Mmene Mungachitire ndi Malingaliro
KODI pali pano mukusamala wokondedwa wodwala kwambiri? Ngati zili choncho, mwina mungasokonezeke maganizo ngakhale kuda nkhaŵa. Kodi mungachitenji? Onani malingaliro amene anthu osamala ena amalimbana nawo ndi njira zotsatirika zomwe zawathandiza kupirira.
Manyazi. Nthaŵi zina, makhalidwe a munthu wodwala angakuchititseni manyazi pamaso pa ena. Koma kufotokozera mabwenzi ndi anansi mkhalidwe wa matenda a wokondedwa wanu kungawathandize kumvetsa ndipo kungawachititsenso kusonyeza ‘chifundo’ ndi kufatsa. (1 Petro 3:8) Ngati kutheka, lankhulani ndi mabanja ena amenenso ali mumkhalidwe wonga wanu. Manyazi anu angachepe pamene musimbirana mmene zimakhalira. Sue akufotokoza zimene zinamthandiza kuti: “Ndinawachitira chisoni kwambiri atate—zinathetsa manyazi alionse. Ndiponso nthabwala zawo zinandithandiza.” Inde, nthabwala—za wodwala ndi omsamala omwe—zili njira yabwino kwambiri yothetsera kupsinjika maganizo.—Yerekezerani ndi Mlaliki 3:4.
Mantha. Kusadziŵa nthendayo kungakhale koopsa zedi. Ngati kutheka, funsani odziŵa bwino kuti akuuzeni zimene muyenera kuyembekezera pamene matendawo akula. Phunzirani kupereka chisamaliro m’mikhalidwe imeneyo. Kwa Elsa, china chimene chinamthandiza kwambiri kupirira mantha ake chinali kulankhula ndi enanso amene akusamala wina ndi manesi a m’nyumba ya odwala nthenda zosachiritsika ponena za zimene ayenera kuyembekezera pamene matenda a wodwala wake akula. Jeanny akulangiza kuti: “Limbanani nawo mantha anu ndi kuwaletsa. Kuopa zimene zingachitike kaŵirikaŵiri kumaposa ndi matendawo.” Dr. Ernest Rosenbaum akunena kuti mantha anu muyenera “kuwafotokoza pamene ayamba” mosasamala kanthu za chimene chikuwachititsa.—Yerekezerani ndi Miyambo 15:22.
Chisoni. Kulimbana ndi chisoni sikwapafupi, makamaka posamala wina. Mungachite chisoni chifukwa chotaya ubwenzi wanu, makamaka ngati wodwala wanu wokondedwa sathanso kulankhula, kumvetsa bwinobwino, kapena kukudziŵani. Ena sangamvetse malingaliro ameneŵa mwamsanga. Kulankhula za chisoni chanu kwa bwenzi lanu lomvetsa limene lidzamvetsera mofatsa ndi mwachifundo kungadzetse mpumulo wofunika kwambiriwo.—Miyambo 17:17.
Mkwiyo ndi Kukhumudwa. Zimenezi nzachibadwa posamala munthu wodwala kwambiri amene makhalidwe ake nthaŵi zina angakhale ovuta kwambiri. (Yerekezerani ndi Aefeso 4:26.) Dziŵani kuti kaŵirikaŵiri ndi nthenda imene imachititsa makhalidwe opsinja maganizo, osati wodwalayo. Lucy akukumbukira kuti: “Nditakwiya kwambiri, ndinali kulira. Ndiyeno ndinali kukumbukira mkhalidwe wa wodwala ndi matenda ake. Ndinadziŵa kuti wodwalayo anali kufuna thandizo langa. Zimenezo zinali kundithandiza kusalefuka.” Nzeru imeneyi ‘ingachedwetse mkwiyo.’—Miyambo 14:29; 19:11.
Liwongo. Ambiri amene akusamala wina amamva liwongo. Komabe, dziŵani kuti mukuchita ntchito yoyenera koma yovuta kwambiri. Dziŵani choonadi chakuti si nthaŵi zonse pamene mudzalankhula kapena kuchita zinthu mwangwiro. Baibulo limatikumbutsa kuti: “Timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mawu, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.” (Yakobo 3:2; Aroma 3:23) Musalole kumva kwanu liwongo kukulepheretsani kuchitapo kanthu tsopano motsimikiza. Pamene simunakondwe nazo zimene mwanena kapena kuchita, kaŵirikaŵiri mudzapeza kuti kunena kuti “Pepani” kudzakuchititsani inuyo ndi wodwala wanu kumva bwino. Mwamuna wina amene anasamala wachibale wake wodwala anati: “Chitani zimene mungathe m’mikhalidweyo.”
Kuchita Tondovi. Mabanja ambiri amene akulimbana ndi matenda aakulu amachita tondovi, ndipo zimenezo nzomveka. (Yerekezerani ndi 1 Atesalonika 5:14.) Wopereka chisamaliro wina amene amachita tondovi akufotokoza zimene zinamthandiza: “Ambiri anali kutiyamikira kuti tinali kupereka chisamaliro. Mawu achilimbikitso angapo okha angakulimbikitse kusalefuka pamene watopa kwambiri kapena kuchita tondovi.” Baibulo limati: “Nkhaŵa iŵeramitsa mtima wa munthu; koma mawu abwino aukondweretsa.” (Miyambo 12:25) Ena nthaŵi zina sangazindikire kuti mukufunikira chilimbikitso. Choncho, nthaŵi zina, mungafunikire choyamba kutchula poyera “nkhaŵa” imene ili mumtima mwanu kuti mulandire “mawu abwino” olimbikitsa kuchokera kwa ena. Komabe, ngati kuchita tondovi kupitiriza kapena kukulirako, kungakhale bwino kuonana ndi dokotala.
Kusoŵa Chochita. Mungaone monga mulibe chochita mutayang’anizana ndi matenda ofooketsa. Khulupirirani kuti zimene zikuchitika nzoona. Dziŵani zimene simungathe kuchita—inu simungasinthe thanzi la wodwala wanu, koma mungapereke chisamaliro chachikondi. Musayembekezere kuti inuyo, wodwala wanu, kapena okuchirikizani mudzachita zinthu mwangwiro. Kachitidwe koyenera kadzachepetsa malingaliro akuti mulibe chochita ndi kuchepetsa mtolo wa ntchito. Ambiri amene asamala wokondedwa akulangiza mwanzeru kuti: Phunzirani kutenga tsiku lililonse palokha.—Mateyu 6:34.
[Mawu Otsindika patsamba 8]
“Limbanani nawo mantha anu ndi kuwaletsa. Kuopa zimene zingachitike kaŵirikaŵiri kumaposa ndi matendawo”
[Bokosi patsamba 7]
Mawu Olimbikitsa a Opereka Chisamaliro
“MUSAPSINJIKE maganizo chifukwa cha kudzisuliza. Nkwachibadwa m’mikhalidwe yotero. Komabe simuyenera kubisa malingaliro anu. Uzani wina mmene mukumvera, ndipo ngati mungathe, pitani kokapuma—pitani kwina kwa kanthaŵi—kuti mukapumule.”—Lucy, amene ntchito yake m’chipatala yaloŵetsamo kuthandiza anthu angapo amene akusamala limodzinso ndi odwala.
“Ngati pali achibale kapena mabwenzi ofunitsitsa kuthandiza, aloleni athandize. Kunyamuzana ndi ena mtolowo nkofunika kwambiri.”—Sue, amene anadwazika atate wake asanamwalire ndi nthenda ya Hodgkin.
“Phunzirani kukonda nthabwala.”—Maria, amene anathandiza kusamalira bwenzi lake lokondedwa limene linamwalira ndi kansa.
“Limbani mwauzimu. Yandikirani kwa Yehova, ndipo pempherani kosaleka. (1 Atesalonika 5:17; Yakobo 4:8) Iye amapereka thandizo ndi chitonthozo mwa mzimu wake, Mawu ake, atumiki ake a padziko lapansi, ndi malonjezo ake. Khalani wolinganizika ndithu. Mwachitsanzo, nkothandiza kupanga ndandanda yamankhwala ndi ya othandiza.”—Hjalmar, amene anasamalira mlamu wake asanafe.
“Dziŵani zonse zimene mungadziŵe ponena za matenda a wodwala wanu. Ndiyeno zimenezo zidzakuthandizani kudziŵa zimene mungayembekezere kuchitika kwa wodwala wanu ndi kwa inuyo ndi kudziŵa mmene mungasamalirire wodwala wanu.”—Joan, amene mwamuna wake ali ndi nthenda ya Alzheimer.
“Dziŵani kuti ena alimbana nazo inuyo musanatero ndi kuti Yehova angakuthandizeni kulimbana ndi zilizonse zimene zingachitike.”—Jeanny, amene anasamalira mwamuna wake asanamwalire.
[Chithunzi patsamba 8]
Kuti muchepetse mantha anu, dziŵani zonse zimene mungadziŵe ponena za matendawo
[Chithunzi patsamba 9]
Kulankhula ndi bwenzi lomvetsetsa kungadzetse mpumulo waukulu