Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 1/8 tsamba 25-27
  • Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kumvera Makolo Anga?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kumvera Makolo Anga?
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Amapanduka
  • Chifukwa Chake Chipanduko Chili Kupusa
  • Mtengo Waukulu wa “Ufulu”
  • Kukhala ndi Moyo Wapaŵiri—Kulekeranji?
    Galamukani!—1994
  • Achichepere—Kodi Mukulondola Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kodi Nchifukwa Ninji Chiletso Chofika Usiku Panyumba Chiri Chopambanitsa pa Ine?
    Galamukani!—1992
  • N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Anandiikira Malamulo Ambirimbiri?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 1/8 tsamba 25-27

Achichepere Akufunsa Kuti

Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kumvera Makolo Anga?

STAN analeredwa ndi makolo owopa Mulungu. Komano pausinkhu wa zaka 16, anapanduka. Stan akufotokoza kuti: “Ndinafuna kudziŵana ndi anthu ndi kulandiridwa nawo. Ndinafuna kukhala ndi zinthu zonse zimene anthu ena ali nazo.” Cholinga cha Stan cha kukwaniritsa zonulirapo zimenezi chinali cha kudzakhala wamalonda a anamgoneka. Motero, iye anakakamizika kunena bodza ponena za mayendedwe ake ndi ndalama zonse zimene anali kubweretsa kunyumba. “Chikumbumtima changa chinali chitafa,” Stan akukumbukira motero.

John anabatizidwa monga Mkristu pausinkhu wa zaka 11. “Koma kwenikweni choonadi sichinali mumtima mwanga,” iye akuvomereza motero. “Ndinatero chifukwa chakuti banja langa linafuna kuti nditero. Pamene ndinaloŵa sukulu ya sekondale, ndinayamba kukhala wosalamulirika. Nazonso nyimbo za rock zinandiyambukira moipa. Ndinaloŵa m’maseŵero a surfing ndi kuyamba kuthera nthaŵi yochuluka kugombe ndi achichepere amene sanali kutsogozedwa ndi malamulo amkhalidwe a Baibulo. Kumeneko kunali anamgoneka ochuluka.” Pasanapite nthaŵi yaitali iye anasamuka panyumba pamakolo ake ndi kukutenga njira ya moyo umene unali wosiyana ndi zonse zimene anaphunzitsidwa.

Chifukwa Chake Amapanduka

Nkwachibadwa kuti achichepere ayese kufika pamene angathere ndi kukulitsa mlingo wa kudziimira. Koma khalidwe lopanduka, lachiwawa, ndi lodziwononga ndilo kanthu kena kosiyana kotheratu. Kodi nchiyani chimene chimalisonkhezera? Zifukwa zake nzambiri ndiponso zosiyanasiyana. “Pamene uli wachichepere,” akufotokoza motero John, “umafunafuna zosangalatsa. Umafuna kukondwera.” Komabe, chifukwa cha kusoŵa chidziŵitso m’moyo, nthaŵi zonse achichepere samasankha zinthu mwanzeru. (Ahebri 5:14) Chifukwa chake makolo anzeru amaikira ana awo ziletso—zoletsa zimene achichepere ena amatsutsa kwambiri.

Nzomvetsa chisoni kuti, achichepere ena akana chiphunzitso chimene anapatsidwa ndi makolo awo owopa Mulungu. (Aefeso 6:1-4) Yesu anati Chikristu chikakhala njira ya moyo ‘yopapatiza’ ndi ‘yochepa.’ (Mateyu 7:13, 14) Chotero achichepere Achikristu kaŵirikaŵiri samachita zinthu zimene akusukulu anzawo amachita. Ochuluka amamvera ziletsozo, akumazindikira kuti malamulo a Mulungu kwenikweni ali osalemetsa. (1 Yohane 5:3) Zoonadi, malamulo ameneŵa amatetezera achichepere pa mavuto onga kukhala ndi mimba za pathengo, anamgoneka, matenda opatsirana mwakugonana. (1 Akorinto 6:9, 10) Koma achichepere ena samafuna kulingalira mwanjira imeneyo; amalingalira kuti malamulo a Baibulo amapanikiza moyo wawo.

Kuipidwa kungakhaledi kwakukulu, ngati wachichepere alingalira kuti makolo ake ngaliuma kwambiri pankhani za chilango, maseŵero, ndi kusanguluka. “Ndiganiza kuti makolo anga amatikaniza kwambiri,” anadandaula motero msungwana wina wachichepere. Zoona, kungakhale kogwiritsa mwala pamene simuloledwa kuchita zinthu zimene makolo ena Achikristu amaloleza. (Akolose 3:21) Achichepere ena amasonyeza kugwiritsidwa mwala kwawo mwa kusamvera.

Komanso, achichepere ena amapanduka chifukwa chakuti makolo awo samasonyeza ulemu uliwonse pa malamulo amkhalidwe aumulungu. “Atate anali chidakwa,” akukumbukira motero John. “Iwo ndi Amayi ankakangana chifukwa chakuti atate anali kumwa kwambiri. Tinasamuka kangapo kuti tiwathaŵe.” Zidakwa ndi omwerekera ndi zinthu zina sangasamalire konse moyenera zosoŵa za ana awo. M’mabanja otero, kutukwanizana ndi kunyazitsana kungakhale mkhalidwe umene wachichepereyo amaona tsiku lililonse.

Achichepere ena amapanduka chifukwa chakuti makolo awo, kwenikweni, amawasiya ali okha kapena kuwanyalanyaza. Chipanduko chingaonekere kukhala njira yopezera chisamaliro cha makolo awo—kapena kuwapweteketsa mtima. “Malinga ndi zimene ndikukumbukira, makolo anga sankapezeka panyumba,” akutero msungwana wina wachichepere wotchedwa Taylor wa m’banja lina lolemera. “Mukudziŵa, ndinali mwana mmodzi yekha, ndipo popeza kuti makolo anga sankapezekapezeka, nthaŵi zonse ankandisiyira ndalama zambiri.” Posoŵa chiyang’aniro, Taylor anayamba kupita ku makalabu ausiku ndi kumaledzera. Makolo ake sanazindikire kuti iyeyo anali ndi vuto kufikira pamene anagwidwa chifukwa cha kuyendetsa galimoto ataledzera.

Ndiponso, pali mkhalidwe wosonyezedwa ndi mtumwi Paulo pamene anafunsa gulu lina la Akristu kuti: “Munathamanga bwino; anakuletsani ndani kuti musamvere choonadi?” (Agalatiya 5:7) Kaŵirikaŵiri mayanjano oipa ndiwo amene amachititsa zimenezo. (1 Akorinto 15:33) “Ndinadziloŵetsa m’mayanjano oipa,” akutero wachichepere wina wotchedwa Elizabeth. Iye akuvomereza kuti chifukwa cha chitsenderezo cha ausinkhu wake, “anayamba kusuta fodya ndi kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka.” Akuwonjezera kuti: “Chisembwere chinali chinthu cha masiku onse.”

Chifukwa Chake Chipanduko Chili Kupusa

Mwina mwake nanunso muli mumkhalidwe umodzimodziwo umene ukuonekera kukhala wogwiritsa mwala—kapena wotsenderezadi. Kunyalanyaza makolo anu ndi kungochita zimene mukufuna kuchita kungakhale kokopa kwa inu. Koma monga momwe munthu wolungamayo Yobu anachenjezedwera, ‘chenjerani, mkwiyo ungakunyengeni muchite [machitidwe a] mnyozo. Chenjerani, musalunjike kumphulupulu.’—Yobu 36:18-21.

Khalidwe lonyoza, losalamulirika lingachititse makolo anu kukhudziŵa mwanjira ina, koma mwachionekere kudzakhala kosakondweretsa. Mwina mwake adzangokuikirani ziletso zowonjezereka. Ndiponso, khalidwe lovulaza lidzachititsa makolo anu kuwawidwa mtima kwambiri. (Miyambo 10:1) Kodi chimenecho nchikondi? Kodi zidzaongolera mkhalidwe wanu? Njira yanzeru kwambiri ndiyo kulankhula nawo nkhaniyo ngati mukulingalira kuti muli ndi madandaulo oona.a Mwina iwo angafune kusintha mmene amachitira nanu.

Nkhani ina yoilingalira ndiyo yonena za chiyambukiro cha zochita zanu pa Mulungu. ‘Pa Mulungu?’ mungafunse motero. Inde, chifukwa chakuti kupandukira makolo anu ndiko kupandukira Mulungu mwiniyo, popeza kuti iye ndiye amene amakulamulani kulemekeza makolo anu. (Aefeso 6:2) Kodi kusamvera kotero kumammvetsa bwanji Mulungu? Baibulo limati ponena za mtundu wa Israyeli: “Kaŵirikaŵiri nanga anapikisana ndi Iye kuchigwako.” Ndi chiyambukiro chotani? “Nammvetsa [Mulungu] chisoni.” (Salmo 78:40) Zoonadi, mungakwiye ndi makolo anu, mukumalingalira kuti ngoletsa kwambiri. Koma kodi mumafunadi kumvetsa chisoni mtima wa Yehova Mulungu—amene amakukondani ndi amene akufuna kuti mukhale ndi moyo kosatha?—Yohane 17:3; 1 Timoteo 2:4.

Mtengo Waukulu wa “Ufulu”

Pamenepa, ndi chifukwa chabwino, tifunikira kumvetsera kwa Atate wathu wachikondi wakumwamba. Musapusitsidwe ndi malonjezo onyenga a “ufulu.” (Yerekezerani ndi 2 Petro 2:19.) Kungaonekere ngati kuti achichepere ena amatha kuzemba chilango cha khalidwe losadzisungira. Koma wamasalmo anachenjeza kuti: “Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa, usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama. Pakuti adzawamweta msanga monga udzu, ndipo adzafota monga msipu wauŵisi.” (Salmo 37:1, 2) Achichepere amene amapanduka kaŵirikaŵiri amalipira mtengo waukulu kwambiri kaamba ka wotchedwa kuti ufulu wawo. Baibulo pa Agalatiya 6:7 limati: “Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.”

Lingalirani za Stan, amene watchulidwa poyambirirapo. Monga momwe anayembekezerera, anakhaladi wokondedwa ndi mabwenzi ake oipawo. “Ndinamva kukhala wolandiridwa,” iye akukumbukira motero. Komabe, mofulumira zinthu zinayamba kuipa. Iye akuti: “Ndawomberedwapo mfuti, kumangidwa, ndipo tsopano ndikumka kundende. Ndipo chinthu chokha chimene ndikudzifunsa nchakuti, ‘Kodi phindu lake nchiyani?’”

Bwanji za kufunafuna “ufulu” kwa John? Pambuyo pa kugwidwa chifukwa cha kupezeka ndi anamgoneka, anathamangitsidwa mumpingo Wachikristu. Kuyambira pamenepo iye anatitimiradi m’khalidwe loipa. “Ndinkaba galimoto kuti ndipeze ndalama,” akuulula motero John. “Ndinali wachiwawa kwambiri.” John anapeza ndalama zambiri ndi machitachita ake aupanduwo. Komano akukumbukira kuti: “Ndinkangoziwawanya. Kuchuluka kwa anamgoneka amene tinkagwiritsira ntchito nkosakhulupiririka.” Ndipo pamene John sanali kumenyana ndi ena, kuba, kapena kuledzera, anali kuthaŵa apolisi. “Ndagwidwa pafupifupi nthaŵi 50. Kaŵirikaŵiri sanali kundipeza ndi mlandu, koma panthaŵi ina ndinamangidwa kwa chaka chonse.” Inde, m’malo mwa kukhala munthu waufulu, John anatitimira mu “zakuya za Satana.”—Chivumbulutso 2:24.

Zinali chimodzimodzinso kwa Elizabeth. Kumasuka kwake ndi mabwenzi adziko potsirizira pake kunamloŵetsa m’ndende. Iye akuulula kuti: “Ndinakhaladi ndi pathupi—ndipo chifukwa cha kugwiritsira ntchito kwanga anamgoneka ndinapita padera. Anamgoneka anali moyo wanga—ndinkakhalira moyo pakuchangamuka ndi anamgoneka. Potsirizira pake ndinathamangitsidwa m’nyumba yanga. Sindikanatha kumka kwathu, ndipo ndinachitadi manyazi kupempha Yehova thandizo.”

Zitsanzo zambiri zotere za achichepere amene akana malamulo amkhalidwe aumulungu ndi kusauka ndi zotulukapo zatsoka zingaperekedwe. Baibulo limachenjeza kuti: “Msewu umene uganiza kuti ngwolondola ungakutsogolere ku imfa.” (Miyambo 14:12, Today’s English Version) Pamenepa, chinthu chanzeru kuchita ndicho kuyesa kugwirizana ndi makolo anu, kukambitsirana—m’malo mwa kupandukira—ziletso zilizonse zimene mukulingalira kuti nzosayenera.

Komabe, bwanji nanga kwa achichepere amene chidziŵitso chino chafika mochedwa kwambiri kwa iwo, achichepere amene aloŵa kale m’khalidwe loipa? Kodi pali njira ina imene iwo angakonzere zinthu ndi makolo awo—ndi Mulungu? Nkhani yathu yotsatira idzayankha mafunso ameneŵa.

[Mawu a M’munsi]

a Nkhani zambiri zapereka chidziŵitso chothandiza pankhani imeneyi. Mwachitsanzo, onani nkhani za “Achichepere Akufunsa Kuti . . . ” m’makope athu a Galamukani! a November 8, 1985, August 8, 1992, ndi November 8, 1992.

[Chithunzi patsamba 26]

Kupandukira makolo anu kungakupatseni “ufulu” kwambiri, koma kodi mwalingalirapo za zotulukapo zake?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena