Kanthu Kabwino Koposa Kupatsa kwa pa Krisimasi
“CHRISTOPHER wazaka zisanu ndi chimodzi zakubadwa anandiuza kuti ‘samalandira kalikonse’ pa Krisimasi, ngati kuti zimenezo ndizo zoyenerera koposa m’dziko. Koma analankhula mosakhumudwa konse. Alexander [wazaka] (8) ananena zofanana, kuti: ‘Ndife Mboni za Yehova.’”
Umu ndimmene nyuzipepala ya ku Jeremani ya Kölner Stadt-Anzeiger inayambira nkhani yonena za banja limene pepalalo linati “limanyalanyaza Krisimasi chifukwa chakuti sindilo deti la kubadwa kwa Yesu ndipo chifukwa chakuti magwero ake ngachikunja.” Koma kodi Christopher ndi Alexander sayenera kuchitiridwa chifundo? Kutalitali, pakuti, monga momwe nkhaniyo inasonyezera, mashelufu a zoseŵeretsa za anyamatawo samasonyeza umboni wa kunyalanyazidwa ndi makolo.
Komabe, makolo ena opezeka pamakambitsirano a makolo ndi aphunzitsi kummwera kwa Jeremani ananena motsimikiza kuti kusalandira mphatso za Krisimasi kwa ana a Mboni za Yehova kumawachititsa kudzimva osatetezereka. Komabe, zimenezi sizowona, monga momwe mphunzitsi wawo ananenera. Iye anati “ana a Mboni za Yehova amalankhula momasuka, ngokhazikika, ndipo amakhoza kwambiri kulongosola chikhulupiriro chawo, zimene ana ena sangachite.”
Ndithudi, mabanja zikwi makumi ambiri padziko lonse aika m’malo mwa Krisimasi kanthu kena kabwino, akumatsimikiza kupatsa ana awo mphatso chaka chonse. Zimenezi zakhaladi magwero a chimwemwe cha onse.
Phindu lina nlakuti kumachititsa nthaŵi zochuluka za chisangalalo chaka chonse, ndipo ana amayamikira kwambiri mphatso iriyonse. Phindu lina nlakuti ana amadziŵa kuti ali makolo awo amene akuwapatsa mphatsozo chifukwa cha chikondi, ndipo chiyamikiro chawo chimamka kwa iwo. Makolo samawononga ndalama ndi nyonga kokha kuti achititse chiyamikiro cha ana awo kupita kwa Santa Claus wongopeka kapena kuwachititsa kukhala osayamika, akumalingalira kuti liri thayo la Santa kubweretsa mphatso ndi kuti sipayenera chiyamiko.
Mphatso ya Mtengo Wapatali
Kaŵirikaŵiri Dominik, wazaka khumi, ndi Tina, wazaka zisanu ndi chimodzi, amapeza tinthu tating’ono tosayembekezera tochokera kwa makolo awo—chokoleti pamtsamiro, peni kapena bukhu lolembamo kusukulu, kapena choseŵeretsa choyenera chowatanganitsa m’miyezi ya chisanu. Koma kodi nchiyani chimene iwo amayamikira kwambiri? Makolo awo akuyankha kuti: “Pamene tikhala nawo—mwachitsanzo, poseŵera m’chipale chofeŵa.”
Makolo ambiri amene ali Mboni za Yehova amavomereza zimenezi. “M’dzikoli lotanganitsa,” Edelgard akufotokoza motero, “nthaŵi ndiyo chinthu chofunika koposa chimene ndingapatse ana anga.” Ndipo ana amavomereza! Ursula akunena kuti ana ake amaŵerengera nthaŵi imene amakhalira pamodzi pamaulendo a banja okacheza kukhala “yabwino koposa.” Ngakhale tcheyamani wa bungwe la aphunzitsi ku Jeremani posachedwapa anati mphatso za pa Krisimasi zabwino koposa zimene makolo angapatse ana awo ndizo nthaŵi ndi kuleza mtima.
Mosakaikira, kudzipereka kwa munthuwe—nthaŵi, chikondi, ndi chisamaliro chako—kaya kukhale kubanja la munthuwe kapena kumabwenzi ako, ndiko mphatso ya mtengo wapatali ndithu. Kuyenera kukhala kwachiwonekere kuti mphatso zotero siziyenera kulekezera pamasiku ena a chaka.
Kupatsa Kwachimwemwe Kumene Kumakhutiritsa
Lingalirani zitsanzo za Mboni za Yehova zimene zimatenga mbali m’kanthu kena kabwino koposa kupatsa kwa pa Krisimasi. Wilfried ndi Inge a ku Jeremani anati: “Kaŵirikaŵiri timapereka mphatso nthaŵi iriyonse imene timasonkhezeredwa kutero, ngakhale kuti timalinganiza zina zazikulu.” Mofananamo, Dieter ndi Debora amachita kuyesayesa kwamphamvu kugaŵira mphatso mwana wawo wamng’ono nthaŵi iriyonse ya chaka. Iwo akufotokoza kuti “ukulu kapena mtengo wa mphatsoyo ngwosafunikira, ndipo mphatso zazikulu kapena zouma mtengo nzakamodzikamodzi.”
Ana ambiri amayembekezera mphatso panthaŵi ya Krisimasi, choncho mkhalidwe wa kulandira kanthu mosayembekezera umataika. Helga akuti “ana ake amakondwera kwabasi atalandira mphatso zosayembekezera koposa pamene alandira zinthu panthaŵi imene mphatso zimayembekezeredwa.” Natascha, wazaka 15 zakubadwa, akuvomereza kuti “nkwabwino kwambiri kulandira mphatso yosayembekezera yochokera mumtima koposa yopatsidwa panthaŵi yoikidwiratu chifukwa chakuti mwambo ukufuna zimenezo.”
Mofananamo, nkofunika kukhala maso ponena za mtundu wa mphatso zimene ana amakonda. Pankhaniyi, Fortunato, amene amakhalanso ku Jeremani, akuti: “Mphatso zimene timapereka ziri kwakukulukulu zinthu zimene ana asonyeza kuti angakonde kukhala nazo. Koma timayesa kuwapatsa panthaŵi yosayembekezereka. Amakondwera chotani nanga!”
Ndiponso makolo amawona kuti kupatsa ana mphatso pamene akudwala panyumba kumawasangalatsa. Ena amapereka mphatso tchuti cha sukulu chisanayambe kuti athandize ana kupeza chochita. Mwachitsanzo, tchuti chisanayambe, Stefan anapatsidwa maikrosikopo. “Sanaiyembekezere konse,” atate ake akutero, “ndipo analumphadi ndi chimwemwe.” Ndithudi, kupatsa kwapanthaŵi iriyonse, kosakakamiza kumadzetsa chimwemwe chachikulu kwa onse aŵiri wopatsayo ndi wolandira.
Zowona, ana ali ndi zimene amakonda. Jörg ndi Ursula akufotokoza kuti: “Pamene mwana wathu wamkazi atiuza chimene akufuna, timakambitsirana naye chinthucho. Kodi chimene akufuna nchotchipa? Kodi chinthucho nchoyenerana ndi msinkhu wake? Kodi tiri ndi malo oika m’nyumba? Ngati sitingakwanitse chimene afuna panthaŵiyo, timachisungabe m’maganizo ndi kuyesa kuchichita panthaŵi yoyenerera pambuyo pake.” Ndithudi, sikuli kwanzeru kupusitsa ana mwa kukhutiritsa zokhumba zawo zirizonse, kumene kungawalande chimwemwe chimene kulandira mphatso kumadzetsa.
Makolo amene ali ndi chizoloŵezi cha kupatsa amapitirizira kwa ana awo mzimu umene udzasonyezedwa mwachimwemwe. Sebastian wazaka khumi zakubadwa akunena kuti: “Sindimatoyembekezera maholide kuti ndisangalatse makolo kapena alongo anga. Ndimangofunikira kukhala mumkhalidwe wabwino ndi kukhala ndi ndalama zochepa m’thumba.”
Mabanja a Mboni za Yehova amawona kuti mphatso za mtundu wina zirinso zabwino koposa kupatsa kwa pa Krisimasi. Zimenezi ndizo maulendo kapena timaulendo tolinganizidwa, tinene kuti kupita kumalo osungira zinyama, myuziyamu, chiwonetsero, kapena malo akumidzi. Mphatso zimenezi ziri ponse paŵiri zophunzitsa ndi zosangalatsa kwambiri kwa achichepere.
Madalitso a Kupatsa Kwachimwemwe
Mwakugwiritsira ntchito malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo pakupatsa, tidzapeŵa chitsenderezo ndi kugwiritsidwa mwala kumene kumadzetsedwa ndi kupatsa kwa pa Krisimasi. Ndipo kumbukirani, kupereka nthaŵi yathu ndi maluso kulimbikitsa ndi kumangirira ena mwamaganizo ndi kuuzimu kuli mphatso yamtengo wapatali koposa mphatso zakuthupi. Kupatsa kopambana kumeneku kumalimbitsa maunansi a banja, kumamangirira maubwenzi, ndipo kumadzetsa chimwemwe chenicheni nthaŵi iriyonse ya chaka osati chabe kwa wolandira koma makamaka kwa wopatsa.—Machitidwe 20:35.
Chotero mmalo mwa kupatsa kwamwambo kokakamiza kwa panthaŵi ya Krisimasi chaka chino, bwanji osayesa njira ina yosiyana? Bwanji osayesa njira yabwino koposa?
[Bokosi patsamba 12]
Koma Kodi Ana Sadzailakalaka?
Rebecca, wazaka 16, akuti: “Sindimalakalaka Krisimasi, chifukwa chakuti ndimalandira mphatso nthaŵi iriyonse ya chaka. Ndimakonda kwambiri mphatso yosayembekezera koposa yokakamiza.”
Tina, wazaka 12, akuti: “Ndimakondwera kwambiri kulandira mphatso zoyenera, osati panthaŵi yoikidwiratu, koma panthaŵi iriyonse ya chaka—ndipo osati mphatso zimene ndiyenera kuyamikira ngakhale kuti sindizifuna.”
Birgit, wazaka 15, akuti: “Mphatso zonse zimene mungalandire zimakhala zachabechabe ngati m’mbanja muli mavuto. Nchifukwa chake timachitira zinthu zambiri pamodzi monga banja.”
Janosch, wazaka 12, akuti: “Anafe timakonda makolo athu ngakhale pamene satipatsa mphatso zirizonse. Chikondi chawo chenichenicho ndicho mphatso yaikulu koposa.”
[Chithunzi patsamba 10]
Mphatso yabwino kwambiri—nthaŵi yanu!