Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 2/8 tsamba 10-13
  • Kusamala Wosamala Ena Mmene Ena Angathandizire

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusamala Wosamala Ena Mmene Ena Angathandizire
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Osamala Ena Amafuna Kulankhula
  • Kuwathandiza mwa Kuwachitira Zinthu
  • Apatseni Mpumulo
  • Kutha kwa Matenda Onse
  • Vuto la Kusamala Wina
    Galamukani!—1997
  • Mmene Mungachitire ndi Malingaliro
    Galamukani!—1997
  • Zimene Odwazika Matenda Angachite
    Galamukani!—1998
  • Kodi Achikulire Tingawasamalire Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 2/8 tsamba 10-13

Kusamala Wosamala Ena Mmene Ena Angathandizire

“INE ndi Lawrie takhala mu ukwati zaka 55—nthaŵi yaitali ndithu—ndipo mmene zakazo zakhalira zosangalatsa! Ngati kunali kotheka kumsunga panyumba, ndikanatero. Koma thanzi langa linayamba kuipa. Pomaliza, ndinapanga makonzedwe akuti apite kunyumba yosamala ofooka. Kuvutika kwanga mtima posimba zimenezi kumandikulira. Ndimamkonda ndi kumlemekeza kwambiri ndipo ndimakamuona nthaŵi zambiri. Thupi langa silikundilola kuchita zambiri.”—Anna, mkazi wazaka zakubadwa 78 amene kwa zaka zoposa 10 wasamala mwamuna wake wodwala nthenda ya Alzheimer ndiponso wasamala mwana wawo wamkazi pazaka 40 zapitazo amene ali ndi nthenda ya Down’s syndrome.a

Mkhalidwe wa Anna suuli wachilendo ayi. Zofufuza ku British Isles zinasonyeza kuti “pakati pa amisinkhu yakutiyakuti (a m’ma 40 ndi ma 50) mkazi mmodzi aliyense mwa aŵiri amasamala ena.” Monga momwe tatchulirapo kale, kuvutika mtima ndi zothetsa nzeru zimene osamala ena amakhala nazo zingakhale zosapiririka nthaŵi zina.

“Ndikhulupirira kuti 50% ya osamala ena amachita tondovi chaka chawo choyamba chosamala ena,” akutero Dr. Fredrick Sherman, wa American Geriatrics Society. Zinthu zimakhala zovuta kwambiri kwa okalamba onga Anna chifukwa cha nyonga yawo yomachepayo ndi thanzi lawo lomaipiraipira.

Kuti tithandize osamala ena kukwanitsa mathayo awo, tiyenera kuzindikira zofuna zawo. Kodi zofuna zawozo nzotani, ndipo tingazipereke motani?

Osamala Ena Amafuna Kulankhula

“Ndinafuna kutula mtolo wanga,” anatero mkazi wina yemwe anathandiza kusamala mnzake asanafe. Monga momwe nkhani yatha yasonyezera, kukhala ndi mavuto ndi kulimbana nawo kumakhala kofeŵa pamene ukambitsirana mavutowo ndi mnzako womvetsa. Ambiri osamala ena amene amadzimva opanikizika ndi mikhalidwe yawo amapeza kuti kulankhula za mkhalidwe wawo kumawathandiza kumveketsa malingaliro awo ndi kufeŵetsa kupanikizika kwawo kwakukuluko.

“Ndinayamikira kwambiri pamene anzathu anazindikira kuti aŵirife tinafunikira kutilimbikitsa,” Jeanny akukumbukira nthaŵi pamene anali kusamala mwamuna wake. Akufotokoza kuti wosamala ena amafuna kumlimbikitsa ndipo, nthaŵi zina, munthu womdandaulira. Hjalmar, amene anathandiza kudwazika mlamu wake, akuvomereza: “Ndinafunikira munthu amene akanamvetsera nkhaŵa zanga ndi zothetsa nzeru ndi kumvetsa mmene ndinkamveramo.” Ponena za bwenzi lapamtima, Hjalmar akuwonjeza kuti: “Kumchezera kunali kosangalatsa kwambiri, ngakhale theka la ola lokha. Anali kundimvetsera. Analidi kusamala. Pambuyo pake ndinali kumva bwino.”

Womvetsera wachifundo angalimbikitse kwambiri osamala ena. Baibulo limalangiza mwanzeru kuti: ‘Mukhale otchera khutu, odekha polankhula.’ (Yakobo 1:19) Lipoti mu The Journals of Gerontology linasonyeza kuti “kungodziŵa kuti alipo okuchirikiza kumatokwanira kukupatsa mpumulo.”

Komabe, kuwonjeza pa kuwamvetsera ndi kuwalimbikitsa, kodi nchiyaninso chimene osamala ena amafuna?

Kuwathandiza mwa Kuwachitira Zinthu

“Wodwala ndi banja lomwe amapindula ndi njira iliyonse imene chikondi ndi chilimbikitso chingasonyezedwere,” akutero Dr. Ernest Rosenbaum. Choyamba, “chikondi ndi chilimbikitso” chimenecho chingasonyezedwe pokawaona, pokambitsirana nawo patelefoni, kapena m’kalata yachidule (mwinamwake yopitira limodzi ndi maluŵa kapena mphatso ina).

“Pamene anzathu anabwera kudzationa kwa nthaŵi yochepa, zinatitonthoza,” Sue akukumbukira mmene ena anachirikizira banja lawo atate wake asanafe ndi nthenda ya Hodgkin. “Mzanga wina,” akupitiriza, “anali kuyankha mafoni ndi kutithandiza kuchapa ndi kutisitira zovala ife tonse.”

Kuchirikiza osamala ena kungaphatikizepo, ndipo kuyenera kuphatikizapo, thandizo lakutilakuti looneka. Elsa akukumbukira kuti: “Zinathandiza kwambiri pamene anzanga anachita zinthu zothandiza. Sanangonena kuti: ‘Ngati pali zimene ndingachite, udzandiuze.’ M’malo mwake, anati: ‘Ndikupita kukagula zinthu. Ndikubweretsere chiyani?’ ‘Kodi ndingasamalire maluŵa anu?’ ‘Ndingakhale ndi wodwala ndi kumuŵerengera.’ Chinanso chimene chinathandiza ndicho kulinganiza kuti alendo azisiya atalemba mauthenga m’buku pamene mzanga wodwalayo anali wotopa kapena anali mtulo. Zimenezo zinatisangalatsa kwambiri tonsefe.”

Thandizo limene mungafune kupereka lingaphatikizepo ntchito zingapo zilizonse. Rose akufotokoza kuti: “Ndinayamikira kwambiri thandizo loyala mbedi, kulemba makalata a wodwala, kucheza ndi alendo a wodwalayo, kugula mankhwala, kuchapa ndi kukonza tsitsi lake, kutsuka mbale.” Banja ndi mabwenzi angathandizenso wosamala enayo mwa kusinthana kukonza chakudya.

Pamene zili zoyenera, kungakhalenso kothandiza kuchita mbali zina zosamalira wodwala. Mwachitsanzo, wosamala enayo angafunikire kumthandiza kudyetsa wodwalayo kapena kumsambika.

Achibale ndi anzake angathandize mwa kuchita zinthu nthendayo itangoyamba, koma bwanji ngati nthendayo itenga nthaŵi yaitali? Potanganidwa ndi ntchito zathu zochuluka, tinganyalanyaze msanga zimene zilipo—ndipo mwinamwake—kupanikizika kumene osamala ena amakhala nako. Zingakhale zachisoni chotani nanga ngati chichirikizo chofunika koposa chiyamba kuchepa!

Zimenezo zitachitika, kungakhale kwanzeru kuti wosamala enayo aitanitse msonkhano wa banja wokambitsirana zosamalira wodwalayo. Nthaŵi zambiri zimatheka kupempha thandizo kwa mabwenzi ndi achibale omwe asonyeza kuti ali okonzeka kuthandiza. Sue ndi banja lawo anachita zimenezo. “Pamene thandizo linafunika,” akutero, “tinakumbukira aja amene analonjeza kuti adzatithandiza ndi kuwaimbira foni. Tinaganiza kuti tikanatha kuwapempha thandizo.”

Apatseni Mpumulo

“Nzofunika kwambiri,” likutero buku lakuti The 36-Hour Day, “kwa inu [wosamala mnzanu] ndi kwa [wodwala wanu]—kuti muzikhala ndi nthaŵi masiku onse ‘yopuma’ pantchito yausana ndi usiku yosamala munthu wodwala matenda osatha. . . . Kupuma pantchito yosamala [wodwala] ndiko chimodzi cha zinthu zimene mungachite zofunika koposa kuti mukhoze kupitiriza kusamala wina.” Kodi osamala ena akuvomereza?

“Nzoona,” akuyankha Maria, amene anathandiza kusamala mnzake wapamtima asanafe ndi kansa. “Nthaŵi ndi nthaŵi, ndinafuna ‘kumasuka m’goli’ ndi kuti wina amsamale kwa kanthaŵi.” Joan, amene amasamala mwamuna wake wodwala nthenda ya Alzheimer, akuvomerezana nazo zimenezo. “Zinthu zimene timafuna koposa,” akutero, “zimaphatikizapo kukhala ndi nthaŵi yopuma kaŵirikaŵiri.”

Nanga angaipeze bwanji nthaŵi yopuma pamene mathayo awo ali opanikiza? Jennifer, amene anathandiza kusamala makolo ake okalamba, akusonyeza mmene anapezera mpumulo: “Nthaŵi zina mnzathu ankatenga amayi tsiku lonse kuti ife tipumeko.”

Mungampatse mpumulo wosamala ena mwa kudzipereka kutenga wodwalayo kwa kanthaŵi, ngati zimenezo zitheka. Joan akuti: “Zimanditsitsimula pamene wina nthaŵi zina atenga mwamuna wanga ndi kupita naye kuti ndikhale ndekha kanthaŵi.” Komanso, mukhoza kucheza ndi wodwalayo kunyumba kwake. Kaya ndi ziti zimene mungachite, perekani mpata wakuti wosamala mnzake apeze mpumulo umene amafuna kwambiri.

Koma kumbukirani kuti nthaŵi zina zimawavuta osamala ena kuti achokepo ndi kukapuma. Angadzimve aliwongo pokhala kutali ndi wokondedwa wawo. “Si kwapafupi kumsiya ndi kukasanguluka kapena kukapuma,” akuvomereza Hjalmar. “Ndinaganiza kuti ndinafunikira kukhala naye nthaŵi zonse.” Koma maganizo ake anakhala pamtendere kwambiri mwa kupuma pamene mlamu wake anafunikira chisamaliro chochepa. Ena alinganiza kuti wokondedwa wawo asamalidwe kwa maola oŵerengeka kunyumba zosamala okalamba.

Kutha kwa Matenda Onse

Kunena zoona, kusamala wokondedwa amene akudwala kwambiri ndi ntchito yovuta. Komabe, kusamala wokondedwa wanu kungakhale kokhutiritsa kwambiri. Ofufuza ndiponso osamala ena amati maunansi m’banja ndiponso ndi mabwenzi amalimba. Nthaŵi zonse, osamala ena amaphunzira mikhalidwe ndi maluso atsopano. Ambiri amapezanso mapindu auzimu.

Chofunika koposa, Baibulo limasonyeza kuti Yehova ndi Mwana wake, Yesu Kristu, ali achifundo koposa posamala ena. Ulosi wa Baibulo umatitsimikiza kuti matenda onse, mavuto, ndi imfa zidzatha posachedwa. Posachedwa, Mlengi wa anthu wosamala adzafupa olungama okhala padziko lapansi ndi moyo wosatha m’dziko latsopano lathanzi langwiro—limene “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:4.

[Mawu a M’munsi]

a Maina ena m’nkhani ino asinthidwa.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Ubwino wa munthu wodwala umayenderana ndi ubwino wanu

[Mawu Otsindika patsamba 12]

Chichirikizo cha mabwenzi abwino chidzakuthandizani kwambiri kupirira nthaŵi zovuta koposa

[Bokosi patsamba 12]

Kusamala Ena Kungakhale Kofupa

‘KOFUPA?’ ena angafunse. ‘Zimenezo zitheka bwanji?’ Chonde tamverani zimene osamala enawa anauza Galamukani!:

“Kudzimana zimene ukonda ndi zimene ufuna sikumakulanda chimwemwe chako. ‘Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.’ (Machitidwe 20:35) Kusamala wina amene umakonda kungakhale kokhutiritsa kwambiri.”​—⁠Joan.

“Ndinakondwera kwambiri kuti ndinatha kuthandiza mlongo wanga ndi mlamu wanga pamene anafuna thandizo kwambiri​—⁠popanda iwo kundilipira. Zinatigwirizanitsa kwambiri. Ndikhulupirira tsiku lina ndidzagwiritsira ntchito chidziŵitso chimene ndapeza kuthandiza wina amene adzakhala mumkhalidwe wonga umenewo.”​—⁠Hjalmar.

“Malinga ndi zimene nthaŵi zambiri ndinkauza mnzanga wodwalayo Betty, zimene ndinalandira zinaposeratu zimene ndinapereka. Ndinaphunzira chifundo ndi kuleza mtima. Ndinaphunzira kuti zitheka kukhalabe wosasokonezeka maganizo m’mikhalidwe yovutitsa.”​—⁠Elsa.

“Ndinakhala munthu wolimba kwambiri. Ndinadziŵa bwino lomwe tanthauzo la kudalira Yehova Mulungu masiku onse ndi kumlola kundipatsa zofuna ­zanga.”​—⁠Jeanny.

[Bokosi patsamba 13]

Pocheza ndi Wosamala Ena

• Mvetserani mwachifundo

• Myamikireni kuchokera mumtima

• Perekani thandizo lotsimikizika

[Zithunzi patsamba 10]

Chirikizani osamala ena mwa kuwagulira zinthu ndi kuwaphikira kapena mwa kuwathandiza kusamala wodwala

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena