Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 5/8 tsamba 3
  • Kodi Dziko Lopanda Nkhondo Nlotheka?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Dziko Lopanda Nkhondo Nlotheka?
  • Galamukani!—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nkhondo Zidzakhalako Mpaka Liti?
    Galamukani!—1999
  • Mitundu Yogwirizana—Kodi Iri Njira Yabwinopo?
    Galamukani!—1991
  • Zolinganiza za Munthu Mkufuna Kudzetsa Chisungiko cha Padziko Lonse
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Nchiyani Chimene Chikuchitika ku Mitundu Yogwirizana?
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 5/8 tsamba 3

Kodi Dziko Lopanda Nkhondo Nlotheka?

TANGOGANIZANI za kusadzaonanso kapena kukumana ndi zochitika zowopsa za nkhondo ndi zotulukapo zake. Tangoganizani za kusadzamvanso kulira kwa mfuti kapena kwa mabomba, kusadzaonanso magulu a anthu otsala pang’ono kufa ndi njala amene akuthaŵa kwawo, kusadzavutikanso maganizo ndi kuti inu kapena wokondedwa wanu adzafera m’nkhondo ina yankhanza ndi yopanda pake. Kudzakhala kwabwino kwambiri chotani nanga kukhala ndi moyo m’dziko lopanda nkhondo!

‘Chimenecho nchiyembekezo chokayikitsa,’ inu mungatero. Komabe, chinthunzithunzi cha dziko la mtendere chinaŵala bwino kwambiri zaka zingapo zokha zapitazo. Mu 1990 ndi 1991, ambiri anali kunena kuti maiko anali atafika pakhomo pa nyengo yatsopano ya chisungiko ndi chigwirizano. Pofotokoza za mkhalidwe wa nthaŵiyo, George Bush, yemwe anali pulezidenti wa United States panthaŵiyo, ananena nthaŵi zambiri za kubuka kwa “dongosolo latsopano la dziko.”

Kodi nchifukwa ninji anali ndi chiyembekezo chabwinocho? Nkhondo ya Mawu inali itatha. Kwa zaka zoposa 40, chiwopsezo cha nkhondo ya nyukliya chinalenjekeka mowopsa pa anthu monga lupanga lolenjekeka pa ulusi waung’ono. Komano ndi kutha kwa Chikomyunisti ndi kugaŵanika kwa Soviet Union, chiwopsezo cha chipululutso cha nyukliya chinachita ngati chikuzimiririka. Dziko linatha kupuma bwinopo.

Panali chifukwa china chachikulu chimene anthu anaonera mtsogolo ndi chidaliro, ndi chifukwa chimene ambiri akali kuchitira motero. Kwa zaka makumi anayi mpikisano wa pakati pa Kummaŵa ndi Kumadzulo wapangitsa United Nations kungokhala ngati bungwe lochitiramo mikangano. Koma kutha kwa Nkhondo ya Mawu kunamasula UN kuti ichite zimene anailinganizira—kumenyera nkhondo mtendere ndi chisungiko chapadziko lonse.

M’zaka zaposachedwapa UN yakulitsa zoyesayesa za kuletsa nkhondo. Pokhala ili ndi magulu ankhondo ochokera m’maiko amene ali mamembala ake, United Nations inachita ntchito zambiri zosungitsa mtendere m’zaka zinayi 1994 asanafike kuposa m’zaka 44 poyambapo. Anthu wamba ndi asilikali ankhondo 70,000 anatumikira m’ntchito 17 pa dziko lonse. M’zaka ziŵiri zokha, ndalama zogwiritsiridwa ntchito pa kusungitsa mtendere zinaŵirikiza kuposa kaŵiri kufikira pa $3.3 biliyoni mu 1994.

Boutros Boutros-Ghali, mlembi wamkulu wa UN, posachedwapa analemba kuti: “Pali zizindikiro zakuti dongosolo la chisungiko cha maiko onse limene linakhazikitsidwa ku San Francisco pafupifupi zaka 50 zapitazo [pa kuyambidwa kwa UN] tsopano likuyamba kugwira ntchito mogwirizana ndi cholinga chake . . . Tili panjira ya kupeza dongosolo lapadziko lonse logwira ntchito.” Ngakhale kuti pali zochitika zonsezi, chithunzithunzi cha dongosolo latsopano la dziko chikuzimiririka mofulumira. Kodi nchiyani chimene chaipitsa ziyembekezo za dziko lopanda nkhondo? Kodi pali chifukwa cha kukhulupirira kuti tidzaonadi mtendere wa padziko lonse? Nkhani zotsatira zidzayankha mafunso ameneŵa.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Ndege za nkhondo: Chithunzithunzi cha USAF

Mfuti zogwetsera ndege: Chithunzithunzi cha U.S. National Archives

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena