Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndimotani Mmene Ndingasinthire pa Kusamuka Kwathu?
KODI banja lanu langosamukira kwina posachedwapa? Pamenepo mwinamwake mudzavomereza kuti zokumana nazo zingapo m’moyo nzovuta—kapena nzopsinja maganizo mofananamo. Ndipo pambuyo pa kumasula katundu wotsiriza ndi kuika mpando wotsiriza pamalo pake, inu mungakhalebe wotsenderezeka maganizo, wachisoni, kapena wankhaŵa. Zilibe kanthu kaya ngati nyumba yanuyo ili yokongola kwambiri kapena yoipa kwambiri poyerekezera ndi nyumba yanu yakale. Mukulakalakabe nyumba yanu yakaleyo, sukulu yanu yakale, ndipo makamaka mabwenzi anu akale.
Zowonadi, kulakalaka za kumene munali kukhala kale nkwachibadwa. Koma Baibulo limalangiza kuti: “Usanene, Kodi bwanji masiku akale anapambana ano? pakuti suli kufunsa mwanzeru pamenepo.” (Mlaliki 7:10) Nzeru imakuthandizani kuona zinthu moyenerera. Kwenikweni, “masiku akale” a kumene kale munali kukhala sanali kwenikweni abwino kopambana—mwinamwake osafika pa kukhala opambana. Popeza kuti sikuli kowononga moyo wanu, kusamuka kungakugaŵireni mipata ndi mapindu. Ngakhale zili choncho, kusintha pa kusamuka nkovuta. Nangano, kodi nchiyani chimene chingakuthandizeni kuchita motero?
Khalani Womasuka
Mawu a nyimbo ina yakale akuti: ‘Kulikonse kumene ndingakupange kukhala kwathu nkondikhutiritsa,’ ngowona. Inde, mmalo mwa kuvutika maganizo ndi kuganiza za kumene munasamuka, bwanji osayesayesa kupangitsa malo anu atsopanowo kukhala kwanu? Buku lotchedwa The Teenager’s Survival Guide to Moving limapereka lingaliro lakuti: “Mutangosamukira kumene m’nyumbamo, yesayesani kupangitsa chipinda chanu kukhala chokondweretsa ndi chozoloŵereka.” Mwachitsanzo, mungakongoletse chipinda chanu ndi zinthu zozoloŵereka ndi zithunzithunzi. Ngati mukukhala m’chipindamo ndi mbale wanu, yesani kuchitira zimenezi pamodzi.
M’nthaŵi za Baibulo wamasalmo analimbikitsa anthu a Mulungu kuzoloŵera mzinda wawo wa malikulu, akumati: “Zungulirani Ziyoni, ndipo muuzinge: Ŵerengani nsanja zake . . . Yesetsani zinyumba zake.” (Salmo 48:12, 13) M’njira yofananayo, dziŵani malo anu okhala. Fufuzani kumene kuli malo a masitolo, sukulu yanu yatsopano, laibulale yamomwemo, ndi kumene kuli malo ena ofunika. Zimenezi zidzakuthandizani kukhala womasuka.
Inu mosakayikira munali ndi chizoloŵezi, kapena njira yochitira zinthu, kwanu kumene munachokera. Pamene mubwerera m’njira yochitira zinthu imeneyo mwamsanga mpamenenso mumakhala womasuka mosataya nthaŵi. Inu muyenera makamaka “kupitirizabe kuyenda molongosoka m’njira imodzimodziyo” pankhani ya zinthu zauzimu monga misonkhano Yachikristu ndi phunziro la Baibulo.—Afilipi 3:16, NW.
Masiku a Sukulu
Kusinthira maganizo kusukulu yatsopano nkovuta, makamaka ngati mwasamuka mkati mwachaka. M’maiko ena mpambo wa zophunziridwa umalinganizidwa momwemo, ndipo ungakhale wosiyana kwambiri ndi maphunziro amene munali nawo kusukulu yanu yakale. Mungakhale wotsalira kwambiri pa ophunzira a pasukulu yanu yatsopano; mwinamwake mungatofunikira kusinthidwira kugiredi lotsika.
Ngakhale kuti zimenezi zingaonekere kukhala zochititsa manyazi panthaŵiyo, musalefulidwe maganizo; kubwerera m’mbuyo m’maphunziro kuli chotulukapo chofala chochititsidwa ndi kusamuka. Ndiponso, ngakhale kuti masukulu a m’dera lanu angakhale ali ndi mpambo umodzimodziwo wa zophunziridwa, chipsinjo cha kusamuka ndi kusinthira maganizo anu kwa anthu osiyanasiyana, mikhalidwe, ndi miyambo, limodzi ndi chitsenderezo cha kuyesayesa kukumbukira maina ambiri atsopano—zinthu zonsezi zingalefulitse nyonga yanu ya kulingalira mosamalitsa. Yankho lake? Yesani kudzipatsa nthaŵi yapadera kaamba ka homuweki yanu, ndipo chepetsani nthaŵi yoonerera TV. M’kupita kwanthaŵi kukhoza kwanu m’maphunziro kudzawongokera.
Kupanga Mabwenzi Atsopano
“Kupanga mabwenzi atsopano kunalidi mfungulo [ya kusintha],” akutero wachichepere wina wotchedwa Brian amene banja lake linasamukira kumbali yakummwera kwa United States. “Nditapeza mabwenzi angapo ausinkhu wanga amene anakonda zinthu zimene ndimakonda, zinthu zonse zinali zosavuta. Chinthu chokha chimene ndimalakalaka ponena za kwathu kwakale ndicho kuseŵera ice hockey.” Monga mmodzi wa Mboni za Yehova, mwanzeru Brian anafunafuna mabwenzi pakati pa achichepere owopa Mulungu osonkhana pa Nyumba Yaufumu yakumaloko. Nanunso ngati mukufuna mabwenzi amene ali ndi miyezo yapamwamba ya makhalidwe abwino ndi amenedi amasamala za inu monga munthu, Nyumba Yaufumu yakumaloko ndiyo malo abwino koposa amene mungakawafunefuneko.—Miyambo 13:20.
Ndithudi, simudzapanga mabwenzi mwa kukhala duu kapena mwa kudzipatula. (Yerekezerani ndi Miyambo 18:1.) “Ndinapeza mabwenzi atsopano,” akutero Anita, “mwa kuyesayesa kwanga ndi kudzidziŵikitsa. Ndapezanso kuti mwa kukhala ndi mkhalidwe wa maganizo wabwino—mwa kungomwetulira ndi kuoneka kukhala wachimwemwe—anthu amadza kwa iwe ndi kudzidziŵikitsa.” Inde, anthu adzakokedwera kwa inu ngati muwasonyeza kanthu kena kokoma—kumwetulira kwaubwenzi ndi mkhalidwe wosangalala! Ndipo khalani woleza mtima. Ubwenzi umatenga nthaŵi yaitali kuti ukule.
Komabe, nthaŵi zina mukhoza kuyamba bwino kuumba ubwenzi mwa kukaona malo anu atsopano musanasamuke. Laura wa zaka 13 akunena kuti: “Ndinalidi wachisoni kwambiri pamene ndinadziŵa kuti tidzasamuka posachedwa. Koma ndakhala ndikuthera nthaŵi pakudziŵana ndi ana ena a kumene tikupita ndipo zimenezo zandithandizadi kwambiri kumva bwinopo ndi kusamukako.”
Maubwenzi Abwino Motsutsana ndi Oipa
Kodi mukunena kuti pali mabwenzi abwino ochepa amene akupezeka pakati pa achichepere m’tauni yanu yatsopano? Pamenepo ‘kulitsani’ maubwenzi anu. (2 Akorinto 6:11-13) Ndi iko komwe, ena a maubwenzi amphamvu kwambiri olembedwa m’Baibulo anali pakati pa anthu osiyana kwambiri zaka zawo zakubadwa—monga ngati Davide ndi Jonatani, ndi Paulo ndi Timoteo. (1 Samueli 18:1; 1 Akorinto 4:17) Chotero chokhalira ndi maubwenzi ausinkhu wanu okha nchiyani? Pali anthu achikulire mumpingo Wachikristu amene mungasangalale kuchita nawo ubwenzi.
Zowona, anthu otero angakhale osakhoza kuseŵera nanu mpira. Kapena angakhale osakonda kumvetsera nyimbo zanu zokondedwa. Chikhalirechobe, iwo angakhale ndi zambiri ponena za ubwenzi wolimbikitsa. Popeza kuti njira yopambana yokhalira ndi bwenzi ndiyo ya kukhala bwenzilo, inu mungayambitse ubwenziwo mwa kupempha kutumikira mmodzi wa anthu achikulire ameneŵa. Kapena bwanji osangopempha ngati kungakhale kwabwino kwa inu kuti mudziŵaona? Ubwenzi wokhutiritsa ungayambike.
Kumbali ina, ngati mukhala nokhanokha m’chipinda chanu ndi kumadzimvera chisoni, inu mukhoza kukhala wosukidwa ndi wotsenderezeka maganizo mosavuta. Zimenezi zingakuikeni paupandu wa kutembenukira kumabwenzi amtundu woipa. Mwachitsanzo, timagulu tachiwawa ta azaka 13-19 ndito vuto lalikulu m’madera ambiri. Timalonjeza ubwenzi kwa achichepere osukidwa ndi kuwachititsa kuona kukhala ofunika. Koma monga momwe kunaliri m’nthaŵi za Baibulo, achichepere otero angayesenso kukuloŵetsani m’kuchita cholakwa, akumati: “Idza kuno . . . Tiye tiukire anthu opanda chifukwa kuti tisangalale!” Koma mfumu yanzeru Solomo inachenjeza kuti: “Mwanawe, usayende ndi anthu otero. Talikirana nawo. Afuna kuchita choipa mofulumira.”—Miyambo 1:10-16, Today’s English Version.a
Lingalirani za Ena
Njira ina yotsimikizirika yochotsera maganizo anu osukidwa ndiyo kufunafuna njira zolimbikitsira ena—makamaka ziŵalo za banja la inu mwini. “Kusamuka ndiko chinthu chovuta ngakhale kwa makolo,” magazini otchedwa Current Health akukumbutsa motero, “ndipo akhoza kugwiritsira ntchito chichirikizo chilichonse chimene angapeze.” Amayi kapena atate angakhale akusinthira maganizo kuntchito zatsopanozo. Nyumba yatsopano singakhale yokondweretsa monga yakale. Ndipo ngati muli ndi abale ndi alongo anu, nawonso angakhale akulimbana ndi kusukidwa ndi kulefulidwa maganizo. Bwanji osalingalira za zimene mungachite kuti muthandize? Funsani makolo anu ngati pali ntchito ina yapadera imene mungachite. Ngati abale anuwo akuonekera kukhala osukidwa, patulani nthaŵi ya kukhala nawo. Kumbukirani “chikondi chimangirira” ochilandira ndi ochisonyeza omwe.—1 Akorinto 8:1.
Pamenepo, potsirizira pake, kaya mukukonda kapena simukukonda malo anu atsopano zonsezo zidzadalira kwakukulukulu pa inu. Tikukumbutsidwa za nkhani ya mwamuna wina wanzeru wokalamba amene anafikiridwa ndi magalimoto aŵiri odzadza ndi anthu achilendo. “Tikuganiza zosamukira kuno,” linatero banja la m’galimoto loyamba. “Kodi anthu akuno ngotani?” Mwamuna wokalambayo anabwezera mawu mwa kufunsa kuti: “Anthu a kumene mwachokera ngotani?” Banjalo linayankha kuti: “Tachokera kutauni ya anthu aubwenzi kwambiri. Anthu ake ngopatsa ndi okoma mtima ndipo amakondwereradi alendo.” Mwamuna wokalambayo anamwetulira. “Ndiganiza kuti mudzakonda kukhala kuno,” iye anatero. “Anthu akuno ngofanana kwambiri ndi anthu amenewo.”
Mwamuna wokalambayo anafunsa banja limene linali m’galimoto yachiŵiri funso lofananalo. Iwo anayankha kuti: “Tachokera kukatauni koipa. Anthu akumeneko ngaulesi ndi ofunafuna zifukwa ndipo ngamiseche kowopsa.” Mwamuna wokalambayo anachita tsinya. “Ndiganiza kuti mudzakhala osakondwa kuno,” iye anatero. “Anthu akuno ngofanana kwambiri ndi anthu amenewo.”
Kodi mfundo ya nkhaniyo njotani? Anthu ali pafupifupi ofanana kulikonse. Ndipo kaya mumasangalala kapena kuipidwa ndi kukhala nawo kwanu zonsezo zimadalira kwambiri pa mkhalidwe wanu wa maganizo, malingaliro, ndi njira zochitira zinthu ndi ena. Chotero khalani ndi mkhalidwe wa maganizo wabwino! Tsimikizirani m’maganizo kuti kusamuka kwanu kudzakhala kwaphindu. Ayi, zinthu sizidzakhala chimodzimodzi. Koma mwa kuyesayesa ndi kuleza mtima, mukhoza kupangitsa zinthu kukhala zabwinopo kuposa kale. Malinga ngati muli ndi awo amene amakukondani kwenikweni, malo alionse akhoza kukhala kwanu.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Achichepere Akufunsa Kuti . . . Kodi Ndiyenera Kuphatikana ndi Gulu?” yotuluka m’kope la Galamukani! la June 8, 1991.
[Chithunzi patsamba 14]
Yambirirani kupanga mabwenzi atsopano