Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 12/15 tsamba 3-4
  • Kupatsa—Kodi Amakuyembekezera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupatsa—Kodi Amakuyembekezera?
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Kanthu Kabwino Koposa Kupatsa kwa pa Krisimasi
    Galamukani!—1993
  • Kodi Kupatsa kwa pa Krisimasi Nkwanzeru?
    Galamukani!—1993
  • “Choonadi Chidzakumasulani”
    Galamukani!—2010
  • Krisimasi—Kodi Ilidi Yachikristu?
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 12/15 tsamba 3-4

Kupatsa​—Kodi Amakuyembekezera?

MWINA inu mungakhale mukudziŵa bwino kuti kaŵirikaŵiri kupereka mphatso kumachitidwa molamulidwa ndi mwambo. M’mafuko ochuluka pali nthaŵi pamene anthu amayembekezera mphatso. Mphatso zimenezo zingakhale chizindikiro cha kupereka ulemu kapena kusonyeza chikondi. Zambiri za zimenezi sizimagwiritsiridwa ntchito ndi wolandira; zina zimakhala zothandiza pa zofunika zina zenizeni ndipo zimayamikiridwa kwambiri.

Ku Denmark pamene mwana abadwa, mabwenzi ndi achibale amafika atanyamula mphatso zimene akukhulupirira kuti zidzakhala zothandiza khandalo. M’maiko ena, mabwenzi amalinganiza phwando limene amaperekapo mphatso zimenezo poyembekezera kubadwa kwa mwana.

Kaŵirikaŵiri, nthaŵi zimene mphatsozo zimayembekezeredwa kuperekedwa, ndizo zochitika zapachaka. Ngakhale kuti mapwando otero sanali kuchitidwa pakati pa Akristu oyambirira, iwo akhala otchuka kwambiri pakati pa anthu onena kuti ali Akristu ndiponso osakhala Akristu. Mchitidwe wa kupereka mphatso patsiku la kubadwa mwina ungakhale ukuzimiririka m’mafuko ena pamene ana akukula, koma mwambo pakati pa Agiriki ngwolimba kwambiri. Ku Greece anthu amasamala kwambiri masiku a kubadwa. Amaperekanso mphatso kwa munthu pa “tsiku la dzina” lake. Nchiyani chimenecho? Aha, mwambo wachipembedzo umagwirizanitsa “woyera mtima” wina ndi tsiku lililonse la chaka, ndipo anthu ambiri amapatsidwa maina a “oyera mtima” ameneŵa. Pamene tsiku la “woyera mtima” lifika, aja amene ali ndi dzinalo amalandira mphatso.

Kuwonjezera pa kukondwerera masiku a kubadwa a ana awo, Akoreya ali ndi tsiku lapadera la dzikolo lotchedwa kuti Tsiku la Ana. Imeneyi ndi nthaŵi pamene mabanja amapita kokacheza ndi pamene ana amapatsidwa mphatso mosasamala kanthu za tsiku limene anabadwa. Akoreya alinso ndi Tsiku la Makolo, pamene ana amapereka mphatso kwa makolo awo, ndiponso Tsiku la Aphunzitsi, pamene ophunzira amachitira ulemu aphunzitsi awo ndi kuwapatsa mphatso. Malinga ndi mwambo Wachikoreya, pamene munthu afika zaka 60, amamchitira phwando lalikulu. Banja ndi mabwenzi amagwirizana kumfunira umoyo wautali ndi chimwemwe, ndipo mphatso zimaperekedwa kwa munthu amene wafika usinkhuwo.

Phwando la ukwati ndilo nthaŵi ina pamene mwambo wofala umafuna kuti anthu apereke mphatso. Pamene anthu akwatirana ku Kenya, banja la mkwati limayembekezeredwa kupereka mphatso kubanja la mkwatibwi. Oitanidwa nawonso amabweretsa mphatso. Ngati mkwati ndi mkwatibwi akufuna kutsatira zimene mwambo umafuna, amakhala pa pulatifomu, pamene oitanidwa amabwera kudzawapatsa mphatso zawo. Pamene mphatso iliyonse iperekedwa, amalengeza kuti “A uje apereka mphatso kwa okwatiranawa.” Opereka mphatso ambiri samakondwera ngati sanayamikiridwe.

Pakati pa Alebano, wina akaloŵa muukwati, mabwenzi ndi anansi, ngakhale anthu amene sakuwadziŵa bwino anthu okwatiranawo, amafika ndi mphatso pambuyo pa masikuwo. Kuyambira paubwana, iwo amaphunzitsidwa kuti kupereka mphatso ndiko thayo, monga ngati mmene zilili ndi kulipira ngongole. “Ngati suchita zimenezi, sumapeza bwino,” anatero mwamuna wina Wachilebano. “Ndi mwambo wathu.”

Komabe, pazochitika zonse pamene anthu amayembekezeredwa kupereka mphatso m’maiko ambiri, Krisimasi ndiyo chochitika chachikulu. Kodi zimenezo sizili choncho kumene mumakhala? Posachedwapa mu 1990, kunayerekezeredwa kuti Aamereka amathera ndalama pafupifupi $40 biliyoni pa mphatso za Krisimasi chaka chilichonse. Abuda ndi Ashinto amasunga holide imeneyinso ndi chikondwerero chachikulu ku Japan, ndipo njira zosiyanasiyana za kuikondwerera kwake zimapezeka mu Ulaya, South America, ndi mbali zina za Afirika.

Krisimasi ndi nyengo pamene anthu amayembekezera kukhala achimwemwe, koma ambiri samatero. Ndipo ambiri amapeza kuti kugula mphatso konyanyuka ndi nkhaŵa yonena za kulipirira ngongole zake zimaphimba chikondwerero chilichonse chakanthaŵi chimene amakhala nacho.

Komabe, Baibulo limati muli chimwemwe m’kupatsa. Zoonadi chilimo, zikumadalira pa mzimu wa kupatsako.​—Machitidwe 20:35.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena