Kupeza Njira Yabwino
MAWU A MULUNGU, Baibulo, amanena za nthaŵi pamene boma lakumwamba la Mulungu lidzakhala litathetsa mavuto onse a anthu, amene tsopano akuphatikizapo vuto la kuipitsa kwa magalimoto. Kodi Ufumu Waumesiya umenewu, umene ambiri aphunzitsidwa kuupempherera, udzapereka njira yabwino mwa kupanga galimoto losakhoza kuipitsa konse? Kapena kodi njira yabwino imeneyo idzachitidwa mwa kuchotsapo galimoto zonse padziko lapansi? Popeza Baibulo silimatipatsa yankho lenileni, palibe chimene tingachite choposa kungoyembekezera.—Mateyu 6:9, 10.
Koma tingatsimikize ponena za izi: Boma la Mulungu silidzalola kuipitsa kuti kuwononge kukongola kwa chilengedwe mu Paradaiso wobwezeretsedwa amene Ufumuwo udzabweretsa.—Yesaya 35:1, 2, 7; 65:17-25.
Popeza awo amene amamatira ku Mawu a Mulungu anayamba kale kuphunzitsidwa kaamba ka moyo m’dziko latsopano lopanda kuipitsa, kodi ayenera kulingalira motani ponena za kugwiritsira ntchito magalimoto lerolino? Galamukani! wa December 8, 1987, anali ndi nkhani yakuti “Kodi Nkhalango Zingasungidwe?” Anasimba kuti asayansi ena amalingalira kuti zoipitsa mpweya zimene zimakhala muutsi wa galimoto ndizo zimachititsanso nkhalango kufa. Zimenezi zinachititsa woŵerenga wina wodera nkhaŵa kulembera Watchtower Society kufunsa kuti kaya polingalira za zenizeni zimenezi kungakhale bwino kwa Akristu kuyendetsa galimoto. Anafuna kudziŵa ngati kuchita zimenezo kungasonyeze kusalemekeza chilengedwe cha Yehova.
Mbali ina ya yankho la kalata yake inayankhidwa motere: “Mboni za Yehova zimalabadira mokhulupirika malamulo onena za malo okhala oikidwapo ndi akuluakuku a boma kuti achepetse kuipitsa. (Aroma 13:1, 7; Tito 3:1) Kuchita mopyola pa zimene boma limafuna kuli chosankha chaumwini. Ngati wina asankha kusayendetsanso galimoto, imeneyo ndi nkhani yake. Komabe, nkhani ya mu Galamukani! patsamba 25 inasonyeza mmene anthu ena amalingalirira, mwa kunena kuti: ‘Ambiri akutenga masitepe okhoza kugwirirapo ntchito akuchepetsako kuipitsa mpweya kumlingo womwe uli wabwino monga mmene kungathekere. Iwo akuyendetsa galimoto mwapang’onopang’ono, kupanga maulendo ocheperako, [kunyamulana pa galimoto], kugwiritsira ntchito petulo [w]opanda lead ndi kumvera ku malamulo a kusaipitsa okhazikitsidwa ndi boma.’”
Kuchita Moyenera Kwachikristu
Yankho limeneli linasonyeza kuchita moyenera kwachikristu. Kuyenera kukumbukiridwa kuti galimoto sindizo zokha zimene zimaipitsa. Ndege ndi sitima—kwenikweni, njira zakayendedwe zambiri zamakono—zimatero. Koma mitundu imeneyi yakayendedwe sinapangidwe ndi chifuno cha kuipitsako. Kuipitsa kwangokhala chotulukapo chosayembekezeredwa, chochititsa chisoni koma chochititsidwa ndi kupereŵera chidziŵitso ndi malingaliro opanda ungwiro.
Nsanja ya Olonda ya January 1, 1993, tsamba 31, inafotokoza nkhani imeneyi, ikumati: “Monga Mboni za Yehova, tili odera nkhaŵa kwambiri ndi mavuto ochuluka okhudza malo okhala zinyama ndi anthu amene tsopano akuyambukira malo athuwa dziko lapansi. Kuposa anthu ochulukitsa, ife timazindikira kuti dziko lapansi linalengedwera kukhala malo okhala oyera, ndi abwino ku banja langwiro laumunthu. (Genesis 1:31; 2:15-17; Yesaya 45:18) . . . Chotero kuli koyenera kupanga zoyesayesa zosankitsa ndi zanzeru kupeŵa kuwonjezera mosafunika kuipitsa chiunda chathuchi kosalekeza kochitidwa ndi munthu. Komabe, taonani, liwu lakutilo ‘zosankitsa.’ . . . Anthu a Mulungu sayenera kukhala osazindikira nkhani zokhudza malo okhala anthu ndi zinyama. Yehova anafuna kuti anthu ake akale achitepo kanthu kutaya zinyansi, michitidwe imene inali ndi cholinga cha kukhala ndi malo okhala audongo ndi aukhondo. (Deuteronomo 23:9-14) Ndipo popeza kuti tidziŵa lingaliro lake la awo amene akuwononga dziko lapansi, ife ndithudi sitiyenera kunyalanyaza zinthu zimene tingachite kusunga malo ali audongo. . . . Komabe, mlingo umene Mkristu adzachita zimenezi, ili nkhani yaumwini kusiyapo ngati afunikira kuti atero mwalamulo. . . . Anthu opanda ungwiro amagwera mosavuta mumsampha wakuchita monkitsa. . . . Zoyesayesa za anthu za kuchotsa padziko lapansi mavuto ake aakulu amalo okhala anthu ndi zinyama, kuphatikizapo kuipitsidwa kwawo, sizidzapambana kotheratu. Pangakhale kupita patsogolo pang’ono cha apa ndi apo, koma njira yokha yokhalitsa yothetsera imafunikiritsa kuloŵerera kwa Mulungu. Chifukwa chake timasumika zoyesayesa zathu ndi chuma panjira ya Mulungu yothetsera, m’malo mwakuyesayesa kuthetsa zizindikiro zachiphamaso.”
Akristu amachita moyenera pamene akulabadira mapulinsipulo a Baibulo, akumakumbukira ntchito yaumulungu imene alandira ya kulalikira uthenga wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse lapansi. (Mateyu 24:14) Palibenso china chofunika kwambiri kapena chofulumira koposa! Ngati njira zamakono za kayendedwe zingathandize Akristu kukwaniritsa thayo limeneli, iwo ali ndi zifukwa zabwino za kuzigwiritsira ntchito. Panthaŵi imodzimodziyo, iwo amapeŵa kuipitsa mopanda nzeru kapena mwadala. Motero iwo amakhala ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa munthu ndi Mulungu yemwe.
Motero ngakhale kuti ifeyo lerolino sitikudziŵa kwenikweni mmene vuto la kuipitsa ndi la galimoto lidzathetsedwera pomalizira pake, tikudziŵa kuti ilo lidzathetsedwa. Kwenikweni, njira yabwino ilidi pafupi kwambiri.
[Bokosi patsamba 23]
Kulimbana ndi Kuipitsa
• Kuyenda pansi kapena kukwera njinga pamene kuli kotheka
• Eni galimoto kunyamulana
• Kukonzetsa magalimoto nthaŵi zonse
• Kuzindikira kufunika kwa mafuta osaipitsa
• Kupeŵa maulendo osafunika
• Kuyendetsa galimoto pamaliŵiro abwino koma osasinthasintha
• Kugwiritsira ntchito zoyendera za onse pamene kuli kotheka ndi kosavuta
• Kuzima injini m’malo mwa kuilekerera ikulira pamene galimoto iima kwa utali uliwonse wa nthaŵi