Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 11/8 tsamba 27-29
  • Bwanji Ngati Kholo Langa Latichititsa Manyazi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bwanji Ngati Kholo Langa Latichititsa Manyazi?
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Sichifukwa Chanu!
  • Kudzitsimikizira Inumwini Kukhala Wosiyana
  • Kugonjetsa Malingaliro
  • Bwanji Ngati Kholo Langa Lichita Molakwa?
    Galamukani!—1995
  • Ndingatani Makolo Anga Akamaledzera Kapena Kumwa Mankhwala Osokoneza Bongo?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Kodi Ndingachite Nalo Motani Kholo Langa Limene Linachoka Panyumba?
    Galamukani!—1990
  • Kodi Ndingakhale Motani m’Banja Logaŵikana Mwachipembedzo?
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 11/8 tsamba 27-29

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Bwanji Ngati Kholo Langa Latichititsa Manyazi?

ATATE a Jacob anali woyang’anira Wachikristu wolemekezeka m’dziko lina la Afirika. Koma pamene anasiya amake a Jacob kukakhala ndi mkazi wina, atate a Jacob anachotsedwa mumpingo Wachikristu. Mikhalidweyo inafikira poipirapo kwambiri pamene atatewo anayamba kumwa mopambanitsa. “Mumkhalidwe umenewu,” akukumbukira Jacob, “iwo ankafika ku sukulu ndi kundichititsa manyazi pamaso pa aphunzitsi anga ndi anzanga akusukulu.”a

Wachichepere wina mu Afirika, amene tidzamutcha David, mofananamo anawona atate wake akuchotsedwa mumpingo Wachikristu monga wochita cholakwa wosalapa. “Sindikatha kuzikhulupirira,” akutero David. “Ine nthaŵi zonse ndinayang’ana kwa iwo monga chitsanzo changa chabwino. Mantha anga aakulu koposa anali akuti palibe munthu amene akafuna kuyanjana ndi banja la munthu wochotsedwa.”

Pamene kholo lilowetsa dzina la banja mu mtonzo mwakuphatikizidwa mu mkhalidwe wochititsa manyazi, kapena ngakhale kumangidwa, sikuli kwachilendo konse kumva mukuchititsidwa manyazi, kululuzika, ndi kuchita mantha onena za mtsogolo. Inu nthaŵi zina mungamve monga momwe anachitira wamasalmo amene analemba kuti: “Tsiku lonse chimpepulo changa chikhala pamaso panga, ndipo manyazi apankhope panga andikuta.”—Salmo 44:15.

Monga chotulukapo chakudzisungira kwa kholo lanu, mungadziwone kukhala woluluzika ndi wamanyazi pamene muli pakati pa mabwenzi ndi atsamwali. Mofananamo ena a iwo angawonekere kukhala osapeza bwino pamene muli nawo. Achichepere ena ankhanza angafikire ngakhale pakukondwera ndi kukuserewulani ponena za mkhalidwe womvetsa chisoni wa kholo lanu, kapena achikulire angakuchenjezeni mwamphamvu kuti inu mukhoza bwino lomwe kuchita mwanjira imodzimodziyo.

Sichifukwa Chanu!

Mawu otchuka a nthaŵi zakale ananena kuti: “Makolo anadya mphesa zowawasa, koma ana anamva kuwawasako.” (Ezekieli 18:2, Today’s English Version) Mofananamo achichepere lerolino angamve kuti akuvutitsidwa ndi khalidwe loipa la makolo awo. Pambuyo pakuchotsedwa mu mpingo kwa atate wake, David wachichepereyo anamva atavulala maganizo kwambiri ndipo anadabwa ngati Mulungu anali kumlanga.

Koma kodi iye anali? Nzowona, Mulungu anachenjeza mtundu wa Israyeli kuti anali “kulanga ana chifukwa cha atate wawo.” (Eksodo 20:5) Mwachitsanzo, panthaŵi ina, Yehova analola mtundu wonse kulowa mu ukapolo ku Babulo wakutaliyo. Pamene kuli kwakuti zimenezi zinali kwakukulukulu chifukwa cha kusadzisungira bwino kwa achikulire, mosakaikira undendewo unadzetsa vuto pa ana Achiisrayeli. Chikhalirechobe, Mulungu anapitirizabe kuyanja achichepere Achiisrayeli, monga Danieli ndi atsamwali ake, amene anapitirizabe mokhulupirika kumlambira.—Danieli 3:28, 30.

Chotero pamene kuli kwakuti kusochera kwa kholo lanu kungakuchititseni chisoni chachikulu ndi ululu, simufunikira kuwopa kuti mwataikiridwa ndi chiyanjo cha Mulungu kapena dalitso. Talingalirani mawu a Yehova pa Ezekieli 18:14, 17 amene anatsatira mawu ogwidwa poyambirirapo onena za mphesa zowawasa akuti: “Tawona tsono, yemweyo akabala mwana uyu, tawona zochimwa zonse adazichita atate wake, nawopa wosachita zoterozo . . . uyu sadzafera mphulupulu ya atate wake, adzakhala ndi moyo ndithu.”

Komabe, tawonani kuti, kuti mupitirizebe kukhala ndi moyo, muyenera kutsatira njira yosiyana ndi yotsatiridwa ndi kholo lanu losochera. “Yense ayesere ntchito ya iye yekha,” likulimbikitsa Baibulo, “ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, sichifukwa cha wina.”—Agalatiya 6:4.

Kudzitsimikizira Inumwini Kukhala Wosiyana

Mwachitsanzo, tayerekezerani, mfumu yachichepere ya Yuda yotchedwa Yosiya. Onse aŵiri atate wake ndi agogo ake anali ndi mbiri yoipa yakulambira mafano. Komabe, Yosiya mwiniyo “anachita iye zowongoka pamaso pa Yehova.” (2 Mafumu 21:19, 20; 22:1, 2) Atate a Mfumu Hezekiya, Ahazi, anali mfumu ina imene inapereka chitsanzo chomvetsa chisoni. Ahazi anatseka makomo akachisi wa Yehova napereka nsembe ana aamuna a iyemwini kufukizira mulungu wachikunja! (2 Mbiri 28:1-3, 24, 25) Komabe, Hezekiya, anatsimikizira kukhala wosiyana ndi atate wake. Pamsinkhu wa zaka 25 anayamba kulamulira ndipo mwamsanga anayamba kubwezeretsa kulambira kowona mu Yuda.—2 Mafumu 18:1-5.

Ana aamuna a Kora anapereka chitsanzo chofananacho. Mtundu wa Aisrayeli usanalowe m’Dziko Lolonjezedwa, Kora, Mlevi wotchuka, anatsogolera chipanduko chotsutsana ndi Mose ndi Aroni. Komabe, chipandukocho, chinalepheretsedwa mofulumira pamene Kora ndi otsatira ake anaphedwa ndi chivomezi ndi moto wochokera kumwamba. Komabe, mokondweretsa, ana a Kora anapulumuka. (Numeri 26:9-11) Kukuwonekera kuti iwo sanachirikize atate wawo m’chipanduko chimenechi. Mosakaikira ana a Kora amenewa anachititsidwa manyazi ndi njira yoipa ya atate wawo. Koma Yehova anadalitsa ana a Kora chifukwa chakuti anamamatira ku Chilamulo chake. Pakati pa mawu okongola koposa opezeka m’Baibulo pali mawu olembedwa ndi ana a Kora.—Wonani Masalmo 45, 48, 84, 85, 87, ndi 88.

Mofanana ndi Yosiya, Hezekiya, ndi ana a Kora, achichepere Achikristu ambiri lerolino atsimikizira kukhala osiyana ndi makolo osochera. Talingalirani wachichepere wina amene tidzamtcha Maxwell. Nthaŵi ina makolo ake anali Mboni zokhulupirika za Yehova koma anafikira kukhala ampatuko otsutsa Chikristu. Panthaŵi ina makolo ake ananyamula mbendera nachita chisonyezero kunja kwa bwalo la msonkhano waukulu Wachikristu umene Maxwell anafikapo. “Kunali kochititsa manyazi kwambiri,” iye akufotokoza. “Ena amene sanadziwe kuti iwo anali makolo anga anati kwa ine, ‘Kodi wawona zitsilu za ampatuko panjapo?’” Komabe, Maxwell sanalondole njira yachipanduko ya makolo ake. Ndipo mochilikizidwa ndi ziŵalo zokhulupirika za banja ndi mabwenzi ena Achikristu, iye wakhala wokhoza kugonjetsa malingaliro akumva chisoni ndi kuchita manyazi.

Ndithudi, Maxwell, Jacob, ndi David (otchulidwa poyambawo) onsewo agonjetsa mkhalidwe wa banja lawo. Pakali pano iwo onse akutumikira monga aminisitala pa ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society mu Afirika. “Ndidziŵa kuti ndingafunikire kuyang’anizanabe ndi kuchititsidwa manyazi kuchokera kwa makolo anga mtsogolo,” akutero Maxwell, “koma ndidziŵanso kuti ngati ndidalira pa Yehova, iye adzandipatsa nyonga yakupirira.”

Kugonjetsa Malingaliro

Kwakukulukulu chithandizo chingafunike kugonjetsa malingaliro omvetsa chisoni ochititsidwa ndi mkhalidwe wochititsa manyazi wa kholo lanu. “Pamene ndiwona amayi [ataledzera],” analemba motero Charmaine wa zaka 15 zakubadwa, “kumachita ngati kuti kanthu kena mkati mwanga kakuzimiririka . . . ndimakwiya kwambiri . . . Mabwenzi anga sayenera kuzindikira vuto la amayi, chifukwa chakuti ndidakadzilemekezabe.” (Alcohol Abuse—The Incredible Lie! lolembedwa ndi Henri Naudé) Komabe, mwambi Wachingelezi umatikumbutsa kuti “chisoni chogawana ndi ena chimapepuka.” Pakutitu, ndiiko komwe, vuto la kholo lanu lingakhale lodziŵika kwa onse. Chotero mulisungiranji kukhala chinsinsi chosakhoza kuululidwa? Ndipo ngakhale kumene kuchita mwanzeru kuli kuchenjera, kodi kuli kwanzeru kulola malingaliro anu amkwiyo kuunjikana? Kodi sikukathandiza kupeza Mkristu wachikulire amene mungawululire chinsinsi? Mwanjira iyi mukalandira mawu abwino achilimbikitso.—Miyambo 12:25; 16:24.

Kusinkhasinkha malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo ndiko njira ina yakugonjetsera malingaliro oipa. Jacob akuvomereza kuti: “Zinthu zimene atate anachita zinandichititsa kudana nawo mumtima mwanga.” Komabe, udani sudzawongolera mkhalidwewo, ndiponso suli wogwirizana ndi lamulo la Baibulo lakulemekeza atate ndi amayi amunthuwe. (Aefeso 6:1-3) Mmalo mwa kuda kholo lanu lenileni, muyenera kukhala ndi udani weniweni wacholakwa cha kholo lanu. (Yerekezerani ndi Miyambo 8:13; Yuda 23.) Kulidi koyenerera kumvera ndi kusonyeza ulemu kwa kholo lanu losochera. Kusonyeza ndi kuwonetsa chikondi chanu chosalekeza kungathandize kusonkhezera kholo limenelo kupanga masinthidwe ofunika.

Jacob wachichepere anali ndi vuto lina lodziŵika—chikhoterero cha kudziyerekezera ndi achichepere ena amene mikhalidwe yawo inali yabwinopo. Komabe, anadzazindikira mmene kuganiza kotero kunaliri kopanda pake. “Mmalo mwa kusumika maganizo pa malingaliro otero,” akutero Jacob, “kuli kothandiza kwambiri kusumika maganizo panjira za mmene mungalimbanirane ndi mkhalidwewo.” Jacob anapeza kuti kuwerenga mabukhu othandizira Baibulo ndi kusinkhasinkha pa njira ya moyo ya Akristu okhulupirika kunali chithandizo chachikulu.

Kuyanjana mwapafupi ndi mpingo Wachikristu kungatsimikizirenso kukhala kothandiza. Kumeneko inu mungathe kupeza “abale ndi alongo ndi amayi” auzimu. (Marko 10:30) David wachichepere anawopa kuti ziŵalo zampingo zingampewe chifukwa cha kuchotsedwa kwa atate wake. Koma iye anapeza kuti mantha ake anali opanda maziko kotheratu. “Mumpingo,” iye akufotokoza, “sitinachititsidwe kumva monga anthu onyanyalidwa, monga momwe ndinalingalilira kuti tikakhala. Mabwenzi anafikabe kudzacheza nafe. Zonsezi zinandikhutiritsa kuti mpingo unalidi wodera nkhaŵa.”

Palibe kukaikira kuti kukhala ndi kholo losochera kungathe kukhala komvetsa ululu ndi kowononga. Koma simufunikira kutaya mtima. Lingalirani zokumana nazo za anthu otchulidwa muno. Funafunani chithandizo cha mabwenzi achikondi. Musanyozere makolo anu; njira yanu yokhulupirika potsirizira pake ingawasonkhezere kukusintha. (Yerekezerani ndi 1 Petro 3:1, 2.) Ndipo mosasamala kanthu za chimene chichitika, kumbukirani kuti mkhalidwe wanu pamaso pa Mulungu sumadalira pa kudzisungira kwa makolo anu. Umadalira pa inu!

[Mawu a M’munsi]

a Maina m’nkhani ino asinthidwa.

[Chithunzi patsamba 27]

Simutofunikira kutsatira njira yosokera ya kholo lanu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena