Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 11/8 tsamba 26-32
  • Sitinachirikize Nkhondo ya Hitler

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sitinachirikize Nkhondo ya Hitler
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mayankho a Mafunso a Atate
  • Utumiki Wachangu
  • Hitler Atenga Ulamuliro
  • Chikakamizo cha Kugwirizana ndi Ena
  • Chitsanzo Chabwino cha Atate cha Kusunga Umphumphu
  • Mayeso Anga Ayamba
  • Kuweruza Mlandu ndi Kuikidwa m’Ndende
  • Moyo Wankhanza wa mu Msasa
  • Kukhala Olimba Mwauzimu
  • Mipata ya Kuchitira Umboni
  • Moyo Wanga Uwongokera
  • Masiku Otsiriza a Nkhondo
  • Kubwereranso Kwathu
  • Kulimba Mtima kwa Kupirira
  • Yehova Anatipulumutsa ku Ulamuliro Wankhanza
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kodi Ndingam’bwezere Chiyani Yehova?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kuvutikira Chikhulupiriro ku Ulaya mu Ulamuliro wa Chipani cha Nazi
    Galamukani!—2003
  • Chimene Matchalitchi Anakhalira Chete
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 11/8 tsamba 26-32

Sitinachirikize Nkhondo ya Hitler

YOSIMBIDWA NDI FRANZ WOHLFAHRT

ATATE, a Gregor Wohlfahrt, anatumikira m’gulu lankhondo la Austria mkati mwa Nkhondo Yadziko I (1914 kufikira 1918) ndipo anamenyana ndi Italy. Panali zikwi mazana ambiri a anthu amene anaphedwa a ku Austria ndi ku Italy komwe. Zowopsa za chochitika chimenecho zinasintha kotheratu lingaliro la Atate pa chipembedzo ndi nkhondo.

Atate anaona ansembe a ku Austria akumadalitsa magulu ankhondo, ndipo anamvanso kuti mbali inayo ansembe Achitaliyana anali kuchita chimodzimodzi. Chotero anafunsa kuti: “Kodi nchifukwa ninji asilikali Achikatolika akulimbikitsidwa kupha Akatolika ena? Kodi Akristu ayenera kumenya nkhondo?” Ansembewo analibe mayankho okhutiritsa.

Mayankho a Mafunso a Atate

Nkhondoyo itatha Atate anakwatira ndi kukakhala kumapiri a Austria kufupi ndi malire a Italy ndi Yugoslavia. Ndinabadwira kumeneko mu 1920, mwana woyamba pa asanu ndi mmodzi. Pamene ndinali ndi zaka zisanu ndi chimodzi, tinasamukira ku St. Martin kummaŵa pamtunda wa makilomita angapo pafupi ndi tauni yosangulukirako ya Pörtschach.

Pamene tinali kukhala kumeneko, atumiki a Mboni za Yehova (panthaŵiyo otchedwa Ophunzira Baibulo) anafikira makolo anga. Mu 1929 iwo anasiya kabuku kakuti Prosperity Sure, kamene kanayankha mafunso ambiri a Atate. Kanasonyeza kuchokera m’Baibulo kuti dziko linali kulamulidwa ndi wolamulira wosaoneka wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana. (Yohane 12:31; 2 Akorinto 4:4; Chivumbulutso 12:9) Chisonkhezero chake pa chipembedzo, ndale, ndi malonda adzikoli ndicho chimene chinali ndi mlandu wa zowopsa zimene Atate anaona mu Nkhondo Yadziko I. Potsirizira pake, Atate anapeza mayankho amene anali kufunafuna.

Utumiki Wachangu

Atate anaoda mabuku ku Watch Tower Bible and Tract Society ndi kuyamba kuwagaŵira kwa achibale awo ndiyeno kunyumba ndi nyumba. Hans Stossier, mnansi wathu yemwe anali mnyamata wa zaka 20 zokha, mofulumira anagwirizana nawo mu utumiki wakunyumba ndi nyumba. Posapita nthaŵi, nawonso asanu a achibale athu anakhala Mboni—akulu awo a Atate a Franz, akazi awo a Anna, pambuyo pake mwana wawo wamwamuna Anton, ndiponso alongo awo a Atate a Maria, ndi amuna awo, a Hermann.

Zimenezi zinabutsa zinthu m’tauni yathu yaing’ono ya St. Martin. Kusukulu wophunzira wina anafunsa mphunzitsi wathu Wachikatolika kuti, “Abambo Loigge, kodi mulungu watsopanoyu Yehova ndani amene a Wohlfahrt akulambira?”

“Iyayi, ananu,” wansembeyo anayankha motero. “Ameneyutu si mulungu watsopano. Yehova ndiye Atate wa Yesu Kristu. Ngati iwo akuwanditsa uthengawo chifukwa cha kukonda Mulungu ameneyo, zimenezo nzabwino kwambiri.”

Ndikukumbukira nthaŵi zambiri atate akumachoka panyumba pa 1:00 a.m. atanyamula mabuku ofotokoza Baibulo ndi masangweji. Iwo ankafika kumalo akutali a gawo lawo, kufupi ndi malire a Italy pambuyo pa maola asanu ndi limodzi, kapena asanu ndi aŵiri. Ndinkatsagana nawo popita kumalo apafupi.

Mosasamala kanthu za utumiki wawo wapoyera, Atate sananyalanyaze zosoŵa zauzimu za banja lawo. Pamene ndinali ndi zaka khumi, iwo anayamba phunziro la Baibulo lokhazikika lamlungu ndi mlungu ndi tonsefe asanu ndi mmodzi, akumagwiritsira ntchito buku lakuti Zeze wa Mulungu. Panthaŵi ina nyumba yathu inkadzaza ndi anansi ndi achibale okondwerera. Posakhalitsa, munakhala mpingo wa olengeza Ufumu 26 m’tauni yathu yaing’onoyo.

Hitler Atenga Ulamuliro

Hitler anatenga ulamuliro mu Germany mu 1933, ndipo posapita nthaŵi chizunzo cha Mboni za Yehova chinawonjezeka. Mu 1937, Atate anakaloŵa msonkhano wachigawo ku Prague, Czechoslovakia. Osonkhanawo anachenjezedwa za mayesero amene anali mtsogolo, chotero pamene anabwerera Atate analimbikitsa tonsefe kukonzekera chizunzo.

Zidakali choncho, pa usinkhu wa zaka 16, ndinayamba kuphunzitsidwa kukhala wopenta nyumba. Ndinakhala ndi katswiri wopenta ndi kumaloŵa sukulu yophunzirira ntchito. Wansembe wina wachikulire amene anali atathaŵa ku Germany kupeŵa ulamuliro wa Nazi anali kuphunzitsa zachipembedzo pasukulupo. Pamene ophunzira anampatsa moni wakuti “Heil Hitler!” iye anasonyeza kunyansidwa ndipo ankafunsa kuti: “Kodi chalakwika nchiyani ndi kukhulupirika kwathu?”

Ndinagwiritsira ntchito mwaŵiwo ndi kufunsa chifukwa chake Akatolika amagwiritsira ntchito maina aulemu onga akuti “Wokwezeka” ndi “Atate Woyera,” popeza kuti Yesu ananena kuti otsatira ake onse ali abale. (Mateyu 23:8-10) Wansembeyo anavomereza kuti kuchita zimenezi kunali kulakwa ndi kuti iye mwiniyo anali m’mavuto chifukwa cha kukana kugwada pamaso pa bishopu ndi kupsompsona dzanja lake. Ndiyeno ndinafunsa kuti: “Kodi kumatheka motani kupha Mkatolika mnzawo ndi dalitso la Tchalitchi?”

“Zimenezi nzochititsa manyazi koposa!” wansembeyo anayankha motero. “Siziyeneranso kuchitika konse. Ife ndife Akristu ndipo Tchalitchi sichiyenera kuloŵerera mu nkhondo.”

Pa March 12, 1938, Hitler analoŵa mu Austria popanda vuto ndipo posapita nthaŵi anampanga kukhala mbali ya Germany. Matchalitchi anagwirizana naye mwamsanga. Kwenikweni, mlungu usanathe, mabishopu onse asanu ndi mmodzi a Austria kuphatikizapo Kadinala Theodore Innitzer anasaina “chilengezo chamwambo” choyanja kwambiri chimene ananenamo kuti m’chisankho chikudzacho “nkofunika ndiponso kuli thayo la dzikoli monga nzika ya Germany, kuti Mabishopufe tiponye voti yosankha Boma la Germany.” (Onani tsamba 9.) Munali kuvomereza kwakukulu mu Vienna kwakuti Kadinala Innitzer ndiye anali pakati pa oyamba kulonjera Hitler ndi suluti ya Nazi. Kadinalayo analamula kuti matchalitchi onse a Austria aimike mbendera ya swastika, alize mabelu awo, ndi kupempherera wolamulira wotsendereza wa Nazi.

Mkhalidwe wa ndale unaoneka monga kuti unasintha kamodzi nkamodzi mu Austria. Asilikali ankhanza apadera a Nazi ovala mayunifolomu ofiirira okhala ndi swastika pamkono anaonekera paliponse mwadzidzidzi. Wansembe amene poyambapo anali atanena kuti Tchalitchi sichiyenera kuloŵerera mu nkhondo anali mmodzi wa ansembe oŵerengeka amene anakana kunena kuti, “Heil Hitler!” Mlungu wotsatira wansembe watsopano anamloŵa mmalo. Chinthu choyamba chimene iye anachita pamene analoŵa m’kalasi chinali kugogodetsa mapazi pansi, kutukula dzanja lake mwa kuchita suluti, ndi kunena kuti: “Heil Hitler!”

Chikakamizo cha Kugwirizana ndi Ena

Aliyense anakakamizidwa kugonjera kwa Anazi. Pamene ndinalonjera anthu ndi mawu akuti “Guten Tag” (Moni) mmalo mwa kunena kuti “Heil Hitler,” iwo anakwiya. Ndinakaneneredwa kwa a Gestapo pafupifupi nthaŵi 12. Panthaŵi ina gulu la asilikali ankhanza linawopseza katswiri wopenta amene ndinali kukhala naye, akumati ngati sindikachita suluti ndi kugwirizana ndi gulu la Hitler Youth, ndidzatumizidwa ku msasa wachibalo. Katswiri wopentayo, amene anali wogwirizana ndi Anazi, anawapempha kuti aleze mtima nane popeza kuti anali wotsimikiza kuti potsirizira pake ndidzasintha. Iye anafotokoza kuti sanafune kuti ndisiyane naye chifukwa chakuti ndinali wantchito wabwino.

Anazi atatenga dziko, panali kuguba kwakukulu kumene kunkachitika kufikira usiku, ndipo anthu anali kufuula motengeka maganizo ndi mawu osonkhezera. Tsiku lililonse wailesi zinali kubangula ndi mawu a Hitler, Goebbels, ndi ena. Kugonjera kwa Tchalitchi cha Katolika kwa Hitler kunakula, pamene ansembe anali kupempherera ndi kudalitsa Hitler nthaŵi zonse.

Atate anandikumbutsa za kufunika kwa kuchirimika ndi kupatulira moyo wanga kwa Yehova ndi kubatizidwa. Analankhula nanenso za Maria Stossier, mlongo wake wamng’ono wa mnansi wathu Hans, amene anaima kumbali ya choonadi cha Baibulo. Maria ndi ine tinali titavomerezana zokwatirana, ndipo Atate anandilimbikitsa kukhala womlimbikitsa mwauzimu. Maria ndi ine tinabatizidwa mu August 1939 ndi mlongo wake Hans.

Chitsanzo Chabwino cha Atate cha Kusunga Umphumphu

Tsiku lotsatira Atate anaitanidwa ku utumiki wankhondo. Ngakhale kuti thanzi lawo lofooka chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo m’Nkhondo Yadziko I, likanawaletsa kutumikira, Atate anauza owafunsa kuti monga Mkristu iwo sakaloŵa konse m’nkhondo kachiŵirinso monga momwe anachitira pamene anali Mkatolika. Chifukwa cha mawu ameneŵa anasungidwa kuti afunsidwe mowonjezereka.

Mlungu umodzi pambuyo pake pamene Germany analoŵa mu Poland, zimene zinayambitsa Nkhondo Yadziko II, iwo anatengeredwa ku Vienna. Pamene anali kusungidwa kumeneko, meya wa chigawo chathu analemba kalata akumanena kuti Atate anali ndi mlandu wa kuchititsa Mboni zina kukana kuchirikiza Hitler ndi kuti chifukwa cha chimenecho Atate ayenera kuphedwa. Motero, Atate anatumizidwa ku Berlin, ndipo mofulumira anaweruzidwa kuti adulidwe mutu. Anamangidwa unyolo usana ndi usiku m’ndende ya Moabit.

Zidakali choncho ndinalembera kalata Atate mmalo mwa banja lonse ndi kuwauza kuti tinali otsimikiza kutsatira chitsanzo chawo chokhulupirika. Atate anali munthu wosakhudzidwa mtima mwawamba, komano tinatha kuona mmene anamvera pamene kalata yawo yomaliza kwa ife inali ndi madontho a misozi. Iwo anali achimwemwe kwambiri chifukwa chakuti tinazindikira kaimidwe kawo. Anatilembera mawu achilimbikitso, akumatchula aliyense wa ife ndi dzina ndi kutilimbikitsa kukhalabe okhulupirika. Chiyembekezo chawo m’chiukiriro chinali champhamvu.

Kupatulapo Atate, panali pafupifupi Mboni zina 24 zimene zinasungidwa m’ndende ya Moabit. Akuluakulu a Hitler anayesa kuwanyengerera kuti agonje pa chikhulupiriro chawo koma mosaphula kanthu. Mu December 1939, Mboni pafupifupi 25 zinaphedwa. Titadziŵa za kuphedwa kwa Atate, Amayi anasonyeza mmene analili oyamikira kwa Yehova kuti Iyeyo anali atapatsa Atate nyonga ya kukhala okhulupirika kufikira imfa.

Mayeso Anga Ayamba

Milungu yoŵerengeka pambuyo pake, ndinaitanidwa ku ntchito ya utumiki koma mofulumira ndinafikira pa kudziŵa kuti ntchito yeniyeni yaikulu inali maphunziro a nkhondo. Ndinafotokoza kuti sindingathe kutumikira m’gulu lankhondo koma ndingachite ntchito ina. Komabe, pamene ndinakana kuimba nyimbo zankhondo za Nazi, maofesala anakwiya.

Mmaŵa wotsatira ndinatulukira nditavala zovala wamba mmalo mwa kuvala yunifolomu yausilikali imene tinapatsidwa. Ofesala wamkulu anati sakanachitira mwina koma kukangonditsekera m’ndende yapansi. Mmenemo ndinkadya buledi ndi madzi basi. Pambuyo pake ndinauzidwa kuti padzakhala mwambo wa kuchitira mbendera suluti, ndipo ndinachenjezedwa kuti ngati ndikana zimenezo ndikawomberedwa.

Pamabwalo ophunzirirapo panali olembedwa usilikali 300 ndiponso maofesala ankhondo. Ndinalamulidwa kuyenda pamodzi ndi maofesala ndi mbendera ya swastika ndi kuchita suluti ya Hitler. Nditapeza nyonga yauzimu mwa kukumbukira chochitika cha Baibulo cha Ahebri atatu, ndinangonena kuti, “Guten Tag” (Moni), pamene ndinali kudutsa. (Danieli 3:1-30) Ndinalamulidwa kudutsanso. Nthaŵi inoyo sindinanene kalikonse, ndinangomwetulira.

Pamene maofesala anayi ananditengeranso kundende yapansi, anandiuza kuti anali kuchita mantha chifukwa chakuti anayembekezera kuti ndikawomberedwa. “Kodi unatha bwanji,” iwo anafunsa motero, “kumwetulira pamene ife tinali ndi mantha kwambiri?” Iwo anati anakhumba kukhala ndi kulimba mtima konga kwanga.

Masiku angapo pambuyo pake, Dr. Almendinger, ofesala wamkulu wochokera kumalikulu a Hitler ku Berlin, anafika pa msasawo. Ndinaitanidwa kukaonekera pamaso pake. Iye anafotokoza kuti malamulo anali atakhwima kwambiri. “Sukudziŵa konse mkhalidwe umene waloŵamo,” iye anatero.

“Inde, ndikudziŵa,” ndinayankha motero. “Atate wanga anadulidwa mutu kaamba ka chifukwa chimodzimodzichi milungu yoŵerengeka yapitayo.” Anasoŵa mawu nangokhala chete.

Pambuyo pake ofesala winanso wamkulu wochokera ku Berlin anafika, ndipo zoyesayesa zinanso za kusintha maganizo anga zinachitidwa. Atamva chifukwa chake sindikanatha kuswa malamulo a Mulungu, anagwira dzanja langa, akukha misozi, nati: “Ndikufuna kupulumutsa moyo wako!” Maofesala onse amene anali kupenyerera anachita chisoni kwambiri. Ndiyeno ndinabwezeretsedwa kundende yapansi kumene ndinathera masiku 33.

Kuweruza Mlandu ndi Kuikidwa m’Ndende

Mu April 1940, ndinasamutsidwira kundende ina ku Fürstenfeld. Masiku oŵerengeka pambuyo pake wotomerana naye wanga, Maria, ndi mbale wanga Gregor anadzandizonda. Gregor anali wamng’ono kwa ine ndi chaka chimodzi chokha ndi theka, ndipo anali ataima mochirimika pa choonadi cha Baibulo ku sukulu. Ndikukumbukira akulimbikitsa aphwathu kukhala okonzekera chizunzo, akumanena kuti panali njira imodzi yokha, kutumikira Yehova! Ola lamtengo wapatali lotheredwa pa kulimbikitsana wina ndi mnzake limeneli linali nthaŵi yomaliza imene ndinamuona ali wamoyo. Pambuyo pake, ku Graz, ndinapatsidwa chilango cha ntchito yakalavula gaga ya zaka zisanu.

Pa mphakasa ya 1940, ndinakwezedwa sitima yomka ku msasa wachibalo ku Czechoslovakia, koma ndinaimitsidwa ku Vienna ndi kuikidwa m’ndende kumeneko. Mikhalidwe yake inali yowopsa. Si njala yokha imene ndinavutika nayo, komanso usiku ndinali kulumidwa ndi nsikidzi zazikuluzikulu zimene zinatulutsa magazi pakhungu langa ndi ululu. Ndiyeno pa zifukwa zosadziŵika bwino kwa ine, ndinabwezeretsedwa ku ndende ya Graz.

Mlandu wanga unachititsa chidwi chifukwa chakuti Agestapo analongosola Mboni za Yehova kukhala ofera chikhulupiriro otengeka maganizo amene anafuna chilango cha imfa kotero kuti akapeze mphotho yakumwamba. Monga chotulukapo chake, kwa masiku aŵiri ndinali ndi mwaŵi wabwino kwambiri wa kulankhula pamaso pa profesa ndi ophunzira asanu ndi atatu a ku Graz University, ndikumafotokoza kuti anthu 144,000 okha ndiwo amene adzatengeredwa kumwamba kukalamulira ndi Kristu. (Chivumbulutso 14:1-3) Chiyembekezo changa, ndinatero, chinali cha kulandira moyo wosatha mu mkhalidwe wa paradaiso padziko lapansi.—Salmo 37:29; Chivumbulutso 21:3, 4.

Pambuyo pa masiku aŵiri a kufunsidwa, profesayo anati: “Ndafikira pa kuzindikira kuti chiyembekezo chako chonse chili cha padziko lino lapansi. Chikhumbo chako sichili chakuti ufe ndi kupita kumwamba.” Iye anasonyeza chisoni ponena za chizunzo cha Mboni za Yehova ndipo anandifunira mafuno abwino.

Kuchiyambiyambi kwa 1941, ndinakwezedwa sitima yomka ku msasa wachibalo wa Rollwald ku Germany.

Moyo Wankhanza wa mu Msasa

Rollwald anali pakati pa mzinda wa Frankfurt ndi wa Darmstadt ndipo anali ndi akaidi 5,000. Tsiku lililonse linkayamba pa 5:00 a.m. ndi kuitanidwa maina, kumene kunatenga pafupifupi maola aŵiri, pamene maofesala anali kukonzanso mwaulesi mpambo wawo wa akaidi. Tinafunikira kuimirira mosatakata, ndipo akaidi ambiri anasauka ndi kukwapulidwa kwakukulu chifukwa cha kusaima bwino.

Mfisulo unali wa buledi wopangidwa ndi ufa wa tirigu, mfumbemfumbe, ndi mbatata za kachewere zimene kaŵirikaŵiri zinali zovunda. Ndiyeno tinkapita kudambo kukagwira ntchito, kukumba ngalande zoumitsira madzi a malowo kaamba ka zifuno zaulimi. Titagwira ntchito m’dambolo tsiku lonse opanda nsapato, mapazi athu ankatupa kwambiri. Nthaŵi ina mapazi anga anayamba kukhala ndi zilonda zimene zinaonekera ngati zonyeka, ndipo ndinaopa kuti mwina akadulidwa.

Masana tili kuntchitoko, tinkapatsidwa zinthu zinazake zoyesera zosapsa zotchedwa msuzi. Zinali kuikidwa turnip kapena kabichi ndipo nthaŵi zina zinasanganizidwa ndi nyama yogayidwa ya zifuyo zofa ndi matenda. M’kamwa mwathu ndi pammero panali kuŵaŵa, ndipo ambiri a ife tinatuluka zithupsa zazikulu. Madzulo tinkalandira “msuzi” winanso. Akaidi ambiri anaguluka mano, koma ine ndinali nditauzidwa za kufunika kwa kugwiritsira ntchito kwambiri mano. Ndinkatafuna timitengo ta mkungudza kapena mphukira za hazel, ndipo anga sanaguluke konse.

Kukhala Olimba Mwauzimu

Poyesayesa kuswa chikhulupiriro changa, alonda anandiika m’malo andekha osaonana ndi Mboni zina. Popeza kuti ndinalibe mabuku ofotokoza Baibulo, ndinkakumbukira malemba amene ndinali nditaloweza, onga ngati Miyambo 3:5, 6, imene imatilimbikitsa ‘kukhulupirira Yehova ndi mtima wathu wonse,’ ndi 1 Akorinto 10:13, amene amalonjeza kuti Yehova ‘sadzalola ife kuyesedwa kuposa kumene tikhoza.’ Mwa kusinkhasinkha malemba otero m’maganizo mwanga ndi mwa kuyedzamira pa Yehova m’pemphero, ndinalimbitsidwa.

Nthaŵi zina ndinali wokhoza kuona Mboni imene inali kusamutsidwira ku msasa wina. Ngati tinalibe mwaŵi wa kulankhulana, tinkalimbikitsana kukhala ochirimika mwa kugwedezerana mitu kapena mwa kutukula nkhonya. Nthaŵi ndi nthaŵi ndinkalandira makalata kuchokera kwa Maria ndi Amayi. M’kalata ina ndinadziŵitsidwa za imfa ya mbale wanga wokondedwa Gregor, ndipo mu ina, cha kumapeto kwa nkhondoyo, ndinadziŵitsidwa za kunyongedwa kwa Hans Stossier, mlongo wa Maria.

Pambuyo pake, mkaidi wina amene anadziŵa Gregor pamene anali onse ku ndende ya Moabit ku Berlin anasamutsidwira mu msasa wathu. Ndinamva zonse zimene zinachitika kuchokera kwa iye. Gregor anali atapatsidwa chilango cha kudulidwa mutu pa makako, koma poyesayesa kuswa umphumphu wake nyengo yalamulo yoyembekezera kuphedwa inatalikitsidwa kufikira ku miyezi inayi. M’nthaŵi imeneyo zitsenderezo za mitundu yonse zinaperekedwa pa iye kuti zimchititse kulolera molakwa—anamangidwa unyolo wolemera m’mikono yake ndi mapazi, ndipo kaŵirikaŵiri sankapatsidwa chakudya. Komabe, sanagwedezeke. Anali wokhulupirika kufikira mapeto—March 14, 1942. Ngakhale kuti ndinamva chisoni ndi mbiriyo, ndinalimbitsidwa nayo kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova, zivute zitani.

M’kupita kwanthaŵi ndinamvanso kuti ang’ono anga Kristian ndi Willibald ndi alongo anga aang’ono Ida ndi Anni anatengeredwa kunyumba ya avirigo yogwiritsiridwa ntchito monga nyumba yophunzitsira ana mwambo ku Landau, Germany. Anyamatawo anamenyedwa kwambiri chifukwa cha kukana kutamanda Hitler.

Mipata ya Kuchitira Umboni

Ambiri amene anali m’malo a ankhondo kumene ndinali kukhala anali akaidi andale ndi apandu. Kaŵirikaŵiri ndinathera usiku ndikuwachitira umboni. Mmodzi anali wansembe Wachikatolika wa ku Kapfenberg wotchedwa Johann List. Iye anamangidwa chifukwa chakuti anali atalankhula ku mpingo wake za zinthu zimene anamva pa British Broadcasting.

Johann anavutika kwambiri chifukwa chakuti sanazoloŵere ntchito yakuthupi yakalavula gaga. Anali mwamuna wokondweretsa, ndipo ndinkamthandiza kumaliza ntchito yake kotero kuti asaloŵe m’mavuto. Iye anati anachita manyazi chifukwa chakuti anamangidwira zifukwa zandale ndipo osati chifukwa cha kumamatira malamulo amkhalidwe Achikristu. “Iwe ukuvutikadi monga Mkristu,” iye anatero. Pamene anamasulidwa pafupifupi chaka chimodzi pambuyo pake, analonjeza kukaona amayi ndi bwenzi langa, lonjezo limene analisunga.

Moyo Wanga Uwongokera

Kumapeto kwa 1943, tinapatsidwa mkulu wa msasa watsopano wotchedwa Karl Stumpf, mwamuna wamtali, watsitsi loyera amene anayamba kuwongolera mikhalidwe mumsasa wathu. Nyumba yake inafunikira kupakidwa penti, ndipo pamene anadziŵa kuti ntchito yanga inali yopaka penti, ndinapatsidwa ntchitoyo. Imeneyi inali nthaŵi yoyamba kuchotsedwa pa kugwira ntchito kudambo.

Mkazi wa mkuluyo sanamvetsetse chifukwa chake ndinamangidwa, ngakhale kuti mwamuna wake anamfotokozera kuti ndinali mmenemo chifukwa cha chikhulupiriro changa monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Anandimvera chisoni chifukwa chakuti ndinali wowonda kwambiri ndipo anandipatsa chakudya. Iye anandilinganizira ntchito zambiri kotero kuti ndilimbenso mwakuthupi.

Pamene akaidi a mu msasawo anali kuitanidwa kukamenya nkhondo kumene inali kulirima chakumapeto kwa 1943, unansi wanga wabwino ndi Mkuluyo Stumpf unandipulumutsa. Ndinamfotokozera kuti ndingalole kufa koposa kukhala waliwongo lokhetsa mwazi mwa kukhala ndi phande mu nkhondo. Ngakhale kuti kaimidwe kanga kauchete kanamuika m’mkhalidwe wovuta, anali wokhoza kuchotsa dzina langa pa mpambo wa oitanidwa.

Masiku Otsiriza a Nkhondo

Mkati mwa January ndi February wa 1945, ndege za ku America zouluka chapansipansi zinatilimbikitsa mwa kugwetsa mapepala amene anati nkhondoyo inali pafupi kutha. Mkuluyo Stumpf, amene anapulumutsa moyo wanga, anandipatsa zovala wamba nandisunga m’nyumba mwake monga mobisalira. Pochoka ku msasawo, ndinaona chipwirikiti chachikulu. Mwachitsanzo, ana ovala zovala za nkhondo ali ndi misozi pankhope zawo anali kuthaŵa ankhondo a ku America. Powopera kuti ndingapezane ndi maofesala a SS amene angadabwe chifukwa chake sindinanyamule mfuti, ndinasankha kubwerera ku msasa.

Posapita nthaŵi msasa wathu unazingidwa kotheratu ndi magulu ankhondo a ku America. Pa March 24, 1945, msasawo unagonja, ukumaimika mbendera zoyera. Ha, ndinadabwa chotani nanga kudziŵa kuti mu msasa wowonjezera munali Mboni zina zimene zinatetezeredwanso pa kuphedwa ndi Mkuluyo Stumpf! Kunali kukumana kosangalatsadi! Pamene Mkuluyo Stumpf anamangidwa, ambiri a ife tinafikira maofesala a ku America ndi kupereka umboni womchinjiriza mwapakamwa ndiponso ndi kalata. Monga chotulukapo chake, iye anamasulidwa pambuyo pa masiku atatu.

Ndinadabwa kwambiri kuona kuti ndinali woyamba wa akaidi 5,000 kumasulidwa. Pambuyo pa ukaidi wa zaka zisanu, ndinaona monga ngati kuti ndikulota. Ndinathokoza Yehova m’pemphero misozi yachisangalalo ili m’maso, chifukwa cha kundisunga wamoyo. Germany sanagonje kufikira pa May 7, 1945, pafupifupi milungu isanu ndi umodzi pambuyo pake.

Nditamasulidwa, ndinaonana nthaŵi yomweyo ndi Mboni zina za m’deralo. Kagulu ka phunziro la Baibulo kanalinganizidwa, ndipo mkati mwa milungu yotsatira, ndinathera maola ambiri ndi kuchitira umboni kwa anthu a dera lozungulira msasawo. Panthaŵi imodzimodziyo, ndinapeza ntchito monga wopaka penti.

Kubwereranso Kwathu

Mu July, ndinagula njinga yamoto ndiyeno kuyamba ulendo wanga wautali kumka kwathu. Ulendowo unatenga masiku angapo, popeza kuti milatho yambiri mu msewu waukulu inali itaphulitsidwa ndi mabomba. Pomalizira pake pamene ndinafika kwathu ku St. Martin, ndinayendetsa njinga yamoto kukwera ndi msewu ndipo ndinaona Maria akututa tirigu. Pamene anandizindikira, anandithamangira. Tangolingalirani za kugwirizananso kwachimwemweko. Amayi anatayira zenga lawo pansi nandithamangiranso. Tsopano, pambuyo pa zaka 49, Amayi ali ndi zaka 96 ndi akhungu. Maganizo awo akali akuthwa, ndipo akali Mboni ya Yehova yokhulupirika.

Maria ndi ine tinakwatirana mu October 1945, ndipo m’zaka zambiri kuyambira pamenepo, tasangalala kutumikira Yehova pamodzi. Tadalitsidwa ndi ana aakazi atatu, mwana wamwamuna, ndi zidzukulu zisanu ndi chimodzi, onsewo akutumikira Yehova mwachangu. M’zaka zonsezi ndakhala ndi chikhutiro cha kuthandiza anthu ambiri kuimira choonadi cha Baibulo.

Kulimba Mtima kwa Kupirira

Nthaŵi zambiri ndafunsidwa mmene ndinalili wokhoza kuyang’anizana ndi imfa popanda mantha monga wachichepere. Ndikhulupirireni—Yehova Mulungu amapereka nyonga ya kupirira ngati muli wotsimikizira kukhalabe wokhulupirika. Munthu amaphunzira mofulumira kumkhulupirira kotheratu mwa pemphero. Ndipo kudziŵa kuti ena, kuphatikizapo atate ndi mbale wanga, anapirira mokhulupirika kufikira imfa kunandithandizanso kukhalabe wokhulupirika.

Sikunali ku Ulaya kokha kumene anthu a Yehova sanachirikize mbali ina mu nkhondo. Ndikukumbukira kuti mkati mwa kuzenga milandu kwa ku Nuremberg mu 1946, mmodzi wa maofesala aakulu wa Hitler anali kufunsidwa ponena za chizunzo cha Mboni za Yehova m’misasa yachibalo. Iye anatulutsa m’thumba mwake kachidutswa ka panyuzipepala kamene kanasimba kuti Mboni za Yehova zikwi zambiri ku United States zinali m’ndende za mu America chifukwa cha uchete wawo mkati mwa Nkhondo Yadziko II.

Ndithudi, Akristu oona amatsatira molimba mtima chitsanzo cha Yesu Kristu, amene anasunga umphumphu kwa Mulungu kufikira pakupuma kwake komaliza. Kaŵirikaŵiri ndimaganiza za ziŵalo 14 za anthu a mpingo wathu waung’ono wa mu St. Martin mkati mwa ma 1930 ndi ma 1940 kufikira lerolino, amene chifukwa cha kukonda Mulungu ndi munthu mnzawo, anakana kuchirikiza nkhondo ya Hitler ndipo chifukwa cha zimenezo iwo anaphedwa. Kudzakhala kugwirizananso kosangalatsa kwambiri chotani nanga pamene adzaukitsidwira kumoyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu!

[Chithunzi patsamba 26]

Atate anga

[Chithunzi patsamba 28]

Mu 1939, Maria ndi ine tinatomerana

[Chithunzi patsamba 31]

Banja lathu. Kuyambira kulamanzere kumka kulamanja: Gregor (anadulidwa mutu), Anni, Franz, Willibald, Ida, Gregor (atate, anadulidwa mutu), Barbara (amayi), ndi Kristian

[Chithunzi patsamba 32]

Maria ndi ine lerolino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena