Mboni za Yehova ku Russia
Lingaliro la Katswiri wa Zaumulungu
KU Roma, atsogoleri a Ayuda m’zaka za zana loyamba anati ponena za Chikristu: “Za mpatuko uwu, tidziŵa kuti aunenera ponse ponse.” Kodi atsogoleri amenewo anatani? Moyamikirika, anapita kwa mtumwi Paulo, amene nthaŵiyo anali atambindikiritsa m’nyumba, nati: “Tifuna kumva mutiuze muganiza chiyani.” (Machitidwe 28:22) Iwo anamvetsera kwa Mkristu wachidziŵitso osati kwa aja amene ankalankhula motsutsa Chikristu.
Sergei Ivanenko, katswiri wa zaumulungu wodziŵika bwino wa ku Russia, anachitanso mofananamo. Ngakhale anakhulupirira nkhani zoipa zambiri zimene zinali kufalitsidwa m’Russia zonena za Mboni za Yehova, anaganiza zoimbira foni ofesi yanthambi ya Mboni yomwe ili pafupi ndi St. Petersburg, kuti apeze chidziŵitso. Analandira chiitano choti akacheze kumeneko, kufunsa mafunso, ndi kudzionera okha Mbonizo.
Pamene a Ivanenko anafika mu October 1996, nyumbazo zimene muli mamembala anthambi pafupifupi 200 a Mboni za Yehova m’Russia zinali pafupi kumalizidwa. Kwa masiku atatu otsatira, iwo anapatsidwa mwaŵi woona malo omangawo, kudya zakudya m’chipinda chodyera, ndi kufunsa aliyense omwe anakonda.
Nkhani yonena za Mboni imene a Ivanenko analemba inafalitsidwa m’nyuzipepala yachirasha yotchuka ya mlungu ndi mlungu ya Moscow News ya February 16-23, 1997. Nkhaniyo, yamutu wakuti “Kodi Mboni za Yehova Tiyenera Kuziopa?,” inatulukanso m’kope lachingelezi la Moscow News, la February 20-26. Popeza oŵerenga Galamukani! ambiri amafuna kwambiri kudziŵa zochita za Mboni za Yehova ku Russia, panopa tatulutsanso mbali yaikulu ya nkhaniyo, ndi chilolezo. A Ivanenko anayamba ndi chokumana nacho chotsatirachi chimene chinalembedwa m’zilembo zazikulu:
“‘Ampatuko, chokani m’Russia!’ chinalembedwa motero chikwangwani chimene a chipani cha Zhirinovsky cha LDPR ananyamula kuchita chisonyezero chotsutsa msonkhano wa Mboni za Yehova. ‘Kodi gululi mumalideranji?’ Ndinafunsa mmodzi wa ochita chisonyezerowo. Anandipatsa kope la Megapolis-Express lokhala ndi mutu wakuti ‘Mliri wa Chindoko Chachipembedzo ku Kamchatka.’ Nyuzipepalayo inanena kuti Mboni za Yehova zinali kupezera mahule makasitomala ndipo zinali ndi magulu a mahule kuti zipezere gulu lawo ndalama, choncho zinali kufalitsa matenda opatsirana mwa kugonana pakati pa amalinyero. ‘Kodi inunso zinakuchitikirani?’ Ndinafunsa mwachifundo, ‘Kodi mukuzikhulupirira nkhanizi?’ ‘Zimenezo zilibe kanthu,’ anandiyankha motero. ‘Nkhani yaikulu njakuti gulu lampatuko lachimereka limeneli likuwononga mkhalidwe wauzimu ndi chikhalidwe cha Russia, ndipo tiyenera kuzithetsa.’”
Nkhani imene a Ivanenko analemba inatsatira pansi pa mzera wakuti: “Yolembedwa ndi Sergei Ivanenko, wamaphunziro a zachipembedzo, wophunzira filosofi.”
“Kuona mtima ngati kumeneku nkosoŵadi, ngakhale nzoona kuti Arasha ambiri samazikonda Mboni za Yehova. Kungotchula gulu limeneli kamodzi kokha kumachititsa anthu kulankhula za kuyaluka kwake kwangozi, za chiyambi chake cha ku America, za chikhulupiriro chakhungu cha mamembala wamba mwa atsogoleri a gululo, za chikhulupiriro chakuti dziko lili pafupi kutha, ndi zina zotero. Kwa ambiri, Mboni za Yehova zimachititsa mantha ndi nkhaŵa.
“Kodi Chipembedzochi Nchiyani, Ndipo Kodi Tiyenera Kuchiopa?
“Kuti ndidzidziŵire ndekha, ndinachezera mudzi wa Solnechnoye m’chigawo cha Kururtnoye, ku St. Petersburg, kumene kuli likulu loyang’anira Mboni za Yehova m’Russia.
***
“[Ameneŵa ali] pamene kale panali msasa wokhalapo m’chilimwe. Podzafika 1992 nyumba [yoyambayo] inali itawonongekeratu, ndipo m’malo mwa ana panali anthu ongoyenda peyupeyu ndi makoswe adzaoneni. Zikuoneka kuti chinali chifukwa cha kuwonongeka kwa malowo chimene chinathandiza Mboni za Yehova kulandira malo a mahekitala asanu ndi aŵiriwo kuti awagwiritsire ntchito kwautali wosadziŵika. Iwo anakonza nyumba zakalezo ndi kumanganso zina zatsopano, kuphatikizapo nyumba yosanjika katatu ya maofesi oyang’anira, [Nyumba ya Ufumu] yomwe mungakhale anthu 500, ndi nyumba yodyeramo. Mboni za Yehova zikubzalanso udzu watsopano (umene anaoda mwapadera ku Finland) ndi mitundu yosiyanasiyana ya mitengo yosapezekapezeka. Ntchitoyo akuti iyenera kutha chilimwe chikudzachi. Ntchito yaikulu ya likulu loyang’anira ndiyo kulinganiza ntchito yolalikira ndi kutumiza mabuku kumipingo ya Mboni za Yehova ya mommuno. Solnechnoye alibe makina akeake osindikizira, choncho mabuku achirasha amasindikizidwa ku Germany, ndi kutumizidwa ku St. Petersburg, kumene amawatumiza kumagawo osiyanasiyana. Pali antchito ngati 190 palikululi. Iwo amagwira ntchito modzifunira ndipo ngakhale samalandira malipiro, amapatsidwa zofunika zonse zazikulu, monga pokhala, zakudya, ndi zovala.
“Ntchito palikululo imatsogozedwa ndi komiti ya akulu 18. Vasily Kalin ndiye wakhala wogwirizanitsa likululo chiyambire 1992. Anabadwira ku Ivano-Frankovsk. Mu 1951, ali ndi zaka zinayi, iyeyo ndi makolo ake anawathamangitsira ku Siberia (mu 1949 ndi 1951 mabanja ngati 5,000 anazunzidwa ndi akuluakulu chifukwa chokhala Mboni za Yehova). Anabatizidwa mu 1965 ndi kukhala m’chigawo cha Irkutsk. Ankagwira ntchito yaukapitao pakampani yopanga matabwa.
“Kusiyapo antchito odzifunira a palikululi palinso antchito yomanga odzifunira 200 a m’Russia, ku Finland, Sweden ndi Norway omwe amakhala ku Solnechnoye: Ambiri a iwo anatenga livi pantchito zawo zolembedwa za nthaŵi zonse. Palinso Mboni za Yehova zambiri za ku Ukraine, Moldova, Germany, United States, Finland, Poland ndi maiko ena. (Mboni za Yehova zilibe tsankhu lautundu. Ngakhale kuti Ajojiya, Aabukhaziya, Aazebaijani ndi Aameniya amakhalira limodzi palikululo, sipanakhalepo ndewu nkamodzi komwe pazaka zinayi.)
“Milimo yambiri ndi ziŵiya zinachokera ku maiko a ku Scandinavia, ndipo zambirinso zinaperekedwa kwaulere ndi okhulupirira anzawo. Anandisonyeza galimoto lakatapila limene Mboni ya Yehova ina ya ku Sweden inabweretsa ku Solnechnoye mu 1993. Anagwira nalo ntchito nthaŵi yonse yomwe anali komweko, ndipo asanapite kwawo analipereka kwa abale ake a m’chikhulupiriro. Antchito yomanga amakhala m’nyumba zabwino za zipinda zambiri zogona. Tsiku lawo limakhala motere: 7:00 a.m.—mfisulo ndi mapemphero; amagwira ntchito kuyamba 8:00 a.m. mpaka 5:00 p.m. ndi ola limodzi lachakudya chamasana. Pa Loŵeruka amagwira ntchito mpaka nthaŵi yachakudya chamasana, ndipo Lamlungu ndi tsiku lopuma.
“Amadya bwino ndipo nthaŵi zonse pazakudya pamakhalanso zipatso. Chipembedzochi sichimasala kudya kwamtundu uliwonse kapena kusadya zakudya izi ndi izi. Ataŵeruka, ambiri amapita ku sauna ndiyeno amamwa moŵa ndi kungokhala phee kumvetsera nyimbo. Pakati pa Mboni za Yehova palibe zidakwa, komanso samaletsa kumwa moŵa. Okhulupirira amaloledwa kumwa vinyo, cognac, vodka ndi zina zotero mosapambanitsa. Komabe, Mboni za Yehova sizimasuta fodya.
***
“Katatu pamlungu kumakhala makalasi ophunzira Baibulo, amene nthaŵi zambiri amadzala ndi achinyamata. Komabe, aja amene akhala Mboni za Yehova zaka 30-40 nawonso amakhalapo nthaŵi zambiri. Pafupifupi achikulire onse akhalapo m’ndende, m’misasa yachibalo ndi m’ndende za maiko ena. Nyengo yopondereza itatha, madokotala, maloya, mainjiniya, aphunzitsi, amalonda, ndi ana a sukulu ambiri anakhala Mboni za Yehova.
“Mipingo imayesa kusunga mzimu wa kulingana pakati pa anthu ake. Mwachitsanzo, ngakhale wogwirizanitsa likulu loyang’anira amatsuka mbale madzulo ikafika nthaŵi yake. Mboni za Yehova zimaitanana maina ndipo zimawonjezeranso ‘mbale’ kapena ‘mlongo’ poitana wina ndi dzina lake.
“Mboni ya Yehova ikaswa ziphunzitso za Baibulo ndi kukana kulapa, imapatsidwa chilango chachikulu koposa—imachotsedwa. Munthuyo angamafikebe pamisonkhano, koma okhulupirira anzake samampatsanso moni. Chilango chopepukapo chimakhala chidzudzulo.
***
“Ndinathera nthaŵi yaitali kupenyerera Mboni za Yehova ndilikuyesa kuona chimene chinabweretsa anthu ambiri choncho osiyanasiyana ku gulu lachipembedzoli. Ndi kusiyana konseko kwa maumunthu awo, maphunziro awo ndi zokonda za aliyense, [Mboni za Yehova sizimaloŵerana pakulambira ndi] zipembedzo zimene zimagwirizana ndi dziko lauchimo. Sizimakondwera pamalo pamene [anthu] amangokhulupirira akuluakulu awo mwakhungu, pamene pali zachinsinsi, pamene anthu amasiyana pakati pa atsogoleri achipembedzo ndi makamu olabadira.
“Mboni za Yehova zimadziŵika ndi kukhulupirira kwawo zolimba kuti ziyenera kutsatira Baibulo. Zimayesa kuchirikiza zochita zawo zonse ndi pulinsipulo ili kapena lija la m’Baibulo, kapena mwa kugwira mawu ndime ina m’Chipangano Chakale kapena Chatsopano. Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti Baibulo lokhalo basi ndilo lili ndi mayankho a mafunso onse. Kwa Mboni za Yehova, Baibulo ndilo lamulo, mpambo wa mapulinsipulo ndi mafotokozedwe apamwamba koposa a choonadi.
“Pachifukwa chimenechi Mboni za Yehova zimadziŵika padziko lonse lapansi monga anthu omveradi malamulo motsimikizika ndipo makamaka pamzimu wawo wosamala kwambiri pankhani yokhoma misonkho. Nthaŵi zonse ofesi yoyang’anira zamisonkho imawayang’anira ndipo imadabwa nthaŵi zonse kupeza kuti palibe aliyense amene waswa lamulo. Eetu, Mboni za Yehova, monga ena ambiri, zikhoza kuyesa kupeza chifukwa chosakhomera misonkho, koma Baibulo limanena kuti munthu ayenera kukhala woona mtima pokhoma misonkho, ndipo kwa Mboni za Yehova lamulo lonse ndi limeneli.
“Komabe, mzimu wawo wosagonja pankhani za Baibulo kaŵirikaŵiri ndiwo umachititsa kusamvana kwakukulu pakati pa Mboni za Yehova ndi boma. Kusafuna kwawo mpang’ono pomwe kuloŵa m’ndale ndiko nkhani yaikulu yobutsa mkangano, ndipo kusafunaku kumaonekera pakukana kwawo kutumikira m’magulu ankhondo.
“Mboni za Yehova zimatenga mawu a Yesu monga alili onena za mmene ophunzira ake ndi ufumu wake sizili za mbali ya dzikoli, ndipo pachifukwa chimenechi zimakana kuloŵa m’ndale ndi m’nkhondo, kulikonse kumene zili ndipo kaya chifukwa choimenyera chikhale chotani. Chifukwa chakuti Mboni za Yehova zinakana kufuula kuti ‘Heil Hitler’ ndi kutumikira m’magulu ankhondo a Hitler, okhulupirira zikwi zambiri anatumizidwa ku misasa yachibalo ya Nazi, ndipo zikwi zambiri anafa. Mboni ya Yehova yachijeremani iliyonse yomwe inalipa moyo wake pokana kukhala ndi mbali poukira Soviet Union, imaonedwa ndi Arasha kukhala munthu amene anasonyeza khalidwe labwino lapamwamba. Komabe, nthaŵi imodzimodziyo, Arasha ambiri samachitira chifundo Mboni za Yehovazo [zachirasha] zimene zinanyongedwa chifukwa chokana kutenga zida ndi kuloŵa m’Nkhondo Yadziko II, kapena zimene zinatsutsidwa chifukwa chokana kutumikira m’gulu lankhondo panthaŵi zamtendere. Koma pazochitika zonse ziŵiri Mboni za Yehova zinali kutsatira zikhulupiriro zawo zachipembedzo ndipo osati zikhulupiriro zandale.
“Osati kale kwambiri vuto lofananalo linabuka ku Japan, kumene ana ena a sukulu amene anali Mboni za Yehova anakana kuphunzira maseŵera a nkhonya onga karate nakhala pangozi yochotsedwa pa yunivesite. Mu 1996 Bwalo Lapamwamba la Japan linapereka chigamulo chochirikiza zoyenera za ophunzira ameneŵa ndi kuwalola kutenga maphunziro ena.
***
“Kodi Mboni za Yehova zili nchiyani chimene chimazunguza mutu anthu oganiza kwambiri amakono? Kwenikweni ndi kulalikira kwawo kosaleka kwakuti mapeto a dziko ali pafupi (zimachita ntchito yaumishonale pamakwalala ndi kukhomo ndi khomo). Posachedwapa akulu alangiza olalikira kuti asamagogomezere kwambiri ‘mapeto a dziko’ ndi tsoka loopsa lodzagwera ochimwa, koma m’malo mwake kuti afotokoze kwa omvetsera kuti Yehova akuwapatsa mpata wokakhala ndi ‘moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi.’
“Nkhani ina yokwiyitsa anthu ndiyo mzimu wa Mboni za Yehova wosafuna kuyanjana ndi zipembedzo zina, ndi kukana kwawo kugwirizana ndi zipembedzo zonse za padziko lapansi. Zimakhulupirira kuti dziko lachikristu lakana Mulungu ndi Baibulo, ndi kuti zipembedzo zina zonse nzolakwika koopsa. Mboni za Yehova zimayerekezera zipembedzo zimenezi ndi ‘mkazi wachigololo wa Babulo,’ ndi kugogomezera kuti tsoka limodzimodzilo lidzazigwera. Kope laposachedwapa la ‘Galamukani!’ limanena kuti mapeto a zipembedzo zosiyanasiyana ali pafupi, ndi kuti chipembedzo chokha chimene chidzatsala ndi chija cholalikidwa ndi Mboni za Yehova.
“Komanso, Mboni za Yehova zimavomera kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wa chikumbumtima.
***
“Maiko angapo atchula kale zoti kaya ziphunzitso za Mboni za Yehova nzangozi kwa anthu kapena si zangozi. Bwalo Lapamwamba la boma la Connecticut, United States (1979) ndi New South Wales, Australia (1972), Provincial Court ya ku British Columbia, Canada (1986) ndi makhoti ena anena kuti palibe umboni wakuti Mboni za Yehova nzangozi pakakhalidwe ka anthu, kapena kuti nzangozi pathanzi la anthu kapena maganizo awo. Khoti la Zoyenera za Munthu la ku Ulaya (1993) linachirikiza choyenera cha Mboni za Yehova cha ufulu wachipembedzo, umene unali wochepa ku Greece ndi Austria. Lero, Mboni za Yehova zikuzunzidwa m’maiko 25 . . .
“Mboni za Yehova zingaonedwe kukhala chitsanzo kwa nzika zinzawo pakudzipereka kwawo pa choonadi cha Baibulo ndi kufunitsitsa kwawo kuchirikiza zikhulupiriro zawo mosadzikonda choncho. Koma pakudzuka funsoli: Kodi ifeyo tili okonzeka kupereka mwalamulo ufulu wachikumbumtima motsimikizika ku magulu amene amagwiritsira ntchito Baibulo pambali zonse za moyo m’njira yosiyana kwambiri imeneyi ndi yosagonja?”
M’chiganizo chomalizachi, a Ivanenko anadzutsa funso lofunika. M’zaka za zana loyamba, mtumwi Paulo, wosankhidwa mwachindunji ndi Kristu kuti atumikire monga womuimira, anavutika ndi “zomangira” zosalungama. Choncho, Paulo analembera okhulupirira anzake za kuyesayesa kwake ‘kudzikanira ndi kutsimikiza [kukhazikitsa mwalamulo, NW] uthenga wabwino.’—Afilipi 1:7; Machitidwe 9:3-16.
Lerolino Mboni za Yehova zikulandira onse kuti afufuze zochita zawo mosamalitsa, monga anachitira a Ivanenko. Tili ndi chidaliro chakuti anthu atachita zimenezo, adzapeza kuti nkhani zoipa zonena za Mboni za Yehova sizoona ayi, monga momwe malipoti onena za Akristu oyambirira sanalinso oona. Mosiyana ndi ena onse, Mboni zimalabadira “lamulo latsopano” limene Yesu anapatsa ophunzira ake: “Mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu.”—Yohane 13:34, 35.
[Bokosi patsamba 15]
Faelo ya MN
(Zotsatirazi za m’mafaelo a Moscow News zinasindikizidwa limodzi ndi nkhaniyi yolembedwa ndi Sergei Ivanenko.)
“Mboni za Yehova za m’Russia zili mbali ya gulu lapadziko lonse lachikristu limene lili m’maiko 233 ndipo lokhala ndi mamembala 5.4 miliyoni. Mboni za Yehova zimatsatira chitsogozo chauzimu cha Bungwe Lolamulira limene lili ku Brooklyn, New York. Gulu lamakono la Mboni za Yehova linayambira m’kalasi la ophunzira Baibulo lopangidwa mu 1870 ndi Charles Taze Russell ku Pittsburgh, Pennsylvania. Gululi linabwera ku Russia mu 1887. Mmodzi wa Mboni za Yehova zoyambirira m’Russia, Semyon Kozlitsky, anamthamangitsa ku Moscow kupita ku Siberia mu 1891. Mosasamala kanthu za chizunzo chimene gululi lapirira, mu 1956 m’Soviet Union munali Mboni za Yehova 17,000. Mboni za Yehova m’Russia zinadzadziŵika m’March 1991, lamulo ‘La Ufulu Wachipembedzo’ litaperekedwa. Lerolino, pali magulu oposa 500 ndi mamembala ngati 70,000 okangalika m’Russia. Gululi limafalitsa makope a ‘Nsanja ya Olonda’ (yofalitsidwa m’zinenero 125, yosindikizidwa makope 20 miliyoni) ndi ‘Galamukani!’ (m’zinenero 81, kusindikizidwa makope 18 miliyoni).”
[Chithunzi patsamba 15]
Mbali ya nyumba za ofesi yanthambi mu Russia
[Chithunzi patsamba 16]
Nyumba ya Ufumu mmene banja la panthambi limakumanira pochita phunziro la Baibulo
[Chithunzi patsamba 17]
Mabanja a Mboni amaphunzira ndi kusangalala ndi zosangulutsa pamodzi
[Chithunzi patsamba 18]
Amagaŵana chidziŵitso cha Baibulo ndi ena