Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 6/8 tsamba 30-32
  • Bwanji Ngati Kholo Langa Lichita Molakwa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bwanji Ngati Kholo Langa Lichita Molakwa?
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chimene Kuwalemekeza Kumatanthauza Kwenikweni
  • Kulimbana ndi Mkwiyo ndi Kuipidwa
  • ‘Ndingathe Kuwasintha’
  • Kumenyera Nkhondo Chipulumutso Chanu
  • Ndingatani Makolo Anga Akamaledzera Kapena Kumwa Mankhwala Osokoneza Bongo?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Kodi Ndingachite Nalo Motani Kholo Langa Limene Linachoka Panyumba?
    Galamukani!—1990
  • Kodi Ndingathandize Motani Kholo Langa Limodzi?
    Galamukani!—1991
  • Bwanji Ngati Kholo Langa Latichititsa Manyazi?
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 6/8 tsamba 30-32

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Bwanji Ngati Kholo Langa Lichita Molakwa?

“Atate akhala Mkristu kwa zaka khumi. Tsopano ali ofooka. Samaphunzira Baibulo, ndiponso samafika pamisonkhano nthaŵi zonse. Amangonena abale awo Achikristu a mumpingo nthaŵi zonse. Ali ndi malingaliro akudziko pamafuko ena ndi pankhani zina zambirimbiri. Ndimawaganizira kuti ali ndi zolakwa zambiri.”—Mtsikana wachichepere.

PALIBE kholo limene lili langwiro. “Onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu,” Baibulo limatero. (Aroma 3:23) Koma ili nkhani yosiyana kotheratu pamene amayi kapena atate a munthuwe amadzisonyeza kukhala chitsanzo chabwino Chachikristu poyera ndi kukhala munthu woipa kumbali. “Pakati pa ena, atate ndi munthu wabwino,” akutero mtsikana wina wachichepere. “Koma amakhala munthu winanso pamene enawo palibe—ngaukali! Amandinena pa chilichonse chimene ndimachita, ndipo amakwiyitsa aliyense m’banja lathu. Moyo sumandikondweretsanso. Ndimangowada.”

Mkwiyo ndi kuipidwa zingakhale zazikulu kwambiri pakati pa achichepere amene makamaka amavutika mtima mwamseri chifukwa cha mitundu ina ya nkhanza. Motero mkazi wina wotchedwa Mary akulemba za “chiwawa, kutukwanidwa, ndi nkhanza zamitundumitundu” zimene anachitiridwa ndi atate wake—chidakwa chamseri. “Anthu ankafikira anafe ndi kutiuza kuti tili ndi atate wabwino koposa ndipo ndife amwaŵidi,” iye akukumbukira choncho moŵaŵidwa mtima.

Baibulo limatsutsa mitundu yonse ya chinyengo. (Yakobo 3:17) Limatichenjeza kuti ngakhale pakati pa olambira Mulungu oona, pakakhala ena amene ali “othyasika.” (Salmo 26:4; yerekezerani ndi Yuda 4.) Komabe kudziŵa zimenezi mwina sikungapangitse zinthu kukhala zosavuta, ngati munthu wochita chinyengoyo ali kholo lanu—munthu amene muyenera kukonda ndi kumchitira ulemu. Achichepere ena amavutitsidwa ndi malingaliro owombana amene amayambika. “Ndikufuna thandizo,” anadandaula motero mtsikana wina. “Baibulo limati ‘lemekeza atate wako,’ koma ine sindingathe.”

Chimene Kuwalemekeza Kumatanthauza Kwenikweni

Nzoona kuti lamulo la Baibulo lakuti munthu alemekeze makolo ake lili ‘losapeŵeka’ kwa achichepere amene amalingalira kuti makolo awo sayenera zimenezo. (Aefeso 6:1, 2) Komabe, kwenikweni kulemekeza kholo sikumatanthauza kuti inu mumavomereza moyo wawo kapena kuti mumasangalala ndi zimene amakuchitirani. M’Baibulo, liwulo “lemekeza” lingangotanthauza kuzindikira moyenera ulamuliro wokhazikitsidwa.

Mwachitsanzo, mtumwi Petro analemba kuti Akristu ayenera ‘kuchitira mfumu ulemu.’ (1 Petro 2:17) Petro anali kudziŵa kale kuti kaŵirikaŵiri mafumu anali anthu ankhanza. Mwachitsanzo, Mfumu Herode Agripa I anali munthu wowononga chuma ndi wosasamala. Roma atamuika kukhala mfumu ya Palestina, anayambitsa chizunzo pa Akristu. “Adapha ndi lupanga Yakobo mbale wa Yohane. Ndipo pakuona kuti kudakondweretsa Ayuda, anawonjezapo nagwiranso Petro.” (Machitidwe 12:1-3) Komabe, Petro sanalimbikitse ena kuukira. M’malo mwake, anachirikiza kumvera mafumu. Ndipo anatero pa chifukwa chabwino. Kumvera olamulira dziko kuli chifuniro cha Yehova. Ndipo m’tsiku la Petro mafumu ena anali ndi mphamvu zambiri. Solomo anati: “Amachita chomwe chimkonda. Pakuti mawu a mfumu ali ndi mphamvu; ndipo ndani anganene kwa iye, Kodi uchita chiyani?”—Mlaliki 8:3, 4.

Mofananamo, kholo lanu—ngakhale litachita cholakwa chotani—lili ndi ulamuliro ndipo lili ndi mphamvu yaikulu pa moyo wanu. Pamenepo, sikuli kwanzeru kulipandukira kapena kulichitira chipongwe. Kuchita motero sikudzangochititsa moyo wanu kukhala wovuta komanso kudzakutayitsani chiyanjo kwa Mulungu. (Yerekezerani ndi Miyambo 30:17; Mlaliki 10:4.) Komano, kugwirizana nalo monga momwe mungathere kungakuthandizeni kusunga mtendere pang’ono ndi bata mu unansi wanu ndi kholo lanulo.—Akolose 3:20.

Kulimbana ndi Mkwiyo ndi Kuipidwa

Komabe, kodi ndimotani mmene mungachitire mwaulemu ndi munthu wina amene wakuvulazani maganizo ndi kukugwiritsani mwala? Zimenezi nzovuta. Koma kumangolingalira machimo ake ndi zophophonyazo kudzangokulitsa kuipidwa naye. Kodi mwina mufunikira kuganizira zabwino za kholo lanulo, kuliyamikira chifukwa cha mikhalidwe iliyonse yabwino imene lingakhale nayo?

Taonani zimene Miyambo 19:11 imanena: “Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo.” Kuyesa kumvetsetsa kholo lanu kungakupatseni lingaliro latsopano pa mkhalidwewo. Kodi ilo likuchitadi moipa? Kapena mwina ilo langokhala ndi chifooko china, lili logwetsedwa ulesi ndi lofunikira thandizo? Kodi khalidwe lawo ladza chifukwa cha kudwala, kupsinjika maganizo, kusukidwa, kapena chitsenderezo cha kuntchito? Ngati ndi choncho, kumvetsetsa mavuto ameneŵa kungakuthandizeni kukhala wachifundo kwambiri kwa kholo lanulo ndipo mwinamwake wosakwiya kwambiri.

Mulimose mmene zilili, kukambitsirana ndi wina za malingaliro anu kumathandiza. (Miyambo 12:25) “Atate anali kumwa kwambiri,” akukumbukira motero mtsikana wina. “Sindinathe kuuza makolo anga mmene ndinamvera, chotero ndinangodzitontholera.” Komabe, inu simufunikira kuvutika nokhanokha choncho. Anthu okhwima maganizo a mumpingo Wachikristu angathandize kwambiri kuchepetsa vuto la kusoŵa chisamaliro chilichonse cha panyumba ndipo kutembenukira kwa iwo sikuli kunyalanyaza makolo anu. (Yerekezerani ndi Marko 10:30.) Miyambo 17:17 imati: “Mabwenzi amasonyeza chikondi chawo nthaŵi zonse. Nanga abale ngachiyani ngati sali othandiza pamavuto?”—Today’s English Version.

‘Ndingathe Kuwasintha’

Achichepere ena amavutika mtima chifukwa cha kudzipatsa thayo lolakwika. Mary akukumbukira ponena za iyemwini ndi abale ake kuti: “Tinkakhala ndi mantha kuti mwina munthu wina adzadziŵa za vuto la kumwetsa kwa atate.” Ena amadzipatsa ntchito yotopetsa mwa kupanga zoyesayesa zosaphula kanthu kuti asinthe khalidwe la kholo lawo lakhalidwe loipalo.

Mulimonse mmene mungakondere ndi kusamala kholo lanulo, mulibe mlandu wa zolakwa zawo. Iwo ‘asenza katundu wawo’ wa thayo pamaso pa Mulungu. (Yerekezerani ndi Agalatiya 6:5; Yakobo 5:14.) Si thayo lanu kusamalira kapena kulamulira khalidwe la kholo lanu. Kudandaulira kapena kumangonena kholo lanu kudzangolikwiyitsa.

Zimenezi sizikutanthauza kuti palibe chilichonse chimene mungachite. Pali mwaŵi wakuti mungathe ‘kupemphera kosaleka’ kuti kholo lanu lisinthe mtimawo. (1 Atesalonika 5:17) Kusonyeza chikondi chanu nthaŵi zonse kwa iwo ndi kuwayamikira moona mtima, pamene kuli koyenera, kungathandizenso kufeŵetsa mkhalidwe wawo wa maganizo. Ngati zimenezi zili zosatheka, mudzangofunikira kupirira ndi mkhalidwewo monga momwe mungathere.a

Zoonadi, ngati inu ndi kholo lanu muli Akristu ndipo iwo akuchita cholakwa china chachikulu, monga ngati kuledzera kapena kuchita ndewu, muyenera kutsimikizira kuti nkhaniyo yadziŵitsidwa kwa akulu a mpingo. (Yakobo 5:14) Kumeneku sikuli mchitidwe wa kusakhulupirika koma ndiko kuyesayesa kwachikondi kwa kutsimikizira kuti kholo lanulo lipeze thandizo limene ilo likufunikira kwambiri. Zoona, makolo ena alandula mwaukali za cholakwa chilichonse ndipo alanga ana mwamseri, koma achichepere amene ‘amva zoŵaŵa chifukwa cha chilungamo’ pankhaniyi ayenera kukhulupirira kuti Yehova amakondwera ndi kachitidwe kawo kolimba mtimako ndi kuti panthaŵi yake yoyenera, adzasonyeza choonadi poyera.—1 Petro 3:14; 1 Timoteo 5:24, 25.

Kumenyera Nkhondo Chipulumutso Chanu

Solomo anati: “Nsautso iyalutsa wanzeru.” (Mlaliki 7:7) Nzachisoni kunena kuti, achichepere ena akhala oŵaŵidwa mtima kwambiri ndi chitsanzo choipa cha makolo awo ndipo iwo nawonso ayamba kukhala ndi makhalidwe oipa. Ena akwiyiradi Mulungu ndipo asiya njira Yachikristu! (Miyambo 19:3) Baibulo limachenjeza: “Muchenjere, mkwiyo ungakunyengeni muchite mnyozo. Chenjerani, musalunjike kumphulupulu.”—Yobu 36:18-21.

M’malo mwa kuvutika mtima mopambanitsa ndi kaimidwe ka makolo anu ndi Mulungu, mufunikira ‘kugwira ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira.’ (Afilipi 2:12) M’nthaŵi zakale, kalonga wina wachichepere wotchedwa Hezekiya anachita motero pansi pa mikhalidwe yofananayo. Atate wake, Mfumu Ahazi, ananena kuti anali wolambira Yehova. (Yesaya 7:10-12) Kwenikweni iye anali wolambira milungu yachikunja, akumaperekadi mmodzi wa ana ake aamuna monga nsembe ya munthu! (2 Mafumu 16:1-4) Tangoganizani mmene mpatuko umenewu umene unaliko unasautsira Hezekiya wachichepereyo! Salmo 119:28, limene ena amakhulupirira kuti linalembedwa ndi kalonga wachichepere ameneyu, limati: “Moyo wanga wasungunuka ndi chisoni: mundilimbitse monga mwa mawu anu.”

Yehova anachitadi zimenezo! Pamene Hezekiya anadzipereka pa kupemphera ndi kuphunzira Mawu a Mulungu, mkhalidwe wake wauzimu wa iyemwiniyo unakula mosasamala kanthu za omzinga. (Salmo 119:97) Anasamalanso kwambiri ndi mabwenzi ake. (Salmo 119:63) Chotulukapo chake? Chinkana kuti anapatsidwa chitsanzo choipa ndi atate wake achinyengowo, Hezekiya mwiniyo “anaumirira Yehova.” (2 Mafumu 18:6) Chotero nanunso mungatero! Mwinamwake kholo lanu likuchita mwachinyengo, komano palibe chifukwa chimene muyenera kutsatirira chitsanzo chawo. Umirirani Yehova, ndipo mwina chitsanzo chanu chabata cha kukhulupirika, tsiku lina chidzasonkhezera kholo lanu kusintha.

Ngati mungakhale ndi mafunso alionse okhudza Baibulo pambuyo poŵerenga magazini ano, chonde khalani aufulu kufikira Mboni za Yehova pa Nyumba Yaufumu yakwanuko, kapena kulembera ofalitsa magazini ano. (Onani patsamba 5.)

[Mawu a M’munsi]

a Zimenezi sizikutanthauza kuti wachichepere ayenera kulekerera kumenyedwa kapena kugonedwa. Wachichepere amene ali mumkhalidwe wotero ayenera kufunafuna thandizo, ngakhale ngati zimenezo zingatanthauze kukalifunafuna kwina.

[Zithunzi patsamba 31]

Inu simufunikira kuchita molakwa chifukwa chakuti kholo lanu limatero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena