Kodi Mulungu Adzathetsa Bwanji Nkhanza?
KODI nkhanza zingathetsedwe bwanji? Nanga chothetsera chake nchiyani? Tikamaphunzira zochitika m’mbiri, zimangoonekeratu kuti anthu alephera. Kunena zoona, atsogoleri adziko akamakambitsirana nkhani imeneyi amasemphana maganizo kwambiri.
Mwachitsanzo, tangoganizani za chaka cha 1995. Chimenecho chinali chaka cha 50 chokumbukira kutha kwa Chipululutso cha a Nazi, kutha kwa Nkhondo Yadziko II, ndi kuphulitsidwa kwa bomba la atomu. M’chaka chimenecho, mapwando akukumbukira zimenezo anachitika m’mbali zambiri zadziko lapansi, ndipo atsogoleri adziko anapezekapo. Chifukwa? Kuti achititse anthu kunyansidwa ndi nkhanza zimenezo kuti zisadzabwerezedwenso. Komabe, ena anaona kuti pamapwando amenewo panali kusemphana maganizo, kapena chinyengo chimene.
Chinyengo
Pamapwando ofalitsidwa kwambiri ameneŵa, oimira onse a maboma ndi azipembedzo anafuna kuonedwa ngati opindulitsa anthu, kapena kungofuna kupeŵa kuonedwa ngati ochita zoipa. Komanso, mitundu imene imadandaula ndi nkhanza zakale zimenezo yamanga nkhokwe zosungiramo zida, ndipo amawononga ndalama zambiri ncholinga chimenecho. Koma panthaŵi imodzimodziyo, sanathebe kuthetsa mavuto aakulu, onga umphaŵi, kupanda khalidwe kwa anthu, ndi kuipitsa zachilengedwe, nthaŵi zonse akumati alibe ndalama zokwanira.
Zipembedzo zadziko zimalemba mbiri imene imabisa zoti achipembedzo anakhala chete kwa nthaŵi yaitali osatsutsapo nkhanza ya maboma ankhanza, ndipo zipembedzozo zimaphimba anthu kumaso kuti asaone kuti azipembedzo amagwirizana ndi olamulira ankhanzawo. Zipembedzo zimenezo sizinachitepo kanthu kuti ziletse anthu achipembedzo chawocho kuphana. Mwachitsanzo, pa Nkhondo Yadziko II, Mkatolika ankapha Mkatolika ndipo Mprotestanti ankapha Mprotestanti chifukwa anali a mitundu yosiyana ndi kuti anali kumbali zotsutsana. A mbali zonse ziŵiri anali kudzitcha kuti Akristu koma anali kuchita zimene zinali kutsutsana ndi zimene Yesu anaphunzitsa. (Mateyu 26:52; Yohane 13:34, 35; 1 Yohane 3:10-12; 4:20, 21) Zipembedzo zinanso zimachita zomwezo. Lerolino, kumbali zambiri zadziko lapansi, mamembala a matchalitchi ameneŵa adakachitirabe anthu nkhanza.
M’nthaŵi ya Yesu, atsogoleri achipembedzo anali onyenga. Yesu anawatsutsa, akumati: “Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mumanga nyumba za pamanda a aneneri, ndipo mukonza manda a anthu olungama, ndi kuti, Ife tikadakhala m’masiku a makolo athu, sitikadakhala oyanjana nawo pa mwazi wa aneneri. Pomwepo mutsimikiza nokha, kuti muli ana a iwo amene anapha aneneri.” (Mateyu 23:29-31) Atsogoleri achipembedzo amenewo ankati ngokonda Mulungu koma anali onyenga amene anazunza Yesu ndi ophunzira ake.
Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Tingaphunzire pa zimene mbiri yadziko imanena, komabe Baibulo nlimene lili ndi maphunziro opindulitsa. Baibulo silimapatsa anthu ntchito yotanthauzira mwa maganizo awo zimene mbiri imanena kapena kupotoza mwadala. Baibulo limafotokoza zochitika m’mbiri ndi za mtsogolo malinga ndi maganizo a Mulungu.—Yesaya 55:8, 9.
Malemba amanena za zochitika zabwino ndi zoipanso, komanso za anthu abwino ndi oipa. Nthaŵi zambiri, tingaphunzire pankhani zimenezo phunziro limodzi loyenera, logwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Mtumwi Paulo, atangotchula kumene zochitika zingapo za m’mbiri ya Israyeli wakale, anamaliza ndi kuti: “Koma izi zinachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife.” (1 Akorinto 10:11) Yesu mwiniyo naye anasonyeza kuti tingaphunzire kanthu pa zochitika m’mbiri pamene anauza ophunzira ake kuti: “Kumbukirani mkazi wa Loti.”—Luka 17:32.
Zimene Mulungu Amakumbukira ndi Zimene Amaiŵala
Timaphunzira m’Baibulo kuti Mulungu amakumbukira kapena kuiŵala anthu malinga ndi zochita zawo. Amene amachimwa koma nkulapa, Mulungu adzawakhululukira “koposa.” (Yesaya 55:7) Ngati woipa alapa, “akabwerera iye kuleka tchimo lake, nakachita choyenera ndi cholungama; . . . Zoipa zake ziri zonse . . . sizidzakumbukika zimtsutse.”—Ezekieli 33:14-16.
