Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 10/8 tsamba 22-24
  • Omwerekera ndi Juga Kwawo ndi Kuluza Basi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Omwerekera ndi Juga Kwawo ndi Kuluza Basi
  • Galamukani!—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Oseŵera Juga Atsopano—Achichepere!
    Galamukani!—1995
  • Kodi Kutchova Juga ndi kwa Akristu?
    Galamukani!—1994
  • Zotulukapo Zoŵaŵa za Kutchova Juga
    Galamukani!—1992
  • Kodi Kutchova Njuga Kuli Ndi Vuto Lanji?
    Galamukani!—2002
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 10/8 tsamba 22-24

Omwerekera ndi Juga Kwawo ndi Kuluza Basi

“KUMWEREKERA ndi juga ndiko nthenda monganso uchidakwa ndi kumwerekera ndi anamgoneka,” anatero Profesa Jean Ades, wa ku France. “Ndiko kumwerekera kumene kulibe mankhwala ake,” anatero, ndipo “anthu ambirimbiri akuzindikira kuti ali omwerekera.” Ngakhale pamene omwerekera ndi juga aluza ndalama zochuluka, kaŵirikaŵiri amatengeka ndi chifuno cha kupezanso zomwe aluzazo mwa kutchova juga kwambiri. “Oluza ochuluka amaiŵala msanga kuluza kwawoko. Koma kwa ena, chikhumbo cha kutchova juga chimakhala chosalamulirika kwakuti chimawononga moyo wawo,” analemba motero mtolankhani wina ku France. “Amaganizabe kuti adzawonjoka pa chizoloŵezicho, koma chimawalamulirabe nthaŵi zonse. Ali omwerekera ndi juga.”

Wajuga wina ku South Africa anavomereza kuti: “Ngati ndiwe womwerekera ndi juga, ndipo wakhala pansi kumbale ya roulette kapena kugome la blackjack, umaiŵala zonse. Adrenalin imasefukira m’mitsempha mwako, ndipo umabetcha khobiri iliyonse imene uli nayo pa kuzungulira kotsatira kumodzi kokha kwa mbaleyo, kapena ulendo wotsatira woponya makadi. . . . Chifukwa cha adrenalin ya m’thupi mwanga, ndinali kukhala maso masiku ambiri usana ndi usiku kosaleka, ndikumapenyerera makadi ndi manambala, ndipo ndikumayembekeza kupambana zochuluka kovuta nthaŵi zonse.” Ndiyeno anati: “Pali ena ambiri onga ine amene sangasiye ataluza marandi mazana kapena ngakhale zikwi zingapo. Timapitiriza kutchova juga mpaka zonse zomwe tili nazo zitatha, ndipo mpaka maunansi athu a banja atawonogeka kosakonzekanso.”

Henry R. Lesieur, profesa wa khalidwe la anthu pa St. John’s University, New York, analemba kuti chikhumbo cha kutchova juga, kaya awine kapena aluze, chimakhala chachikulu koposa “kwakuti otchova juga ambiri amakhala masiku ambiri osagona, osadya, ndipotu osapita ndi kuchimbudzi komwe. Kutengeka mtima kwawo kumatsekereza zinthu zina zonse zofunika. Pamene akuyembekeza, pamakhalanso ‘kupanikizika,’ kumene kaŵirikaŵiri kumasonyezedwa ndi zikhato zochita thukuta, kugunda kofulumira kwa mtima, ndi nseru.”

Yemwe kale anali womwerekera ndi juga akuvomereza kuti kuwina sindiko kunasonkhezera chizoloŵezi chake cha nthaŵi yaitalicho, komatu ndi “kupanikizika,” kusangalatsa kwa juga yeniyeniyo. “Juga imakuyalutsa mtima kowopsa,” iye anatero. “Pamene mbale ya roulette ikuzungulira, ndipo iwe ukuyembekeza Mwaŵi kupereka yankho lake, pamakhala nthaŵi pamene umazunguzika mutu ndipo umatsala pang’ono kukomoka.” André wajuga Wachifrenchi akuvomereza: “Ngati wabetcha FF10,000 pa hachi imodzi ndipo kwangotsala mamita 100, wina akhoza kukuuza kuti mkazi wako kapena amako amwalira ndipo sungasamale zimenezo.”

André akufotokoza mmene anapitirizira kutchova juga ngakhale ataluza ndalama zochuluka. Anabwereka ndalama ku mabanki, kwa mabwenzi, ndi kwa okongoza ndalama mofuna phindu lalikulu. Anaba macheke ndi kusintha ziŵerengero za ndalama m’mabuku akupositi ofesi. Atapita ku makasino, anali kunyengerera akazi okhala okha ndiyeno anali kuthaŵa ndi ma credit card awo. “Nthaŵiyo,” analemba motero mtolankhani wina Wachifrenchi, André “sanasamalenso zakuti adzabwezera ngongole zake zowopsazo. Chimene chinasonkhezera zochita zake makamaka ndicho kumwerekera kwake.” Anayamba upandu ndipo anaponyedwa m’ndende. Ukwati wake unasweka.

Nthaŵi zambiri, omwerekera ndi juga mofanana ndi omwerekera ndi anamgoneka ndi zidakwa, amatchovabe juga ngakhale ngati potsirizira pake iwachotsetsa ntchito, kuwawonongera bizinesi yawo, thanzi lawo, ndipo ndi banja lawo.

Posachedwapa mizinda yambiri ku France yatsegulira mpata juga. Kumene mabizinesi ena alephera, malonda m’mashopo a pinyolo akuyenda. Eni ake akuti otchova juga nthaŵi zambiri amataya ndalama zonse zimene amakhala nazo ndipo amagulitsa mphete, mawatchi, zovala, ndi zinthu zina zamtengo wapatali kuti apeze ndalama zogulira petulo yopitira kunyumba. M’matauni ena akunyanja ku United States, kwatsegulidwa mashopo atsopano a pinyolo; nthaŵi zina amakhala atatu kapena oposerapo otsatizana.

Ena ayambadi kuchita upandu kuti achirikize chizoloŵezi chawo cha juga. Kufufuza komwe kwachitidwa kufikira lero, malinga ndi kunena kwa Profesa Lesieur, “kwavumbula makhalidwe oipa amitundumitundu a omwerekera ndi juga . . . kudzipangira macheke, upyuta, kuba, umbala wamfuti, kulotera amene adzapambana, kupeza ndalama mwachinyengo, kubera anthu ndalama mwa kuwapusitsa, ndi kugulitsa zinthu zakuba.” Kuwonjezera pamenepa pali upandu wa m’maofesi kumene otchova juga amabera owalemba ntchito. Malinga ndi kunena kwa Gerry T. Fulcher, mkulu wa Institute for the Education and Treatment of Compulsive Gamblers, 85 peresenti ya zikwi za omwerekera ndi juga odziŵika anavomera kuti anaberapo owalemba ntchito. “Kwenikweni, pankhani ya zandalama yokha, kumwerekera ndi juga nkoipa kwambiri kuposa uchidakwa ndi anamgoneka zonse pamodzi,” iyeyo anatero.

Kufufuza kowonjezera kwasonyeza kuti pafupifupi aŵiri mwa atatu a omwerekera ndi juga omwe sanamangidwepo ndiponso 97 peresenti ya omangidwapo amavomereza kuti anadziloŵetsa m’khalidwe loipa kuti apeze ndalama za juga kapena zolipirira ngongole zokhudza juga. Mu 1993 kumatauni a ku Gulf Coast ku United States, kumene juga zololedwa zili zofala, mbala zamfuti zinabera mabanki 16, chiwonjezeko choŵirikiza kanayi kuposa chaka chinapitacho. Mwamuna wina anabera mabanki okwana 8 ndalama zokwana $89,000 kuti apitirize chizoloŵezi chake cha juga. Ajuga okhala ndi ngongole zochuluka kwa owakongoza abera mabanki ena mwa kuwopseza anthu ndi mfuti.

“Pamene omwerekera ndi juga ayesa kusiya chizoloŵezi chawocho, amavutika ndi zizindikiro za kuleka, mofananadi ndi osuta fodya kapena omwerekera ndi anamgoneka,” ikutero The New York Times. Komabe, ajuga amavomereza kuti kusiya juga kungakhale kovuta kuposa kusiya zizoloŵezi zina. “Ena a ife tinakhalapo zidakwa ndiponso tinagwiritsirapo ntchito anamgoneka,” anatero wina, “ndipo tonsefe tikuvomereza kuti kumwerekera ndi juga nkovuta kwambiri kuposa kumwerekera ndi zinthu zinazo.” Dr. Howard Shaffer, wa Center for Addiction Studies pa Harvard University, anati osachepera 30 peresenti ya omwerekera ndi juga omwe amayesa kusiya “amakhala ndi mtima wapachala kapena amadwala m’mimba, samapeza tulo, kukankha kwa mwazi [BP] ndi kugunda kwa mtima kumawonjezeka kwambiri.”

Ngakhale ngati apitiriza kubetchera, anatero Dr. Valerie Lorenz, mkulu wa National Center for Pathological Gambling ku Baltimore, Maryland, U.S.A., omwerekera ndi “juga amadwalabe: mutu wosaleka, mutu wa litsipa, kuvutika popuma, ululu wa angina, arrhythmia ya mtima ndi kuzizira mikono ndi miyendo.”

Ndiyenonso pali kudzipha. Kodi pangakhalenso china choipa kwambiri kuposa imfa yochititsidwa ndi chimene ambiri amati “kumwerekera kosapha”? Mwachitsanzo, m’chigawo china cha America kumene kwatsegulidwa makasino posachedwapa, “chiŵerengero cha odzipha chawonjezeka modabwitsa kuŵirikiza kaŵiri,” inatero The New York Times Magazine, “ngakhale kuti palibe wa zaumoyo amene anafuna kugwirizanitsa kuwonjezekako ndi juga.” Ku South Africa, ajuga atatu anadzipha pamlungu umodzi. Chiŵerengero chenicheni cha odzipha chifukwa cha juga ndi ngongole zimene anakhala nazo mwa njira imeneyi, mololeka kapena mosaloleka, sichikudziŵika.

Kudzipha sindiko njira yabwino yowonjokera m’goli la juga. M’nkhani yotsatira, taonani mmene ena apezera njira yabwino yowonjokeramo.

[Mawu Otsindika patsamba 23]

Mashopo a pinyolo ngofala—momwemonso upandu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena