Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb19 June tsamba 7
  • Kodi Mumasankha Zosangalatsa Mwanzeru?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumasankha Zosangalatsa Mwanzeru?
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Nkhani Yofanana
  • Muzisankha Zosangalatsa Zomwe Sizingakhumudwitse Yehova
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Tingasankhe Bwanji Zosangalatsa?
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Kodi Mungasankhe Bwanji Zosangalatsa Zabwino?
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Mukhoza Kupeza Zosangulutsa Zabwino
    Galamukani!—1997
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
mwb19 June tsamba 7

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mumasankha Zosangalatsa Mwanzeru?

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala tikamasankha zosangalatsa? Chifukwa chake n’chakuti tikamasankha mafilimu, nyimbo, mawebusaiti, mabuku komanso masewera a pakompyuta, timakhala tikusankha zinthu zoti tilowetse m’maganizo athu. Zimene timasankha zimakhudza khalidwe lathu. N’zomvetsa chisoni kuti zosangalatsa zambiri masiku ano zimakhala ndi mbali zina zomwe Yehova amadana nazo. (Sal. 11:5; Agal. 5:19-21) N’chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziganizira zinthu zimene zingalemekeze Yehova.​—Afil. 4:8.

ONERANI VIDIYO YAKUTI KODI NDIYENERA KUSANKHA ZOSANGALATSA ZOTANI? KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Katswiri wochita masewera achiwawa ku Roma

    Kodi masewera achiwawa omwe Aroma ankachita akufanana bwanji ndi zosangalatsa za masiku ano?

  • Mpainiya wachinyamata akulalikira limodzi ndi mnzake wina wamumpingo

    Kodi abale ndi alongo a mumpingo angathandize bwanji achinyamata kusankha bwino zosangalatsa?

  • Msilikali

    Kodi lemba la Aroma 12:9 lingatithandize bwanji kuti tizisankha zosangalatsa mwanzeru?

  • Achinyamata a Mboni akusewera mpira

    Kodi ndi zosangalatsa zabwino ziti zomwe zimapezeka m’dera lanu?

MUZISONYEZA LUSO LANU

Zosangalatsa zambiri masiku ano zimachititsa kuti munthu azingokhala. Mwachitsanzo, mukamaonera mafilimu, TV kapena mukamawerenga mabuku, mumakhala mukusangalala ndi luso la anthu ena. N’zoona kuti kuchita zimenezi si kulakwa. Koma mungasangalale kwambiri ngati mutasankha zosangalatsa zomwe inunso mukhoza kusonyezapo luso lanu. Mwachitsanzo, ena amasangalala akamaimba nyimbo ndi chida chinachake kapena akamajambula zinthu pamanja. Ena amakonda kusewera mpira kapena kuchita masewera ena. Kaya tasankha zosangalatsa zotani, tiyenera ‘kuchita zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.’​—1 Akor. 10:31.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena