Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 7/8 tsamba 7-11
  • Kukhala Pamodzi Mwachikondi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukhala Pamodzi Mwachikondi
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chikondi—“Chomangira cha Mtima Wamphumphu”
  • “Imvi Ndiyo Korona wa Ulemu”
  • Mapindu a Kukulitsa Maunansi a Banja
  • Mapindu a Kuchitirana Ulemu
  • Mbali ya Kuphunzitsa ya Agogo
  • Kuchita Mogwirizana ndi Chiphunzitso Chaumulungu
  • Kodi Ena a Mavutowo ndi Otani?
    Galamukani!—1995
  • Kukhala Gogo—Kusangalatsa Kwake Ndiponso Mavuto Ake
    Galamukani!—1999
  • Kodi Nditani Kuti Ubale Wanga ndi Agogo Ulimbe?
    Galamukani!—2001
  • Pamene Agogo Amakhala Makolo
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 7/8 tsamba 7-11

Kukhala Pamodzi Mwachikondi

Agogo aakazi ndi aamuna okondedwa,

Kodi muli bwino? Ndiganiza kuti ndigwidwa ndi chimfine.

Ndikukuthokozani chifukwa choseŵera nane tsiku lija. Munandipititsa ku paki ndi kudziŵe. Ndinasangalala kwambiri.

Chaka chamaŵa pa February 11, tidzakhala ndi konsati kusukulu kwathu. Ngati mudzafika kuno, chonde mudzafikeko.

Agogo, timasangalala mukabwera kuno.

Chonde mudzisamalire, ndipo ndikufunirani mafuno abwino. Kunja kudzazizira, choncho samalani kuti musagwidwe ndi chimfine.

Ndikuyembekezera pamene mudzafika kuno ndi kudzaseŵera nane. Chonde mundiperekere moni kwa Yumi ndi Masaki.

Mika (Mjapani)

KODI mdzukulu wanu anayamba wakulemberanipo kalata yonga imeneyi? Ngati ndi choncho, inu mosakayikira munasangalala kwambiri pamene munailandira. Makalata otero ali umboni wa ubale wabwino kwambiri ndi wachikondi pakati pa agogo ndi adzukulu. Koma kodi nchiyani chimene chimafunika pa kukhazikitsa, kusamalira, ndi kulimbitsa unansi wa mtundu umenewu? Ndipo kodi ungakhale wopindulitsa motani ku mibadwo yonse itatu?

Chikondi—“Chomangira cha Mtima Wamphumphu”

Roy ndi Jean, agogo aŵiri Achibritishi, akuti: “Mfundo zazikulu, monga momwe tikuonera, ndizo kuzindikira umutu ndi kumvana mwachikondi.” Mboni za Yehova ziŵiri zimenezi zinatchula mwapadera Akolose 3:14, amene amafotokoza chikondi cha Chikristu monga “chomangira cha mtima wamphumphu.” Chikondi chimatulutsa ulemu, kuderana nkhaŵa, kukondana, ndi umodzi wa banja. Pamene tate afika kuchokera ku ntchito, banja lonse limamthamangira kukakumana naye ndi kumlandira mwachikondi. Ngati chikondi chili m’banja, chinthu chimodzimodzicho chimachitika pamene agogo afika. “Agogo aakazi ndi aamuna abwera!” amafuula motero mwana wokondwa. Usikuwo, banja lonselo limadyera pamodzi chakudya, ndipo agogo aamuna, mwamwambo, amakhala pamalo awo osungidwa monga mutu. Kodi mungadziike inuyo ndi banja lanu mu mkhalidwe umenewu wachikondi? Kodi muli ndi dalitso limeneli?

“Imvi Ndiyo Korona wa Ulemu”

Mwachionekere, chikondi ndi kuchitira ulemu agogo ziyenera kusonyezedwa nthaŵi zonse, osati pa nthaŵi zina zapadera chabe. Motero nkofunika kuphunzitsa ana mosalekeza. Ana amaphunzira kukonda achibale ndi anthu ena m’banja, potsatira chitsanzo choperekedwa ndi makolo awo. Chitsanzo chawo nchofunika, monga momwe ambiri amene anafunsidwa za nkhaniyi anasonyezera. Macaiah, atate wa ku Benin City, Nigeria, akuti: “Ndiganiza kuti chitsanzo changa cha kuchitira ulemu apongozi anga chathandizanso ana anga kukhala odzichepetsa ndi aulemu. Ndimatcha apongozi anga kuti ‘Atate’ ndi ‘Amayi.’ Ana anga amamva zimenezi ndi kuona kuti ndimawalemekeza monga makolo anga enieni.”

Ngati adzukulu alephera kuchitira ulemu agogo awo, iwowo angakwiye, kwenikweni osati chifukwa cha kulakwako koma chifukwa chakuti makolowo samawadzudzula. Demetrio, gogo wachimuna wa ku Rome, Italy, akuti: “Nditha kuona chikondi chimene mwana wanga wamkazi ndi mkamwini wanga ali nacho pa ife ndi mmene amaphunzitsira adzukulu athu kutilemekeza.” Nthaŵi zina, adzukulu angachite ndi agogo m’njira yomasuka monkitsa kwambiri, monga ngati kuti ali oseŵera nawo ausinkhu wawo wamba, kapena kuchita modzikweza pa iwo. Ndi thayo la makolo kuwongolera khalidwe lililonse lotero. Paul, Mboni ya ku Nigeria, akuti: “Pafupifupi chaka chapitacho, ana anayamba kuderera mayi wanga. Pamene ndinaona zimenezi, ndinawaŵerengera Miyambo 16:31: ‘Imvi ndiyo korona wa ulemu,’ ndinawakumbutsanso kuti Agogo aakaziwo ndi mayi wanga. Monga momwe iwo amandilemekezerera, ayenera kulemekezanso agogowo. Ndinaphunzira nawonso mutu 10 wa buku la Your Youth—Getting the Best Out Of It,a wakuti ‘How Do You View Your Parents?’ Tsopano, alibe vuto lililonse pa kuchitira ulemu agogo awo aakazi.”

Mapindu a Kukulitsa Maunansi a Banja

Kukondana kungakulitsidwe ngakhale pamene ziŵalo za banja zikukhala motalikirana. Stephen, gogo wachimuna wa ku Nigeria, akuti: “Timalembera mdzukulu wathu aliyense payekha. Imeneyi ndi ntchito yaikulu, koma mfupo yake ya kumanga ndi kusamalira ubale wamphamvu ndi adzukulu yakhala yaikulu kwambiri.” Zoyesayesa za makolo nzofunika pankhaniyi. Ena, malinga ndi mikhalidwe yawo, amadziŵitsana za umoyo pa telefoni.

Giuseppe, gogo wachimuna wa ku Bari, Italy, amene ali ndi zidzukulu 11, akufotokoza mmene amakulitsira ubwenzi wachikondi ndi ziŵalo za banja lake zapafupi: “Pakali pano, atatu a mabanja asanu ndi limodzi amene ali ‘mbumba’ zanga amakhala kutali. Koma zimenezo sizili chopinga pa kucheza kwathu kokondweretsa ndi kusonkhana kwathu pamodzi. Tili ndi chizoloŵezi cha kusonkhana pamodzi mwinamwake kamodzi pa chaka, anthu 24 tonse.”

Pamene agogo akhala okha, ngati kuwachezera, kuwaimbira telefoni, kapena kulemberana makalata ndi ziŵalo za banja kuli kwa kamodzikamodzi, unansiwo ungakhale wotalikirana. Chikondi chiyenera kusonyezedwa nthaŵi zonse. Agogo ena amene adakali anyonga kapena athanzi labwino amafuna kukhala pa okha pamene adakali ndi nyonga ndi okhoza kudzichitira zinthu. Komabe, ngati adzipatula kotheratu ku ziŵalo za banja, iwo adzapezanso kuti pamene adzafuna kusonyezedwa kwambiri chikondi, icho chidzachedwa kudza.

Lingaliro lina lothandiza likuchokera kwa Michael, gogo wachimuna wa ku Nigeria: “Ndimagwiritsira ntchito Lamulo la Makhalidwe Abwino la Yesu—la kuchita kwa ena zimene munthuwe ukufuna kuti akuchitire. Pa chifukwa chimenecho ana anga amandikonda kwambiri. Timamvana bwino kwambiri.” Iye akuwonjezera kuti: “Ngati mdzukulu wanga aliyense achita kanthu kondikhumudwitsa, ndimakambitsirana naye ngati kuli kofunika. Ngati kali kanthu kamene ndingakanyalanyaze, ndimangonyalanyaza nkhaniyo.”

Mphatso zazing’ono ndi mawu oyamikira onenedwa ndi agogo zimatulutsa zipatso zabwino. Mawu okoma mtima ndi olimbikitsa, m’malo mwa kungodandaula nthaŵi zonse, amachititsa moyo wa banja kukhala wokondweretsa. Kupatula nthaŵi kaamba ka adzukulu, kuwaphunzitsa maseŵero osangalatsa ndi ntchito zina zazing’ono zothandiza, kuwasimbira nkhani za m’Baibulo kapena mbiri ya banjalo, kumawachititsa kukhala ndi zikumbukiro zabwino ndi zosatha. Zinthu zazing’ono zoterozo komanso zimene zili zofunika zimapangitsa moyo kukhala wosangalatsa.

Mapindu a Kuchitirana Ulemu

“Agogo” akutero dokotala Gaspare Vella, “afunikira kusamala pa kutsutsana kapena kuchita mpikisano ndi ulamuliro wa kulera ana wa makolo.” “Atapanda kutero,” iye akuwonjezera motero, “amapyola malire a ntchito yawo monga agogo ndi kukhala makolo augogo.” Lingaliro limeneli lili logwirizana ndi zimene Malemba amanena, kuti makolo ndiwo ali ndi thayo lalikulu la kuphunzitsa ana awo.—Miyambo 6:20; Akolose 3:20.

Chifukwa cha kudziŵa kwawo zinthu m’moyo, kuli kosavuta kuti agogo apereke chilangizo. Komabe, iwo ayenera kuchita zimenezi mosamala kuti asapereke uphungu umene uli wosafunika kapena umene nthaŵi zina sudzalandiridwa. Roy ndi Jean akuti: “Kuli kofunika kuzindikira kuti makolo ndiwo amene ali ndi thayo lalikulu la kuphunzitsa ndi kulanga ana awo. Nthaŵi zina munthu angalingalire kuti iwowo ali oumitsa zinthu pang’ono ndipo nthaŵi zina olekerera pang’ono. Motero pali kufunika kwa kulimbana ndi chiyeso chenicheni cha kuloŵerera m’zochitika.” Michael ndi Sheena, agogo ena aŵiri Achibritishi, akuvomereza mfundo imodzimodziyi: “Ngati ana athu apempha chilangizo chathu, timawapatsa, komano sitimayembekezera kuti achilandire, ndiponso sitimakhumudwa ngati sanatero.” Ndi bwino kuti makolo okalamba azidalira ana awo aamuna ndi aakazi a mabanja. Chidaliro chotero chimalimbitsa maunansi pakati pa mibadwo itatuyo.

Vivian ndi Jane, amene amakhala kummwera kwa England, amayesayesa nthaŵi zonse kuchirikiza chilango choperekedwa kwa adzukulu awo ndi mwana wawo wamwamuna ndi mpongozi wawo, amene amakhala nawo: “Sitimayesa kuumiriza malingaliro athu pambali zimene tikulingalira mosiyana nawo. Pozindikira kuti timachirikiza amawo ndi atate wawo, anawo samayesa nkomwe ‘kutimenyanitsa.’” Ngakhale pamene makolo palibe, agogo ayenera kukhala osamala ponena za kulanga adzukulu. Harold, wa ku Britain, akuti: “Chilango chilichonse cholingaliridwa ndi gogo kukhala chofunika pamene makolo palibe chiyenera kukambitsiridwa pasadakhale ndi makolowo.” Harold akuwonjezera kuti mawu okoma mtima, komabe amphamvu kwa anawo kapena kungowakumbutsa za “zimene kholo likufuna” kaŵirikaŵiri nkokwanira.

Pamene Christopher, gogo wina wachimuna wa ku Nigeria aona cholakwa china kwa ana ake, samalankhula nawo chinthucho pamaso pa adzukulu ake: “Ndimapereka uphungu uliwonse wofunikira pamene ndili ndi makolowo.” Nawonso makolowo, afunikira kuchita mbali yawo kutsimikizira kuti mbali ya agogo ikulemekezedwa. “Kuli kofunika,” akutero Carlo, atate wina amene amakhala ku Rome, Italy, “kusadandaula ndi zophophonya za agogo kapena za ziŵalo zina za banja pamaso pa ana.” Hiroko, nakubala Wachijapani, akuti: “Pamene pabuka vuto ndi apongozi anga, choyamba ndimakambitsirana nkhaniyo ndi mwamuna wanga.”

Mbali ya Kuphunzitsa ya Agogo

Banja lililonse lili ndi mbiri yake, miyambo, ndi zokumana nazo zimene zimalisiyanitsa ndi ena. Kaŵirikaŵiri, agogo ndiwo njira yokumbukirira mbiri ya banjalo. Malinga ndi kunena kwa mwambi wina wa mu Afirika, “nkhalamba iliyonse imene imafa ndiyo nkhokwe imene imanyeka ndi moto.” Agogo amauza ena za achibale amene amawakumbukira ndi zochitika zina zofunika za m’banja, ndiponso makhalidwe a banjalo amene kaŵirikaŵiri amagwirizanitsa mwamphamvu banjalo. Kupatulapo chitsogozo cha makhalidwe abwino chimene Baibulo limapereka, katswiri wina anati ngati “achichepere sadziŵa za mbiri ya banja lawo, amakula alibe maziko a chidziŵitso chimene chinalipo iwo asanabadwe, amakhala opanda makhalidwe, osadziŵa bwino zinthu ndi osasungika.”—Gaetano Barletta, Nonni e nipoti (Agogo ndi Adzukulu).

Adzukulu amakonda kumva mbiri yonena za pamene amayi ndi atate ndi achibale ena anali aang’ono. Kuona zithunzithunzi za mu alabamu kungakhale kopereka chidziŵitso kwambiri ndi kosangalatsa. Ha, ndi chikondi chapadera chotani nanga chimene chingayambitsidwe pamene agogo asimba za mbiri ya zochitika zakaleyo mogwirizana ndi zithunzithunzi.

Reg ndi Molly, agogo aŵiri Achibritishi amene ali Mboni za Yehova, akuti: “Takhala ndi chimwemwe pokhoza kukhala ndi adzukulu ndi kuchita nawo zinthu, popanda kudodometsa kukondana kwawo ndi Amawo ndi Atate wawo, kuyankha mafunso awo ambiri, kuseŵerera pamodzi, kuŵerengera pamodzi, kuwasonyeza mmene angalembere, kumvetsera akumaŵerenga, kutsatira zochitika zawo za kusukulu ndi chidwi chachikondi.”

Cholakwa chachikulu chimene agogo ambiri ndi makolo amapanga ndicho kuvutika maganizo ndi ubwino wakuthupi wokha wa ana ndi adzukulu. Reg ndi a Molly, otchulidwawo, akunena kuti: “Choloŵa chachikulu koposa chimene tingapatse ana athu ndi adzukulu ndicho kuwaona akuleredwa mogwirizana ndi chidziŵitso choona cha Mawu a Mulungu.”—Deuteronomo 4:9; 32:7; Salmo 48:13; 78:3, 4, 6.

Kuchita Mogwirizana ndi Chiphunzitso Chaumulungu

Baibulo Lopatulika, Mawu a Mulungu, ‘ali akuchitachita’ mwa anthu. Akhoza kuwathandiza kulamulira kapena kuchotsa mikhalidwe yogaŵanitsa, yonga dyera ndi kunyada. (Ahebri 4:12) Motero, awo amene amagwiritsira ntchito ziphunzitso zake amakhala ndi mtendere ndi umodzi m’banja. Limodzi la malemba ambiri amene amathandiza mibadwo itatu kuthetsa kusiyana kumene kungakhale pakati pawo ndilo Afilipi 2:2-4, limene limalimbikitsa onse kusonyeza chikondi ndi kudzichepetsa mtima, kusunga umodzi, ‘kusapenyerera zawo za iwo okha, komanso za anzawo.’

Pochita mogwirizana ndi chiphunzitso chaumulungu, makolo ndi adzukulunso amaona mwamphamvu chilangizo cha “kubwezera akuwabala,” mwakuthupi, mwamalingaliro, ndi mwauzimu. (1 Timoteo 5:4) Limodzi ndi kuwopa Yehova kwabwino, iwo amasonyeza ulemu waukulu kwa agogo, akumakumbukira mawu ake: “Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba; nuwope Mulungu wako.” (Levitiko 19:32) Agogo amasonyeza ukoma mwa kuchirikiza ubwino wa mbadwa zawo: “Wabwino asiyira zidzukulu zake choloŵa chabwino.”—Miyambo 13:22.

Agogo, makolo, ndi zidzukulu, kaya amakhalira pamodzi kapena ayi, onse angathe kupeza mapindu m’maunansi abwino ozikidwa pa chikondi ndi ulemu, monga momwe Miyambo 17:6 imanenera: “Zidzukulu ndizo korona wa okalamba; ndipo ulemerero wa ana ndiwo atate awo.”

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 8]

Kugwirizananso kwa banja kungachirikize umodzi wa banja

[Chithunzi patsamba 9]

Agogo anu amalimbikitsidwa pamene muwalembera makalata

[Chithunzi patsamba 10]

Kuona zinthunzithunzi za mu alabamu ya banja ndi zidzukulu zanu kungakhale kopindulitsa kwambiri

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena