene linamchititsa kuloŵa m’chisembwere chakugonana, kuba magalimoto, ndi kumwa mankhwala oledzeretsa. Potsirizira, anaponyedwa m’ndende. Kodi ndinkhani yonkitsa? Mwinamwake. Koma imasonyeza bwino kwambiri kuwona kwa Miyambo 1:32 imene imati: ‘Pakuti kubwerera m’mbuyo kwa achibwana kudzawapha.’
Achichepere ena sangatsutse kwenikweni lingaliro la kufika msanga panyumba, koma amaipidwa ndi chenicheni chakuti akulu awo amawonekera kukhala ndi ufulu wowonjezereka kuwaposa. “Mchimwene wanga wamkulu Mark ankafika panyumba usiku kwambiri pamene anafunira,” anadandaula tero wachichepere wina wotchedwa Patti, “koma sanaletsedwe kuyenda. Ineyo—nditafika panyumba mochedwako pang’ono, basi zonse zithera pompo! Zimandinyansa zimenezo.” Kuli kosavuta kuwona chifukwa chake mkhalidwe wotero ungakukwiitseni. Koma musanadandaule kuti “zimandinyansa!” tapendani lamulo la Baibulo lamakhalidwe abwino lotchulidwa pa Agalatiya 6:4, 5 lomwe limati: ‘Koma yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, sichifukwa cha wina. Pakuti yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.’
Inuyo ndinu munthu wina. Ndipo chenicheni chakuti mkulu wanu ali ndi maubwino akutiakuti sichimakuyeneretsani kukhala ndi maubwino ofananawo. Mwachiwonekere mkulu wanu anasonyeza kudalirika kwake mkupita kwa nthaŵi. Nanunso mudzatero. Ndiponso, kodi simumaipidwa pamene makolo anu akuyerekezerani ndi mchimwene wanu wamkulu kapena mchemwali? Nanga muchitanso bwanji zofanana mwakuyerekezera maubwino anu osiyana? M’bukhu lake lakuti “After All We’ve Done for Them,” Dr. Louis Fine anati: “Kaŵirikaŵiri makolo amachita ndi ana awo ndi kuwalanga mosiyana. Mwachiwonekere zimenezi ziri chifukwa chakuti amazindikira kuti ana awo ali anthu osiyana okhala ndi zosoŵa ndi maluso osiyana ndipo ayenera kutengedwa mosiyana.”
Komabe, nthaŵi zina achichepere amadzimva kuti amavutikira zolakwa za akulu awo. “Kokha chifukwa chakuti mchemwali wanga anatenga galimoto kupita kokayenda nabwerako usiku kwambiri, basi pamenepo sindimaloledwa kufika usiku. Sindimapatsidwa ngakhale mpata wakusonyeza mmene ineyo ndingachitire!” Ngakhale nditero, mkhalidwe umenewu sungakhale wosalungama kwenikweni monga momwe ukuwonekeramu. Makolo anu tsopano ngachikulirepo ndi anzerupo koposa mmene analiri polera mchimwene kapena mchemwali wanu. Posafuna kubwereza kulakwa kwawo, angakhale oletsa kwa inu kuposa momwe analiri kwa iye.
Koma kodi nchifukwa ninji muyenera kulangidwa kaamba kobwera mochedwa pang’ono? Kunena zowona, kuletsedwa kuyenda sikumasangalatsa. Choncho inuyo nthaŵi zonse mumakhala wosamala kuti musabwerezenso kufika mochedwa panyumba. Marcus wachichepere akunena kuti: “Ndinalangidwa nthaŵi zambiri. . . . Ngati simunalangidwepo, simudzaphunzira kalikonse.” Monga momwe Baibulo limanenera, “wosunga mwambo ali m’njira ya moyo.”—Miyambo 10:17.
Makolo Otetezera Mopambanitsa
Kunena zowona, nthaŵi zina kumawonekera kuti chilango chimaposa “upandu” wochitidwawo. Makolo angakhale otetezera mopambanitsa ndipo mwinamwake kufuna zinthu zochuluka. Komabe, kulankhulana kwabwino, nthaŵi zambiri kumathetsa mavuto poyamba. Ngati mudziŵitsa makolo anu kumene mukupita, zimene mudzakhala mukuchita, amene mudzakhala naye, ndi pamene mudzabwerako, mwachiwonekere adzakhala ofunitsitsa kukupatsani ufulu wakutiwakuti. Ngati muwona kuti achita mopambanitsa, yesani kuwafikira “pa nthaŵi yake”—mwina atakhazikika ndipo atapuma. (Miyambo 25:11) Zindikirani nkhaŵa zawo. Asonyezeni kuti mumawakonda ndipo ndinu wofunitsitsa kugwirizana nawo. Athandizeni kuzindikira kuti kupeza ufulu wowonjezereka kuli mbali yakukula kwanu.
“Muyeneranso kuwadziŵitsa mmene mkhalidwe uliri,” akutero msungwana wina. “Kaŵirikaŵiri, mutawafotokozera chifukwa chimene simudzafikira msanga panyumba tsiku lina, amamvetsera.” Mwakukambitsirana zinthuzo mwauchikulire, mumawasonyeza bwino lomwe makolo anu kuti ndinu wokhulupirika—munthu yemwe angadaliridwe. Ngati makolo anu akukaikirabe, mwina mukhoza kuwapempha kukupatsani mpata.
Bwanji ngati akupatsani chilolezo? Pamenepo ‘Inde wanu akhale Inde,’ ndipo muyenera kufika panyumba panthaŵi yabwino! (Mateyu 5:37) Zowona, ngakhale makonzedwe opangidwa bwino koposa angasinthe. (Yerekezerani ndi Yakobo 4:13, 14.) Pakhoza kubuka chochitika chamwadzidzidzi kapena kusintha. Zitatero, imbirani foni kunyumba ngati kutheka, ndipo adziŵitseni makolo anu zimene zikuchitika. “Amayi atangodziŵa kumene ndiri ndikuti ndikubwera, zimawakhalira bwino,” anatero msungwana wina.
Kukhala ndi mbiri yabwino kuli mbali ina yofunika kwambiri. Miyambo 20:11 imati: ‘Ngakhale mwana adziŵika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.’ Mutasonyeza chitsanzo chabwino chakumvera ndi khalidwe lolungama, makolo anu sangadandaule ngati nthaŵi ina mwachedwako kufika panyumba. Ndithudi, ngakhale kuti Yesu anali ndi mbiri ya khalidwe langwiro, makolo ake ‘anada nkhaŵa’ pamene iye anasoŵa. (Luka 2:48) Choncho musadabwe ngati makolo anu akwiya—mwina kukwiya kwambiri poyamba moti nkusakulolani kupereka zifukwa zimene mwachedwera!
Miyambo 29:11 imati: ‘Chitsiru chivumbulutsa mkwiyo wake wonse; koma wanzeru auletsa nautontholetsa.’ Tayembekezerani kufikira mkwiyo wawo utatha. Patakhalanso bata, perekani zifukwa zanu. Koma ‘lankhulani zowona.’ (Aefeso 4:25) Osapereka zifukwa zosakhulupirika; zimenezo zingangosonyeza kuti sindinu wodalirika. Ngati simunasamale kapena munaiŵala, pepesani mowona mtima, ndipo khalani ofunitsitsa kulandira chilango. Mwinamwake makolo anu sadzapeza chifukwa chokulitsira nkhaniyo. Komano, angaganize kuti ayenera kupereka ziletso zina, ndipo inu mudzangofunikira kuwamvera kuti adzikukhulupirirani.
Ziletso zakufika usiku kwambiri panyumba zingakhale zovutitsa, koma siziri zankhanza kapena zilango zopambanitsa. Zipirireni. Ngati mugwirizana ndi makolo anu ndi kupeŵa mzimu wachipanduko, iwo mwina angagamule kuti ayenera kupepusako ziletsozo ndi kukupatsani ufulu wokulirapo.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Achichepere Akufunsa . . . Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kufika Msanga Panyumba?” m’kope la Galamukani! wa May 8, 1992.
[Chithunzi patsamba 17]
Kaŵirikaŵiri kupandukira makolo anu kumachepetsa ufulu wanu