Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 10/8 tsamba 15
  • Mboni za Yehova Zilemekezedwa Pankhondo ya Kuyenera kwa Kusunga Ana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mboni za Yehova Zilemekezedwa Pankhondo ya Kuyenera kwa Kusunga Ana
  • Galamukani!—1993
  • Nkhani Yofanana
  • Kumenyera Ufulu Wolambira Mulungu Momasuka
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • Kuteteza Uthenga Wabwino Mwalamulo
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Mboni za Yehova ‘Ziperekedwa kwa Akulu Amilandu’
    Galamukani!—1992
  • Olalikira Ufumu Anayamba Kupititsa Milandu Yawo Kukhoti
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 10/8 tsamba 15

Mboni za Yehova Zilemekezedwa Pankhondo ya Kuyenera kwa Kusunga Ana

INGRID HOFFMANN wakhala akumenya nkhondo kuti apatsidwe kuyenera kwa kusunga ana ake aŵiri chiyambire pakati pa zaka khumi zapitazo. Iye ndimkazi wa ku Austria, anabadwa ndi kuleredwa monga Mroma Katolika. Anakwatiwa kwa Mkatolika mnzake, nabala mwana wamwamuna mu 1980 ndi wamkazi mu 1982. Koma mu 1983 iwo anasudzulana; makolo onse aŵiriwo anafuna kupatsidwa kuyenera kwa kusunga anawo. Tateyo anapereka chifukwa chakuti chipembedzo cha mayiyo—anali atakhala mmodzi wa Mboni za Yehova—chikawononga anawo, chikawalepheretsa kukula ndi nzeru zabwino. Iye anatchula nkhani zonga ngati kukana kwa Mboni kukondwerera maholide ofala m’dziko lake ndi kukana kwawo kuthiridwa mwazi.—Machitidwe 15:28, 29.

Zifukwa zamachenjera zimenezi zinalephera kukhutiritsa bwalo lamilandu. Onse aŵiri, bwalo lamilandu lopenda mlandu ndi lozenga mlandu, anatsutsa zinenezo za tateyo napatsa mayiyo kuyenera kwa kusunga ana. Komabe, mu September 1986, bwalo lamilandu la Supreme Court of Austria linasintha ziweruzo za bwalo lamilandu laling’onolo. Linanena kuti ziweruzo zimenezo zinaswa lamulo la Austrian Religious Education Act, limene limalamula kuti ana obadwa kwa Akatolika ayenera kuphunzitsidwa monga Akatolika. Bwalo lamilandulo linanenanso kuti sikukakhala kopindulitsa kwa anawo ngati akaloledwa kuleredwa monga Mboni za Yehova!

Kodi Ingrid Hoffmann anatenga njira yotani motsutsana ndi tsankho lachipembedzo lapoyera loterolo? Mu February 1987 mlandu wake unaperekedwa ku bungwe la European Commission of Human Rights. Pa April 13, 1992, bungwe limeneli, alopangidwa ndi oweruza oimira maiko osiyanasiyana amene ali ziŵalo za gulu la Council of Europe, linatumiza mlanduwo kuti ukamvedwe wonse pamaso pa bwalo lamilandu la European Court of Human Rights.

Bwalo lamilandulo linapereka chigamulo pa June 23, 1993. Ilo linati: “Bwalo lamilandu la European Court likuvomereza kuti pakhala kusiyana m’kusamalira mlanduwu ndipo kusiyanako kunazikidwa pachipembedzo; mfundo imeneyi ikuchilikizidwa ndi kamvekedwe ndi kalembedwe ka mawu a zifukwa zoperekedwa ndi Supreme Court [ya Austria] ponena za ziyambukiro zotsatirapo za chipembedzo cha wochita apiloyu. Kusiyana m’kusamalira mlandu kotereku kuli kwatsankho.” [Kanyenye ngwathu.] Linapitiriza kunena kuti Supreme Court “inapenda mfundozo mosiyana ndi mabwalo amilandu aang’onowo, amene malingaliro awo anachilikizidwa ndi lingaliro laukatswiri wa malingaliro. Mosasamala kanthu za zifukwa zilizonse zimene zingaperekedwe motsutsana ndi zimenezo, chiweruzo chozikidwa kwakukulukulu pa kusiyana kwa zipembedzo kokha sichovomerezeka.”

Mwa voti la asanu kwa anayi, oweruzawo anaweruza moyanja Ingrid Hoffmann ndi kutsutsa Austria, akumanena kuti, kwenikweni, Austria anachita mwatsankho kwa mkaziyo pamaziko a chipembedzo chake ndi kulakwira kuyenera kwake kwa kulera banja lake. Ndiponso, mwa voti la asanu ndi atatu kwa mmodzi, oweruzawo analamula kuti mkaziyo anafunikira kupatsidwa faindi ya ndalama.

Chilakiko chapadera chimenechi cha ufulu wa chipembedzo chinafika patapita mwezi umodzi wokha pambuyo pa chilakiko china m’bwalo lamilandu limodzimodzilo—mlandu wa pakati pa Kokkinakis (ndi boma la) Greece, umene unasonyeza kuti Greece anaswa kuyenera kwa munthu wina kwa kuphunzitsa Mawu a Mulungu kunyumba ndi nyumba. Okonda ufulu kuzungulira dziko lonse lapansi amasangalala pamene zoyesayesa zoterozo zakupondereza ufulu wa chipembedzo zilephera ndipo kuyenera kwa anthu kwa kulambira Mulungu ndi kulera mabanja awo mogwirizana ndi ziphunzitso za Baibulo kutetezeredwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena