Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 7/8 tsamba 29-30
  • Kodi Mtumwi Paulo Anali Kudana ndi Akazi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mtumwi Paulo Anali Kudana ndi Akazi?
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ziyeneretso za Paulo
  • Akazi m’Makalata a Paulo
  • Kodi Nchikhoterero Chodana ndi Akazi?
  • “Mkazi . . . Akhale Chete”
  • Mwamuna ndi Mkazi Onse Ali ndi Udindo Wolemekezeka
    Nsanja ya Olonda—2007
  • ‘Akazi Amene Agwiritsa Ntchito mwa Ambuye’
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Akazi ali Mbali ya pa Guwa la Nsembe?
    Galamukani!—1988
  • Timoteo—‘Mwana Weniweni m’Chikhulupiriro’
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 7/8 tsamba 29-30

Lingaliro la Baibulo

Kodi Mtumwi Paulo Anali Kudana ndi Akazi?

“ZIPHUNZITSO za [mtumwi] Paulo zagwiritsiridwa ntchito monga maziko a chikhoterero cha kusankha akazi mkati mwa tchalitchi . . . Chachikristu.” Anatero Woweruza Cecilie Rushton wa ku Auckland, New Zealand, m’chikalata chimene chinaperekedwa kuchiyambi kwa 1993 ku msonkhano wa Commonwealth Law Conference ku Cyprus. “Kalata yake kwa Timoteo,” iye anawonjezera motero, “imavumbula kulingalira kwake: ‘Koma sindilola kuti mkazi aphunzitse, kapena kuchita ulamuliro pa mwamuna, koma akhale chete.’”—1 Timoteo 2:12, King James Version.

Pamene Paulo analemba ponena za mbali kapena malo a akazi, kodi anali malingaliro ake aumwini amene anali kulongosoledwa, kapena kodi iye anauziridwa mwaumulungu? Ataonedwa onse, kodi zolembedwa, kapena makalata, a Paulo amasonyezadi chikhoterero cha kudana ndi akazi? Kodi mawu a m’nkhani ya Paulo kwa Timoteo ogwidwa pamwambawo amagwira ntchito m’lingaliro lotani?

Ziyeneretso za Paulo

Mwa mabuku 27 a Malemba Achigiriki Achikristu, 14 amanenedwa kuti nga Paulo. Chomwe chimasonyeza kuti mzimu woyera unagwira ntchito pa iye chinali kukhoza kwake kozizwitsa kwa kulankhula m’malilime ambiri. Ndiponso, iye anachitira umboni wa kuona masomphenya odabwitsa. (1 Akorinto 14:18; 2 Akorinto 12:1-5) Chitsanzo chake chodzipereka, cha moyo wonse, ndi chachikondi chinachititsa chigwirizano champhamvu cha chikondi cha ubale chotentha pakati pa iye ndi Akristu anzake. (Machitidwe 20:37, 38) Zolemba zake, kuphatikizapo zimene ananena ponena za akazi, zimapanga mbali ya ‘lemba lililonse louziridwa ndi Mulungu ndi lopindulitsa pa chiphunzitso.’—2 Timoteo 3:16.

Akazi m’Makalata a Paulo

Kuzindikira ndi kulingalira akazi kwa Paulo kuli ndi umboni wochuluka m’zolembedwa zake zonse. Mobwerezabwereza, iye amawatchula m’mathayo awo osiyanasiyana a mpingo ndi banja. Mu imodzi ya makalata ake, anayerekezera mikhalidwe yokhumbirika ya abusa Achikristu ndi ija imene imasonyezedwa ndi mayi woyamwitsa.—1 Atesalonika 2:7, NW.

Ambiri a alongo Achikristu a mtumwiyo, otchulidwa maina m’makalata ake, ali anthu amene akuyamikiridwa kwambiri ndi iye. Amene anaphatikizidwa m’moni wake wopita ku ziŵalo za mpingo m’Roma anali uja wopita mwachindunji kwa akazi ena amene “agwiritsa ntchito mwa Ambuye.” (Aroma 16:12) Ponena za Euodiya ndi Suntuke, iye analimbikitsa abale m’Filipi kupitiriza ‘kuthandiza akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu uthenga wabwino.’ (Afilipi 4:3) M’kalata yake kwa Timoteo, Paulo anavomereza chikhulupiriro chopereka chitsanzo cha agogo a mnyamata ameneyo a Loisi ndi amayi ake, a Yunike.—2 Timoteo 1:5.

Motero, kodi pali chisonyezero chilichonse cha mmene alongo Achikristu a Paulo anamverera ponena za iye? Mokondweretsa, iye anachitira umboni za Akula ndi Priska, aŵiri okwatirana amene anayanjana nawo kwambiri, kuti osati Akula yekha komanso mkazi wake, Priska, “anapereka khosi lawo chifukwa cha moyo” wake.—Aroma 16:3, 4.

Kodi Nchikhoterero Chodana ndi Akazi?

“Mkulu usamdzudzule, komatu umdandaulire ngati atate; anyamata ngati abale; akazi aakulu ngati amayi; akazi aang’ono ngati alongo, m’kuyera mtima konse.” (1 Timoteo 5:1, 2) Kodi mawu ameneŵa a Paulo kwa Timoteo samasonyeza ulemu woyenerera kwa akazi? Paulo anapereka kwa amuna ndi akazi mumpingo Wachikristu ulemu wofanana. “Mulibe Myuda, kapena Mhelene,” iye analemba motero, “mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Kristu Yesu.”—Agalatiya 3:28.

Akumanena za mathayo ogaŵiridwa ndi Mulungu m’banja, Paulo analemba kuti: “Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye. Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa Eklesia, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo.” (Aefeso 5:22, 23; yerekezerani ndi 1 Akorinto 11:3.) Inde, mbali za mwamuna ndi mkazi zimasiyana, koma zimenezi sizimatanthauza kuti mmodzi ali wotsika. Mbalizo nzothandizana, ndipo kukwaniritsidwa kwa mbali iliyonse kumapereka chitokoso chimene chimachirikiza ubwino wa banja ngati chafikiridwa. Ndiponso, kusonyeza umutu kwa mwamuna sikunayenere kukhala kopondereza kapena kopanda chikondi. Paulo anapitiriza kuti: “Amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha,” kukhala ofunitsitsa kudzimana kaamba ka iwo. (Aefeso 5:28, 29) Ana anayenera kumvera atate ndi amayi omwe.—Aefeso 6:1, 2.

Ofunikanso kuonedwa bwino ali mawu a Paulo onena za unansi wa m’banja. Paulo analemba mosakondera kuti: “Mwamunayo apereke kwa mkazi mangawa ake; koma modzimodzinso mkazi kwa mwamuna. Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi la iye yekha, koma mkazi ndiye.”—1 Akorinto 7:3, 4.

“Mkazi . . . Akhale Chete”

Posonya ku mawu a Paulo a pa 1 Timoteo 2:12, ogwidwa m’ndime yotsegulira, kodi kuchirikiza kwake kukhala “chete” kwa akazi kunazikidwa pa chikhoterero cha kudana ndi akazi? Ayi! “Chete” amene akutchulidwa anali ponena za kuphunzitsa ndi kusonyeza ulamuliro wauzimu mumpingo, mosasamala kanthu za unansi woperekedwa mwaumulungu wotchulidwa poyambawo wa mwamuna ndi mkazi.a

Zimenezi sizikutanthauza kuti akazi sangakhale aphunzitsi a choonadi chaumulungu. Paulo analimbikitsa akazi okalamba kukhala “akuphunzitsa zokoma” kwa akazi aang’ono. Mwa kutsatira chitsanzo cha Yunike ndi Loisi, amene analangiza Timoteo, anakubala Achikristu ayenera kuphunzitsa ana awo m’njira zaumulungu. (Tito 2:3-5; 2 Timoteo 1:5) Lerolino, m’mipingo ya Mboni za Yehova, mazana zikwi za akazi Achikristu amapeza chikhutiro chauzimu mwa kutsatira zitsanzo za Euodiya ndi Suntuke m’kulalikira mbiri yabwino poyera ndi kupanga ophunzira aamuna ndi aakazi.—Salmo 68:11; Mateyu 28:19; Afilipi 4:2, 3.

Motero, kodi kupenda kwanu nkotani? Kodi zolembedwa za Paulo, zitalingaliridwa zonse, zimalungamitsa chinenezo cha chikhoterero cha kudana ndi akazi?

[Mawu a M’munsi]

a Ponena za mawu akuti “chimvero chonse” pa 1 Timoteo 2:11 (New International Version), wophunzira Baibulo W. E. Vine akuti: “Lamulolo silinali kunena za kulepa maganizo ndi chikumbumtima, kapena kuleka mathayo odzisankhira; mawu akuti ‘ndi kugonjera konse’ ali chenjezo loletsa kulanda ulamuliro, monga, mwachitsanzo, m’vesi lotsatira.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena