Atolankhani a ku Russia Athokoza Mboni za Yehova
OFESI ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Russia inapatulidwa pa June 21, 1997. Nthambiyo ili ndi nyumba zisanu ndi ziŵiri zogona, Nyumba ya Ufumu yaikulu, chipinda chodyera, ndi nyumba yaikulu momwe muli maofesi ndiponso malo osungira katundu. Ili pamtunda wa makilomita 40 kumpoto chakumadzulo kwa St. Petersburg, pafupi ndi mudzi wa Solnechnoye.
Kupatulirako kunalengezedwa kwambiri ndi atolankhani amene anaitanidwa ku programuyo. Mmodzi wa iwo analemba m’nyuzipepala ya ku Moscow yotchedwa Literaturnaya gazeta, yomwe imafalitsidwa makope pafupifupi 250,000 kuti: “Ganizo loyamba limene munthu angakhale nalo nlakuti, Iyi ndiyo nyumba yabwino yofunika kutengerapo chitsanzo!”—Onani zinthuzi pa masamba 14 ndi 15.
Wolemba nkhani, Sergey Sergiyenko analongosola kuti: “Kuno chilichonse anachipanga ndi okhulupirira, ndi manja awo: ntchito yomangayo inapangidwa ndi anthu a ku Finland, Sweden, Denmark, Norway, ndi Germany. Misewu yomangidwa ndi njerwa yosesedwa bwino; udzu wotchetchedwa bwino; nyumba zofoleredwa bwino ndi matayilosi, mawindo akuluakulu, ndi zitseko za magalasi—awa ndiwo maofesi oyang’anira gulu la chipembedzo la Mboni za Yehova m’chigawo cha Russia.”
Atolankhani a ku Moscow, mtunda wa makilomita 650 kummwera chakummaŵa kwa nthambiyo, anaitanidwa ku programu yopatulirayo ndipo anawakonzera mayendedwe. Anasonyezedwa malowo, pambuyo pake panali nthaŵi yamafunso ndi mayankho pomwe panalinso zakumwa. Malinga ndi zimene anaona, a Sergiyenko analemba kuti:
“Mboni nzofatsa ndi zosadzionetsera . . . Kuti tinene pakanenedwe ka ku Russia kotchuka, ‘Mboni zimakhala [m’nyumba zawo] monga pa chifukato cha Yehova,’ . . . Mboni zimasamala abale awo mwapadera ndipo nthaŵi zonse zimakhala zokoma mtima.”
Nkhani yolembedwa ndi S. Dmitriyev inasindikizidwa mu Moskovskaya Pravda, nyuzipepala yofalitsidwa tsiku lililonse pafupifupi makope 400,000. M’nkhani yake yokhala ndi mutu wakuti “Mukhoza Kupanga Pokhala Pabwino Malinga Mutachita Khama,” mlembiyo anati:
“Gulu lachipembedzo la Mboni litaloledwa mwalamulo mu Russia [mu 1991], linayamba kulingalira zomanga likulu lawo. Anali kufunafuna malo pafupi ndi mzinda wa Moscow pamene mosayembekezereka kunamveka kuti malo omwe kale anali kampu ya achinyamata pafupi ndi St. Pete[rsburg] anali kuwagulitsa. Anagula malowo, ndipo anayamba kumanga. . . .
“Chaka chimodzi ndi theka zapitazo, pa January 1, 1996, malo ameneŵa m’mudzi wa Solnechnoye anakhala nthambi ya gulu lachipembedzoli. Chamkati mwa June, gulu la atolankhani a ku Moscow linali ndi mwaŵi wokathera nthaŵi mu St. Pete[rsburg], kufufuza kuti kodi Mboni za Yehova zimenezi ndi ndani?”
Kodi a Dmitriyev’s anayankha kuti chiyani? “Ndi anthu monga ena onse.” Komabe, ndi osiyanako, monga mmene anasonyezera pamapeto pa nkhani yawo: “Amakhala mwamtendere okhaokha, mwamtendere paliponse. Kodi ndi maloto? Inde. Komatu zikuchitikadi.”
Mtolankhani wina wa ku Moscow, Maksim Yerofeyev, analemba mu Sobesednik, nyuzipepala yomwe imafalitsidwa makope 300,000. Iye anati: “Maunansi onse pamalo ameneŵa agona pa mfundo yakuti: Palibe amene amakakamizidwa kugwira ntchito, komabe aliyense amangogwira ntchito modzifunira.”
Atalongosola za chipinda chogona cha mgwirizanitsi wa Komiti ya Nthambi, Vasily Kalin, a Yerofeyev anati: “Gulu la atolankhani athu osakhulupirira anafuna kuona zipinda zina zomwe anafuna okha. Kunapezeka kuti kukula kwa zipinda zinazo ndi katundu wambiri amene analimo sanasiyane ndi mmene analili m’chipinda cha Vasily Kalin.”
Mtolankhani wina, Anastasiya Nemets, analemba nkhani yakuti “Kukhala Mwamtendere Iwe Mwini.” Mutu wina waung’ono pa nkhani imeneyo yomwe inali mu nyuzipepala yotchedwa Vechernyaya Moskva unali wakuti: “Izi Ndizo Zimene Anthu Akuphunzira m’Kamudzi Kosadziŵika Bwino Kunja kwa St. Pete[rsburg].”
Polongosola za malo ndi kaonekedwe ka ofesi ya nthambiyo, analemba kuti: “Malo onse ozungulira, pali nkhalango ndi udzu ufupiufupi. Nyanja ya Finland sili patali kwenikweni. Kuno kuli nyumba zabwino zomangidwa mwa chimangidwe cha ku Ulaya, misewu yosesedwa bwino yopangidwa ndi njerwa, ndiponso maluŵa a mitundu yokongola.
“Makampani a malonda amamanga nyumba zabwino zoterozo kwa ‘a Russia apamwamba’ okha. Komabe, anthu a ndalama zochepera amakhala m’mudzi umenewu . . . Amakhala bwino, ndipo chofunika kwambiri, amakhala monga mabwenzi. Pali anthu okwana 350 okha pamenepa, ochokera ku mbali zosiyanasiyana za dziko lapansi; ukhoza kumva anthu akulankhula zilankhulo zosiyanasiyana—kuyambira Chispanishi ndi Chipwitikizi mpaka chilankhulo cha ku Finland ndi cha ku Sweden.
“Kunena zoona, malo ameneŵa ndi dziko palokha: M’mudziwu muli mashopu opanga zinthu zatsopano ndi kukonza zowonongeka, ndipo kumatheka kukonza chilichonse chimene banja lolankhula zilankhulo zosiyanasiyanalo likufuna; ali ngakhale ndi chipatala chawochawo.”
Ndithudi, kupatulira nthambiko kunali chochitika chapadera kwa anthu 1,492 ochokera m’maiko 42 omwe analipo ku Solnechnoye. Kumeneko ambiri anali akuluakulu amene anatumikira kwa zaka makumi ambiri pamene ntchito yolalikira inali yoletsedwa. Kodi mungayerekezere mmene akuluakulu ameneŵa analiri odabwa ndiponso achimwemwe pamene ankayendera ofesi yokongolayi imene ili m’munda wamaekala 17 umenewu? Tikhoza kuwakhululukira ngati ankalingalira kuti akulota.
[Zithunzi patsamba 22]
Atolankhani akuyendera ofesi yanthambi
Nthaŵi ya mafunso ndi mayankho