Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndiyenera Kuphunzira Kudzitetezera?
“Pasukulu pali gulu la anyamata oipa kwambiri,” akutero Jesse. “Ngati akuona m’likole ndipo afuna ma sneaker ako, jekete, ngakhale talauza, amangokulanda. Ngati uwanenera, amadzakumenyanso.”
KULIMBANA ndi chiwawa kwakhala mkhalidwe wa moyo wa achichepere ambiri. Magazini a USA Today anati: “Pafupifupi mmodzi pa ophunzira a kusekondale asanu alionse nthaŵi zonse amanyamula mfuti, mpeni, lumo, chibonga, kapena chida china. Ambiri amapita nazo kusukulu.” Mnyamata wina wotchedwa Jairo anadzionera yekha zimenezi. “Sukulu yathu inali yoyamba [mu New York City] kukhala ndi ziŵiya zodziŵira munthu amene wanyamula chitsulo,” anatero, “koma zimenezo sizimaletsa anawo kukhala ndi mipeni ndi mfuti. Sindidziŵa mmene amadziloŵetsera izo, koma amaterodi.”
Momvekera bwino, kuwopa kumenyedwa kwachititsa achichepere ambiri kulingalira za mmene angadzitetezerere. Lola wachichepere anati: “Pamene mtsikana wina pasukulu pathu anaphedwa mwa kubayidwa ndi mpeni kuti amlande ndolo, pasukulupo anayamba kuphunzitsa maphunziro a kudzitetezera. Pafupifupi aliyense analembetsa.” Achichepere ena ayamba kunyamula mankhwala owaza ndi zida zina. Funso nlakuti, Kodi njira zodzitetezera zimakutetezeranidi?
Maluso a Kumenya
Amawasonyeza pa TV nthaŵi zonse—akatswiri a maluso a kumenya akumalumpha m’mwamba, kuponda zidyali ndi kuponya zibakela moonekera bwino ngati wovina. Pakamphindi chabe, adani ake amagwetsedwa pansi osauka. Zodabwitsa eti! Maluso a kumenya amaoneka kukhala chitetezo chenicheni. Komabe, zenizeni sizimakhala ngati za m’mafilimu. Mwamuna wina wodziŵa karate kwa zaka zambiri anati: “Chipolopolo chimodzi chabe chimathetsa zonse. Ngati munthu wina patali ali ndi mfuti, ulibe chako. Ngati munthu uli naye pafupi kwambiri kwakuti ulibe kofutukira, malusowo samathandizanso kwenikweni.”
Dziŵani kuti, kuti munthu akhale katswiri m’zamaluso a kumenya, ayenera kutaya ndalama zambiri ndi kutha zaka zambiri za kuphunzira kwamphamvu. Ndipo ngati simupitirizabe kuphunzira, mphamvu yanu ya maluso amenewo ikhoza kutha moipa mwamsanga. Nchimodzimodzinso ndi mitundu ina ya kumenya kodzitetezera, monga nkhonya. Ndiponso, kukhala ndi mbiri ya kudziŵa kumenya kumachititsa anthu oipa kukudziŵani. Anthu andewu angafune kumenyana nanu kuti akuyeseni.
Komabe, kuphunzira maluso a kumenya kulinso ndi ngozi ina yaikulu. Magazini a The Economist posachedwapa anasimba kuti: “Maluso akumenya ochuluka, ngati si onse, amagwirizanitsidwa kwambiri ndi zipembedzo zitatu zazikulu za Kummaŵa kwa Asia, Chibuda, Chitao, ndi Chikomfyushasi.” Buku lina linaonjezera kuti: “Chilichonse chimene chichitidwa mu karate—kusuntha kulikonse, kumva kulikonse—kungagwirizanitsidwe ndi mkhalidwe wa Zen.” Zen ndi mpatuko wa Chibuda umene umagogomezera kusinkhasinkha za chipembedzo. Magwero achipembedzo ameneŵa amaikapo vuto lalikulu kwambiri kwa Akristu malinga ndi mawu a Baibulo pa 2 Akorinto 6:17: “Chifukwa chake, Tulukani pakati pa [olambira onyenga], ndipo patukani, ati Ambuye, ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka.”
Kugwiritsira Ntchito Zida
Koma bwanji za kunyamula mfuti kapena mpeni? Zimenezo zingakuchititsenidi kumva wodzidalira. Koma chidaliro chimenecho chingakhale chakupha ngati muyamba kuseŵera ndi ngozi. Baibulo limachenjeza kuti: “Zoipa zidzamfikira wozilondola.” (Miyambo 11:27) Ndipo ngati mukumana ndi vuto la dzidzidzi, kusolola chida kudzangokulitsa nkhondoyo. Mukhoza kuphedwa—kapena mukhoza kupha munthu wina. Kodi Mulungu, Magwero a moyo, angaone motani machitidwe anu ngati mukanapeŵa kugwiritsira ntchito chiwawa?—Salmo 11:5; 36:9.
Zoona, ena amakhala asakufunadi kugwiritsira ntchito chida chakupha. Anganene kuti amangochinyamula kuti awopseze anthu ovutitsa. Koma magazini a Health amanena kuti: “Ophunzitsa za zida amavomereza kuti: Musanyamule mfuti ngati simufuna kuigwiritsira ntchito. Kusonyeza mfuti kungawopseze oukira, koma kudzangoputa ena.”
Bwanji za zida “zosavulaza kwambiri” monga zowazira mankhwala oŵaŵa? Kuwonjezera pa kukhala kwake zosaloledwa m’malo ena, zida zimenezi zimakhala ndi zotulukapo zoipa. M’malo mwa kuingitsa mdani womwerekera ndi anamgoneka, zingangomputa. Zingachitikenso kuti mphepo ingaulutsire mankhwalawo kunkhope kwanu m’malo mwa kwa mdaniyo—ngati kuti ndinu mwayamba kutulutsa chowazira mankhwalacho. Poona kuti mukupisa dzanja m’matumba anu kapena m’chikwama, woukirayo angalingalire kuti mukutenga mfuti choncho angaganize za kuchitapo kanthu mwamsanga. Wofufuza milandu wina wapolisi ananena kuti: “Sikotsimikizirika kuti mace [kuwaza mankhwala oŵaŵa], kapena chida china chilichonse chidzathandiza. Kapena kuti mudzakhoza kuchitulutsa mwamsanga. Zida sizimathandiza pavuto. Anthu amangozidalira mopambanitsa.”
Zida—Mmene Mulungu Amazionera
Ngozi ya chiwawa inaliko ngakhale kalelo m’nthaŵi ya Yesu. Umodzi wa miyambi yake yotchuka kwambiri, wotchedwa mwambi wa Msamariya Wachifundo, unasimba za chochitika cha kufwamba kwachiwawa. (Luka 10:30-35) Pamene Yesu anapempha ophunzira ake kukhala ndi malupanga, sikunali kaamba kodzitetezera. Kwenikweni, zinachititsa kunena kwake mwambo wa chikhalidwe wakuti: “Onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.”—Mateyu 26:51, 52; Luka 22:36-38.
Motero, Akristu oona samakonzekera m’njira yakuti avulaze anthu anzawo. (Yerekezerani ndi Yesaya 2:4) Amatsatira uphungu wa Baibulo wa pa Aroma 12:18: “Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.” Kodi zimenezi zimatanthauza kudzilekerera? Kutalitali!
Nzeru—Ipambana Zida
M’nyengo ya nthaŵi mmene chinthu chilichonse chili ndi chipangizo chake, mungadabwe kudziŵa kuti mukhoza kukhala ndi njira yodzitetezera yoposa chipangizo chilichonse chopangidwa ndi munthu. Pa Mlaliki 9:18, timaŵerenga kuti: “Nzeru ipambana zida za nkhondo.” Nzeru imeneyi imaposa zimene ena amatcha “machenjera a m’khwalala.” Ndiyo kugwiritsira ntchito zitsogozo za Baibulo, ndipo nthaŵi zonse ikhoza kukuthandizani kupeŵa mikhalidwe yachiwawa.
Jairo, mwachitsanzo, amene poyambapo wasimba za chiwawa cha pasukulu pawo, amapeŵa mavuto mwa kugwiritsira ntchito mawu a Baibulo a pa 1 Atesalonika 4:11: “Muyesetse kukhala chete ndi kuchita za inu eni.” Jairo akunena kuti: “Ngati mwadziŵa kuti kudzakhala ndewu, muyenera kusamalira za inu eni ndi kupita kunyumba. Ena amazengereza ali pamenepo, ndipo mpamene amaloŵadi m’vuto.”
“Kuchititsa aliyense kudziŵa kuti ndine mmodzi wa Mboni za Yehova kumanditetezera kwambiri,” akutero Lola wachichepere. “Anthu samandivutitsa chifukwa amadziŵa kuti sindingawachite kalikonse.” “Nzoposa kungonena kuti ndiwe Mboni,” akuwonjezera Eliu. “Ayenera kuona kuti ndiwe wosiyana.” Akristu sayenera kukhala “a dziko.” (Yohane 15:19) Koma samalani kuti musaoneke kukhala wodzionetsera. (Miyambo 11:2) Wachichepere wina ananena motere: “Suyenera kuyenda m’likole monga kuti ndi mwako.” Zimenezi zingapute ena. Wachichepere wina Wachikristu wotchedwa Luchy akusimba kuti: “Ndili waubwenzi, ndipo ndimakambitsirana ndi anzanga a m’kalasi; koma sindimangochita monga iwo.”
Mavalidwe anu ngofunikanso kwambiri. “Ndimasamala kusavala zinthu zimene zimakopa anthu ena,” akutero wachichepere wina. “Ndimadziŵa kuti kuoneka bwino sikumalira kuti ndivale zovala zamtengo kwambiri.” Kutsatira uphungu wa Baibulo wa kuvala bwino kungakuthandizeni kusakhala wodzionetsera ndi kupeŵa mavuto.—1 Timoteo 2:9.
Mutayang’anizana ndi Chiwawa
Koma bwanji ngati mwayang’anizana ndi chiwawa, mosasamala kanthu za kuyesayesa kupeŵa njira zangozi? Choyamba, yesani kugwiritsira ntchito chitsogozo cha pa Miyambo 15:1 chakuti: “Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mawu oŵaŵitsa aputa msunamo.” Eliu wachichepereyo anachita zimenezo pamene anali pasukulu. Iye akuti: “Nthaŵi zina kumathandiza kungonyalanyaza mawu ena andewu. Kaŵirikaŵiri, mayankhidwe anu ndiwo amene amabutsa vuto.” Mwa kukana ‘kubwezera choipa pa choipa,’ mungakhoze kuletsa mkhalidwewo kufika poipa.—Aroma 12:17.
Komabe, ngati njira zosungitsa mtendere zilephera, muyenera kuchitapo kanthu kuti mupeŵe ngozi. Ngati kagulu ka achichepere kakufuna kuti muwapatse ma sneaker anu kapena chinthu china chamtengo, apatseni zimenezo! Moyo wanu uli wofunika kwambiri kuposa zinthu zimene muli nazo. (Luka 12:15) Ngati pakuoneka kuti padzakhala chiwawa, chokaniponi—ndipo kuthaŵa kungakhale bwinopo! Miyambo 17:14 imati: “Kupikisana kusanayambe tasiya makani.” (Yerekezerani ndi Luka 4:29, 30; Yohane 8:59.) Ngati kuthaŵa sikutheka, mudzangofunikira kupeŵa chiwawacho mmene mungakhozere. Pambuyo pake, tsimikizirani kuuza makolo anu zimene zachitika. Mwinamwake angathandize mwa njira inayake.
Monga momwe Baibulo linaloserera, tikukhala m’nthaŵi zachiwawa. (2 Timoteo 3:1-5) Koma kuseŵeretsa mfuti kapena kuphunzira karate sikudzakutetezerani konse. Chenjerani. Gwiritsirani ntchito nzeru yaumulungu pamene muyang’anizana ndi vuto. Ndipo chofunika koposa, khalani ndi chikhulupiriro ndi chidaliro mwa Yehova. Monga wamasalmo, mungapemphere mwa chidaliro kuti: “Mundikwatula kwa munthu wachiwawa.”—Salmo 18:48.
[Chithunzi patsamba 30]
Maluso a kumenya sali yankho kwa Akristu