Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 2/8 tsamba 8-9
  • Otayidwa ndi Othaŵa Kwawo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Otayidwa ndi Othaŵa Kwawo
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Otayidwa
  • Othaŵa Kwawo
  • Kulimidwa Pamsana ndi Kusautsidwa Maganizo
  • Kufunafuna “Ufulu”
  • Kodi Kuthaŵa Kuli Yankho?
    Galamukani!—1988
  • Nchifukwa Ninji Pali Ana Othaŵa Ambiri?
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Tsokalo Lidzatha Liti?
    Galamukani!—1995
  • Mmene Mungalimbitsire Zomangira za Banja
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 2/8 tsamba 8-9

Otayidwa ndi Othaŵa Kwawo

“NDINAMETA tsitsi langa, kuvala ngati mwamuna, kuvala unyolo ndi maloko m’khosi mwanga, ndi kubayitsa phinifolo patsaya, ndipo mwanjira imeneyi ndinayamba moyo wanga monga m’panki.”—Tamara.

Ngati mukanaona Tamara pamsewu, kodi mukanadziŵa kuti anali wachichepere wosukidwa ndi wochitiridwa nkhanza amene moyo wake wa panyumba unali wopanda chisamaliro ndi chikondi zimene anali kupempha? Kodi mukanaganiza kuti iye anali chigaŵenga chofuna kuvutitsa boma ndipo mwina mwake cha moyo waupandu? Tamara akuulula kwa Galamukani! zochitika zowopsa zimene zinamchititsa kukhala ndi moyo umene anali nawo kuyambira pausinkhu wa zaka 14, moyo umene sanafune konse.

Otayidwa

Tamara akusimba kuti: “Ndinakulira m’tauni ina yaing’ono ya kumapiri ku Italy, m’banja limene munalibe chikondi. Mwachisoni, ndinapenyerera mikangano yaikulu imene inabuka pakati pa makolo anga ndi kutukwanizana koipitsitsa kumene anachitirana pa zochitika zimenezo. Kaŵirikaŵiri ndinkadziloŵetsa mu mkangano ndi kumenyedwa mopanda chifundo ndi atate wanga okakala mtima. Ndinkapirira ndi kulembeka pathupi kwa zikoti kwa masabata ambiri.

“Pamene ndinali ndi zaka 14, atate anandipatsa ndalama pang’ono ndi tikiti yokwerera sitima ulendo umodzi wokha kumka ku mzinda wina wapafupi, kumene kunali ngozi zambiri. Ndinapanga ubwenzi ndi achichepere ena amene, mofanana nane, analibe munthu aliyense wowakonda. Ambirife tinakhala zidakwa. Ndinakhala wonyada, wotukwana, ndi wandewu. Kaŵirikaŵiri ndinkakhala wosadya. Madzulo ena m’nyengo yozizira ine ndi mabwenzi anga tinatentha mipando kuti tiwothe. Ndinakhumba kwambiri banja londisamalira, lofuna kudziŵa za malingaliro anga, nkhaŵa zanga, ndi mantha anga. Komano ndinali ndekhandekha.”

Pali “Atamara” zikwi mazana ambiri lerolino m’dziko. Pa kontinenti iliyonse, pali ana amene asiyidwa ndi makolo amene anyalanyaza mathayo awo.

Othaŵa Kwawo

Achichepere ena amasankha zochoka panyumba chifukwa chakuti “akhaladi malo owopsa kwa iwo kupitiriza kukhalabe pomwepo; mpopweteka kwambiri, mpowopsa kwambiri, ndipo amathaŵapo ndi kukakhala m’misewu.”—New York State Journal of Medicine.

Pa msinkhu wa zaka zisanu ndi zinayi, Domingos anangosiyidwa kunyumba ya ana amasiye pamene amake anakwatiwanso. Chifukwa cha kumenyedwa kumene anakumana nako ndi ansembe, analinganiza zothaŵa. Amake anamtenganso, komano anali kumenyedwa nthaŵi zonse ndi atate wake ompeza. Kuthaŵa ndiko kunali njira yokha imene anapezera mpumulo pa nkhanza ya panyumba.

Mwachisoni, “mamiliyoni ambiri a ana samakhulupirira kuti achikulire m’mabanja awo angapereke chisamaliro chotetezera ngakhale chochepa motani,” akulemba motero Anuradha Vittachi m’buku lake lakuti Stolen Childhood—In Search of the Rights of the Child. Iye akulembanso kuti: “Kukuyerekezeredwa kuti pamakhala ana atatu amene amafa pa tsiku chifukwa cha kuchitiridwa nkhanza ndi makolo awo mu United States.” M’zochitika zambirimbiri, mwana amagonedwa m’malo mwa kutetezeredwa ndi chiŵalo china cha banja.

Kulimidwa Pamsana ndi Kusautsidwa Maganizo

Domingos anakakamizika kukakhala ndi ana ena a mu msewu amene anali kulanda anthu zinthu ndi kuba, ndiponso kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka ndi kuwagulitsa. Mwatsoka, ambiri amene amathaŵa mikhalidwe yoipa panyumba amalimidwa pamsana ndi ogula mahule, ogona ana, ndi magulu osonyeza zithunzithunzi zaumaliseche. Pokhala anjala ndi osukidwa, achichepere ameneŵa amapatsidwa malo okhala ndi malonjezo a kukhala ndi munthu wachikulire wina “wosamala,” akumangotulukira kuti ayenera kulipirira mtengo wake ndi matupi awo m’moyo wa uhule. Pokhala osadziŵa ntchito iliyonse, ambiri amaphunzira kukhala ndi moyo m’misewu mwanjira iliyonse imene angathe, kuphatikizapo kunyengedwa ndi kunyenga ena m’kugonana. Ena amafa. Anamgoneka, uchidakwa, mbanda, ndi kudzipha zimapulula achichepere ambiri.

Pothirira ndemanga za ana okhala m’misewu, yemwe kale anali mwana wochita uhule anati: “Munomo umakhala wamantha. Mwaona nanga, chimene chimandikwiyitsa nchakuti [anthu] ambiri pamene aona mwana amene ali mtulo m’sitima, kapena pamene aona mwana ali m’mbali mwamsewu usiku wonse, amaganiza kuti nchifukwa chakuti amafuna zimenezo. Tsopano popeza kuti ndakula, simmene ndimaonera. Ana ameneŵa aliyense akupempha thandizo mofuula m’njira yakeyake. Sakufuna kukhala otero, koma makolo awo sawafuna.”

Kufunafuna “Ufulu”

Pali achichepere ena zikwi mazana ambiri amene amasimbidwa kukhala osoŵa kwawo amene anyengedwa kukhala m’mbali mwa msewu ndi ufulu umene amalingalira kukhala uli kumeneko. Ena amafuna kumasuka ku umphaŵi. Ena amakhumba kumasuka ku ulamuliro wakholo ndi malamulo amene amalingalira kuti ali okhwima.

Wachichepere wina amene analaŵa wotchedwa kuti ufulu mwa kuchoka mu ulamuliro ndi m’malamulo amkhalidwe a makolo a banja Lachikristu anatchedwa Emma. Atachoka panyumba ndi kuloŵa m’moyo wina ndi mabwenzi ake, anakhala kapolo wa anamgoneka. Koma atakumana ndi nkhanza za m’misewu, Emma anasonyeza chikhumbo cha kubwerera ndi kuleka chizoloŵezi chake cha anamgoneka. Komabe, mwachisoni, sanathetse mayanjano ake ndi mabwenzi oipa, ndipo pamadzulo ena otentha ali pamodzi ndi mabwenzi akewo, anadzibaya jekeseni wa heroin. Imeneyo inali nthaŵi yomaliza kwa Emma. Anakomoka kwanthaŵi yaitali nafa tsiku lotsatira, atasiyidwa yekhayekha ndi “mabwenzi” ake.

Kodi mtsogolo mwa ana ochitiridwa nkhanza ndi makolo awo kapena ndi ena mungakhale mwabwinopo? Kodi padzakhaladi dziko limene silidzalima pamsana achichepere? Kodi nchiyembekezo chotani chimene chilipo chakuti moyo wa banja ungakonzedwe ndi kulemekezedwa kotero kuti achichepere sangafune kuthaŵa panyumba? Mayankho ake angapezedwe m’nkhani yotsatira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena