Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 10/8 tsamba 26-30
  • Zaka za Kuumbika—Zimene Mufesa Tsopano Mudzazituta Pambuyo Pake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zaka za Kuumbika—Zimene Mufesa Tsopano Mudzazituta Pambuyo Pake
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Amayi ndi Atate Amakhala ndi Phande m’Kumamatirana
  • Kututa Ngakhale Tsopano Zimene Tafesa
  • Nthaŵi Yambiri Njofunika
  • Kakonzedwe ka Yehova
  • Phunzitsani Mwana Wanu M’njira Yabwino—Ndipo Kuchiteni Kuchokera ku Ukhanda!
    Galamukani!—1987
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Mmene Mungatetezere Ana Anu
    Galamukani!—2007
  • Mfungulo Zopezera Maphunziro Abwino
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 10/8 tsamba 26-30

Zaka za Kuumbika—Zimene Mufesa Tsopano Mudzazituta Pambuyo Pake

UBONGO wa mwana ndiwo siponji imene imamwerera madzi oizinga. M’zaka ziŵiri eni akewo amaphunzira choloŵanecholoŵane wa chinenero mwa kungochimva. Ngati mwana amvetsera zinenero ziŵiri, amaphunzira zonsezo. Osati chinenero chokha komanso maluso a nyimbo ndi zopangapanga, mayendedwe athupi, kufunika kwa makhalidwe ndi chikumbumtima, chikhulupiriro ndi chikondi ndi chikhumbo cha kulambira—zonsezo zimachokera m’mphamvu ndi m’kuthekera koikidwiratu muubongo wa mwana. Umangoyembekezera chidziŵitiso chochokera kwa owazinga kaamba ka kuukulitsa. Ndiponso, pali programu ya nthaŵi yoyenera kaamba ka kuloŵetsedwa kwa chidziŵitso chimenechi kuti chikhale ndi zotulukapo zabwino koposa, ndipo nthaŵi ya phindu imeneyo ndiyo m’zaka za kuumbika.

Mchitidwe umenewu umayamba pakubadwa. Umatchedwa kumamatirana. Amayi amayang’anitsitsa mwachikondi m’maso mwa mwana, amamlankhula motonthoza, amamkhumbatira ndi kuseŵera naye. Mikhalidwe yachibadwa ya unakubala imasonkhezeredwa pamene mwanayo ayang’anitsitsa dwi kwa amake akumamva kukhala wotetezereka. Ngati pachiyambipa kuyamwitsa kuchitika, zimenezo nzabwino kwambiri kwa onsewo. Kuyamwa kwa mwana kumasonkhezera kupangika kwa mkaka. Kukhudzidwa ndi khungu lake kumachititsa amake kutulutsa mahomoni amene amachepetsa mwazi umene umakha atabala. Mkaka wa amayi umakhala ndi maselo otetezera thupi amene amatetezera mwanayo kuyambukiridwa ndi matenda. Kumamatirana kumachitika. Ndiko kuyambika kwa kukondana. Komatu ndiko chiyambi chabe.

Mwamsanga aŵiri omamatiranawo amakhala atatu pamene atate aloŵetsedwamo, monga momwedi ayenera kuchitira. “Mwana aliyense amafuna . . . atate,” akutero Dr. T. Berry Brazelton, “ndipo atate aliyense angakwaniritse mbali yotsalayo. . . . Amayi anayedzamira pakukhala ofatsirira zinthu pang’ono ndi odekha kwa ana awo. Kumbali inayo, atate, anali okonda kuseŵera nawo kwambiri, kugiligisa ndi kuseka ndi ana awo koposa mmene anachitira amayi.” Makandawo amalabadira kuchitiridwa motere mwamphamvu mwa kufuula ndi chisangalalo ndi kukuwa mokondwerera, akumasangalala mopokosera ndi kumafunsira kwinanso. Ndiwo mchitidwe wa kumamatirana wopitirizabe woyambidwa pakubadwa, ‘mlunzanitso wa chikondi pakati pa makolo ndi mwana umene mwachibadwa kwakukulukulu umapangidwa kapena kuphonyedwa m’miyezi yoyamba khumi ndi isanu mphambu itatu ya moyo wa mwana,’ akutero Dr. Magid, mmodzi wa alembi a bukhu lakuti High Risk: Children Without a Conscience. Ngati uphonyedwa, iye akutero, ana otero angakule kudzakhala osasamala ena ndi osakhoza kukonda ena.

Amayi ndi Atate Amakhala ndi Phande m’Kumamatirana

Chifukwa chake, nkofunika chotani nanga kwa amayi ndi atate kugwirizana pakulimbikitsa chogwirizanitsa chimenechi cha chikondi, kumamatirana kumeneku ndi chikondi pakati pa makolo ndi mwana m’zaka zake za kuumbika asanamke kusukulu yanasale! Pakhaletu kukhumbatirana ndi kumpsompsonana kochuluka kwa makolo onsewo. Indedi, atatenso! Men’s Health, June 1992, imati: “Kukhumbatirana ndi kusonyezana chikondi mwa kuthupi ndi makolo kumasonyezeratu ubwenzi wamphamvu, maukwati ndi ntchito zodzisankhira zachipambano zamtsogolo mwa mwanayo, kukusonyeza motero kupenda kwa zaka 36 kofalitsidwa mu Journal of Personality and Social Psychology. Peresenti yokwanira 70 ya ana a makolo owakonda inayanjana ndi ena bwino lomwe, poyerekezera ndi 30 peresenti yokha ya ana a makolo osalabadira; ndipo kukhumbatira kwa Atate kunapezedwa kukhala kofunika monga kwa Amayi.”

Ndiponso, mgwirireni pamene mukumuunguza chauko ndi uku. Muŵerengereni pamene akumva kukhala wotetezereka pamiyendo yanu. Lankhulani naye ndi kumvetsera, mlangizeni zimene ziri zabwino ndi zoipa, ndipo tsimikizirani kukhala zitsanzo zabwino, mukumazichita inu eni. Ndipo kumbukirani nthaŵi zonse za msinkhu wa mwanayo. Zipangitseni kukhala zosavuta, zokondweretsa, ndi zonga seŵero.

Mwana wanu ali ndi chidwi chachibadwa, chikhumbo cha kufufuza zinthu, kuphunzira zinthu zonse zomzinga. Kuti mukhutiritse njala ya kufuna kudziŵa imeneyi, mwana amakhoterera pakukufunsani mafunso osatha. Kodi chimapanga mphepo nchiyani? Kodi nchifukwa ninji thambo liri lobiriŵira? Kodi nchifukwa ninji kunja kumafiira pamene dzuŵa liloŵa? Yankhani mafunsowo. Nkovuta nthaŵi zina. Mafunso ameneŵa ndiwo kutseguliridwa kwanu njira kusonkhezera maganizo a mwana wanu, kuloŵetsamo chidziŵitso, mwinamwake kusonkhezera chiyamikiro kaamba ka Mulungu ndi chilengedwe chake. Kodi ndiko kachirombo kakang’ono koyenda patsamba kamene kakumkondweretsa? Kapena kodi ndimpangidwe wa kaduŵa? Kapena kuwonerera kangaude akumanga nyumba yake? Kapena kufukula m’zinyalala? Ndipo musanyalanyaze kuphunzitsa ndi tinkhani, monga momwe anachitira Yesu ndi mafanizo ake. Zimapangitsa kuphunzirako kukhala kosangalatsa.

M’zochitika zambiri makolo onse aŵiri amafunikira kugwira ntchito kuti apeze ndalama zokhalira moyo. Kodi iwo angapange kuyesayesa kwapadera kuthera maola a madzulo ndi a pakutha kwa mlungu ndi ana awo? Kodi nkotheka kwa amayi kugwira ntchito theka la tsiku tsiku lirilonse kuti akhale ndi nthaŵi yambiri ndi ana ake? Lerolino pali makolo ambiri olera ana ali okha, ndipo ayenera kugwira ntchito kuti adzisamalire limodzinso ndi ana awo. Kodi iwo angakhale akhama m’kupereka maola ambiri amadzulo ndi a pakutha kwa milungu monga momwe angathere kwa ana awo? M’zochitika zambiri nkofunika kwa amayi kusiya ana awo. Ngakhale ngati zifukwa zowasiyira ziri zololeka, mwana wamng’ono samamvetsetsa zimenezo ndipo angalingalire kukhala atanyanyalidwa. Chotero kuyesayesa kwapadera kuyenera kuchitidwa kupezera nthaŵi mwana wanu.

Tsopano, kodi “nthaŵi yaphindu” imeneyi imene tikumva nchiyani? Makolo otanganitsidwa angathere mphindi 15 kapena 20 tsiku lirilonse ndi ana awo, mwinamwake ola pakutha kwa mlungu, ndi kulitchula kuti nthaŵi yaphindu. Kodi zimenezi nzokwanira kaamba ka zosoŵa za mwana? Kapena kodi cholinga chake ndicho kutonthoza chikumbumtima cha makolo? Kapena kupumitsa maganizo a amayi amene amagwira ntchito yodzikhutiritsa pamene akusiya maganizo a ana ake ali osakhutira? Komano mukunena kuti, ‘Komatu ine ndithudi, ndimatanganitsidwa ndiribiretu nthaŵi yotero.’ Zimenezo nzoipa kwambiri ndi zomvetsa chisoni kwambiri kwa inu ndi ana anu omwe chifukwa chakuti palibe njira zachidule. Pezani nthaŵi m’zaka za kuumbika, kapena konzekerani kudzakhala ndi mpata wa mbadwo m’zaka za ana zapakati pa 13 kufikira 19.

Sikokha kuti mwana wosiyidwa kusukulu yanasale angavulazike malingaliro, komanso makolo amatayikiridwa pamene aphonya kusangalala ndi mwanayo pamene akukula. Mwanayo samvetsetsa nthaŵi zonse zifukwa za kusiyidwa yekha zimenezo; angalingalire kukhala wonyalanyazidwa, wokanidwa, wosiyisidwa, wosakondedwa. Podzafika m’zaka zake za kusinkhuka, angakhale atapanga maunansi ndi anzake oloŵa m’malo mwa makolo osoŵa nthaŵi ya kukhala nayewo. Mwanayo angayambedi kukhala ndi moyo wapaŵiri, mbali ina kukondweretsa makolo ake ndi inayo kudzikondweretsa. Mawu, kupereka zifukwa, kupepesa—palibe chirichonse cha zimenezi chimene chimatseka mpatawo. Kulankhula naye kwachikondi kwa makolo tsopano sikumveka kukhala kothandiza kwa mwana amene ananyalanyazidwa m’zaka zimene anafunikira chithandizo choposa cha makolo ake. Kunena zachikondiko tsopano kukumvekera kuli konyenga; mawuwo amamvekera kukhala osawona mtima. Mofanana ndi chikhulupiriro, chikondi chonenedwa popanda ntchito yake nchakufa.—Yakobo 2:26.

Kututa Ngakhale Tsopano Zimene Tafesa

Mumbadwo uno wa kufuna kukhala woyamba, dyera likukula, ndipo limeneli nlowonekera makamaka m’kusiyidwa kwa ana athu. Tinawabala, ndiyeno timawaika m’sukulu zanasale. Sukulu zina zanasale zingakhale zabwino kwa ana, koma zambiri siziri zotero, makamaka kwa ana achichepere. Zina zimafufuzidwadi chifukwa cha kuipitsa ana mwa kuwagona. Wofufuza wina anati: “Mtsogolomu, popanda chikayikiro, tidzakhala ndi mavuto amene adzapangitsa a lerolino kuwoneka aang’ono ngati tii pate.” Mavuto aang’onowo ngati “tii pate” a lerolino ali owopsa kale, monga momwe ziŵerengero zoperekedwa ndi Dr. David Elkind mu 1992, zimasonyezera:

“Pakhala 50 peresenti ya kuwonjezereka m’kunenepa mwa ana ndi achichepere m’zaka makumi aŵiri zapitazi. Timatayikiridwa ndi achichepere okwanira zikwi khumi pachaka m’ngozi za kugwiritsiridwa ntchito kwa zoledzeretsa, osaphatikizapo ovulala ndi opunduka. Mmodzi mwa achichepere anayi amamwa kwambiri milungu iŵiri iriyonse, ndipo tiri ndi zidakwa za achichepere mamiliyoni aŵiri.

“Asungwana achichepere mu Amereka amatenga mimba pamlingo wa miliyoni imodzi pachaka, kuŵirikiza kaŵiri mlingowo wa dziko lina Lakumadzulo, England. Kudzipha kwaŵirikiza katatu pakati pa achichepere m’zaka 20 zapitazi, ndipo pakati pa achichepere zikwi zisanu ndi zisanu ndi chimodzi amadzipha chaka chirichonse. Kukuyerekezeredwa kuti mmodzi mwa asunguwana anayi achichepere amasonyeza pafupifupi chizindikiro chimodzi cha kudya kosalongosoka, makamaka kudzimana chakudya kwakukulu. Kagulu ka a zaka 14 kufikira 19 kali kachiŵiri pamlingo wa kudzipha kwakukulu koposa kagulu kena kalikonse.”

Wonjezerani paziŵerengero zochititsa mantha zimenezi kuphedwa kwa makanda oposa mamiliyoni 50 akali m’mimba, ndipo mavuto aang’ono ngati “tii pate” a lerolino ali osanunkha kanthu. Polingalira kugwa kwa mabanja, Dr. Elkind anati: “Kusintha kofulumira kwa chitaganya ndiko tsoka kwa ana ndi achichepere, amene amafunikira kukhazikika ndi chitetezero cha kukula ndi thanzi labwino ndi kupeza chidziŵitso.” Wolemba wina wonena za dyera la kufuna kukhala woyamba analengeza motsutsa kuti: “Komatu palibe aliyense amafuna kunena kwa anthu okwatirana kuti, Tawonani, musalekane muukwati. Ngati muli ndi ana, musalekane!”

Kukonda mwana kumafunikira kupatula nthaŵi. Zaka zapitazo Robert Keeshan, woulutsa nkhani pawailesi kwa ana wotchedwa Captain Kangaroo, anachenjeza za zotulukapo za kusapereka nthaŵi yanu kwa ana anu. Iye anati:

“Kamwana kamayembekezera, chala cha manthu chiri m’kamwa, chidole chake chiri m’manja, kakulakalaka, kufika panyumba kwa kholo. Kamakhumba kufotokoza zimene kawona koseŵera. Nkokondwera kunena za chikondwerero chimene kanali nacho tsikulo. Nthaŵiyo imafika, kholo limadza. Pokhala lotopa kuchokera kuntchito kaŵirikaŵiri kholo limangonena kwa mwanayo kuti, ‘Osati tsopano, wokondedwa. Ndiri wotanganitsidwa, kawonerere wailesi yakanema.’ Mawu onenedwa kwambiri m’mabanja ambiri a ku Amereka, ‘Ndiri wotanganitsidwa, kawonerere wailesi yakanema.’ Ngati osati tsopano, liti? ‘Nthaŵi ina.’ Komatu nthaŵi ina simadza . . .

“Zaka zimapita ndipo mwanayo amakula. Timampatsa zoseŵeretsa ndi zovala. Timampatsa zovala zotchuka ndi siteriyo koma sitimpatsa chimene amafuna kwambiri, nthaŵi yathu. Ngwazaka 14, maso ake ngofiira, waledzera. ‘Wokondedwa, chikuchitika nchiyani? Tandiuza, tandiuzatu iwe.’ Mwachedwa. Mwachedwa. Nthaŵi ya chikondi inatithera. . . .

“Pamene tinena kwa mwanayo kuti, ‘Osati tsopano, nthaŵi ina.’ Pamene tinena kuti, ‘Kawonerere TV.’ Pamene tinena kuti, ‘Usafunse mafunso ambirimbiri.’ Pamene tilephera kupatsa ana athu chinthu chimodzi chimene amafuna kwa ife, nthaŵi yathu. Pamene tilephera kukonda mwana wathu. Sikuti sitisamala. Tiri chabe otanganitsidwa kwakuti tiribe nthaŵi ya kukonda mwana wathu.”

Nthaŵi Yambiri Njofunika

Chofunika sindicho kupereka “nthaŵi yaphindu” yogaŵiridwa mwakamodzikamodzi; “nthaŵi yambiri” iyeneranso kuphatikizidwa. Baibulo, limene liri ndi nzeru yochuluka koposa kuposa mabuku onse olembedwa ponena za maphunziro azamaganizo, limati pa Deuteronomo 6:6, 7: “Ndipo mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” Muyenera kuloŵetsa m’mitima mwa ana anu makhalidwe enieni a m’Mawu a Mulungu amene ali mumtima mwanu. Ngati muwasiya, ana anu adzakutsanzirani.

Kodi mukukumbukira mwambi wogwidwa m’ndime yoyamba ya nkhani yapitayo? Nawunso: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.” (Miyambo 22:6) Zimenezi zimakhala zowona kokha ngati mapindu a kuphunzitsawo aloŵetsedwa, ndiko kuti, aikidwa mwa iye, ndi kupangitsidwa kukhala mbali ya kuganiza kwake, malingaliro ake a pansi pamtima, zimene iye ali mumtima. Zimenezi zimachitika kokha ngati mapindu ameneŵa sanangophunzitsidwa kwa iye ndi makolo ake komanso kuchitidwa ndi makolo ake.

Iye wawaloŵetsa mumtima monga njira ya moyo. Akhala miyezo yake imene iri mbali ya moyo wake. Kutsutsana nawo sikudzakhala kutsutsana ndi zimene makolo ake anamphunzitsa koma zimene iye mwiniyo wakhala. Akakhala wosawona mtima kwa iye mwini. Akakhala akudzikana. (2 Timoteo 2:13) Amakhala ndi mphamvu ya kusafuna kuchita zimenezi kwa iye mwini. Chifukwa chake, ngwosalingalirika ‘kupatuka panjira imeneyi’ imene yasonkhezeredwa mwa iye. Chotero ana anu atengeretu khalidwe lanu. Phunzitsani kukoma mtima mwa kusonyeza kukoma mtima, makhalidwe abwino mwa kuwachita, kudekha mwa kukhala wodekha, kuwona mtima ndi kunena zowona mwa kuwakhazikitsira chitsanzo.

Kakonzedwe ka Yehova

Banja linali kakonzedwe ka Yehova kwa munthu kuyambira pachiyambi. (Genesis 1:26-28; 2:18-24) Pambuyo pa zaka zikwi zisanu ndi chimodzi za mbiri ya anthu, kamazindikiridwabe kukhala kwabwino koposa kwa achikulire ndi ana omwe, monga momwe kwatsimikizidwira ndi bukhu lakuti Secrets of Strong Families m’mawu aŵa:

“Mwinamwake chinthu china chachikulu mwa ife chimazindikira kuti banja ndilo maziko a kutsungula. Mwinamwake mwachibadwa timadziŵa kuti pamene tifika paphata m’moyo sindizo ndalama, ntchito yodzisankhira, kutchuka, nyumba yabwino, munda, kapena chuma chakuthupi chimene chiri chofunika koposa—ali anthu amene amatikonda ndi kutisamalira m’moyo wathu. Anthu a m’moyo wathu amene amatidera nkhaŵa ndi amene tingawadalire kutichirikiza ndi kutithandiza ndiwo ali nkanthu. Palibe kulikonse kumene kuthekera kwa chikondi, chichirikizo, chisamaliro, ndi thayo timakuwona kukhala kokulira koposa m’banja.”

Chifukwa chake, kuli kofunika kukhala wakhama ndi kuphunzitsa bwino tsopano m’zaka za kuumbika kotero kuti zimene mudzakolola mtsogolo zidzakhala, kwa inu ndi ana anu omwe, moyo wabanja wachimwemwe.—Yerekezerani ndi Miyambo 3:1-7.

[Bokosi patsamba 30]

Kodi Ndidzakhala Kholo Liti?

“Ndakhoza ma A aŵiri,” kamnyamatako kanafuula motero, liwu lake lokondwera. Atate wake anamfunsa modula mawu, “Chifukwa ninji sunakhoze ambiri?” “Amayi, ndatsiriza kutsuka mbale,” msungwanayo analankhula ataima pakhomo la kukichini. Mwamphwayi amakewo anati, “Kodi wakataya zinyalala zija?” “Ndatsiriza kudulira kapinga uja,” Mnyamata wamtaliyo anatero, “ndipo ndabwezera makina ake pamalo ake.” Atate wake akumfunsa ndi nsunamo “Kodi wadulira hejinso?”

Ana okhala m’nyumba yoyandikana nayo akuwonekera kukhala okondwa ndi okhutira. Zofananazo zinachitikanso kumeneko, ndipo umu ndimo mmene zinayendera:

“Ndakhoza ma A aŵiri,” kamnyamatako kanafuula motero, liwu lake lokondwera. Monyadira atate wake anati, “Nzabwino kwambiri zimenezo; ndikukondwa kuti wachita bwino kwambiri.” “Amayi, ndamaliza kutsuka mbale,” msungwanayo analankhula ataima pakhomo la kukichini. Amakewo anamwetulira ndi kunena mofatsa kuti, “Ndimakukonda kwambiri tsiku lirilonse.” “Ndatsiriza kudulira kapinga uja,” mnyamata wamtaliyo anatero, “ndipo ndabwezera makina ake pamalo ake.” Atate wake anayankha mwachimwemwe kuti, “Ndimanyada nawe.”

Ana amafuna chiyamikiro pang’ono pantchito zimene amachita tsiku lirilonse. Ngati ati akhale ndi moyo wachimwemwe, zambiri zikudalira pa inu.

[Zithunzi patsamba 27]

Atate agwirizana ndi amayi mumchitidwe wa kumamatirana

[Chithunzi patsamba 28]

Pamene nzeru za kuyerekezera zikukula, kuthamanga kwa kamnyamata katatambasulira mikono m’mbali kumakhala ndege youluka, katoni yaikulu imakhala nyumba yoseŵereramo, ndodo ya tsache imakhala kavalo waliŵiro lalikulu, mpando ungakhale pokhala woyendetsa galimoto la mpikisano

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena