Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 5/8 tsamba 28-31
  • Chiwawa—Mungadzichinjirize Inumwini

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chiwawa—Mungadzichinjirize Inumwini
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Bwanji Ponena za Kudzichinjiriza Kwaumwini?
  • Kuchita Ndi Achifwamba
  • Kugwirira Chigololo ndi Chisungiko cha m’Nyumba
  • Njira Zopeŵera Kugwiriridwa Chigololo
    Galamukani!—1993
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kodi Ndiyenera Kuphunzira Kudzitetezera?
    Galamukani!—1995
  • Njira Yogonjetsera Kugwiriridwa Chigololo
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 5/8 tsamba 28-31

Chiwawa—Mungadzichinjirize Inumwini

OFESI ya Dipatimenti Yoyang’anira Zamdzikomo ya ku Britain posachedwapa inayambirira kuyambitsa mtundu watsopano wa maphunziro kaamba ka utumiki wa m’ndende, wotchedwa “kulamulira ndi kuletsa.” Maphunzirowo agawidwa m’mitu itatu:

◼ Kulamulira ndi kuletsa munthu mwa ntchito ya gulu

◼ Maluso othaŵira kaamba ka ogwira ntchito omwe ali okha

◼ Kusamalira kuwukira kogwirizana, monga ziwawa za gulu

Kosiyo “sinakonzedwe kukhala mtundu wa kuwukira wa kulimbana kopanda zida,” akulongosola tero mlankhuli wa Ofesi ya Dipatimenti Yoyang’anira Zamdzikomo. “Chosankha china chirichonse kapena njira ya kulamulira ndi kuthetsa mkhalidwe iyenera kuyesedwa choyamba.” M’mawu ena: Peŵani Kuyang’anizana! Kodi kuganiza koteroko kuli kogwira ntchito motani?

Bwanji Ponena za Kudzichinjiriza Kwaumwini?

Ngakhale kuti maluso a kumenya kaŵirikaŵiri amachirikizidwa, kugwiritsiridwa ntchito kwake mu kudzichinjiriza kwaumwini molimbana ndi aupandu sikukuvomerezedwa monga chosankha kwa anthu ambiri. Chofalitsidwa cha Violence—A Guide for the Caring Professions chikulongosola kuti:

“Nthaŵi zonse pakhala kuchirikiza kochepera kaamba ka kuphunzitsa kocholowanacholowana kwa maluso a kudzichinjiriza kwaumwini, osati kokha chifukwa chakuti cholinga chachikulu cha kuphunzitsa chikuwoneka kukhala kudzichinjiriza komanso chifukwa cha kusagwira ntchito kwake kwa kaŵirikaŵiri. . . . Moposerapo njira zoterozo zingakhale ndi polekezera m’kugwiritsiridwa ntchito kwake m’makhazikitsidwe onga malo obindikiritsidwa, ovutitsa ndipo kaŵirikaŵiri adzaloŵetsa wophunzirayo m’kupwetekeka ndi kuvulazika kowonjezereka mkati mwa kuphunzirako kuposa kumene akakumana nako m’nthaŵi ya moyo ya ntchito yake ya ngozi ya kuwukiridwa.”

Mu Self Defence in Action, Robert Clark, mphunzitsi wa British Jiu Jitsu Association, akupita patsogolo pang’ono, akumanena kuti: “Mofanana ndi zinthu zonse zophunziridwa pa nthaŵi yoyamba, izo [maluso a kumenya] zidzafunikira ukulu wochuluka wa kuyesayesa koyambirira kagwiridwe kake ka ntchito kasanakhale kachiŵiri ndipo kangachitidwe popanda kuzindikira kwa maganizo. Pamene mwaukiridwa, simudzakhala ndi nthaŵi ya kuganiza ponena za ndi kachitidwe kati komwe kamatsatira kati.”

Suzy Lamplugh Trust, bungwe lothandiza osoŵa lokhazikitsidwa m’chikumbukiro cha mkazi wa zaka 25 zakubadwa yemwe anazimiririka mwachinsinsi mkati mwa nthaŵi ya ntchito yake yakuthupi mu London mu 1986, mofananamo likuyamikira kudzichinjiriza kwaumwini kokha monga thandizo lotsirizira.

Ngati maluso a kumenya sali yankho ku kulimbana ndi kachitidwe kachiwawa kosayembekezeredwa, kodi nchiyani chomwe chiri?

Kuchita Ndi Achifwamba

Yankho ku kuchita ndi achifwamba liri kupeŵa kudzipanga inu eni kukhala mnkhole. Monga mmene woyang’anira apolisi mu Leeds, England, anadziŵitsira kuti: “Uchifwamba uli kachitidwe kongokumanizidwa, chimenecho ndicho chinthu chofunikira kukumbukira.” Chotero ngati mikhalidwe ikukakamizani kukhala m’malo opanda chisungiko, khalani ogalamuka. Musapatse achifwamba mwaŵi. Chitani m’chigwirizano ndi prinsipulo la Baibulo lakuti: “Munthu wanzeru amawoneratu patali ngozi, nabisala; koma osachenjera amapitiriza, nalangidwa.”—Miyambo 22:3, An American Translation.

Sungani maso anu akuyang’anayang’ana m’khwalala kutsogolo ndipo kamodzikamodzi penyani kumbuyo. Penyani kutsogolo musanaloŵe m’chimango—khalani ndi ngozi m’malingaliro. Yesani kupeŵa kuyenda nokha kutada. Ngati muli pa malo osonkhanira, yembekezani kupita kunyumba ndi mnzanu. Pamene muyendetsa galimoto yanu, tsimikizirani kuti zitseko zonse zakhomedwa. Ngati siziri tero, mpandu angaloŵe mosavuta pamene muima pa chizindikiro cha pamsewu.

Koma bwanji ngati, mosasamala kanthu za kusamalitsa kwanu, mwadzidzidzi mudzipeza inu eni mutayang’anizana pamaso ndi pamaso ndi winawake yemwe ali ndi mpeni kapena mfuti? Kumbukirani: Moyo wanu uli chinthu chanu choyambirira. Palibe chinthu chokhala nacho chomwe chingapambane mtengo wake. Chotero ngati wokuwukirani afuna ndalama, ziperekeni kwa iye. Anthu ena okhala m’malo a ngozi amanyamula ‘ndalama za achifwamba’—ndalama zochepera m’chola kapena thumba la ndalama kuti akhutiritse wachifwambayo.

Kumbukirani kachiŵirinso: Chitani modekha. Lankhulani molimba ndipo ndi liwu lanu lachibadwa. Penyani munthuyo m’maso, ndipo yesani kusamala kapenyedwe kake. Musayankhe mu mkhalidwe wodzetsa kutukwana ndi ziwopsyezo. Gwiritsirani ntchito uphungu wa Baibulo: “Yankho, pamene liri lodekha, limabweza mkwiyo.” “Khalani oleza kwa onse.” (Miyambo 15:1; 2 Timoteo 2:24, NW) Khalani wokonzekera kupepesa ngakhale kuti kwenikweni pangakhale palibe chirichonse chopepesera.

Kugwirira Chigololo ndi Chisungiko cha m’Nyumba

“Ogwirira chigololo ambiri amadabwitsidwa pa mmene chiriri chopepuka kugwirira chigololo mkazi,” akulemba tero Ray Wyre mu Women, Men and Rape. “Kuthedwa mphamvu kwa mantha kwa mkazi kumatanthauzidwa kukhala kusoŵeka kwa kutsutsa kumene mofala kumakhala chodzikhululukira cha wochita mlanduyo kaamba ka kupitirizabe ndi kuwukirako.” Chotero, musasinthesinthe! Chimveketseni kuti inu simudzagonjera. Mungagwiritsire ntchito njira iriyonse imene muli nayo pa nthaŵiyo kuti mupeŵe kugonana. Ngakhale ngati simuli womenya wamphamvu, inu muli ndi chida champhamvu—liwu lanu.

Kuwani mofuula monga mmene mungathere. Chimenecho chiri m’chigwirizano ndi chilangizo cha Baibulo. (Deuteronomo 22:23-27) Wa zaka za pakati pa 13 ndi 19 wina, atakokedwera m’malo a parki obindikiritsidwa, anafuula mwamphamvu ndi kukana. Chimenechi chinadabwitsa wowukira wake kotero kuti anathaŵa. Kukuwa kungakhwethemule wowukira wanu ndipo motero kungakupatseni mwaŵi wa kuthaŵa, kapena kudzagalamutsa ena kubwera kudzakuthandizani.a

Mu Britain, nkhani zambiri za kugwirira chigololo zimachitikira m’nyumba, kaŵirikaŵiri m’nyumba ya mkazi yemwe akuwukiridwa. Chiŵerengero chowonjezereka cha kuwukira kumeneku kumachitika mkati mwa kuthyola ndi kuloŵa m’nyumba. Chimapanga nzeru, chotero, kutsimikizira kuti nyumba yanu iri yachisungiko monga mmene kungathekere. M’mbali iyi, kodi nchiyani chimene inu mungachite?

Muyenera kutseka molimba njira zonse zothekera zoloŵera mwa kugwiritsira ntchito zotsekera mazenera zamphamvu ndi maloko a dead-bolt kaamba ka zitseko. Loko yoteroyo imafuna kugwiritsira ntchito mfungulo yanu kutembenuza bolt pamene mukuchoka ndi kutembenuza bolt pamene muli mkati. M’kuwonjezerapo, chingakhale chanzeru kupeza unyolo wa chitseko. Koma kumbukirani, chiwiya choterocho chiri kokha cholimba monga doorframe ndi mabolt amene amalimbitsa unyolowo.

Kusamalitsa kwina kwanzeru kuli kufufuza zizindikiritso zaumboni za obwera panyumba onse. Funsani kaamba ka makardi awo a ID.

Chiwawa sichikuchepekera. Ndithudi, ziŵerengero kuchokera ku dziko lonse zikuvumbula kuti chikuwonjezereka. Kuchita zomwe tingathe tsopano kudzichinjiriza ife eni ndi okondedwa athu kuli kwanzeru, koma iko sikumathetsa vuto kotheratu. Kodi nchiyani kwenikweni chimene chiri yankho?

[Mawu a M’munsi]

a Kaamba ka kukambitsirana kwa tsatanetsatane kwa nkhani ya kugwirira chigololo, onani makope a Galamukani! a May 22, 1986, February 22, 1984, ndi July 8, 1980 (Chingelezi).

[Bokosi patsamba 28]

Chimene Inu Mungachite

◼ Konzekerani ulendo wanu, makamaka ngati ndi usiku, kupeŵa njira zopanda nyali ndi makwalala opanda anthu. Kumbukirani, kachiŵirinso, kuti inu mungathamange mwamsanga mu nsapato zazifupi kuposa zazitali chitende.

◼ Musalole konse kunyamulidwa m’galimoto ndi munthu wachilendo. Musanamizidwe kuchoka m’galimoto yanu pa chinyengo chirichonse. Kukonza galimoto kulikonse kumachitidwa bwino koposa ndi munthu amene mumadziŵa ndipo pa malo a chisungiko, osati ndi mlendo pambali pa msewu.

◼ Yendani pafupi ndi khoma, yokhala patali ndi zimango kumene wowukira wothekera angabisale poloŵera kapena m’khonde.

◼ Ngati muwona gulu la anthu owoneka okaikiritsa kutsogolo kwanu, dutsani khwalala kuwapeŵa iwo, kapena sinthani njira. Ngati inu mutsatiridwa, lowani m’khwalala. Ngati ngozi iwoneka kuyandika, thaŵani kapena itanani kaamba ka thandizo.

◼ Nyamulani alamu yanu yoliza m’dzanja lanu, osati m’chola chanu. Phokoso kaŵirikaŵiri lingapangitse wofuna kuwukirayo kuthaŵa.

◼ Pewani kuloŵa mu elevator (chikepe) ngati inu muzindikira ngozi kuchokera kwa okweramo. Ngati muli m’chikepe, imirirani pafupi ndi malo ochiyendetsera. Ngati munthu wowoneka mokaikiritsa aloŵa, chingakhale chanzeru kutulukamo.

◼ Nyamulani makardi a ngongole ndi zofunikira zina m’malo anu apambali. M’njira imeneyi, ngakhale ngati chola chanu chatsompholedwa, kutaikiridwa kwanu sikudzakhala kokulira chotero.

[Bokosi patsamba 31]

Yang’anirani kaamba ka “Chimkupiti”

Mu Britain, “chimkupiti” liri liwu latsopano lolongosola machitachita a azaka za pakati pa 13 ndi 19 amene amaloŵa mwa gulu mu sitolo, basi, kapena sitima, kuwopsyeza awo amene akumana nawo. Iwo amadalira pa chiŵerengero chokulirako kuti awopsyeze ndi kuba, nthaŵi zina ndi chiwawa. Chotero, mwanzeru, musavale zokometsera kapena zinthu zina za mtengo wapatali zimene zingawonedwe mopepuka ndi kutsompholedwa. Nyamulani chola kapena chikwama cha ndalama chokhala ndi ndalama zochepera—mukumasunga mapepala ofunika kwambiri ndi makardi angongole kwinakwake—ndipo khalani okonzekera kuchipatsa icho. Ngati mupatsa “chimkupiti” chinthu chinachake mosavuta, iwo angakusiyeni inu ndipo mwamsanga kupitirira.

[Chithunzi patsamba 29]

Kodi mudzalimbana kuti musunge ndalama zanu ndipo mwinimwake kutaya moyo wanu?

[Chithunzi patsamba 29]

Pamene wawukiridwa mwa kugonana, chinthu chabwino koposa chimene mkazi angachichite ndi KUKUWA

[Chithunzi patsamba 30]

Maloko abwino ali ofunika kaamba ka kusunga nyumba yanu

[Chithunzi patsamba 30]

Fufuzani zizindikiritso zaumboni musanalole winawake kuloŵa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena