Zimenezo Anazitcha Zosangulutsa
M’BWALO la maseŵero munadzala chisangalalo chadzaoneni. Anthu zikwi makumi ambiri anasonkhana kuti aonerere chimodzi cha zochitika zochititsa nthumanzi kwambiri m’Roma wakale. Mbendera, maluŵa, ndi nsalu zamisoko yochititsa kaso zinakongoletsa malo oseŵererapo. Panali akasupe otulutsa madzi onunkhira, onunkhiritsa mphepo ndi fungo lokoma. Achuma anavala zovala zawo zamtengo wapatali koposa. Mkati mwa phokoso la chisangalalo cha anthuwo, mumamveka kuseka kwambiri, koma kukondwa kwa khamulo kunabisa zoopsa zomwe zinali pafupi kuchitika.
Posapita nthaŵi lipenga lodzetsa tsoka lotchedwa tubæ linaomba, kuitana aŵiri ochita maseŵero omenyana mpaka wina atafa. Khamulo linachita nthumanzi pamene omenyanawo anayamba kugwazana mopanda chifundo. Kuombana kwa malupangawo sikunamveke chifukwa cha kuchemerera kogonthetsa m’makutu kwa openyererawo. Mwadzidzidzi, mmodzi wa olimbanawo anagwetsera pansi mnzake pomkantha mwamphamvu. Tsopano moyo wa wogwetsedwayo unali m’manja mwa openyererawo. Ngati iwo akupiza nsalu zawo zakumanja, ndiye kuti sadzamupha. Koma ngati atukula zala zawo zamanthu, ndiye kuti khamulo—kuphatikizapo akazi ndi atsikana—analamula kuti amtsiriziretu. Posachedwa, anaduduluza mtembowo kuuchotsa poseŵererapo, dothi lokhathamira ndi mwazi analifotsera ndi mafosholo, nawazapo mchenga watsopano, khamulo nilikonzeka likumayembekeza kuona ena omwe adzaphedwa.
Kwa ambiri okhala m’Roma wakale, zimenezo zinali zosangulutsa. Buku lakuti Rome: The First Thousand Years limati: “Ngakhale ochirikiza kwambiri makhalidwe abwino sanatsutse mpang’ono pomwe chisangalalo chimenechi chokhetsa mwazi.” Ndipo maseŵero ophana amenewo anali mtundu umodzi chabe wa zosangulutsa zoipa za m’Roma. Nkhondo zenizeni zapamadzi zinachitikanso monga maseŵero osangalatsa openyerera a ludzu la mwazi. Ngakhale kunyonga anthu poyera kunachitika, pamene mpandu woweruzidwa kuti aphedwe anamangidwa pamtengo nadyedwa ndi zilombo zanjala.
Kwa aja osakonda kuona imfa ya munthu, analipo maseŵero ena kwa iwo mu Roma. Pamaseŵero osalankhula—maseŵero aafupi chabe osonyeza zochitika za moyo wa tsiku ndi tsiku—“chigololo ndi chisembwere ndizo zinali mitu yaikulu ya maseŵerowo,” analemba motero Ludwig Friedländer m’buku lakuti Roman Life and Manners Under the Early Empire. “Chinenero chake chinali cha zotukwana, ndipo zoseketsa zinali zonyazitsa, kuyang’ana ndi diso la nkhwezule, majesichala otukwana, ndi mavinidwe onyanyula poimba chitolilo.” Malinga ndi kunena kwa The New Encyclopædia Britannica, “pali umboni wakuti machitidwe achisembwere anachitikadi pamaseŵero osalankhula pamalo oseŵerera m’nthaŵi ya Ufumu wa Roma.” Ndi chifukwa chomveka, Friedländer akunena kuti maseŵero osalankhula anali “maseŵero onyansa koposa pamaseŵero achisembwere ndi a zonyansa,” nawonjezera kuti: “Zionetsero zoipitsitsa ndizo zinali zosangalatsa koposa.”a
Nanga bwanji lero? Kodi mtundu wa zosangulutsa za munthu wasintha? Onani umboni wofotokozedwa m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Nthaŵi zina, anali kunyonga munthu pamalo oseŵererapo kuti seŵero lioneke lenileni. Buku lakuti The Civilization of Rome limati: “Sikunali kwachilendo kuona mpandu woweruzidwa kuti aphedwe akutenga mbali m’seŵero panthaŵi ya kuphedwa kwake.”
[Chithunzi patsamba 17]
The Complete Encyclopedia of Illustration/J. G. Heck