Paulo analemba kuti “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.” (Ahebri 6:10) Choncho, Yehova adzafupa anthu amene akuwakumbukirabe. Yobu wokhulupirika anapemphera kuti: “Ha! mukadandibisa kumanda, . . . Mukadandiikira nthaŵi, ndi kundikumbukira.”—Yobu 14:13.
Komanso, ponena za munthu woipa wosalapa, Mulungu adzachita naye malinga ndi mawu amene anauza Mose kuti: “Ndifafaniza yemweyo kumchotsa m’buku langa.” (Eksodo 32:33) Inde, Mulungu adzaiŵaliratu oipa kwamuyaya.
Woweruza Wosatsutsidwa
Mulungu ndiye Woweruza wosatsutsidwa pa zonse zochitika m’mbiri. (Genesis 18:25; Yesaya 14:24, 27; 46:9-11; 55:11) Malinga ndi chiweruzo chake cholungama, sadzaiŵala nkhanza zambiri zimene anthu anachitidwapo. Patsiku lamkwiyo wake wolungama, adzaweruza anthu ndi mabungwe onse omwe anapalamula.—Chivumbulutso mitu 18, 19.
Mwa amenewo padzakhala dongosolo lonse lachipembedzo chonyenga, lomwe lapatsidwa dzina lophiphiritsira m’Malemba lakuti “Babulo Waukulu.” Kwalembedwa za iye kuti: “Machimo ake anaunjikizana kufikira m’Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake.”—Chivumbulutso 18:2, 5.
Zipembedzo zimenezi zinafunikira kuphunzitsa anthu ake kuchita zoyenera koma zinalephera. Ndiye Mawu a Mulungu ponena za zipembedzo zonse zadziko, amati: ‘Ndipo momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.’ (Chivumbulutso 18:24) Chifukwa cholephera kuphunzitsa mamembala awo kukonda anthu ena ndiponso a m’tchalitchi chawo, zipembedzo zimenezi zikuimbidwa mlandu wakupha.
Dziko Latsopano Layandikira!
Tsiku limene kuipa kudzawonongedwa tsopano layandikira. (Zefaniya 2:1-3; Mateyu 24:3, 7-14) Kenako, idzafika nthaŵi yoti anthu achimwemwe okhala padziko ‘sadzaliranso ndipo sadzamvanso chopweteka chilichonse.’ (Chivumbulutso 21:3-5) Nkhanza ndi kupululutsa anthu sizidzachitikanso chifukwa anthu adzalandidwa mphamvu yolamulira padziko ndipo mphamvu idzakhala ya Ufumu wa Mulungu wa Kumwamba m’manja mwa “Kalonga Wamtendere,” Yesu Kristu.—Yesaya 9:6, 7; Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10.
Panthaŵi imeneyo, ulosi wa pa Salmo 46:9 udzakwanira wonse, wakuti: “[Mulungu] aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi.” (Salmo 46:9) Mtendere umenewo udzakhala wokhalitsa, chifukwa Yesaya 2:4 ananeneratu kuti: “Mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” Nchifukwa chakenso Salmo 37:11 linalonjezeratu kuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” Inde, pamenepo tidzaterodi kuti “dziko lonse lapuma, lili du; iwo ayamba kuyimba nyimbo.”—Yesaya 14:7.
Zonsezi zikutanthauza kuti dziko latsopano lolungama layandikira. Ndipo m’dziko latsopano limenelo, lolamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu kumwamba, chinthu china chodabwitsa chidzachitika—kuuka kwa akufa! Mawu a Mulungu amalonjeza kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”—Machitidwe 24:15.
Yesu, pamene anali padziko lapansi, anasonyeza zimenezo mwa kuukitsa anthu akufa. Mwachitsanzo, pamene anaukitsa mtsikana wina wamng’ono, nkhaniyo imati: “Pomwepo buthulo linauka, niliyenda; . . . ndipo [amene anaona zimenezo] anadabwa pomwepo ndi kudabwa kwakukulu.” (Marko 5:42) Panthaŵi youkitsa akufa, omwe anaphedwa mwankhanza ngakhalenso ena amene anafa kale adzaukitsidwa kwa akufa ndipo adzapatsidwa mwayi wakukhala m’paradaiso padziko lapansi kwamuyaya. (Luka 23:43) Ndiyeno, “zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.”—Yesaya 65:17.
Mungachite mwanzeru mutati mupeze chidziŵitso cholongosoka cha Mawu a Mulungu, Baibulo ndi kumachita chifuniro chake. Pamenepo Mulungu adzakukomerani mtima mwa kukukumbukirani pamene adzawabwezera anthu moyo wawo. Yesu anatero kuti: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”—Yohane 17:3.
[Zithunzi pamasamba 8, 9]
Mulungu adzasanduliza dzikoli likhale paradaiso wamtendere
[Zithunzi patsamba 10]
Mulungu adzapoletsa mabala a nkhanza zakale mwa kuukitsa akufa