Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 9/8 tsamba 3
  • Vuto la Imfa za Achinyamata

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Vuto la Imfa za Achinyamata
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mbiri Yaitali Yonena za Imfa za Achinyamata
  • Tasmania Chisumbu Chaching’ono, Nkhani Yake Yapadera
    Galamukani!—1997
  • Kodi Achinyamata Amakumana ndi Mavuto Otani?
    Galamukani!—2009
  • Achichepere Amakono Zitokoso Zimene Amakumana Nazo
    Galamukani!—1990
  • Baibulo ndi Makhalidwe Abwino a Achichepere
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 9/8 tsamba 3

Vuto la Imfa za Achinyamata

“Ndimangoona kuti mbadwo wathu ukutha nkufa.”—Johanna P., wazaka 18 wongoyamba kumene maphunziro payunivesite ku Connecticut, U.S.A.

MAOFESALA apolisi anaona zinthu zochititsa nthumanzi pafamu kunja kwa mzinda wa Hobart, likulu la chilumba cha Tasmania ku Australia. M’nyumba munali atsikana anayi a zaka zapakati pa 10 ndi 18. Onsewo anali akufa, ataphedwa ndi atate wawo, amene nayenso anali gone pafupi nawo ali ndi bala la mfuti m’mutu mwake. Anali atadzidula dzanja ndi nkhwangwa. Kupha ndiponso kudzipha kumeneku kunapangitsa anthu onse a ku Tasmania kugwedezeka. Ndipo kunadabwitsa anthu nkumadzifunsa m’malingaliro kuti—Aferanji? Aferanji atsikana osalakwa anayiwo?

Anthu ku Belgium adakali okwiya chifukwa cha zomwe anachita munthu wina amene anali atangomtulutsa kundende kuti akhale kunja koma azimuona mmene akukhalira, anagwirira chigololo atsikana asanu ndi mmodzi ndiye kenaka nkupha anayi mwa iwo. Panalinso funso lofananalo kuti—Aferanji atsikanaŵa? Ku Argentina amayi ambiri amakhulupirira kuti anthu okwana 30,000 amene ambiri mwa iwo anali ana awo aamuna ndi aakazi, anasoŵa panthaŵi imene tsopano imatchedwa kuti nkhondo yauve (dirty war).a Ena mwa anthu atsoka ameneŵa ankaŵazunza, kuŵamwetsa mankhwala osokoneza bongo, ndiye nkuŵakweza ndege kukaŵataya m’nyanja yamchere. Ambiri mwa iwo amakaŵataya adakali amoyo. Anaferanji? Mpaka pano amayi awo akufunafuna mayankho.

Mu 1955 pamsonkhano wa World Congress of Mothers analengeza kuti nkhondo ilibe phindu ndikuti msonkhanowo “ndichilengezo, chachikulu chochenjeza kuchokera kwa amayi onse amene akulimbana ndi kutetezera ana awo, akulu ndi ang’ono, kuti asakumane ndi mavuto obwera chifukwa cha nkhondo ndiponso kukonzekera nkhondo.” Mosemphana nzimenezo, chiŵerengero cha achinyamata amene afa pankhondo zoopsa chichitikire msonkhano umenewo chikuchulukirachulukirabe padziko lonse—kuwonongeka kwa mbadwo umene ukanabala ana okhala ndi maluso osiyanasiyana.

Mbiri Yaitali Yonena za Imfa za Achinyamata

M’mbiri yonse muli nkhani yonena za kuphedwa kwa achinyamata. Ngakhale m’zaka za zana la 20 zino zodziŵika monga nthaŵi yomwe timadziŵa zambiri, kumenyana kwa mitundu ndi mafuko kwaphetsa achinyamata ambiri. Zikuoneka kuti achinyamata amataya miyoyo yawo chifukwa cha zolakwa ndi zofuna za akuluakulu awo.

M’dziko lina mu Africa, gulu la ana ogwira ntchito ya usilikali omwe amadzitcha kuti Lord’s Resistance Army anapangitsidwa kukhulupirira kuti zipolopolo sizingaloŵe pamatupi awo, inatero nyuzipepala yotchedwa The New Republic. Nzosadabwitsa kuti mutu wa nkhaniyo unali wakuti “Achinyamata Opanda Pake”! Motero mabanja amene ana awo amuna ndi akazi anafa—popeza sizinali zoona kuti zipolopolo sizingaloŵe pamatupi awo—anafunsa moyenerera kuti: Ana athu anaferanji? Chifukwa chake chenicheni nchiyani?

Kuwonjezera pamadandaulo ndi kuvutika kumeneku, pali chiŵerengero chachikulu cha achinyamata omwe amadzipha.

[Mawu a M’munsi]

a Yomwe imatchedwa kuti nkhondo yauve inachitika panthaŵi imene bungwe la asilikali linkalamulira (1976—83) pamene anthu ambiri amene ankaŵaganizira kuti ndi oukira anaphedwa. Ena amayerekezera kuti chiŵerengero cha omwe anaphedwa ndi pakati pa 10,000 ndi 15,000.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena