Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 5/8 tsamba 27-29
  • Vairasi Yakupha Isakaza Zaire

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Vairasi Yakupha Isakaza Zaire
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nthenda Yakupha
  • Kuletsa Mliriwo
  • Kufunafuna Magwero Ake
  • Mliriwo Uzimiririka
  • Kodi Mankhwala Ake Nchiyani?
    Galamukani!—1996
  • ‘Miliri M’malo Akuti Akuti’
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Ndani Amene Ali Pangozi?
    Galamukani!—1986
  • AIDS—Vuto la Azaka Zapakati pa 13 ndi 19
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 5/8 tsamba 27-29

Vairasi Yakupha Isakaza Zaire

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! MU AFIRIKA

KIKWIT, Zaire, ndi tauni ya nyumba zomangidwa mwachisawawa yokhala kumalire kwa nkhalango ya mvula ya m’dera lotentha. Gaspard Menga Kitambala wazaka 42 zakubadwa, yemwe anali kukhala kunja kwa mzindawo, anali Mboni yokha ya Yehova m’banja lake. Menga anali wogulitsa makala. Anali kuwotchera makala akewo m’nkhalangoyo, kuwalongedza, ndi kuwanyamula pamutu kupita nawo ku Kikwit.

Pa January 6, 1995, iye anadwala. Anagwa kaŵiri popita kunyumba kuchokera ku nkhalango. Atafika kunyumba kwake, anati akumva mutu ndi malungo.

Masiku angapo otsatira, matenda ake anakula. Pa January 12, banja lake linampititsa ku chipatala cha Kikwit General Hospital. Mboni za mumpingo wa Menga zinathandiza banjalo kumsamalira m’chipatala. Mwachisoni, matenda ake anakulirakulira. Anayamba kusanza mwazi. Mwazi unatuluka kosaleka m’mfuno mwake ndi m’makutu. Pa January 15, anamwalira.

Posapita nthaŵi ena m’banja la Menga amene anakhudza thupi lake anadwala. Chakuchiyambi kwa March, anthu 12, achibale apafupi a Menga anali atamwalira, kuphatikizapo mkazi wake ndi aŵiri mwa ana awo asanu ndi mmodzi.

Chapakati pa April, ogwira ntchito m’chipatala ndi ena anayamba kudwala ndi kufa monga Menga ndi banja lake. Mwamsanga nthendayo inafalikira ku matauni ena aŵiri m’deralo. Ndithudi, panafunikira thandizo lakunja.

Profesa Muyembe, katswiri wapamwamba wa mavairasi m’Zaire, anapita ku Kikwit pa May 1. Pambuyo pake anauza Galamukani! kuti: “Tinapeza kuti Kikwit anali ndi miliri iŵiri: woyamba unali kutseguka m’mimba kochititsidwa ndi mabakiteriya, ndi wachiŵiri nthenda yoipa ya kukha mwazi yochititsidwa ndi vairasi. Komabe, tinafunikira kutsimikizira nthenda imeneyi. Chotero tinatengako mwazi kwa odwalawo ndi kuutumiza ku Centers for Disease Control (CDC) ku Atlanta, U.S.A kuti ukapimidwe.”

CDC inatsimikizira zimene Muyembe ndi madokotala ena ku Zaire anali ataganizira kale. Nthendayo inali Ebola.

Nthenda Yakupha

Vairasi ya Ebola njowopsa. Imapha msanga. Ilibe katemera, ndipo ilibe mankhwala ake odziŵika ochiritsira odwala.

Ebola inayamba kudziŵika mu 1976. Dzina lake linatengedwa ku dzina la mtsinje m’Zaire, ndipo nthendayo inabuka kummwera kwa Sudan ndipo pambuyo pake kumpoto kwa Zaire posapita nthaŵi. Mu 1979 mliri wake waung’ono unabukanso ku Sudan. Zitachitika zimenezo, nthendayo inazimiririka kwa zaka zambiri kusiyapo anthu omwe anali kufa apa ndi apo ndi matenda onga a Ebola.

Vairasi ya Ebola njakupha zedi kwakuti asayansi amene amaiphunzira ku Atlanta amatero m’laboletale yotetezereka kwambiri yokhala ndi makina oloŵetsa mphepo amene amaletsa kachilombo kalikonse ka matenda koyenda ndi mphepo kutuluka. Asanaloŵe m’laboletale, asayansi amavala ma “space suit” owatetezera (zovala zonga zopita nazo kumwezi). Potuluka iwo amasamba m’mankhwala ophera tizilombo. Madokotala amene anafika ku Kikwit anali ndi zovala zawo zowatetezera—magulovu otaya atatha ntchito yake ndi zophimba kumutu, magalasi, ndi maovololo apadera amene samalola vairasi kuloŵa.

Komabe, anthu ochuluka a mu Kikwit analibe chidziŵitso ndi ziŵiya zodzitetezera nazo. Ena modziŵa anaika moyo wawo pangozi kapena kuutaya posamalira okondedwa awo odwala. Mabwenzi ndi mabanja anabereka odwala awo ndi akufa kapena kuwanyamula pamapeŵa popanda kudzichinjiriza. Zotsatirapo zake zinali kutayika kowopsa kwa miyoyo; vairasiyo inapulula mabanja athunthu.

Kuletsa Mliriwo

Maiko akunja anayankha pempho la Kikwit la thandizo mwa kupereka ndalama ndi ziŵiya zachipatala. Magulu a ofufuza anafika kuchokera ku Ulaya, South Africa, ndi United States. Kudza kwawo kunali ndi zolinga ziŵiri: choyamba, kuthandiza kuletsa mliriwo; ndi chachiŵiri, kupeza kumene vairasiyo imakhala pamene kulibe mliriwo.

Kuti athandize kuletsa mliriwo, antchito ya zaumoyo anayenda m’khwalala lililonse kufunafuna aliyense amene anasonyeza zizindikiro za nthendayo. Odwala anawapititsa kuchipatala, kumene anabindikiritsidwa ndi kusamaliridwa mwachisungiko. Amene anafa anakulungidwa m’mapulasitiki ndi kuikidwa mwamsanga.

Panakhala mkupiti waukulu wopereka chidziŵitso cholondola cha nthendayo kwa antchito ya zaumoyo ndi anthu onse. Uthengawo unaphatikizapo chenjezo lamphamvu loletsa miyambo yoikira maliro, imene mabanja amatsatira mwa kugwira ndi kusambitsa wakufa.

Kufunafuna Magwero Ake

Asayansi anafuna kudziŵa kumene vairasiyo inachokera. Zodziŵika ndi izi: Mavairasi sali tizilombo tokhala ndi moyo patokha, tokhoza kudya, kumwa, ndi kuswana patokha. Kuti tikhale ndi moyo ndi kuswana, tiyenera kuloŵa m’maselo ocholoŵana kwambiri ndi kuwagwiritsira ntchito.

Pamene vairasi iloŵa m’nyama, nthaŵi zambiri pamakhala unansi womvana—nyamayo simapha vairasiyo, ndipo vairasiyo simaphanso nyamayo. Koma pamene munthu akhalirana pafupi ndi nyama imene ili ndi vairasi ndipo iyo mwa njira ina yake nkuloŵa mwa munthu, vairasiyo ingakhale yakupha.

Popeza vairasi ya Ebola imapha anthu ndi apusi mofulumira kwambiri, asayansi aganiza kuti vairasiyo imakhalabe ndi moyo m’chamoyo china. Ngati antchito ya zaumoyo angapeze chamoyo chimene chimanyamula vairasiyo, pamenepo angakhoze kutenga njira zamphamvu zoletsera ndi kupeŵera miliri yamtsogolo. Funso losayankhidwa lonena za Ebola nlakuti, Kodi vairasiyo imakhala kuti pamene anthu sakudwala?

Kuti apeze yankho, ofufuza ayenera kupeza magwero a vairasiyo. Zoyesayesa za kupeza nyama yonyamula vairasiyo pambuyo pa miliri yapapitapo sizinaphule kanthu. Koma mliri wa ku Kikwit unapereka mpata watsopano.

Asayansi anakhulupirira kuti amene anayamba kudwala ndi mliriwo ku Kikwit anali Gaspard Menga. Koma kodi anautenga kuti? Ngati ndi ku nyama ina yake, ndi nyama yanji imeneyo? Ndithudi, yankho linayenera kupezeka m’nkhalango imene Menga anali kugwiramo ntchito. Magulu osonkhanitsa zinthu anatchera misampha 350 m’malo osiyanasiyana kumene Menga anali kuwotchera makala. Anagwira mbeŵa, aswiswili, achule, abuluzi, njoka, udzudzu, ma sandfly, nkhufi, nsikidzi, nsabwe, ma chigger, ndi utata—tonse pamodzi tinyama tating’ono 2,200 ndi tizilombo 15,000. Asayansi, ovala zowatetezera, anapha tinyamato ndi mpweya wakupha. Ndiyeno anatumiza minofu yake ku United States, kuti akaipime kuona ngati inali ndi vairasi.

Popeza malo amene vairasiyo ingabisalemo ngambirimbiri, palibe amene akutsimikiza kuti adzapeza magwero ake. Dr. C. J. Peters, mtsogoleri wa nthambi ya CDC ya tizilombo tapadera ta matenda, anati: “Ndiganiza kuti kuli kokayikitsa ngati tidzapeza nyama imene vairasi ya Ebola imakhalamo.”

Mliriwo Uzimiririka

Pa August 25, boma linalengeza kuti mliriwo watha, popeza kuti panalibe odwala atsopano kwa masiku 42, nyengo yoŵirikiza kaŵiri kuposa nyengo yonse imene kachilomboko kamaloŵa mwa munthu ndi pamene kamayambitsa matenda. Kodi nchifukwa ninji nthendayo sinafalikire kwambiri? Chochititsa china chinali zoyesayesa pa zamankhwala zimene maiko akunja anachita kuti aletse mliriwo. China chimene chinaletsa mliriwo chinali ukulu wake wa nthendayo. Chifukwa chakuti inabuka ndi kupha anthu mofulumira kwambiri ndipo inapatsiridwa kwa wina kokha mwa kukhalirana pafupi kwambiri, sinafalikire kwa anthu ochuluka.

Kaundula wa boma akusonyeza kuti anthu 315 anadwala nthendayo ndipo 244 anafa—chiŵerengero cha imfa cha 77 peresenti. Ebola yalekeka kwa kanthaŵi. M’dziko latsopano la Yehova, idzatontholetsedwa kosatha. (Onani Yesaya 33:24.) Pakali pano, anthu akufunsa kuti, ‘Kodi Ebola idzabukanso kudzaphanso anthu?’ Mwinamwake. Koma palibe adziŵa kumene idzabukira ndi nthaŵi yake.

[Bokosi patsamba 29]

Kuyerekezera Mliriwo ndi Nthenda Zina

Ebola njakupha, komabe ngozi yaikulu kwa Aafirika imadza ndi matenda osamveka kwambiri. Mliriwo uli mkati, matenda ena anapha anthu mwakachetechete. Zinamveka kuti makilomita angapo kummaŵa kwa Kikwit, anthu 250 posachedwapa anadwala poliyo. Kumpoto koma chakumadzulo, mtundu wakupha wa kolera unasakaza Mali. Kummwera, ku Angola, anthu 30,000 anadwala nthenda yakawodzera. M’dera lalikulu la ku West Africa, anthu zikwi zambiri anafa ndi mliri wa meningitis. The New York Times inati: “Kwa Aafirika, funso lovutitsa limene limabuka nlonena za chifukwa chimene kubuka kwa nthenda zilizonse za masiku onse [za Afirika] zochuluka zimene zili zakupha ndi zokhoza kuletsedwa sikumavutitsa chikumbumtima cha dziko.”

[Chithunzi patsamba 28]

Asayansi akufunafuna magwero a vairasi yakupha

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena