Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 7/8 tsamba 9-11
  • Maseŵera Ochititsa Nthumanzi—Kodi Ndiyenera Kuwayesa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Maseŵera Ochititsa Nthumanzi—Kodi Ndiyenera Kuwayesa?
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nchiyani Chimakopa?
  • Kodi Ngaupandudi?
  • Kodi nga Akristu?
  • Kuganiza Musanachite
  • “Maseŵera Angozi”—Kodi Muyenera Kuika Moyo Wanu Pachiswe Mwakuwachita?
    Galamukani!—2000
  • Kodi Anthu Okonda Zinthu Zonyamula Mtima Amakopekeranji Ndi Maseŵera Angozi?
    Galamukani!—2002
  • Kudzipereka kwa Mulungu N’kofunika Kuposa Kuchita Masewera
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Kodi Ndiyenera Kuloŵa Timu Yamaseŵero?
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 7/8 tsamba 9-11

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Maseŵera Ochititsa Nthumanzi—Kodi Ndiyenera Kuwayesa?

“IMENEYI idzakhala nthaŵi yochititsa mantha kopambana m’moyo wanu,” mukuuzidwa choncho mutaima pa pulatifomu muli njenjenje. Kuŵerengera kukuyamba: “Zisanu, zinayi, zitatu, ziŵiri, chimodzi—LUMPHA!” Kugwako kukuchititsani kuleka kupuma kwa kamphindi. Mukugwa mwaliŵiro kutsikira ku imene ikuonekera kukhala imfa yeniyeni, koma mwadzidzidzi mumva kukoka kodzidzimutsa kwa chingwe chotamuka. Mwadzazidwa ndi mpumulo. Mwapulumuka!

Kulumpha kwa bungee.a Maseŵerawo akopa chiŵerengero choyerekezera cha otengamo mbali miliyoni imodzi kufikira ku aŵiri mu United States mokha. Ali kokha amodzi a maseŵera ambiri amene atchuka kwambiri posachedwapa—kukwera matanthwe, paragliding, kuseŵera ndi bwato pa mathithi, ndi kuuluka m’mlengalenga ndi thabwa, kutchula oŵerengeka okha. “Ma 90 ali zaka za khumi za maseŵera ochititsa nthumanzi,” akutero wochirikiza kulumpha kwa bungee.

Machitachita aupandu sali zochita za olemera okha. Ofunafuna zochititsa nthumanzi a m’matauni amachita maseŵera owopsa (ndi oletsedwa) monga ngati elevator surfing (kukwera pamwamba pa zikepe zoyenda), tunneling (kukwawa m’michera ya nyumba zazikulu), subway surfing (kukwera pamwamba pa masitima oyenda pansi panthaka), ndi stair diving (kutsetsereka pa masitepe opakidwa mafuta).

Kodi Nchiyani Chimakopa?

“Ndidzayesa chilichonse chimene chimandichititsa mantha,” akutero Norbert wachichepere. “Ndimakondwa ndi maseŵera onse—baseball, basketball—koma kulumpha pa ulalo kunandichititsa mantha! Nkwapadera kotheratu.” Douglas wachichepere akuvomereza. “Maseŵera anthaŵi zonse ngosangalatsa, koma amakhala ndi cholinga,” iye akutero. “Nthaŵi zonse umakhala womangika. Ndimakonda lingaliro la kugwa. Ndi liŵirolo . . . Sumakhala ndi lingaliro limenelo m’maseŵera ena.”

Maseŵera odzetsa nthumanzi amapyola pa kupima luso lanu la kuseŵera; amakuchititsani kuyang’anizana mwachindunji ndi imfa! Otengamo mbali amaonekera kukhala akukondwera ndi kukwera kwa adrenaline yotulutsidwa. Akatswiri ena amanena kuti anthu ena mwachibadwa analinganizidwa kukhala a maumunthu a Type-T, kapena ofuna zochititsa nthumanzi. Komabe, achichepere ochuluka amaloŵa m’maupandu a mtundu wina; ndiyo njira yawo yopimira pamene angafike ndi kukulitsa kudzidalira.

Momvetsa chisoni, nthaŵi zonse achichepere samagwiritsira ntchito kulingalira kwabwino pochita motero. “Ulemerero wa anyamata ndiwo mphamvu yawo,” imatero Miyambo 20:29. Koma ena amaonekera kukhala akulingalira kuti mphamvu yawo ili yopanda malire. Dr. David Elkind akunena kuti kaŵirikaŵiri achichepere azaka zapakati pa 13 ndi 19 amakhulupirira kuti “ali anthu enieni ndi apadera—opatulidwa ku malamulo a kuthekera amene amagwira ntchito kwa ena. Chili chikhulupiriro chimenechi cha kukhala enieni, kukhala okutidwa m’malingaliro a kusayambukiridwa, chimene chimachititsa azaka zapakati pa 13 ndi 19 ochuluka kusankha kuloŵa m’maupandu.” Dr. Robert Butterworth mofananamo akuti: “Pamene uchita chinachake monga ngati kulumpha kuchokera m’ndege, chimakupatsa lingaliro la kutsutsana ndi zodziŵikiratu, kulamulira choikidwiratu chako.”

Komabe, kuloŵa mu upandu kungasonkhezeredwenso ndi zolinga zoipa. M’buku lake lakuti Childstress!, wolemba Mary Susan Miller akusonyeza kuti achichepere ambiri opanda mantha amaloŵa m’maupandu mopusa chifukwa chakuti sangathe kulaka zitsenderezo za miyoyo yawo. Motero maseŵera ochititsa nthumanzi angavumbule zikhoterero za kudziwononga kapena ngakhale kudzipha. “Iwo amadziika dala pa mikhalidwe yangozi,” akutero Miller, “monga ngati kuti akuletsa choikidwiratu kuwachitira ntchitoyo.”

Kodi Ngaupandudi?

Mosasamala kanthu kuti amasangalatsa motani, maseŵera ochititsa nthumanzi angakhale angozi. Ena amatsutsa kuti: ‘Ngakhalenso kudutsa khwalala.’ Komatu munthu amene akudutsa khwalala sakufuna dala ngozi kapena kuchititsa nthumanzi. Ndipo pamene kuli kwakuti maseŵera ambiri, monga ngati kulumpha kwa bungee, ali ndi zolembedwa zabwino za chitetezo, zinthu zingalakwike. Mark Bracker, M.D., ananena motere: “Pokhala ndi maseŵera ambiri ameneŵa okhala ndi maupandu aakulu, pamene chinachake chilakwika angakhale angozi kwambiri. Pamene kudzetsa nthumanziko kukhala kokulirapo, kaŵirikaŵiri upandu umakhalanso wokulirapo kwambiri, kaya ndi kulumpha m’ndege kapena hang gliding kapena kuyendetsa njinga yamoto.” Wachichepere wina wazaka 20 anachita kulumpha kwa bungee kuchokera pa chibaluni cha mpweya wotentha choyandama m’mlengalenga pa mtunda wa mamita 58 kuchokera pansi. Vuto lake? Chingwe chake chinali cha utali wa mamita 79! Iye analumpha ndi kufa moipa.

Zoona, machitachita ena, monga ngati kukwera njinga yamoto, kungasangalalidwe mumkhalidwe wotetezereka ndi wodekha pang’ono. Koma katswiri wina wa mankhwala a maseŵera akunena motere za ofuna kuchititsidwa nthumanzi: “Pamene maluso awo awongokera kwambiri, iwo amasankha chinthu chovuta kwambiri, ndipo amavulala potsirizira.” Wachichepere wina anaulula kuti: “Ndine womwerekera. Nkovuta kwambiri tsopano kufikira mlingo umenewo wa mantha ndi nthumazi.”

Kodi nga Akristu?

Kodi Baibulo limaletsa kotheratu maseŵera onse? Ayi. Kuli kupambanitsa kopusa kumene kumatsutsidwa. Monga kwalembedwa pa Mlaliki 7:17, Solomo anafunsa kuti: “Uferenji nthaŵi yako isanakwane?”

‘Moyo ngwaufupi. Seŵerani mwamphamvu,’ kumasonkhezera motero kusatsa malonda kwina kwa nsapato za maseŵera. Koma tili athayo kwa ife eni, kwa awo amene amatikonda, ndi kwa Mlengi wathu la kuona moyo wathu kukhala wamtengo wake. Moyo uli mphatso yochokera kwa Mulungu. (Salmo 36:9) M’nthaŵi za Baibulo zilango zazikulu zinaperekedwa ngati moyo unaphedwa mwangozi. (Eksodo 21:29; Numeri 35:22-25) Motero anthu a Mulungu analimbikitsidwa kupeŵa maupandu opanda pake.—Yerekezerani ndi Deuteronomo 22:8.

Mofananamo Akristu lerolino ali ndi thayo la kulemekeza moyo. Kodi kukakhala koyenera kulondola maseŵera amene angakuikeni paupandu wosayenerera? Pamene Satana Mdyerekezi anayesa kuyesa Yesu, iye ananena kuti angelo akaŵakha Yesu ngati anadziponya kuchokera pachimbudzi cha kachisi. Yesu anayankha kuti: “Usamuyese Ambuye Mulungu wako.”—Mateyu 4:5-7.

Ndiponso, mosasamala kanthu ndi mmene mungadzimvere kukhala wamphamvu ndi wathanzi, simuli wokhoza kupeŵa chivulazo. Nkopanda pake kulingalira kuti: ‘Sizingachitike kwa ine.’ Baibulo limachenjeza kuti ‘timangoona zotigwera m’nthaŵi yathu.’—Mlaliki 9:11.

Kuganiza Musanachite

Nkwanzeru kulingalira mwamphamvu ponena za zotulukapo zothekera za kulumpha pa makako, kulumpha kuchokera m’ndege, kapena kuchita chilichonse chimene chingaonekere kukhala chaupandu kwambiri. Musangodalira pa manenanena kapena pa malipoti osangalatsa a achichepere ena. (Miyambo 14:15) Pezani umboni weniweni.

Mwachitsanzo, kodi pali ngozi zochuluka motani pa maseŵerawo? Kodi ndi njira zachitetezo zotani zimene zimatengedwa? Katswiri wina akunena za kusambira pansi pa madzi ndi chiwiya chothandizira kupuma motere: “[Anthu amaganiza kuti] kuchoka pamtunda ndi kuloŵa m’madzi nkowopsa. . . . Koma nkowopsa kokha ngati muchita zimenezo popanda malangizo oyenera.” Chotero muyeneranso kufunsa kuti, Kodi ndi maphunziro ndi ziŵiya zotani zimene zimafunikira kaamba ka maseŵera ameneŵa? Kodi pali mapindu alionse abwino, monga ngati kuseŵera? Kodi maupandu alionse amangochitika mwangozi, kapena kodi cholinga chachikulu cha maseŵerawo ndicho kunyalanyaza imfa?

Ngati zili choncho mogwirizana ndi mfundo yomalizirayo, mungadzifunse kuti nchifukwa ninji kudziika paupandu kumakukopani kwambiri. Kodi kuli chabe kochitidwa chifukwa cha kusukidwa kapena kupsinjika maganizo? Pamenepo bwanji osapeza njira yotetezereka, yabwino kwambiri yochitira ndi malingaliro otero?b Buku lakuti Teenage Stress limatikumbutsa kuti kudziika paupandu kuli “njira yangozi ndi yosagwira ntchito konse yochitira ndi kupsinjika maganizo koipa.”—Yerekezerani ndi Miyambo 21:17.

Pambuyo pofufuza zinthu mosamalitsa—ndi kulankhula ndi makolo anu—kunganenedwa kuti kungakhale kwabwino kwambiri kupeŵa maseŵera ochititsa nthumanzi opambanitsa. Makolo anu angakonde kuti muchite maseŵera amene amaonekera kukhala opanda upandu mwachibadwa, monga ngati kutchova njinga, kutsetsereka pa chipale chofeŵa, skiing, ndi snorkeling, kutchula oŵerengeka okha. Ndithudi, ngakhale maseŵera otetezereka angakhale angozi ngati chisamaliro choyenerera sichinatengedwe.

Zimenezi zinachitika kwa kagulu kakang’ono ka achichepere Achikristu amene anasankha kukakwera mapiri. Iwo anapambuka mu ka mkwaso ndi kuyamba kukwera mpata wopapatiza pa therezi lotsetsereka. Pasanapite nthaŵi yaitali anadzipeza kukhala atatsekerezeka, olephera kupita motetezereka kutsogolo kapena kumbuyo. Ndiyeno wachichepere amene anali kutsogolera kaguluko anamva phokoso la mwadzidzidzi. Mabwenzi ake aŵiri anagwa nafa. Nzachisoni chotani nanga!

Chotero chonde khalani ochenjera! ‘Kondwerani ndi unyamata wanu,’ kusangalala ndi mphamvu ndi nyonga zimene mwadalitsidwa nazo. (Mlaliki 11:9) Koma musanavomere pempho la kuchita chinachake chaupandu, chitani zimene Brian wachichepere amachita. Iye akuti: “Ndimadzifunsa ndekha kuti, ‘Kodi Yehova akalingalira motani za zimenezo? Kodi zikasonyeza motani mkhalidwe wanga wamaganizo kulinga ku mphatso ya moyo imene wandipatsa?’” Inde, pendani maupanduwo, santhulani zolinga zanu. Moyo uli wamtengo wapatali wosafuna kuseŵeretsedwa.

[Mawu a M’munsi]

a “Kulumpha kwa bungee” ndiko maseŵera amene olumpha, atamangiriridwa ku chingwe chotamuka chotchedwa bungee, amalumpha pa maulalo, makako, ndipo ngakhale m’mabaluni okhala ndi mpweya wotentha. Zimenezi zimalola kugwa kotheratu popanda choletsa chingwecho chisanatamuke, kuimitsa kugwera pansiko.

b Ngati mwachita tondovi kapena mukulimbana ndi zisonkhezero za kudziwononga, bwanji osalankhula ndi winawake ndi kupeza thandizo mmalo modziika pa maupandu osayenerera?—Onani “Achichepere Akufunsa Kuti . . . Kodi Kudzipha Ndiko Yankho?” m’kope lathu la Galamukani! la April 8, 1994.

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi achichepere Achikristu ayenera kulondola maseŵera ochititsa nthumanzi monga ngati kulumpha kwa “bungee”?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena