Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 11/8 tsamba 8-10
  • Kodi Ndizosangulutsa Zotani Zimene Mudzasankha?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndizosangulutsa Zotani Zimene Mudzasankha?
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Zitsogozo Zabaibulo Ndiziti?
  • Mmene Mungasankhire
  • Kodi Kupambanitsa Nkwakukulu Motani?
  • Zimene Zosankha Zanu Zimavumbula Ponena za Inu
  • Kodi Tingasankhe Bwanji Zosangalatsa?
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Kodi Mungasankhe Bwanji Zosangalatsa Zabwino?
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Muzisankha Zosangalatsa Zomwe Sizingakhumudwitse Yehova
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Mumasankha Zosangalatsa Mwanzeru?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 11/8 tsamba 8-10

Kodi Ndizosangulutsa Zotani Zimene Mudzasankha?

KUKHALA ndi lingaliro lachikatikati la zosangulutsa ndiko kanthu kena. Kusonyeza uchikatikati ponena za kuti ndizosanguluka zotani zimene tisankha ndinkhani inanso. Nkosavuta kwambiri kutsimikizira kuti zosangulutsa ziri ndi malo ake oyenera, koma zambiri za izo nzachabechabe ndi zongotaitsa nthaŵi. Chikhalirechobe, tiri ndi zosankha zatsiku ndi tsiku zoti tipange—ndipo sinthaŵi zonse pamene ziri zokhweka.

Monga momwe tawonera, indasitale ya zosangulutsa siimapangitsa kusankha kukhala kokhweka. Pali zosankha zochuluka kwadzawoneni, koma kwazaka zikwi zambiri, Baibulo lapatsa anthu owona mtima chitsogozo chimene afunikira. Luso lazopangapanga lamakono silinapangitse malamulo amakhalidwe abwino Abaibulo kukhala osagwira ntchito; mosiyana, ali othandiza kwambiri ndi ofunika m’nthaŵi zovuta zino koposa ndi kale lonse. Chotero tiyenitu tiwone mmene tingagwiritsirire ntchito malamulo amakhalidwe abwino oterowo ponena za mbali zowopsa ziŵiri za zosangulutsa—mkhalidwe wake ndi nthaŵi imene zimatenga.

Kodi Zitsogozo Zabaibulo Ndiziti?

Wachichepere akudzipha, ndipo kukudziŵika kuti iye anamwerekera kwambiri m’nyimbo za roko zosokosa kwambiri zimene zinalimbikitsa kudzipha. Msungwana wina wazaka 14 zakubadwa akukantha amake kufikira atafa, ndipo kukuwonekera kuti iye nayenso anamwerekera ndi nyimbo zosokosa. Mnyamata wina wazaka 15 zakubadwa akupha mkazi, ndipo loya wake akunena kuti anasonkhezeredwa ndi akanema oipa osonyeza chiwawa chowopsa. Kanema wosonyeza chiwawa cha timagulu akuyamba, ndipo timagulu ta achichepere tikumenyana pamalo osonyezera kanema pompo ndi pakati pa awo amene ali pamzere wolowera m’kanemayo.

Mwachiwonekere, mkhalidwe wa zosangulutsa zimene tisankha uli ndi chiyambukiro pa ife. Akatswiri ena angalandule zochitika zapamwambapa monga umboni wozikidwa pa zochitika zakamodzikamodzi ndi wosatsimikizirika. Komabe, malamulo amakhalidwe abwino Abaibulo, amathandiza kuchita ndi vutolo. Mwachitsanzo, talingalirani mawu amphamvu awa: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Kodi zosangulutsa zina sizimaterodi—kuyenda, kapena kuyanjana ndi, anthu amene ali zitsiru, kapena opanda pake mwamakhalidwe? Mofananamo, 1 Akorinto 15:33 imaŵerengedwa kuti: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” Amenewa sali mawu ovuta kumvetsetsa, palibe akatswiri okhala ndi malingaliro osiyana amene angatsutse umboni wa ziŵerengero. Liri lamulo losavuta la mkhalidwe wachibadwa wa anthu. Ngati tiyanjana ndi awo amene ali oluluzika mwamakhalidwe, zizolowezi za ife eni zidzayambukiridwa moipa.

Malamulo amakhalidwe abwino oterowo ngothandiza mofananamo ponena za kulambira ngwazi zamasewera, akanema, TV, ndi za nyimbo. Ngakhale kuti ngwazizo kaŵirikaŵiri zimatama chiwawa kapena chisembwere, ponse paŵiri m’masewera awo ndi m’miyoyo yawo, achirikizi awo—makamaka achichepere—akuwonekerabe kukhala akuwalambira. Nyuzipepala yotchedwa The European posachedwapa inati “Odziŵa zamaganizo akunena kuti m’chitaganya chadziko chomakulakulachi ngwazi zanyimbo za pop zingakhale zikukwaniritsa thayo limene panthaŵi ina linali kuchitidwa ndi chipembedzo m’miyoyo ya achichepere ambiri.” Koma tawonani zimene Salmo 146:3 limanena: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.” Ndipo Miyambo 3:31 imati: “Usachitire nsanje munthu wachiwawa; usasankhe njira yake iriyonse.”

Lamulo lamakhalidwe abwino lina lalikulu nlakuti: Popanga zosankha, Akristu ayenera kulingalira chiyambukiro osati kokha pa iwo eni komanso pa ena mumpingo Wachikristu, kuphatikizapo awo amene ali ndi zikumbumtima zanthete koposerapo. (1 Akorinto 10:23-33) Kumbali yabwino, malamulo amakhalidwe abwino Abaibulo amatithandizanso kukhazikitsa miyezo ya zosangulutsa zimene tingasankhepo motetezereka. Mtumwi Paulo anapereka uphungu wakuti: “Chotsalira, abale, zinthu ziri zonse zowona, ziri zonse zolemekezeka, ziri zonse zolungama, ziri zonse zoyera, ziri zonse zokongola, ziri zonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.”—Afilipi 4:8.

Malamulo amakhalidwe abwino amenewa atsogoza anthu a Mulungu kwazaka mazana ambiri. Akristu a m’Roma wakale sanafunikire lamulo lachindunji lowauza kuti masewera okhetsa mwaziwo, limodzi ndi kuphana kwake konse ndi nkhalwe zopambanitsazo, sizinali zosangulutsa zoyenera. Iwo anangogwiritsira kokha malamulo amakhalidwe abwino onga apamwambapawa ndipo mwa kutero anadzitetezera iwo eni, mabanja awo, ndi mipingo yawo.

Mmene Mungasankhire

Akritsu owona amachita zofananazo lerolino. Posankha zosangulutsa, iwo amapenda choyamba mkhalidwe wake wamakhalidwe, Motani? Eya, mwachitsanzo, asanagule rekode, amawona chikuto chake. Kodi nyimboyo ikutsatsidwa malonda motani? Kodi imachilikiza makhalidwe oluluzika? Udani? Chipanduko? Mkwiyo? Chisembwere kodi ndi chinyengo? Nthaŵi zina mawu amapezeka kuti apendedwe. Mofananamo, zikuto zamabukhu kaŵirikaŵiri ziri ndi mawu achidule a zamkati, ndipo nthaŵi zina mfundo zazikulu zimakhala zopezeka. Ponena za akanema nawonso kaŵirikaŵiri pamakhala mawu achidule m’manyuzipepala ndi magazini amomwemo. Maiko ena amapereka madongosolo openda akanema amene angathandizire kupeza zitsogozo. Mwachiwonekere, ngati dziko loluluzika lamakonoli lipeza zosangulutsa zina kukhala zopambanitsa kwambiri m’zakugonana, chisembwere, kapena chiwawa, nkovuta kuganiza kuti Mkristu akadziikira muyezo wotsika ndi kuzilowetsa mofunitsitsa m’maganizo ndi mtima wake.

Kumbali ina, Mfumu Solomo yanzeruyo panthaŵi ina inachenjeza kuti: “Usapambanitse kukhala wolungama; usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziwononga wekha?” (Mlaliki 7:16) Kudzilungamitsa ndiko msampha wosavuta kwambiri kugweramo ponena za zosangulutsa. Tingakhale ndi lingaliro lamphamvu ponena za chosankha chimene tapanga, pokhala titapenda mosamalitsa ndi mwapemphero malamulo amakhalidwe abwino Abaibulo. Komabe, tingapeze kuti ena amene amagwiritsira ntchito malamulo amakhalidwe abwino amodzimodziwo akusankha mosiyana pang’ono. Musalole zimenezo kukuberani chisangalalo. Aliyense wa ife ayenera kukhala ndi thayo la zosankha za iyemwini.—Agalatiya 6:4.

Kodi Kupambanitsa Nkwakukulu Motani?

Dongosolo lopendera ladziko nlosayerekezereka momvetsa chisoni ponena za zinthu zofunika zimene limawona kukhala zosangulutsa. Mwachitsanzo, nkhani yamkonzi yaposachedwapa m’magazini azamalonda akuti Parks & Recreation inatcha kusanguluka kukhala “mbali yaikulu ya kukhala ndi moyo.” Mofananamo, The New York Times Magazine posachedwapa inalankhula za usiku wa Loweruka, nthaŵi yotchuka ya kukasanguluka kuti: “Ngati muwawonkhetsa, pali masiku ena ambiri a pamlungu m’miyoyo yathu koposa mausiku a pa Loweruka okha, koma usiku wa Loweruka ndiwo wofunikira kukhalira moyo.” Akatswiri ena amakhalidwe a anthu akuwiringuladi kuti m’maiko olemera koposerapo a dziko, chitaganya tsopano chazikidwa pa zosangulutsa, pokhala chipembedzo chenichenicho chiri kokha ntchito ya panthaŵi yosanguluka ina.

Akristu samadabwa ndi chisokonezo cha zoikidwa pamalo oyamba molakwa chimenechi. Baibulo kalekale lidaneneratu kuti mu “masiku otsiriza” oŵaŵitsa amenewa, anthu akakhala “odzikonda okha, . . . okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” (2 Timoteo 3:1-4) Koma malamulo amakhalidwe abwino Abaibulo amatithandiza kuika zinthu zofunika zathu zazikulu pamalo oyenera. Monga momwe Yesu adanenera kuti, “uzikonda Ambuye [Yehova NW] Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse.” (Marko 12:30) Chotero, kwa anthu a Mulungu, kumkonda kwawo kumadza poyamba m’moyo. Mosiyana kwambiri ndi kupambutsira uminisitala wawo Wachikristu kuntchito zapanthaŵi yosanguluka, ndichinthu chokhala pamwamba mumpambo wa zofunika zawo. Ngakhale ntchito yawo yakudziko imachirikiza kokha ntchito yofunika imeneyo.—Mateyu 6:33.

Chotero ponena za zosangulutsa, Mkristu ayenera kuŵerengera mtengo, kuwona kuti ndinthaŵi yochuluka motani imene zidzatenga poiyerekezera ndi nthaŵi imene zifunikira. (Luka 14:28) Ngati kulondola zosangulutsa kulikonse kudzatanthauza kunyalanyaza zinthu zofunika, zonga phunziro Labaibulo laumwini kapena labanja, nthaŵi ya kukhala limodzi ndi okhulupirira anzathu, uminisitala Wachikristu, kapena mathayo aakulu abanja, pamenepo sizofunikira mtengowo.

Zimene Zosankha Zanu Zimavumbula Ponena za Inu

Kuchuluka kwa nthaŵi imene timathera m’zosangulutsa kudzavumbula zambiri ponena za zimene timaika poyamba, monga momwe mkhalidwe wa zosangulutsa zimene tisankha udzavumbulira zambiri ponena za makhalidwe athu ndi kuwona mtima kwa kudzipereka kwathu. Zosankha zathu zidzauza anthu m’chitaganya mtundu wa anthu amene ife tiri, makhalidwe amene timachirikiza. Zosankha zathu zidzauza mabwenzi athu, banja lathu, ndi mpingo wathu kuti kaya tiri achikatikati kapena ouma, owona mtima kapena onyenga, olungama kapena odzilungamitsa.

Zosankha zanu zisonyezetu chimene inu ndi banja lanu muli, pamene muimirira pamaso pa Mlengi, amene amapenda mitima ndi zolinga za tonsefe. Ahebri 4:13 amati: “Ndipo palibe cholengedwa chosawonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.” Mulungu yekha ndiye amene angawone yankho la funso lalikulu m’nkhani ino: Kodi tidzatsogozedwadi ndi malamulo ake amakhalidwe abwino m’mbali iriyonse ya moyo?

[Chithunzi patsamba 8]

Zosangulutsa zimene musankha zimavumbula zambiri ponena za inu ndi banja lanu

[Chithunzi patsamba 9]

Kodi mumasamala ponena za zimene mumapenyerera, kumvetsera, ndi kuŵerenga?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena