Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 1/8 tsamba 14-15
  • Tsoka la Maggy ndi Dalitso Langa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tsoka la Maggy ndi Dalitso Langa
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Wodalitsidwa ndi Khanda Lathanzi
  • Kuyang’anizana Nayo Imfa ndi Kupirira Pambuyo Pake
  • Chichirikizo cha Akristu Anzanga
  • Chisangalalo Tsopano ndi Chiyembekezo cha Mtsogolo
  • Otayidwa ndi Othaŵa Kwawo
    Galamukani!—1995
  • “Panopa Ndimakonda Kwambiri Utumiki”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Sitili Amatsenga Kapena Milungu
    Galamukani!—1994
  • Kuthana ndi Ziyeso Mwamphamvu ya Mulungu
    Galamukani!—2000
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 1/8 tsamba 14-15

Tsoka la Maggy ndi Dalitso Langa

Lachiŵiri, May 2, 1995, ndi tsiku limene mwana wanga wamkazi anabadwa ndi limene mkazi wanga anamwalira. Mwachisoni, Maggy sanaone konse nkhope ya khanda lake. Tsopano chiyembekezo changa ndicho kudzasonyeza Tamara kwa mayi wake pamene aukitsidwa.

TITAKHALA zaka 16 muukwati, mkazi wanga, Maggy, anauzidwa ndi dokotala wake kuti anali ndi kansa yakumaŵere ndipo anatsala chabe ndi miyezi yoŵerengeka akali moyo. Izi zinachitika zaka zisanu zapita. Mwamwaŵi, Maggy anakhoza kukhala ndi moyo wabwinopo m’zaka zotsirizira zimenezo za moyo wake. Chabe kuti chakumapeto ululuwo unadzakhala wosapiririka kwenikweni.

Chifukwa cha ukulu wa kansa yake, madokotala anatero kuti kunali kokayikitsa kuti iye angatenge pakati. Choncho, mungaone mmene tinadabwira pamene anaonamo khanda m’mimba mwake pomampimapima kuti apende kuwongokera kwa zithupsya za kansazo! Linali mtsikana. Maggy anali ndi pakati pa miyezi inayi ndi theka. Anali wokondwa kwabasi podziŵa kuti adzaona mwana woyamba.

Maggy anachitadi chilichonse chimene anakhoza kuti atsimikizire kuti mwanayo adzabadwe wathanzi. Anali kumasankha zakudya zake mosamala, ndipo ngakhale mkati mwa milungu iŵiri yotsirizira yamoyo wake pamene ululu unakhala wong’amba mtima, anali kumamwa mankhwala opha ululu kokha pamene anali wosakhoza kuupirira.

Wodalitsidwa ndi Khanda Lathanzi

Loŵeruka, April 29, mtima wa Maggy unayamba kuthamanga ndipo anati: “Ndikuganiza kuti ndifa basi.” Ndinakhala naye mapeto a mlunguwo. Nditaitana dokotala pa Lolemba, nthaŵi yomweyo ndinamtengera kuchipatala ku Montreal, Canada, pafupi ndi kwathu, ku St. Jérôme.

Pafupifupi 5:30 mmaŵa mwake, nesi anadutsa pakhomo la chipinda cha Maggy, ndi kuona kuti anali kupilipitika. Mwachionekere, unali mtima. Mwamsanga dokotala anaitanidwa m’chipinda choyandikana. Ngakhale kuti Maggy anafa, gulu la madokotalalo linakhoza kupulumutsa khanda lathu. Tamara anabadwa wosakhwima kutatsala miyezi iŵiri ndi theka ndipo anali wolemera makilogalamu 1.1 basi.

Popeza kuti mlingo wa mwazi wa Tamara unali wotsika, madokotala anafuna kumuika mwazi. Komabe, analimbikitsidwa kuti agwiritsire ntchito mankhwala owonjezera mwazi. Anaterodi, ndipo pamene mankhwala ameneŵa anakhala othandizadi kuwonjezera mwazi wake, nesi wina anati: “Bwanji samagwiritsira ntchito ameneŵa kwa makanda onse?”

Tamara anali ndi mavuto ena ochititsidwa ndi kubadwa wosakhwima, koma onsewo anathetsedwa. Ndithudi, pamene a Watters, dokotala wazaminyewa anampima pambuyo pake, anamuuza nesiyo kuti: “Ndikukhulupirira kuti mwandipatsa khanda lina kuti ndilipime; kwa ine likuoneka lathanzi kwambiri.”

Kuyang’anizana Nayo Imfa ndi Kupirira Pambuyo Pake

Kuonerera Maggy alinkufa kunali kovuta kwa ine. Ndinangosoŵeratu chochita. Kunali kovuta kulankhula za imfa ya Maggy. Komabe, ndinatero pamene abale ndi alongo anga achikristu anabwera kuchipatala. Kupwetekako kunayamba kuchepa pang’onopang’ono mmene ndinapitiriza kulankhula za iyo. Paliponse pamene ndiŵerenga nkhani mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! imene imandikhudza kwenikweni, ndimaiika pambali pa laibulale yanga ndipo ndimaitenga ndi kuiŵerenga pamene ndimva chifundo.

Vuto lina lakhala lakufika panyumba pa duu. Kusungulumwa nkovuta. Maganizowo amabwerabe, ngakhale kuti ndimapindula ndi ubwenzi wachikristu womangirira. Ine ndi Maggy tinali kuchitira zinthu pamodzi, ndipo tinalankhulapo za vuto la kusungulumwa limene ndinali kudzayang’anizana nalo. Iye anafuna kuti ndidzakwatirenso. Komabe, sizokhweka motero.

Chichirikizo cha Akristu Anzanga

Kaya kuti ndikanatani popanda chithandizo cha Komiti Yolankhulana ndi Chipatala (HLC) ya Mboni za Yehova. Mmaŵa umene Maggy anamwalira, Mboni ina yachidziŵitso ya HLC inaliko kuchipatalako ndipo inandipatsa chithandizo chimene ndinafunikira.

Antchito apachipatala anachita chidwi ndi chithandizo chimene ndinalandira ku mpingo wathu wachikristu mu St. Jérôme ngakhalenso ku mipingo ina m’deralo. Madzulo amene imfa ya Maggy inalengezedwa pamsonkhano wathu wachikristu, mabwenzi okondedwa oposa 20 anachitapo kanthu mwa kupereka chithandizo chawo. Chichirikizocho chinali chachikulu ndithu.

Mabwenzi anandikonzera chakudya; firiji yanga inali yodzaza kwa miyezi ingapo. Achibale ndi abale ndi alongo achikristu anathandizira kugulira mwana wanga zovala. Anandibweretsera zinthu zochuluka kwakuti ndinasoŵa malo ozisungira zonse.

Chisangalalo Tsopano ndi Chiyembekezo cha Mtsogolo

Tamara amandithandiza kuiŵala chisoni changa. Wafikira pakukhala wapamtima panga kwambiri. Tsiku lililonse pamene ndimpatsa moni mwachimwemwe kuti “wadzuka bwanji?” amayankha mwa kumwetulira ndi kuyamba “kulankhula,” akumaponya mikono ndi miyendo yake, ali wokondwa.

Monga wokonda kupenda zakuthambo, ndikuyembekeza kudzamkhazika Tamara pa miyendo ndi kum’yang’anitsa m’telesikopo yanga zodabwitsa za kumwamba za Mpangi wathu Wamkulu, Yehova. Kusinkhasinkha za moyo wopanda mapeto m’dziko lapansi la Paradaiso kumatonthozadi. Ndipo kudziŵa kuti chomwechinso ndicho chiyembekezo cha Tamara kumawonjezera chimwemwe changa.—Salmo 37:9-11, 29.

Pomalingalira zochitika pazaka zisanu zapitazo, ndingazifotokoze bwino monga zopsinja maganizo ndi zosangalatsa, ponse paŵiri. Ndaphunzira zochuluka ponena za ine mwini ndi za moyo weniweniwo. Mwachidwi, ndikudikira mtsogolo pamene, monga momwe Baibulo likufotokozera, “sipadzakhalanso imfa, ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

Pamenepo, pa chiukiriro, Maggy adzakhala wokhoza kupuma wefuwefu popanda ululu. Koposa zonse, chiyembekezo ndi chikhumbo changa champhamvu ndicho kudzakhalapo kuti ndidzasonyeze Maggy kwa Tamara, kotero kuti adzaone kamtsikana kamene anavutikira kwambiri.—yosimbidwira ndi Lorne Wilkins.

[Chithunzi patsamba 14]

Ndili ndi mkazi wanga

[Chithunzi patsamba 14]

Mwanathu wamkazi, Tamara

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena