Kuchotsedwa kwa Mbola ya Imfa
SIKWACHILENDO kuŵerenga za imfa monga yachibadwa kapena yozoloŵereka. Ndithudi siyachilendo, mogwirizana ndi cholembedwa cha Baibulo. Imfa ndimdani wochokera kuuchimo. “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa,” limatero Baibulo pa Aroma 5:12.
Popeza kuti imfa siinali chifuniro cha Mulungu pa mtundu wa anthu, iye mwachikondi wapereka njira yotulukira. Mwakulola Mwana wake kutifera, anapereka dipo lolinganira lakuchotsa chilango cha imfa. (Mateyu 20:28; 1 Yohane 2:2) Iye walonjezanso paradaiso wapadziko lapansi ndi boma latsopano kotheratu lodzalamulira pa anthu onse. Bomalo lidzafafaniza kotheratu ziyambukiro zauchimo ndi imfa. (Luka 18:30) Baibulo limati pa Chivumbulutso 21:3, 4: “Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; Ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; Zoyambazo zapita.” Koma bwanji ponena za awo amene anafa kale?
Iwo ali ndi chiyembekezo chachiukiriro—chiyembekezo chakukhalanso ndi moyo monga anthu padziko lapansi Laparadaiso, ndi matupi angwiro athanzi ndi maganizo. Inde, “ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) Amene anatumidwa ndi Mulungu kudzawombola mtundu wa anthu, Yesu Kristu, akutitsimikiziranso kuti: “Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wakuyang’ana Mwana, ndi kukhulupirira iye, akhale nawo moyo wosatha; ndipo ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.”—Yohane 6:40.
Chiri chiyembekezo chachiukiriro chimenechi chimene chimalimbikitsa ambiri amene afedwa okondedwa awo. Amazindikira kuti okondedwa awowo “agona [chabe] tulo mu imfa,” chotero iwo “samalira mofanana ndi anthu enawo, amene alibe chiyembekezo.” (1 Atesalonika 4:13, The New English Bible) Iwo amayang’ana mtsogolo kudzayanjananso nawo mwachisangalalo m’dongosolo limenelo la zinthu latsopano lolonjezedwa ndi Mulungu. Amakhulupirira Mulungu amene amapereka chitonthozo ndi chiyembekezo.—Aroma 15:4, 13; 2 Akorinto 1:3; 2 Atesalonika 2:16.
Ndicho chifukwa chake mautumiki amaliro a Mboni za Yehova amakhala osiyana ndi ena. Kuti apeze chiyanjo cha Mulungu, Mboni zimapeŵa machitachita alionse amene amawombana ndi Mawu ake, Baibulo. Miyambo ndi zinthu zovala zozikidwa pazikhulupiriro zosaphunzitsidwa m’Baibulo zimapeŵedwa. Pamene zimalambira Mulungu wowona yekha, Yehova, zimakana kupereka ulemu wakulambira woterowo kwa akufa awo. Ndipo sizimadzitamandira ndi chuma kapena malo apamwamba, popeza zimadziŵa kuti kutero sikumamkondweretsa Mulungu. (1 Yohane 2:16) Maliro awo amakhala osacholoŵana ndi olemekezeka ndipo amathandiza kutonthoza mitima ya ofedwawo. Nkhani imakambidwa kukumbukira malemu, kupereka chiyembekezo chopezeka m’Baibulo. Zimalira, koma osati mopambanitsa.
Mboni za Yehova zimadziŵa kuti posachedwapa “mdani wotsiriza, . . . imfa” adzachotsedwa. Ndiyeno mawu otsatiraŵa adzakwaniritsidwa: “Imfayo yamezedwa m’chigonjetso. Imfawe, chigonjetso chako chiri kuti? Imfawe, mbola yako iri kuti.”—1 Akorinto 15:26, 54, 55.