Kodi Nzotheka Kukhululukira ndi Kuiŵala?
KUYAMBIRA pamene Nkhondo Yadziko II inatha mu 1945, papita zaka zoposa 50. Nkhondo yadziko lonse imene ija inali yoipitsitsa zedi ndipo inawonongetsa ndalama kwabasi m’mbiri yonse ya anthu.
Nkhondo Yadziko II inakhalako zaka zisanu ndi chimodzi ndipo inapha anthu ngati mamiliyoni 50, kuphatikizapo anthu wamba. Anthu enanso osaŵerengeka anapundulidwa thupi, maganizo, ndi mtima. Anthu ambiri amene anaona zaka zimenezo za tsoka lankhondo, sanaiŵalebe chifukwa anachitidwa nkhanza yopweteka ndiponso anafedwa okondedwa awo.
Anthu amakumbukiranso nkhanza zimene a Nazi ankachita m’Nyengo Yakupululutsa, namapha anthu mamiliyoni ambiri osachimwa. Ku Ulaya ndi ku Asia, nkhanza zambiri zinkachitidwa ndi magulu ankhondo oukira, amene ankapha anthu wamba, kugwirira akazi, kulanda katundu, ndi kuwopseza anthu. Komanso, anthu ena ambiri ankaukiridwa ndi asilikali a pandege omwe ankasakaza zinthu, kuvulaza ndi kupha amuna osaŵerengeka, akazi, ndi ana osachimwa. Ngakhale asilikali mamiliyoni ambiri anaonanso mavuto osapiririka pankhondo zosiyanasiyana padziko lonse.
Mabala a m’Maganizo ndi a Mumtima
Mabala ambiri a m’maganizo ndi a mumtima amene anthu anakhala nawo chifukwa cha zinthu zoopsa zimene zinachitika pa Nkhondo Yadziko II, adakali m’maganizo a anthu ambiri amene analiko panthaŵi imeneyo ndipo amene adakalipo lero. Angakonde kungoiŵaliratu zinthu zonse zopweteketsa mtima zimene adakakumbukirabe. Koma sangathe kuziiŵala. Zinthu zoopsa zimenezo ena amazionabe m’maganizo mwawo ndipo amavutika nazo ngati maloto oipa owalotalotabe.
Komabe, ena samafuna kuiŵala, mwina chifukwa akufuna kudzabwezera kapena akungofuna kumalemekeza akufawo mwa kuwakumbukira. Ndiponso, anthu ambiri amaganiza kuti nkhanza zakale zimenezo ziyenera kumakumbukikabe m’mitima ya anthu onse, ndi chiyembekezo chakuti nkhanza zoterozo zisadzachitikenso.
Zaka zingapo zapitazo, pakati pa 1994-95, zimene munthu aliyense anali kuchita paphwando la 50 lokumbukira D day (kukumbukira tsiku limene Magulu Ankhondo Ogwirizana anaukira Normandy m’June 1944) ndi kukumbukiranso mapeto a nkhondo yachiŵiri ku Ulaya (m’May 1945) zinasonyeza kuti mboni zambiri zimene zinaona ndi maso zochitika zimenezo, nkowavuta kuti akhululuke ndi kuiŵala. Nthaŵi zambiri, samafuna kuti pakamwa pawo patuluke ngakhale liwu limodzi lowayanjanitsa ndi adani awo akale. Motero asilikali omwe anamenya nawo nkhondoyo a ku Britain anakana kuitana oimira Germany kudza paphwando lokumbukira tsiku limene Magulu Ankhondo Ogwirizana anaukira Normandy.
Ponena za nkhanza zimene a Nazi anachita pa Nkhondo Yadziko II ndi mmenenso zimavutira kukhululuka ndi kuiŵala, wolemba mabuku, Vladimir Jankélévitch, ananena maganizo ake motere: “Chifukwa cha nkhanza yonyansa ngati imeneyi, chimene munthu aliyense angachite mwachibadwa . . . ndiko kupsa mtima ndi kuyesetsadi kuti asaiŵale zimenezo, ndiyeno nkuwasaka apanduwo mpaka kumalekezero a dziko lapansi,” monga mmene linalonjezera bungwe la Nuremberg Tribunal limene linaweruza mlandu wawo. Wolemba mabuku mmodzimodziyo anatinso: “Sitingazengerezenso kunena motembenuza mawu amene Yesu ananena popemphera kwa Mulungu mu Uthenga Wabwino, malinga ndi kunena kwa Woyera Mtima Luka, kuti: “Ambuye, musawakhululukire iwo, pakuti akudziŵa zimene akuchita.”—Yerekezerani ndi Luka 23:34.
Nzachisoni kuti kuyambira 1945 mpaka lero, anthu akhala akukhetsa mwazi chifukwa cha nkhanza zina zosaneneka—ku Cambodia, ku Rwanda, ku Bosnia, kungotchula maiko oŵerengeka chabe. Nkhondo zankhanza zimenezi zapha anthu mamiliyoni ambirimbiri, ndiponso zasiya akazi ndi ana amasiye ambiri, zapatsa anthu umphaŵi, nkuwasiya akukumbukira zinthu zosautsa maganizo.
Mosakayikira, m’zaka za zana la 20 zino, mwachitika nkhanza imene siinachitikepo kale lonse. Zangokhaladi monga mmene ulosi wa Baibulo unaneneratu molondola ponena za nyengo ino—anthu ‘ngaukali’ ndipo ‘ngosakonda abwino.’—2 Timoteo 3:1-5; Chivumbulutso 6:4-8.
Kodi Tingatani?
Anthu akakumana ndi nkhanza ngati imeneyo, zimawakhudza mosiyanasiyana. Koma nanga ifeyo? Kodi tiyenera kumaikumbukirabe? Kapena kodi tiyenera kuiŵala? Kodi kukumbukira kumatanthauza kuwasungira udani kukhosi adani athu akale, nkukana kuwakhululukira? Komanso, kodi kukhululukira kumatanthauza kungoiŵaliratu osakumbukiranso zinthu zoipa zija?
Kodi Mlengi wa anthu, Yehova Mulungu, amaganiza bwanji za upandu wankhanza umene ukuchitidwa m’nthaŵi yathu ino ndi umenenso unachitidwa kale? Kodi adzawakhululukira apanduwo? Kodi Mulungu sanachedwe kwambiri kuwalipa anthu amene anaphedwa mwankhanzawo? Kodi pali chiyembekezo chenicheni chakuti nkhanza zidzathadi, popeza kuti zakhala zikuchitika kwa zaka zikwi zambiri? Kodi Mulungu Wamphamvuyonse potsirizira adzazithetsa bwanji nkhani zovuta zimenezi?
[Chithunzi patsamba 4]
Ana a anthu amene anapululutsidwa akusonkhana kumisasa yothaŵirako
[Mawu a Chithunzi]
UN PHOTO 186797/J. Isaac
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
U.S. Navy photo