Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 11/15 tsamba 4-7
  • “Mdani Wotsiriza” Adzagonjetsedwa!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Mdani Wotsiriza” Adzagonjetsedwa!
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Dziŵani Mdani Wanu
  • Kuchita ndi Imfa ya Wokondedwa
  • Kugonjetsedwa kwa Imfa
  • Kuchotsedwa kwa Mbola ya Imfa
    Galamukani!—1992
  • “Imfayo Yamezedwa M’chigonjetso”
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kodi Imfa Idzagonjetsedwa Bwanji?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
  • Musataye Mtima Ngati Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Wamwalira
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 11/15 tsamba 4-7

“Mdani Wotsiriza” Adzagonjetsedwa!

PAMENE munali mwana, mungakhale munali kuwopa mdima. Nkhani zowopsa ndipo ngakhale nthano zina zingakhale zinakudetsani nkhaŵa. Kunali kotonthoza chotani nanga pamene amayi kapena atate anu anasiya nyale ikuyaka pamene munali kuyesa kugona tulo!

Mofananamo imfa imawopsa ambiri. Komabe, sifunikira kutero. Chifukwa ninji? Chifukwa cha zimene imfa ili kwenikweni.

Dziŵani Mdani Wanu

Mfumu yanzeru Solomo ya Israyeli wakale inati: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Malinga ndi lingaliro louziridwa ndi Mulungu limeneli lopezeka m’Baibulo lanu, imfa yangokhala chosiyana ndi moyo. Akufa sazindikira kalikonse.

Akumatchula imfa mwafanizo, mtumwi Wachikristu Paulo akulemba kuti: “Imfawe, chigonjetso chako chili kuti? Imfawe, mbola yako ili kuti?” Kodi mbola imene imadzetsa imfa nchiyani? Paulo akuti: “Mbola ya imfa ndiyo uchimo.” (1 Akorinto 15:55, 56; Hoseya 13:14) Pamenepo, kodi magwero a mbola yakupha imeneyi nchiyani? Pamalo ena m’Malemba, Paulo akuti: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Mtumwiyo sakusiya chikayikiro chilichonse ponena za “munthu mmodzi” ameneyo pamene akuti: “Mwa Adamu onse amwalira.” (1 Akorinto 15:22) Inde, chifukwa cha kusamvera kwa kholo lathu loyambirira, Adamu, tonsefe timayambukiridwa ndi mbola ya imfa.​—Genesis 3:1-19.

Ngati tili ndi thanzi labwino ndi banja lachikondi m’mikhalidwe yabwino, palibe aliyense wa ife angasankhe kufa. Komabe, monga momwe Baibulo limasonyezera, “nthaŵi ndi zochitika zosaonedweratu” zingatilande moyo. (Mlaliki 9:11, NW) Kwenikweni, sitidziŵa zimene zidzachitikira moyo wathu maŵa. (Yakobo 4:14) Chinthu chimodzi nchotsimikizirika​—tonsefe tinalandira choloŵa cha uchimo ndi imfa. Chotero, imfa imatilondalonda ndi kukantha monga mdani.

Kuchita ndi Imfa ya Wokondedwa

Imfa imakhala mdani makamaka pamene ikantha wokondedwa. “Zidzakuipirani kwambiri,” anatero mkazi wodwala nthenda yosachiritsika kwa mwamuna wake poganiza za imfa yake. Kodi nchifukwa ninji ananena zimenezo? Chifukwa Baibulo limati: “Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda [a anthu onse] ulikupitako.” (Mlaliki 9:10) Akufa samavutikanso. Koma chisoni chimakhala pa achibale ndi mabwenzi otsala. Kodi pali chilichonse chimene chingachitidwe ponena za kuvutika kotero?

Masamba a Mawu a Mulungu, Baibulo, ali ndi mawu ambiri a chitonthozo. Mwachitsanzo, kuŵerenga ndi kusinkhasinkha za masalmo kulidi ena a magwero a chitonthozo. Otonthoza kwambiridi, ali mawu onga aŵa: “Wolemekezeka [Yehova, NW], tsiku ndi tsiku atisenzera katundu, ndiye Mulungu wa chipulumutso chathu.”​—Salmo 68:19.

Magwero ena a chitonthozo ndiwo mpingo Wachikristu. M’zaka za zana loyamba C.E., mtumwi Paulo analemba kuti: “Chitira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu. Koma ngati wamasiye wina ali nawo ana kapena adzukulu [amene angamsamalire mwakuthupi], ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m’banja lawo, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu. Asaŵerengedwe wamasiye ngati sanafikire zaka makumi asanu ndi limodzi, atakhala mkazi wa mwamuna mmodzi, wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.” (1 Timoteo 5:3, 4, 9, 10) Mofananamo Mboni za Yehova lerolino zimathandiza ndi kutonthoza okhulupirira anzawo otero.

Kaŵirikaŵiri kusintha kwakukulu koposa kumene woferedwayo ayenera kuchita nkwamaganizo. “Ndinali kumkonda kwambiri mkazi wanga,” analemba motero mwamuna wina amene mnzake wamuukwati anafa zaka ziŵiri kumbuyoko. “Chimenechi nchochitika chomvetsa chisoni koposa m’moyo wanga, ndipo ndimapeza vuto kuchipirira.” Munthu amene wakhala wokwatira kwa nthaŵi yakutiyakuti wakhala ndi phande m’zochitika za moyo wa mwamunayo kapena mkaziyo muunansi waumunthu wathithithi koposa. Pamene mnzake wamuukwati afa, wotsalayo mwachibadwa amakhala wotayikiridwa kwambiri. Kodi ameneyo angatembenukire kwa yani kaamba ka chithandizo?

M’mikhalidwe yotero, atsamwali abwino Achikristu angakhale omangirira. “Bwenzi lowona limakonda nthaŵi zonse, ndipo ndimbale wobadwira kukuthandiza pamene pali tsoka,” umatero mwambi wanzeru. (Miyambo 17:17, NW) Mkazi wamasiye kapena mwamuna wamasiye amafunikira chithandizo​—mabwenzi amene amapereka chichirikizo chenicheni. Mabwenzi anzeru amalimbikitsa wachisoniyo kuti alankhule, ngakhale ngati kuteroko kumadzetsa misozi. Mwinamwake Mkristu amene anavutikapo ndi ululu ndi kusweka mtima kwa kutayikiridwa ndi mnzake wamuukwati angapereke chithandizo chokoma mtima. “Lankhulani motonthoza kwa opsinjika,” limalangiza motero Baibulo. (1 Atesalonika 5:14, NW) Koma kumbukirani kuti akazi amasiye ndi amuna amasiye amalakalaka anzawo amuukwati. Nchifukwa chake, oferedwawo ayenera kuululira ena zakukhosi kokha m’mikhalidwe imene imakhozetsa onse kusunga khalidwe loyera.​—1 Petro 2:12.

Mankhwala abwino koposa a ululu umene imfa imadzetsa ndiwo kukhala wotanganitsidwa kuthandiza ena​—chinthu chovuta kwa awo amene amaganiza kuti ndiwo afunikira chithandizo! Panopa mpamene kupanda dyera kumachita mbali yaikulu. Kuchitira zinthu ena mopanda dyera kumathandiza kuthetsa chisoni ndi kuusa moyo, pakuti Yesu anati: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

Kugonjetsedwa kwa Imfa

Kuluma kwa njuchi kungakhale kopweteka kwambiri, ngakhale kwakupha. Komabe, kaŵirikaŵiri kuchotsa mbola ya kachilomboko m’khungu lanu kudzathandiza kudzetsa mpumulo. Koma kodi pali ziyembekezo zotani za mpumulo ku mbola ya imfa?

Atafotokoza kuti uchimo ndiwo mbola ya imfa, Paulo akufuula kuti: “Ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Kristu.” (1 Akorinto 15:57) Kodi ndimotani mmene kugonjetsedwa kwa imfa kumaloŵetseramo Kristu? Yesu anasonyeza kuti zimenezi zili choncho pamene ananena za iye mwini kuti: “Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Inde, kwa awo osonyeza chikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, ndi nsembe ya dipo imene Yehova wapereka kupyolera mwa iye, imfa ya choloŵa yochokera kwa Adamu sidzawatenga kwa nthaŵi yonse.​—Yohane 3:16.

Mawu a Yesu otsatirawa alidi osangalatsa: “Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.”​—Yohane 5:28, 29.

Zaka mazana ambiri pasadakhale, mneneri wa Mulungu Yesaya anali atalosera kuti: “Iye [Yehova Mulungu] wameza imfa ku nthaŵi yonse; ndipo [Mfumu Ambuye Yehova, NW] adzapukuta misozi pa nkhope zonse.” (Yesaya 25:8) Ndiponso, pa Chivumbulutso 21:4, Baibulo limapereka chiyembekezo chabwino koposa ichi: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” Polimbikitsidwa ndi chiyembekezo cha Baibulo chimenechi cha awo ogona mu imfa, oferedwa sayenera ‘kulira monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.’​—1 Atesalonika 4:13.

Yesani kuona mwamaganizo anu zimene Mulungu wasungira mtundu wa anthu, monga momwe zavumbulidwira m’Baibulo. “Chisautso chachikulu” chomayandikiracho chimatanthauza chiwonongeko cha dongosolo loipa la zinthu lilipoli. (Chivumbulutso 7:14) Awo otsatira chipembedzo chonyenga awonongedwa. Madongosolo adyera andale ndi amalonda osonkhezera njala ndi nkhondo apita. Yesu Kristu akuponyera m’phompho Satana Mdyerekezi, amene wachititsa imfa zochuluka za anthu. Ndiyeno Kristu akuyamba Ulamuliro wake wa Zaka Chikwi, mmene akugwiritsira ntchito mtengo wa nsembe ya dipo pa mtundu wa anthu. Akufa abwerera kumoyo m’chiukiriro choyembekezeredwacho, ndipo kuunika kwa Mawu a Mulungu kukuŵala kwambiri kwakuti malingaliro a kukhulupirira malaulo ponena za imfa, mdani wa mtundu wa anthu, kulibenso. Onse okhala ndi moyo panthaŵiyo ali ndi mpata wa kuphunzira za njira za Mulungu ndi kutsatira miyezo yake yolungama.​—Miyambo 4:18; Machitidwe 24:15; Ahebri 2:14, 15; Chivumbulutso 18:4-8; 19:19-21; 20:1-3.

‘Pomwepo pali chimaliziro,’ akutero Paulo, ‘pamene [Kristu Yesu] apereka ufumu kwa Mulungu, Atate wake. Pakuti ayenera kuchita ufumu kufikira [Mulungu] ataika adani onse pansi pa mapazi ake. Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.’ (1 Akorinto 15:24-26) Kupunduka kulikonse kochititsidwa ndi uchimo wa Adamu kulibenso. Chiyeso chomalizira chichitika, ndipo okonda Mulungu akuchipyola mokhulupirika. (Chivumbulutso 20:4-10) Pokhala atabwezeretsedwa kuungwiro, anthu omvera ameneŵa akukhala ndi moyo, osati chabe kwa zaka makumi asanu ndi aŵiri kapena ngakhale kwa zaka zana limodzi ndi khumi, koma kosatha. Ndimphatso yochokera kwa Mulungu yotani nanga yodzera mwa Mwana wake wokondedwa!​—Aroma 6:23.

Nangano, kodi mungakhale ndi moyo kwautali wotani? Moyo wanu ukhoza kupitirizabe kwamuyaya. Pamene muli ndi moyo mu “nthaŵi ya chimaliziro” ya dzikoli, mungathe kukhalabe ndi moyo osafa konse. (Danieli 12:4; Yohane 11:25, 26; 17:3) Ngati muchita chifuniro cha Mulungu, mungakhoze kukhala ndi moyo mpaka kuloŵa m’dziko latsopano lolonjezedwa la Mulungu.​—2 Petro 3:13.

Komabe, ngati muli wokalamba, mufunikira mowona mtima kulingalira za kuthekera kwa kumwalira. Ndithudi, chiyembekezo cha chiukiriro chimadzetsa chimwemwe. Koma mungafune kudziŵa mmene Yehova adzakonzera moyo wabanja m’dongosolo latsopano la zinthu limenelo. Musade nkhaŵa ndi nkhani zotero, pakuti Yehova adzatsimikizira kuti awo okhulupirika kosatha kwa iye apeza chimwemwe chosatha.

Pamene “masiku otsiriza” ovuta ameneŵa a dongosolo loipa la Satana akufika kumapeto ake, musalole kuwopa imfa kukulandani mwaŵi wanu wa kutumikira Yehova tsopano lino. (2 Timoteo 3:1) Ngati mwatayikiridwa ndi wokondedwa wanu mu imfa, pezani chitonthozo m’chidziŵitso chakuti imfa ili yakanthaŵi chabe. (Chivumbulutso 20:13, 14) Khulupirirani chiyembekezo cha chiukiriro. Ndiyeno, kaya mudzaloŵa m’dziko latsopano mwa kupulumuka chisautso chachikulu kapena chiukiriro, khalani ndi chidaliro m’chitsimikiziro chouziridwa chakuti imfa, mdani wotsiriza, idzathetsedwa.​—Chivumbulutso 7:9, 14.

[Chithunzi patsamba 5]

Atsamwali abwino Achikristu angamangirire mwauzimu oferedwa

[Chithunzi patsamba 7]

Kukhala wotanganitsidwa kuthandiza ena kumachepetsa chisoni chochititsidwa ndi imfa ya wokondedwa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena