Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 10/8 tsamba 9
  • Ngati Mwana Wanu Wagonedwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ngati Mwana Wanu Wagonedwa
  • Galamukani!—1993
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Mungatetezere Ana Anu
    Galamukani!—2007
  • Tizisonyeza Chikondi ndi Chilungamo M’dziko Loipali
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Mabala Obisika a Kuchitira Nkhanza Ana
    Galamukani!—1991
  • Chitetezo m’Nyumba
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 10/8 tsamba 9

Ngati Mwana Wanu Wagonedwa

KUTI muletse nkhanza yogona ana, muyenera kuidziŵa mutaiona. M’mabuku ambiri pankhaniyi, akatswiri andandalika zizindikiro zambiri zodziŵira nkhanza yogona ana zimene makolo ayenera kuona. Zimenezi zimaphatikizapo: madandaulo akumva kupweteka pokodza kapena pochita chimbudzi, matenda a kumpheto, zilonda kumpheto, kuyamba kukodzera pabedi mwadzidzidzi, kusamva njala kapena mavuto ena a kadyedwe, kusonyeza chilakolako cha kugonana, mantha amwadzidzidzi a malo onga ngati kusukulu kapena mbali zina za nyumba, nyengo za kutekeseka, kuwopa kwambiri kuvulidwa zovala, kuwopa kukhala yekha ndi munthu amene samdziŵa, ndi kudzivulaza.

Koma musafulumire kuganiza zimene palibe. Zambiri za zizindikiro zimenezi mwa izo zokha sizimatanthauza kwenikweni kuti mwanayo wagonedwadi. Chizindikiro chilichonse chingasonyeze vuto lina losiyana. Koma ngati muona zizindikiro zovutitsa mwa mwana, kambitsiranani nkhaniyo mofatsa, mwinamwake ndi mawu onga: “Ngati munthu aliyense akukhudza mwanjira imene sumamva bwino, ndifuna kuti udziŵe kuti ukhoza kundiuza nthaŵi iliyonse, ndipo ndidzachita zilizonse zimene ndingathe kukutetezera. Kodi zimenezi zinakuchitikirapo?”—Miyambo 20:5.

Ngati mwana wanu avumbula kuti anagonedwa, inu mosakayikira mudzakwiya kwambiri. Koma kumbukirani: Njira imene mudzachitira idzakhala ndi chiyambukiro chachikulu pakuchira kwa mwanayo. Mwana wanu wakhala akunyamula mtolo wosasenzeka ndipo akufuna inu, ndi mphamvu zanu zonse zauchikulire, kuti muuchotse pamapeŵa pake. Mthokozeni mwanayo chifukwa cha kulimba mtima kwake pokuuzani zimene zinachitika. Mlimbikitseni mwanayo mobwerezabwereza kuti mudzachita zimene mungathe kumtetezera; kuti nkhanzayo ndimlandu wa yemwe anamgona, osati wa mwanayo; kuti mwanayo sali “woipa”; kuti mumamkonda mwanayo.

Akatswiri ena a zamalamulo amalangiza kukanena nkhanzayo kwa apolisi mwamsanga ndithu. M’maiko ena mabungwe a malamulo angafune zimenezi. Koma m’malo ena mabungwe amalamulo angapereke chiyembekezo chochepa cha kuzenga mlanduwo mwachipambano.

Komabe, bwanji ngati wogona mwanayo ndimwamuna wanu? Mwachisoni, akazi ambiri amalephera kuchitapo kanthu mwamphamvu. Ndithudi, kuli kovuta kwambiri kuyang’anizana ndi chowonadi choŵaŵa chakuti mwamuna wanu ali wogona ana. Unansi wachikondi, ndipo ngakhale kumdalira m’zandalama kungakhale kolimba. Mkazi wolakwiridwa angazindikirenso kuti kuchitapo kanthu kungachititse mwamuna wake kutayikiridwa ndi banja lake, ntchito yake, ndi mbiri yake yabwino.a Komabe, chowonadi nchakuti angakhale akututa zimene wafesa. (Agalatiya 6:7) Kumbali ina, ana opanda liŵongo akhoza kutayikiridwa zambiri ngati sakhulupiriridwa ndi kutetezeredwa. Mtsogolo mwawo monse muli pangozi. Iwo alibe nyonga yochitira ndi mavuto imene achikulire ali nayo. Kusweka mtima kungawawononge ndi kuwaumba moipa kwa moyo wonse. Ndiwo afunikira ndi kuyenerera kuchitiridwa mokoma mtima.—Yerekezerani ndi Genesis 33:13, 14.

Chotero makolo ayenera kuchita kuyesayesa kulikonse koyenera kutetezera ana awo! Makolo ambiri osamala amasankha kufuna chithandizo cha akatswiri cha mwana wogonedwa. Monga momwe mungachitire ndi dokotala weniweni, tsimikizirani kuti katswiri aliyense wotero adzalemekeza zikhulupiriro zanu zachipembedzo.b Thandizani mwana wanu kukulitsanso ulemu wake wowonongedwawo mwakupitiriza mosaleka kumsonyeza chikondi cha ukholo.

[Mawu a M’munsi]

a Kwenikweni, wogona mwanayo ali kale m’vuto ndipo afunikira chithandizo kwambiri. Ngakhale ngati wogona mwanayo apepesa, wamuukwati wolakwiridwa angalingalire kuti: Nchifukwa ninji sanaulule asanavumbulidwe ndi yemwe anagonedwa?

b Mwachitsanzo, pamene Mboni za Yehova ziyang’anizana ndi zosankha zokhudza kuthira mwazi, zimatsimikizira kuti dokotala adzalemekeza zikhulupiriro zawo zachipembedzo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena