Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • pe mutu 18 tsamba 148-154
  • “Mapeto a Dziko” Ayandikira!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Mapeto a Dziko” Ayandikira!
  • Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Nkhani Yofanana
  • Ufumu wa Mulungu Uyamba Kulamulira Pakati pa Adani Ace
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kodi Chiwonongeko cha Dziko Chonenedweratucho Chidzadza Liti?
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Masiku Otsiriza
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Kodi Dongosolo Lamakonoli Lidzakhala Kwautali Wotani?
    Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
Onani Zambiri
Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
pe mutu 18 tsamba 148-154

Mutu 18

“Mapeto a Dziko” Ayandikira!

1. Kodi atsatiri apadziko lapansi a Kristu akadziwa motani nthawi pamene iye adayamba kulamulira kumwamba?

PAMENE YESU KRISTU anachotsa Satana ndi angelo ake kumwamba nayamba ulamuliro wake Waufumu, kunatanthauza kuti mapeto a Satana ndi dongosolo lake loipa anayandikira. (Chivumbulutso 12:7-12) Koma kodi atsatiri a Kristu padziko lapansi akadziwa motani kuti chochitika chimenechi kumwamba, chosawoneka ku maso awo, chidachitika? Kodi iwo akadziwa motani kuti Kristu anafika mosawoneka mu ulamuliro Waufumu ndi kuti “mapeto a dziko” anali pafupi? Iwo akadadziwa mwa kupenda kuti awone ngati “chizindikiro” chimene Yesu anapereka chinalinkukwaniritsidwa.

2. Kodi ophunzira a Kristu anamfunsa funso lotani?

2 Imfa ya Yesu iri pafupi kwenikweni, pamene anali chikhalire pa Phiri la Azitona, anai a atumwi ake anadza kudzamfunsa “chizindikiro.” Umu ndimo mmene funso lawo lawerengedwera, mu King James Version, ndi mamiliyoni ambiri a anthu: “Tiuzeni, kodi zinthu zimenezi zidzakhala liti? ndipo kodi nchiyani chimene chidzakhala chizindikiro cha kudza kwanu, ndi cha mapeto a dziko?” (Mateyu 24:3) Koma kodi manenedwe amenewa, “kudza kwanu” ndi “mapeto a dziko,” amatanthauzanji kwenikweni?

3. (a) Kodi manenedwewo “kudza kwanu”ndi “mapeto a dziko” amatanthauzanji kwenikweni? (b) Pamenepa, kodi ndimotani mmene funso lofunsidwa ndi ophunzira a Kristu latembenuzidwira molondola?

3 Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa pano kukhala “kudza” ndilo parousia, ndipo limatanthauza “kukhalapo.” Chotero, pamenepa, pamene “chizindikirocho” chiwoneka, zimenezi zikutanthauza kuti tikadziwa kuti Kristu wafika ngakhale ngosawoneka, kuti iye wadza kale mu ulamuliro Waufumu. Kanenedweko “mapeto a dziko” nkosokeretsanso kwambiri. Sikamatanthauza mapeto a nthakayi, koma, m’malo mwake, mapeto a dongosolo la zinthu la Satana. (2 Akorinto 4:4) Chifukwa cha chimenecho funso la atumwiwo mosalakwitsa limati: “Tiuzeni, Kodi zinthu zimenezi zidzakhala liti, ndipo kodi nchiyani chimene chizakhala chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a dongosolo la zinthu?’—Mateyu 24:3, New World Translation.

4. (a) Kodi nchiyani chimene chimapanga “chizindikiro” chimene Yesu anapereka? (b) Kodi “chizindikirocho” chingayerekezeredwe ndi chidindo cha chala m’njira yotani?

4 Yesu sanapereke chochitika chimodzi chokha monga “chizindikiro.” Iye anasimba zochitika ndi mikhalidwe yambiri. Olemba Baibulo ena kuphatikizapo Mateyu anatchula zochitika zina zimene zikasonyeza “masiku otsiriza.” Zinthu zonsezi zimene zinanenedweratu zikachitika mkati mwa nthawi imene olemba Baibulo anatcha “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1-5; 2 Petro 3:3 ,4) Zochitika zimenezi zikakhala ngati mizera yosiyanasiyana imene imapanga chidindo cha chala cha munthu, chidindo chimene sichingakhale cha munthu wina aliyense. “Masiku otsiriza” ali ndi malukidwe awoawo a zizindikiro, kapena zochitika. Zimenezi zimapanga “chidindo cha chala” chotsimikizika chimene sichingakhale cha nyengo ina iriyonse yanthawi.

5, 6. Pamene mupenda maumboni 11 a “masiku otsiriza” pamasamba otsatirapowa, kodi mukuzindikira chiyani ponena za “mapeto a dongosolo la zinthu?”

5 M’mutu 16 wa bukhu lino tinalingalira umboni Wabaibulo wakuti Kristu anabweranso nayamba kulamulira pakati pa adani ake m’chaka cha 1914. Tsopano yang’anitsitsani mbali zosiyanasiyana za “chizindikiro” cha kukhalapo kwa Kristu ndi umboni wowonjezereka wa “masiku otsiriza” a dongosolo la zinthu loipa la Satana. Pamene mupenda zinthu zonenedweratu zimenezi pa masamba anai otsatirapowo, wonani mmene izo zakhala zikukwaniritsidwira chiyambire 1914.

“MTUNDU UMODZI WA ANTHU UDZAUKIRANA NDI MTUNDU WINA, NDI UFUMU NDI UFUMU WINA.”—Mateyu 24:7.

Ndithudi mwawona mbali imeneyi ya “chizindikiro” ikukwaniritsidwa chiyambire 1914! M’chaka chimenecho Nkhondo Yoyamba ya Dziko inayamba. Mu mbiri simunakhale nkhondo yowopsa yotero. Inali nkhondo yanamkukule. Nkhondo Yoyamba ya Dziko inali yokulirapo kwambiri koposa nkhondo zazikulu zonse zomenyedwa mkati mwa zaka 2,400 1914 isanafike. Komabe zaka 21 zokha nkhondo imeneyo itatha, Nkhondo Yoyamba ya Dziko inayamba. Ndipo inali yowononga ngati Nkhondo Yachiwiri ya Dziko kowirikiza kanai.

Nkhondo zowopsa zikupitiriza kumenyedwa. Chiyambire pamene Nkhondo Yachiwiri ya Dziko inatha mu 1945, oposa anthu mamiliyoni 25 aphedwa m’nkhondo zokwanira 150 zomenyedwa padziko lonse lapansi. Pa tsiku lirilonse, pakhala, pa avereji, nkhondo 12 zochitika kwina kwake m’dziko lapansi. Ndipo pali chiwopsezo chosalekeza cha nkhondo ina yadziko. United States yokha iri ndi zida zankhondo zanyukliya zokwanira kupha mwamuna aliyense, mkazi ndi mwana padziko lapansi koposa nthawi 12!

“KUDZAKHALA NJALA.”—Mateyu 24:7.

Motsatizana ndi Nkhondo Yoyamba ya Dziko panadza njala yaikulu koposa mu mbiri yonse. Chakumpoto kwa China kokha 15,000 anafa tsiku lirilonse ndi njala. Koma kusoweka kwa chakudya kunalidi kokulirapo pambuyo pa Nkhondo Yachiwiri ya dziko. Chigawo chimodzi mwa zinai za dziko pa nthawi imeneyo chinali ndi njala! Ndipo chiyambirecho, chakudya chakhalabe chosowa kwa anthu ambiri padziko lapansi.

“Masekendi 8.6 alionse munthu wina m’dziko losatukuka akufa ndi kudwala kochititsidwa ndi kudya kosakwanira,” inatero New York Times mu 1967. Mamiliyoni ambiri akufabe ndi njala—okwanira mamiliyoni 50 pa chaka! Pofika 1980, pafupifupi chigawo chimodzi mwa zinai cha anthu padziko lapansi (anthu 1,000,000,000) anali ndi njala chifukwa chakuti iwo sanathe kupeza chokwanira kuti adye. Ngakhale m’malo kumene chakudya chiri chochuluka, ambiri ngosowa kwambiri kosakhoza kuchigula.

“MILIRI M’MALO AKUTIAKUTI.”—Luka 21:11.

Pambuyo penipeni pa Nkhondo Yoyamba ya Dziko anthu ambiri anafa ndi flu Yachispanya koposa amene adafa ndi mliri wa nthenda ina iriyonse mu mbiri ya anthu. Chiwerengero cha akufa chinalo chokwanira anthu mamiliyoni 21! Komabe mliri ndi nthenda zikupitiriza kufala. Mamiliyoni ambiri amafa chaka chirichonse ndi nthenda yamtima ndi khensa. Nthenda yopatsana mwa kugonana ikufala mofulumira. Nthenda zina zowopsa, monga ngati malungo, likodzo ndi khungu lochititsidwa ndi kulumidwa ndi ntchentche za m’mitsinje ina, zimapezeka m’dziko ndi dziko, makamaka mu Asia, Africa ndi Latin America.

“KUDZAKHALA . . . ZIVOMEREZI M’MALO AKUTIAKUTI.”—Mateyu 24:7.

Kuyambira 1914 kufikira tsopano, pakhala zivomerezi zazikulu zambirimbiri koposa m’nyengo ina iriyonse yofananayo mu mbiri yolembedwa. Kwa zaka zoposa 1,000, kuyambira m’chaka cha 856 C.E. kufikira 1914, kunali zivomezi zazikulu 24 zokha, zikumachititsa akufa okwanira 1,973,000. Koma m’zaka 63 kuyambira 1915 kufikira 1978, chiwonkhetso cha anthu okwanira 1,600,000 anafa m’zivomerezi zazikulu 43.

“KUCHULUKA KWA KUSAYERUZIKA.”—Mateyu 24:12.

Padziko lonse lapansi pakuchokera malipoti a kusayeruzika ndi upandu zowonjezereka. Maupandu a chiwawa, monga ngati mbanda, kugwirira chigololo ndi kulanda, zikuwonjezeka kwambiri tsopano. Mu United States mokha, upandu waukulu umachitidwa, pa avereji, pafupifupi sekendi iriyonse. M’malo ambiri palibe amawona kukhala wosungika pamakwalala, ngakhale masanasana. Usiku anthu amakhala m’nyumba zawo kutseri kwa zitseko zokhomedwa loko ndi zoipichizidwa, owopa kupita kunja.

“ANTHU AKUKOMOKA NDI MANTHA.”—Luka 21:26.

Mantha mwina mwake ndiwo lingaliro limodzi lalikulu koposa m’miyoyo ya anthu lerolino. Sipanapite nthawi yaitali pambuyo pa kuphulika kwa mabomba oyamba anyukliya, wasayansi ya maatomu Harold C. Urey anati: “Tidzadya mantha, tidzagona mantha, kukhala m’mantha ndi kufa m’mantha.” Kwa ochuluka a anthu zimenezi ndizo zimene zikuchitika. Ndipo sikuli chabe chifukwa cha chiwopsezo chachikhalire cha nkhondo yanyukliya. Anthu amawopanso upandu, kuipitsa, nthenda, kukwera mitengo kwa zinthu ndi zinthu zina zambiri zimene zimawopseza chisungiko chawo ndi miyoyo yawo yeniyeniyo.

‘KUSAMVERA MAKOLO.’—2 Timoteo 3:2.

Makolo lerolino kawirikawiri amakhala ndu ulamuliro wochepa pa ana awo. Ana amapandukira ulamuliro wonse. Motero dziko lirilonse padziko lapansi layambukiridwa ndi mliri wa upandu wa ana. Lopitirira theka la maupandu onse aakulu m’maiko ena amachitidwa ndi ana ausinkhu wa zaka 10 kufikira 17. Mbanda, kugwirira chigololo, kuukira, kulanda, kuswa nyumba, kuba magalimoto—ana akuchita zinthu zonsezi. Kusamvera makolo sikunakhale kofala kwambiri mu mbiri ngati tsopano.

“OKONDA NDALAMA.”—2 Timoteo 3:2.

Kulikonse kumene mukuyang’ana lerolino mungawone machitidwe a umbombo. Ambiri adzachita pafupifupi chirichonse kaamba ka ndalama. Iwo adzaba kapena ngakhale kupha. Sikwachikendo kwa anthu aumbombo kupanga ndi kugulitsa zinthu zimene zikudziwika, m’njira ina, kukhala zikupangitsa ena kudwala kapena kuwapha. Mwina poyera, kapena mwa njira imene iwo akukhalira ndi moyo, anthu ponena za ndalama akuti: ‘Imeneyi ndiyo mulungu wanga.’

“OKONDA ZOKONDWERETSA MUNTHU OSATI OKONDA MULUNGU.”—2 Timoteo 3:4.

Anthu ochuluka lerolino amaganizira kokha za kuchita chimene chimakondweretsa iwo kapena mabanja awo, osati chimene chimakondweretsa Mulungu. Makamaka ambiri amakonda zimene Mulungu amatsutsa, kuphatikizapo dama, chigololo, kuledzera, kugwiritsira ntchito moipa mankhwala ndi zina zotchedwa zokondweretsa. Ngakhale zokondweretsa zimene, mwa izo zokha, zingakhale zabwino zimaikidwa patsogolo pa kuyesayesa kulikonse kwa kuphunzira za Mulungu ndi kumtumikira.

“AKUKHALA NAWO MAWONEKEDWE A CHIPEMBEDZO, KOMA MPHAMVU YAKE ADAIKANA.”—2 Timoteo 3:5.

Atsogoleri adziko ndi anthu wamba mofanana kawirikawiri amapanga kudzisonyezera kwakunja kwa kukhala opembedza. Iwo angafike pamaserevesi atchalitchi ndi kupereka zopereka za ntchito zachipembedzo. Awo okhala m’boma angaike dzanja lawo pa Baibulo pamene iwo akuyamba ulamuliro. Koma kawirikawiri kumangokhala “mawonekedwe a chipembedzo” Monga momwedi Baibulo linaneneratu, kulambira kowona kwa Mulungu sikulidi mphamvu Yosonkhezera m’miyoyo ya anthu ochuluka lerolino. Iwo sakusonkhezeredwa ndi mphamvu yeniyeni ya chabwino.

“KUWONONGA DZIKO.”—Chivumbulutso 11:18.

Mpweya umene tikupuma, madzi amene tikumwa ndi nthaka pa imene zakudya zathu zikulimidwa zirinkuipitsidwa. Nkwakukulu kwambiri chakuti wasayansi Barry Commoner anachenjeza kuti: “Ndikukhulupirira kuti kuipitsidwa kwa dziko lapansi kopitirizabe, ngati sikuletsedwa, potsirizira pake kudzawononga kuyenerera kwa pulaneti lino kukhala malo a moyo waanthu.”

6 Pambuyo pa kulingalira zapitazo, kodi sikwachiwonekere kuti “chizindikiro” chimene Kristu anapereka ndi maumboni onenedweratu ndi ophunzira ake tsopano zirinkukwaniritsidwa? Ngakhale kuli kwakuti pali maumboni ena ambiri, awo ondandalikidwa pano ayenera kukhala okwanira kusonyeza kuti ife tirinkukhaladi m’nthawi imene Baibulo linaneneratu kukhala “masiku otsiriza.”

7. (a) Kodi nchiyani chimene chimapangitsa maulosi Abaibulo onena za kukhalapo kwa Kristu ndi “masiku otsiriza” kukhala apadera kwambiri? (b) Mosiyana ndi zimene Baibulo linaneneratu, kodi atsogoleri adziko anali kuneneratu chiyani 1914 isanafike?

7 Komabe anthu ena anganene kuti: ‘Zinthu zonga ngati nkhondo, njala, miliri ndi zivomerezi zachitika kawirikawiri mu mbiri yonse. Motero sikukanakhala kovuta kuneneratu kuti izo zikachitikanso.’ Koma taganizirani: Baibulo silinaneneretu zinthu zokhazi, koma linasonyeza kuti izo zikachitika padziko lonse. Ndiponso, Baibulo linanena kuti zinthu zonsezi zikachitika pa mbadwo umene unali wamoyo mu 1914. Komabe kodi atsogoleri adziko otchuka anali kuneneratu chiyani 1914 itatsala pang’ono kufika? Iwo anali kunena kuti mikhalidwe yosonyeza mtendere wadziko inali yabwino kwambiri koposa kale lonse. Komabe mavuto owopsa amene Baibulo limaneneratu anayamba pa nthawi yeniyeni, mu 1914! Kunena zowona, atsogoleri adziko tsopano akunena kuti 1914 inali posinthira mu mbiri.

8. (a) Kodi ndimbadwo uti umene Yesu anasonyeza kuti ukawona mapeto a dongosolo lino la zinthu? (b) Motero kodi ife tingakhale otsimikizira za chiyani?

8 Atasonyeza zinthu zambiri zimene zasonyeza nyengoyo kuyambira 1914 kumkabe mtsogolo, Yesu anati: “Mbadwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonse [kuphatikizapo mapeto a dongosolo lino] zidzachitidwa.” (Mateyu 24:34, 14) Kodi Yesu anatanthauza mbadwo uti? Anatanthauza mbadwo wa anthu amene anali ndi moyo mu 1914. Anthu otsalabe amenewo a mbadwo umenewo tsopano akalamba kwambiri. Komabe, ena a iwo adzakhalabe amoyo kuti awone mapeto a dongosolo loipa lino. Motero tingakhale otsimikizira za zimenezi: Posachedwapa tsopano kudzakhala mapeto amwadzidzidzi a kuipa konse ndi anthu oipa pa Harmagedo.

[Chithunzi patsamba 149]

Yesu anauza ophunzira ake chimene chikakhala umboni wowoneka wa kukhalapo kwake kosawoneka mu ulamuliro Waufumu

[Chithunzi patsamba 154]

1914—HARMAGEDO

Ena a mbadwo wokhala ndi moyo mu 1914 adzawona mapeto a dongosolo la zinthu ndi kuwapyola

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena