Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 5/8 tsamba 31
  • Ŵerengerani Mtengo wa Kusamuka!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ŵerengerani Mtengo wa Kusamuka!
  • Galamukani!—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nchifukwa Ninji Tiyenera Kusamuka?
    Galamukani!—1994
  • Alendo—Kodi Amasamukiranji?
    Galamukani!—1992
  • Kodi ‘Mungawolokere ku Makedoniya’?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Alendo—Vuto la Dziko Lonse
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 5/8 tsamba 31

Ŵerengerani Mtengo wa Kusamuka!

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU SOUTH AFRICA

KODI mukuganiza zosamukira ku dziko lina? Kodi mwaŵerengera mtengo wake? Sitikutanthauza kuŵerengera ndalama chabe. Ndiponso, anthu ambiri amasamuka ncholinga chakuti akapeze chuma. Tikutanthauza mtengo womwe umakadziŵika pokhapokha mutasamuka. Panthaŵi imeneyi kaŵirikaŵiri zimakhala zosatheka kuti mubwerere kwanu. Mfundo zotsatirazi sizinalembedwe ncholinga chokuopsezani, koma nzoyenera kuzilingalira:

“Pamafunikira kudzichepetsa ndiponso khama kuti muphunzire chilankhulo chatsopano. Nzogwetsa mphwayi kwa munthu wamkulu kuona kuti ndi ana omwe akumuona monga wosokonezeka chifukwa choti sali kumva zimene akulankhula. Ambiri amaona ngati akuyesedwa pa kudzichepetsa kwawo chifukwa cholakwitsalakwitsa polankhula ndiye nkumasekedwa mosalekeza chifukwa cha zophophonya zawozo. Alendo amene sangathe kulankhula chilankhulo cha kumaloko amakhala osungulumwa kwambiri.”—Rosemary, mmishonale ku Japan.

Mwinamwake mukudzimva kuti mumadziŵako ndithu chilankhulocho kwakuti mutha kumakamvana ndi anthu. Koma kodi mukutsimikiza kuti banja lanu lonse limachidziŵa chilankhulocho kwakuti lingakonde kusamuka?

Ngati ena a m’banjamo achita kuŵanyengerera kuti asamuke pamene iwo sanafune, kodi muganiza kuti zidzalikhudza motani banjalo? “Azimayi ena [a ku Mexico],” ikutero nyuzipepala ya Psychology of Women Quarterly, “sananenepo chilichonse pa za lingaliro losamuka ndipo sanafune nkomwe kusamuka, ndiponso sanafune kupitiriza kumakhala ku United States atasamuka.” Zitakhala motero, kusamuka kochita kukakamiza kungawononge mgwirizano wa banja. Koma bwanji ngati mwamuna asamuka yekha?

M’buku lakuti Population, Migration, and Urbanization in Africa linanena za chiŵerengero choyerekezera kuti m’dziko lina laling’ono la kummwera kwa Afirika lomwe mulibe matauni ambiri, “azibambo amachoka pakhomo kwa nthaŵi yakutiyakuti,” ndipo ameneŵa amakhala oposa 50 peresenti. Kuchokapo kumeneku kumawononga mtendere ndi bata za banja. Ndiponso zimenezi zimapereka mpata waukulu wakuti mmodzi wa okwatiranawo akhoza kuchita chisembwere. Zimakhala bwino chotani nanga kuti banja, kaya liganiza zosamuka kapena ayi, likhalirebe limodzi! Umodzi wa banja ndi chinthu chimene sumungagule ndi ndalama.

Ndiye, pali ntchito ina yoŵaŵa yolimbana ndi tsankho. “Nditafika ku England mpamene ndinazindikira kuti kuli ‘tsankho,’” akukumbukira tero Mmwenye wina yemwe anasamuka. “[Kuzindikira] zimenezi kunandiŵaŵa. Zinandikhumudwitsa. Ndinafuna kubwerera kwathu, kuti ndithawe zimenezi.”—The Un-melting Pot.

Choncho musananyamuke, dzifunseni kuti: ‘Kodi palibe njira ina yomwe ndingachitire? Kodi sitingasinthe zinthu tili kwathu konkuno? Kodi kusamukira kudziko lina nkoyenereradi?’ Kusamuka kungakhale kapenanso sikungakhale koyenera, koma musanagamule, lingalirani za mawu a Yesu: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, naŵerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza?”—Luka 14:28.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena