Lingaliro la Baibulo
Ubwino Wakukhala Panokha
NTHAŴI ina Yesu “anakwera m’phiri payekha, kukapemphera: ndipo pamene panali madzulo, iye anakhala kumeneko yekha.” (Mateyu 14:23) Nthaŵi inanso, “kutacha anatuluka Iye namka kumalo achipululu [ayekha NW],” (Luka 4:42) Malemba ameneŵa ndi umboni wakuti Yesu Kristu ankadziŵa ubwino wa kukhala payekha nthaŵi zina.
Baibulo limanenanso zitsanzo zina za anthu amene monga Yesu ankaona kuti kukhalako pawekha nthaŵi zina nkwabwino. Nthaŵi imene ankakhala payekha usiku ndi kumayang’ana kumwamba pamene wamasalmo ankalingalira za ukulu wa Mlengi Wamkulu. Ndipo ponena za Yesu Kristu uja, atangomva za imfa ya Yohane Mbatizi, ananyamuka kupita “kumalo achipululu payekha.”—Mateyu 14:13; Salmo 63:6.
Lerolino, pamene chiwawa ndi phokoso nzofala pa chikhalidwe cha makono, anthu sakonda kukhala paokha kwa kanthaŵi, kaya mosayembekezereka kapena mochita kufuna. Kodi mukukumbukira pamene munakhalako panokha? Mayi wina wachitsikana yemwe ali pabanja anati: “Sindinayambe ndakhalapo pandekha m’moyo wanga.”
Koma kodi kukhala pawekha nkofunikadi? Ngati nchoncho, kodi ndi motani mmene nthaŵi yongokhala phee tingaigwiritsire ntchito mopindulitsa? Ndipo kodi pamene tikufuna nthaŵi yokhala patokha, nchifukwa chiyani tiyenera kusamala?
Kukhala Panokha—Nchifukwa Chiyani Kuli Kopindulitsa?
Baibulo limatiuza kuti munthu wa Mulungu wakale, Isake, anakhalapo payekha “m’munda madzulo.” Chifukwa? Limati, kuti ‘akalingalire.’ (Genesis 24:63) Malinga ndi dikishonale ina, kulingalira ndi “kuganiza mofatsa kapena mwapang’onopang’ono.” Zimasonyeza “kuikapo mtima pachinthu kwanthaŵi yaitali.” Kwa Isake amene anali pafupi kutenga maudindo olemera, kulingalira kwa mtundu umenewu kuyenera kuti kunamthandiza, kuganiza mofatsa ndi kusankha zoyenera kuchita.
Katswiri wa zamaganizo, amati ‘malinga ngati kukhala kwanu panokhako mukukuchita mosamala, kungatithandize kuganiza mofatsa ndi kulingalira mwakuya.’ Ambiri angachitire umboni kuti mukhoza kukhala omasuka, olimbikitsidwa, ndi athanzi.
Ena mwa mapindu a kulingalira mwakuya ndiwo kufatsa ndi kuchita zinthu molongosoka, khalidwe lofunika kuti muzilankhula ndi kuchita zinthu mwanzeru, limene, mapeto ake limathandiza kukulitsa mgwirizano. Mwachitsanzo, munthu amene amadziphunzitsa kulingalira akhozanso kudziphunzitsa kukhala chete. Mmalo molankhula mwansontho, amaganiza kaye zimene zidzatsatirapo akalankhula. Mlembi wa Baibulo wouziridwa anafunsa kuti, “Kodi uona munthu wansontho m’mawu ake?” Iye anapitiriza kunena kuti: “Ngakhale chitsiru chidzachenjera, koma ameneyo ayi.” (Miyambo 29:20) Mankhwala oletsa kugwiritsira ntchito lirime mwansontho nchiyani? Baibulo limati: “Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe.”—Miyambo 15:28; yerekezerani ndi Salmo 49:3.
Kwa Mkristu, kulingalira ali chete kumene amachita nthaŵi yomwe amakhala kwayekha nkothandiza kwambiri kuti afike pauchikulire wauzimu. Mawu a mtumwi Paulo ndi othandiza pa nkhani imeneyi: “Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima [“kupita patsogolo,” NW] kwako kuonekere kwa onse.”—1 Timoteo 4:15.
Gwiritsirani Ntchito Nthaŵi Yokhala Panokha Kuyandikira kwa Mulungu
Mlembi wina wachingelezi anati: “Pamene tili patokha ndiwo mpata womfikira Mulungu m’pemphero ndiponso mpamene iye amatimva.” Nthaŵi zina, Yesu ankaona kufunika kwa kusiyana ndi anthu nkukapemphera kwa Mulungu pamene ali payekha. Chitsanzo chimodzi cha zimenezi chinalembedwa m’Baibulo: “M’maŵa mwake anauka usikusiku, natuluka namuka kuchipululu, napemphera kumeneko.”—Marko 1:35.
M’Masalmo, muli mawu ambiri osonyeza kuti ankalingalira za Mulungu. Polankhula ndi Yehova, Mfumu Davide anati: ‘Ndilingalira za Inu.’ Zili chimodzimodzinso ndi mawu a Asafu: ‘Ndipo ndidzalingalira ntchito yanu yonse, ndi kulingalirabe zimene munazichita Inu.’ (Salmo 63:6; 77:12) Motero, kulingalira zamakhalidwe a Mulungu ndi zochita zake kumabweretsa mphotho. Kumapangitsa kuti muziyamikira Mulungu ndi kumyandikira.—Yakobo 4:8.
Kuchita Mosamala
Kunena zoona, tiyenera kusamala pamene tikufuna kukhala patokha. Kukhala panokha tingakulongosole monga kopindulitsa koma kowononga ngati munthu atapitiriza kukhalabe payekha. Kukhala panokha nthaŵi yaitali kumaombana ndi zofunika za munthu za kukhalira pamodzi ndi ena, kulankhulana ndi kusonyeza chikondi. Kuwonjezera apo, kudzipatula kungapangitse kupusa ndi kudzikonda kukula mumtima mwathu. Mwambi wa m’Baibulo umachenjeza kuti: “Wopanduka [“wodzipatula,” NW] afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.” (Miyambo 18:1) Kuti tikhale osamala pamene tifuna kukhala patokha, tiyenera kuzindikira kuipa kwa kudzipatula.
Monga Yesu ndi anthu ena okonda zauzimu m’nthaŵi za Baibulo, Akristu lerolino amayamikira nthaŵi imene amakhala paokha. Nzoona, popeza tili ndi maudindo ambiri ndi zinthu zozidera nkhaŵa, nkovuta kuti tipeze nthaŵi ndi mpata woti nkumalingalira tili patokha. Komabe, monga mmene timachitira zinthu zonse zaphindu lenileni, tiyenera “kuwombola.” (Aefeso 5:15, 16, NW) Motero monga wamasalmo tikhoza kunena kuti: “Mawu a m’kamwa mwanga ndi maganizo am’mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova.”—Salmo 19:14.