Mphamvu ya Osatsa Malonda
KALE uthenga wa malonda pawailesi yakanema unkayamba ndi mawu akuti, “Tsopano, timve uthenga wachidule wochokera kwa otipatsira programuyi.” Opatsirawo ndi makampani amene amalipira ndalama kuti zinthu zawo ziulutsidwe. Pamene kuli kwakuti ‘uthenga wachidule wochokera kwa opatsira’ wachuluka, opatsirawo adakali kupereka ndalama kuchirikiza oulutsa nkhani ndi zosangalatsa—wailesi yakanema, magazini, manyuzipepala, ndi wailesi. Ndiponso, opatsira amayesa kulamulira zimene ziyenera kutuluka m’nkhani ndi zimene siziyenera.
Mwachitsanzo: Mu 1993 kampani yopanga galimoto zambambande ya ku Germany inalembera magazini 30 kuwauza kuti mauthenga alionse onena za galimoto yawo alembedwe “kokha pamasamba oyenera okhala ndi nkhani za akonzi.” Kalatayo inafotokoza kuti magazini okhala ndi mauthenga awo asakhale ndi nkhani zilizonse zonyoza galimoto yawo, zinthu za ku Germany, kapena dziko la Germany. Inde, nzosadabwitsa kuti kampani imeneyi, imene imawononga $15,000,000 pa kusatsa malonda ake m’magazini, ingafune “masamba oyenera okhala ndi nkhani za akonzi.”
Nzosadabwitsanso pamene magazini olengeza zovala za akwati zatsopano salola mauthenga a zovala akwati zakale kapena pamene manyuzipepala amene amapereka mndandanda wa othandiza kugula malo kapena nyumba samakuuzani mmene mungagulire nyumba popanda wokuthandizani. Momwemonso, siziyenera kutidabwitsa pamene manyuzipepala osatsa malonda a fodya kapena malotale satsutsa kusuta kapena kutchova juga.
Chikhalidwe cha Ogula
Chotero mphamvu ya kusatsa malonda simangothera pa kugulitsa katundu. Kumalimbikitsa ogula kuti akhale ndi moyo wakutiwakuti, chikhalidwe cha dziko lonse chimene chimagogomezera chuma.
Kodi cholakwa ndi zimenezo nchiyani? Zimadalira ndi amene mwafunsa. Osatsa malonda amati anthu amakonda kugula ndi kukhala ndi zinthu; kusatsa malonda kumakwanitsa zofuna zawo. Amanenanso kuti kusatsa malonda kumapezetsa ntchito, kuchirikiza maseŵero ndi maluso, kumatheketsa kukhala ndi zoulutsira nkhani zokwanira, kumalimbikitsa mpikisano, kumawongolera zinthu, kumatsitsa mitengo, ndipo kumatheketsa anthu kudziŵa zimene akusankha pogula.
Ena amati kusatsa malonda kumasokoneza anthu ndi kuwapangitsa kusakhutira ndi zomwe ali nazo, ndipo kumachirikiza ndi kukulitsa zikhumbo zosatha. Alan Durning wochita kafukufuku analemba kuti: “Kusatsa malonda, mofanana ndi nyengo yathu, kumasinthasintha, kumalimbikitsa zokondweretsa, kumasonyeza zikhulupiriro zimene ambiri ali nazo, ndipo mafashoni ndiwo amakusonkhezera; kumatchukitsa anthu, kumanena kuti chuma ndicho njira yoposa yopezera chikhutiro, ndipo kumatsimikiza kuti kutukuka kwa tekinoloji ndiko kumapatsa munthu mwayi.”
Mphamvu Yake pa Inu
Kodi kusatsa malonda kumaumba umunthu wathu ndi zokhumba zathu? Mwinamwake. Komabe, kaya kumatikhudza kwambiri kapena pang’ono zimadalira pa zinthu zina.
Ngati timatsata mapulinsipulo ndi malangizo a Baibulo, tikudziŵa kuti kukhala ndi chuma sikulakwa. Ndi iko komwe, Mulungu anadalitsa Abrahamu, Yobu, Solomo, ndi ena, kuwapatsa chuma chochuluka.
Komanso, tikatsata mapulinsipulo a m’Malemba, sitidzakhala osakhutira mofanana ndi aja amene nthaŵi zonse amafunafuna chikhutiro ndi chimwemwe m’chuma. Uthenga umene Baibulo lili nawo siwakuti “Muzigulabe kufikira mutatopa.” M’malo mwake, limatiuza kuti:
Khulupirirani Mulungu. “Lamulira iwo achuma m’nthaŵi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziŵika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo.”—1 Timoteo 6:17.
Zikukwanireni. “Sitinatenga kanthu poloŵa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano; koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.”—1 Timoteo 6:7, 8.
Khalani osapambanitsa. “Akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golidi kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali; komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino.”—1 Timoteo 2:9, 10.
Dziŵani kuti nzeru yaumulungu iposa chuma. “Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golidi woyengeka. Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye. Masiku ambiri ali m’dzanja lamanja lake; chuma ndi ulemu m’dzanja lake lamanzere. Njira zake zili zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere. Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira ngwodala.”—Miyambo 3:13-18.
Muzipatsa. “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
Wina angatsutse kuti nkhani zimenezi ndi mtundu wina wake wa kusatsa, umene “umapezera malonda” chikhulupiriro chakuti chuma sichiyenera kukankhira pambali zinthu zauzimu. Mosakayikira mukuvomerezana ndi ganizo limenelo.
[Bokosi patsamba 27]
Kusatsa Ufumu wa Mulungu
Kodi njira yabwino kwambiri yofikira anthu ndi uthenga wokopa ndi yotani? Buku lakuti Advertising: Principles and Practice limati: “M’dziko labwino aliyense wopanga zinthu akhoza kumalankhula ndi munthu mmodzi ndi mmodzi za zinthu zimene akugulitsa kapena ntchito imene afuna kumgwirira.” Akristu oona mwaufulu akhala akulengeza Ufumu wa Mulungu mwanjira imeneyi kwa zaka pafupifupi 2,000. (Mateyu 24:14; Machitidwe 20:20) Kodi nchifukwa chiyani eni mabizinesi ochuluka sagwiritsa ntchito njira imeneyi kufikira anthu? Bukulo likuti: “Njira imeneyo imalira ndalama zambiri. Maulendo opangidwa ndi osatsa malonda angafune ndalama zoposa $150 ulendo umodzi.” Komatu Akristu “amasatsa” Ufumu wa Mulungu kwaulere. Ndi kulambira kwawo.
[Zithunzi patsamba 26]
Uthenga umene Baibulo lili nawo siwakuti “Muzigulabe kufikira mutatopa”