Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 10/8 tsamba 20-22
  • Juga—Kumwerekera kwa m’Ma ’90

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Juga—Kumwerekera kwa m’Ma ’90
  • Galamukani!—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Kutchova Njuga Kuli Ndi Vuto Lanji?
    Galamukani!—2002
  • Oseŵera Juga Atsopano—Achichepere!
    Galamukani!—1995
  • Kodi Kutchova Juga ndi kwa Akristu?
    Galamukani!—1994
  • Kodi Baibulo Limaletsa Kutchova Juga?
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 10/8 tsamba 20-22

Juga—Kumwerekera kwa m’Ma ’90

KAMERA yolongedwamo filimu yakaladi ijambula chithunzithunzi. Chithunzithunzicho chikwana pamasamba anayi a nyuzipepala ya pa Sande—kufikira pogomera maso m’nyumba yaikulu ya katundu imene anasandutsa nyumba ya juga ya bingo, mamita zikwi zambiri mbali zonse mkatimo, yodzala otchova juga a misinkhu yonse ndi amitundu yonse ali piringupiringu mmenemo. Kodi mukuona nkhope zawo zotopazo ndi maso awo ofiira, chizindikiro chakuti akhala akuseŵera maola ambiri osaleka? Akuyembekeza, nkhaŵa ili bi, kumva kulengezedwa kwa nambala imene akhulupirira kuti idzawawinitsa usikuwo umene akanachokapo chimanjamanja.

Tembenuzani masamba a nyuzipepalayo. Kodi mukuona nkhope za anthuwo zosonyeza nkhaŵa atafumbata makadi ajuga ochuluka, akudodoma kuti mwina anyamula makadi oluzitsa? Nthaŵi zambiri amawina kapena kuluza madola zikwizikwi mwa kungotenga khadi lotsatira. Yesani kuona zosaoneka pa zithunzithunzizo. Kodi mukuona zikhato zochita thukuta za manja onjenjemerawo? Kodi mukumva kugunda kothamanga kwa mtima, pemphero lakachetechete lakuti iye awine tsopano ndi kuti enawo aluze?

Taloŵani m’makasino ambambande a m’mahotela ndi m’maboti apamwamba. Kodi mwazingidwa konsekonse ndi makina otchovera juga ochuluka amaonekedwe okongola? Kodi kulira kwa zogwirira zawo zimene akukoka ndi phokoso la mbale zozungulira zakugonthetsani m’kutu? Kaya awine kapena aluze, kulira kwa mbale zozungulirazo kuli ngati nyimbo kwa oseŵerawo. “Chimene chiwadya moyo ndicho nthumanzi ya kuyembekeza zimene zidzachitika atakokanso chogwirira makina otchovera juga,” anatero mkulu wa kasino ina.

Pyolani pakati pa piringupiringu wa anthu ndi kupita ku magome a juga ya roulette ozingidwa ndi anthuwo. Kuzungulira kwa mbale yokhala ndi mbali zake zofiira ndi zakuda imene mukuona kungakugonekeni tulo. Kulira kwa m’bulu womakunkhunika kukuwonjezera kutengeka kwanu maganizo. Mbaleyo ikungozungulira, ndipo pamene iimira ndipo powinira kapena poluzira munthu. Madola zikwi zambiri amatayika kaŵirikaŵiri mbaleyo itazungulira kamodzi kokha.

Ŵirikizani nthaŵi zikwi makumi ambiri zithunzithunzizo ndi zochitikazo, oseŵerawo nthaŵi mamiliyoni osaŵerengeka, ndi malowo nthaŵi zikwi zambiri padziko lonse. Amabwera pandege, patireni, pabasi, pangalaŵa, ndi pagalimoto kuchokera kumbali zonse za dziko kudzakhutiritsa chilakolako chawo cha juga. Kwatchedwa “nthenda yobisika, kumwerekera kwa m’ma ’90: Kumwerekera ndi juga.” “Ndikulosera kuti ma 1990 adzakhala kaindeinde wa juga zololedwa m’mbiri padziko lonse,” anatero wofufuza Durand Jacobs, katswiri wa boma wa za juga.

Mwachitsanzo, ku United States, Aamereka ochuluka mu 1993 anapita kumakasino kuposa amene anapita ku mipikisano yaikulu ya baseball—maulendo 92 miliyoni. Kumanga nyumba za juga sikutha. Enimahotela kudera la East Coast amasoŵa chochita ndi makamuwo. “Zipinda zomwe zilipo sizitha kusunga alendo ngati 50,000 amene amafika pamakasino patsiku.”

Mu 1994, m’maboma ambiri akummwera, kumene zaka zingapo zapitazo juga inayesedwa uchimo, tsopano amailandira ndi manja aŵiri ndipo amaiyesa mpulumutsi. “Lerolino, Bible Belt ingangosinthidwa kukhala Blackjack Belt, yokhala ndi makasino oyandama ndi akumtunda m’Mississippi ndi Louisiana yense ndipo pali mapulani akumanga ena ku Florida, Texas, Alabama ndi Arkansas,” inatero U.S.News & World Report. Atsogoleri ena achipembedzo tsopano akusinthiratu maganizo akuti juga ndi uchimo. Mwachitsanzo, pamene akuluakulu a mzinda wa New Orleans, Louisiana, anatsegula ndi kudalitsa kasino yawo yoyamba yoyandama mumtsinje wa Mississippi mu 1994, mtsogoleri wina wa chipembedzo anapereka pemphero, kuyamika Mulungu kaamba ka “luso la kuseŵera juga: mphatso imene,” anatero, “mwadalitsa nayo mzindawu.”

Pofika chaka cha 2000, kukuyembekezeredwa kuti 95 peresenti ya Aamereka onse adzakhala ndi kasino pafupi nawo pamtunda wa galimoto wa maola atatu kapena anayi. Amwenye a ku America nawonso alandira mbali yaikulu ya malonda a juga. Kufikira pano boma la United States lawalola kuyendetsa makasino 225 ndi nyumba za bingo zobetchera pinyolo yokwera m’dziko lonseli, inatero U.S.News & World Report.

Pamene nyumba zotchovera juga, kubetchera maseŵero, mipikisano ya mahachi ndi agalu, bingo ya tchalitchi, ndi zina zotero ziphatikizidwapo, chifukwa chake chimamveka chimene Aamereka mwalamulo anabetchera $394 biliyoni mu 1993, chiwonjezeko cha 17.1 peresenti kuposa chaka chinapitacho. Aja otsutsa juga amazizwa. “Zinthu zazikulu zimene tili nazo zimene zingathandize anthu ndizo matchalitchi ndi akachisi ndi boma,” anatero mkulu wina wa Council on Compulsive Gambling. “Komano zonsezo zili m’malonda a juga.” Nyuzipepala ina ya ku America inatcha United States “Dziko la Juga” niiti juga ndiyo “seŵero lenileni la dziko la America.”

England wayamba lotale yake chiyambire 1826, ndipo akuti malonda ake akuyenda mofulumira. Ndiponso akuona kuwonjezeka kwakukulu kwa juga ya bingo, inatero The New York Times Magazine. “Moscow tsopano wadzala makasino apiringupiringu. Ndipo otchova juga Achilebanizi akuika moyo wawo pangozi pomapita kunyumba za juga za ku West Beirut kumenenso kumapezeka apolisi ndi anthu achipembedzo oyaluka ndi changu amene angawaphe,” inatero Times. “Anthu opata ndalama zochuluka amaperekezedwa kunyumba ndi alonda a makasino onyamula mfuti zachiwaya.”

“Akanada sadziŵa kuti ali mtundu wa otchova juga,” anatero woyang’anira za juga Wachikanada wa chigawo china. Iye anawonjezera kuti, “M’mbali zina, maseŵero a juga ngochuluka kwambiri m’Canada kuposa ku United States.” “Chaka chatha Akanada anawononga ndalama zoposa $10 biliyoni pa juga ndi kubetchera kololedwa—kuŵirikiza pafupifupi nthaŵi 30 kuposa zimene anawonongera pamafilimu,” inatero nyuzipepalayo The Globe and Mail. “Maseŵero a juga ya bingo m’Canada ngopita patsogolo kwambiri kuposa mmene alili kapena mmene analili ndi kalelonse ku United States. Maseŵero a juga ya lotale ngopita patsogolo kwambiri m’Canada. Ndi mmenenso mpikisano wa mahachi ulili,” pepalalo linatero.

“Palibe amene adziŵa chiŵerengero cha omwerekera ndi juga amene ali mu South Africa,” nyuzipepala ina ya ku South Africa inalemba motero, “komatu aliko ‘zikwizikwi.’” Komabe, boma la Spain likudziŵa bwino za vuto lake ndi za otchova juga omawonjezereka. Ziŵerengero za boma zimasonyeza kuti ambiri mwa nzika zake 38 miliyoni anabetchera $25 biliyoni chaka chimodzi, akumachititsa Spain kukhala mmodzi wa okhala ndi ziŵerengero zapamwamba koposa za otchova juga. “Aspanya ali otchova juga omwerekera,” anatero mwamuna wina yemwe anakhazikitsa bungwe lothandiza otchova juga. “Akhala otero nthaŵi zonse. . . . Amabetchera pa mahachi, mpira, malotale, ndipotu roulette, poker, bingo ndi makina aja oipa ogwidiza ndalama.” Ndi posachedwapa pamene Spain wazindikira kuti kumwerekera ndi juga kuli nthenda ya maganizo.

Umboni womwe ulipo umasonyeza kuti ngakhale Italy wasesedwera pamodzi ndi mliri wa juga. Ndalama zambirimbiri zikubetchedwa m’malotale ndi maseŵero ndiponso m’mipikisano ya m’nyuzipepala ndi pamagome a juga. “Juga yaloŵa m’mbali iliyonse ya moyo wa tsiku ndi tsiku,” linatero lipoti loperekedwa ndi kagulu kofufuza kochirikizidwa ndi boma. Lerolino “mlingo wa juga wafika pamene kale sunalingaliridwe kuti udzafika,” inatero The New York Times, “ndipo kuyambira kwa akuluakulu a Boma mpaka kwa ansembe aparishi pali mpikisano wopeza njira zimene angapezere phindu pa juga.”

Ntheradi! Nthaŵi zambiri juga imakhudza mbali iliyonse ya moyo wa anthu, monga momwe nkhani zotsatira zikusonyezera.

[Mawu Otsindika patsamba 21]

Kale unali uchimo—lero ndi “mpulumutsi”

[Mawu Otsindika patsamba 22]

Mliri wa juga ukufalikira padziko lonse

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena