Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 6/8 tsamba 22-24
  • Mukhoza Kupeza Zosangulutsa Zabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mukhoza Kupeza Zosangulutsa Zabwino
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Muzisankha
  • Ntchito ya Makolo
  • Sangalalani ndi Zochita Zinanso
  • Kodi Mungasankhe Bwanji Zosangalatsa Zabwino?
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Muzisankha Zosangalatsa Zomwe Sizingakhumudwitse Yehova
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Tingasankhe Bwanji Zosangalatsa?
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Kodi Mumasankha Zosangalatsa Mwanzeru?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 6/8 tsamba 22-24

Mukhoza Kupeza Zosangulutsa Zabwino

BAIBULO silimaletsa kusangalala ndi zosangulutsa, ndipo silimanena kuti kukondwera ndi zosangulutsa ndi kutaya chabe nthaŵi. M’malo mwake, Mlaliki 3:4 amanena kuti pali “mphindi yakuseka” ndi “mphindi yakuvina.”a Anthu a Mulungu m’Israyeli wakale anasangalala ndi zosangulutsa zosiyanasiyana, kuphatikizapo nyimbo, kuvina, ndi maseŵero. Yesu iye mwini anapezeka pa madyerero aakulu aukwati, ndipo nthaŵi ina pa “phwando lalikulu.” (Luka 5:29; Yohane 2:1, 2) Choncho Baibulo silimaletsa kukhala ndi nthaŵi ya kusangalala.

Komabe, pakuti zosangulutsa zambiri za lero zimatamanda makhalidwe osakondweretsa Mulungu, pamakhala funso lakuti, Kodi mungachitenji pofuna kutsimikiza kuti zosangulutsa zimene musankha zili zoyenera?

Muzisankha

Posankha zosangulutsa zawo, Akristu ayenera kutsatira mapulinsipulo a Baibulo. Mwachitsanzo, wamasalmo Davide analemba kuti: “Yehova ayesa wolungama mtima: koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.” (Salmo 11:5) Ndipo Paulo analembera Akolose kuti: “Chifukwa chake fetsani ziŵalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, . . . tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka mkamwa mwanu.”—Akolose 3:5, 8.

Zosangulutsa zambiri zomwe zilipo lero zimasemphana kotheratu ndi uphungu wouziridwa umenewu. ‘Koma sindingachite zinthu zomwe ndimaona m’kanema,’ ena angatero. Zimenezo zingakhale zoona. Koma ngakhale ngati zosangulutsa zimene mukonda sizingasonyeze mtundu wa munthu amene mudzakhala, zingasonyeze kanthu kena ponena za munthu amene muli kale. Mwachitsanzo, zingasonyeze ngati muli pakati pa aja ‘okonda chiwawa’ kapena olingalira za ‘dama, chilakolako choipa, chisiriro, ndi kulankhula zonyansa’ kapena ngati muli pakati pa aja amene ‘amadanadi nacho choipa.’—Salmo 97:10.

Paulo anati polembera Afilipi: “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.”—Afilipi 4:8.

Koma kodi lemba limeneli limatanthauza kuti filimu iliyonse, buku, kapena kanema ya pa TV mmene nkhani yake imaphatikizapo chisalungamo, kapena upandu, basi ndi yoipa? Kapena kodi nkhani zonse zanthabwala nzosafunika chifukwa sizili “zolemekezeka”? Ayi, pakuti nkhaniyo imasonyeza kuti Paulo sanali kulankhula za zosangulutsa koma kusinkhasinkha kwa mumtima, kumene kuyenera kusumika pazinthu zimene zimakondweretsa Yehova. (Salmo 19:14) Komabe, zimene Paulo ananena zingatithandize posankha zosangulutsa. Pogwiritsira ntchito chilangizo cha pa Afilipi 4:8, tingadzifunse kuti, ‘Kodi zosangulutsa zomwe ndimakonda zimandichititsa kulingalira zinthu zodetsedwa?’ Ngati zili choncho, pamenepo tiyenera kusintha.

Komabe, posankha zosangulutsa, Akristu ayenera kuona kuti ‘kufatsa kwawo kuzindikirike kwa anthu onse.’ (Afilipi 4:5) Mwachionekere, zilipo zosangulutsa zina zonyanya zosayenera kwa Akristu oona. Komanso, munthu aliyense ayenera kupenda zinthu mosamalitsa ndi kusankha zimene zidzamkhalitsa ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Mulungu ndi munthu. (1 Akorinto 10:31-33; 1 Petro 3:21) Sikungakhale koyenera kuweruza ena pazinthu zazing’ono kapena kuika malamulo athu ouza ena zimene ayenera kuchita.b—Aroma 14:4; 1 Akorinto 4:6.

Ntchito ya Makolo

Makolo ali ndi ntchito yaikulu kwambiri pankhani ya zosangulutsa. Paulo analemba kuti: “Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.” (1 Timoteo 5:8) Choncho, makolo ali ndi udindo wodzisungira a m’banja lawo, si mwakuthupi chabe komanso mwauzimu ndi mwamaganizo. Zimenezi zikuphatikizapo kulinganiza nthaŵi yabwino yakupuma.—Miyambo 24:27.

Nthaŵi zina mbali imeneyi ya moyo wa banja imanyalanyazidwa. Mmishonale wina ku Nigeria anati: “Mwa tsoka lake, makolo ena amaona zosangulutsa kukhala kungotaya nthaŵi. Chifukwa cha zimenezo, ana ena amangodzifunira okha zosangulutsa, choncho amapeza mabwenzi ndi maseŵera osayenera.” Makolo, musalole zimenezi kuchitika! Pezerani ana anu zosangulutsa zowatsitsimuladi.

Koma tiyenera kupereka chenjezo pano. Akristu sayenera kukhala ngati anthu ambiri lero amene ali “okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” (2 Timoteo 3:1-4) Inde, zosangulutsa ziyenera kusungidwa m’malo ake. Ziyenera kukhala zotsitsimula—osati zolamulira moyo wa munthu. Chotero ana limodzinso ndi achikulire sangofunikira mtundu woyenera wa zosangulutsa komanso mlingo woyenera.—Aefeso 5:15, 16.

Sangalalani ndi Zochita Zinanso

Zosangulutsa zotchuka zambiri zimaphunzitsa anthu kungokhala osachita kanthu m’malo mochitako kanthu kena. Mwachitsanzo, talingalirani za wailesi yakanema. Buku lakuti What to Do After You Turn Off the TV limati: “Mmene yakhalira [wailesi yakanema] imatiphunzitsa kungokhala osachita kanthu: Kusanguluka, ndipo ngakhale kuphunzira, timakulandira popanda kuchitapo kalikonse, sitimagwiritsira ntchito luso lathu.” Inde, zilipo zosangulutsa zina zongokhala osachitapo kanthu, koma zoyenera. Komabe ngati zitenga nthaŵi yaikulu kwambiri, zimamana munthu mpata wa zochita zina zosangalatsa.

Mlembi wina Jerry Mander, yemwe akunena kuti “anakulira m’nthaŵi yakale TV isanakhaleko,” akulongosola nthaŵi zina pamene ankasungulumwa paubwana wake: “Ndinaderanso nkhaŵa kwambiri,” akutero. “Kunali konyong’onya kwambiri, kosautsa moti potsirizira pake ndinkaganiza zochita kanthu kena. Ndinkaimbira anzanga foni, ndinkachoka panyumba kukawongola miyendo. Ndinkapita kukaseŵera mpira. Ndinkaŵerenga. Ndinkachita kanthu kena. Ndikakumbukira, ndimaona kuti nthaŵi yakusungulumwayo, ‘yosoŵa chochita,’ inali mpata wondisonkhezera kuchita zinthu zopindulitsa.” Lero, Mander akunena kuti, ana amagwiritsira ntchito TV monga mankhwala apafupi othetsera kusungulumwa. “TV imathetsa zonse ziŵiri nkhaŵa ndi chifuno chochita kanthu kena kothandiza,” anatero.

Motero, ambiri aona kuti zosangulutsa zofuna wina kuchita kanthu kena m’malo mwa kungokhala chabe zingakhale zopindulitsa kwambiri kuposa ndi mmene ankaganizira. Ena apeza kuti kuŵerenga mofuula limodzi ndi ena kumapatsa chisangalalo. Ena amachita zinthu zapamtima, monga kuliza choimbira kapena kulemba zithunzi. Ndiyeno pali mipata ina yolinganiza macheza oyenera.c (Luka 14:12-14) Zosangulutsa zokachitira kwina nazonso zimapindulitsa. Mtolankhani wa Galamukani! ku Sweden analemba kuti: “Mabanja ena amapita ku kampu kapena kukaŵeza nsomba kapena kukacheza kutchire, kupita paulendo wa m’bwato, kukayendayenda m’mapiri, ndi zina zotero. Ana amasangalala kwabasi.”

Sitiyenera kudabwa poona zinthu zoipa m’zosangulutsa. Mtumwi Paulo analemba kuti anthu a mitundu “angoyenda, m’chitsiru cha mtima wawo.” (Aefeso 4:17) Chifukwa chake, nzosadabwitsa kuona kuti zambiri zimene amaona kukhala zosangalatsa zimangothandiza pa “ntchito za thupi.” (Agalatiya 5:19-21) Komabe, Akristu akhoza kudziphunzitsa kusankha bwino mtundu ndi mlingo wa zosangulutsa. Akhozanso kulinganiza zokondweretsa pamodzi monga banja ndipo angayesenso kuchita zinthu zatsopano zimene zingakhale zotsitsimula ndi zokumbutsa nthaŵi zabwino m’zaka zamtsogolo. Inde, mukhoza kupeza zosangulutsa zoyenera!

[Mawu a M’munsi]

a Mawu ena achihebri otembenuzidwa kuti “kuseka” angatembenuzidwe kuti “kuseŵera,” “kuseketsa,” “kukondwerera,” kapena “kusangalala.”

b Kuti mumve zambiri, onani makope achingelezi a Galamukani! a March 22, 1978, masamba 16-21, ndi December 8, 1995, masamba 6-8.

c Kuti mupeze zitsogozo za m’Malemba pamacheza, onani Nsanja ya Olonda ya August 15, 1992, masamba 15-20, ndi ya October 1, 1996, masamba 18-19.

[Chithunzi patsamba 23]

Zosangulutsa zoyenera zingakhale zopindulitsa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena