Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 11/8 tsamba 13-15
  • Kodi Zidzatheka Kuti Anthu Onse Adzakondanedi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Zidzatheka Kuti Anthu Onse Adzakondanedi?
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chozizwitsa cha m’Zaka za Zana Loyamba
  • Nanga Bwanji Lero?
  • Chikondi Chipambana Udani
  • Kodi Anthu Onse Adzakondanapo?
    Kodi Anthu Onse Adzakondanapo?
  • Tanthauzo la Kukonda Mnansi Wathu
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Akristu Oona ndi Nkhondo
    Galamukani!—1994
  • Kodi Chikondi Chanu N’chosefukira Motani?
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 11/8 tsamba 13-15

Kodi Zidzatheka Kuti Anthu Onse Adzakondanedi?

LOYA wina anali atangonena kumene kuti, kuti tipeze “moyo wosatha,” tiyenera kukonda Mulungu ndi mtima wathu wonse ndi kukondanso anansi athu monga timadzikondera tokha. Yesu anamyamikira wachilamuloyo nkumuuza kuti: “Wayankha bwino; chita ichi, ndipo udzakhala ndi moyo.” (Luka 10:25-28; Levitiko 19:18; Deuteronomo 6:5) Koma munthuyo, pofuna kudziyesa yekha wolungama, anafunsanso kuti: “Mnansi wanga ndani?”

Mosakayikira wachilamuloyo ankaganiza kuti Yesu akanati: “Ayuda anzako.” Koma Yesu anasimba nkhani ina yonena za Msamariya wachifundo, yomwe inasonyeza kuti anthu a mitundu ina angakhalenso anansi athu. (Luka 10:29-37; Yohane 4:7-9) Mu utumiki wake Yesu ankanena monenetsa kuti kukonda Mulungu ndi kukondanso anansi athu ndiwo malamulo ofunika kwambiri a Mlengi wathu.—Mateyu 22:34-40.

Komabe, kodi pali gulu lina lililonse la anthu amene anakondanapo ndithu ndi anansi awo? Kodi zingathekedi kuti anthu onse adzakondane?

Chozizwitsa cha m’Zaka za Zana Loyamba

Yesu anauza otsatira ake kuti adzazindikiridwa mwa kukondana ndi anthu a mafuko ena, ndi a mitundu ina, popanda kusankhana nkomwe. Iye anati: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake.” Ndiyeno anadzatinso: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”—Yohane 13:34, 35; 15:12, 13.

Zinthu zimene Yesu ankaphunzitsa ponena za kukondana, zomwenso ankazisonyeza mwa kuchita, zinali zozizwitsa m’zaka za zana loyamba. Ophunzira ake anayamba kutsanzira Mbuye wawo, namaphunzira kukondana mwa njira imene inapangitsa anthu ambiri kuwazindikira ndi kuwasirira. Tertullian, wolemba wa m’zaka za zana lachiŵiri ndi zana lachitatu C.E., ananena kuti anthu ena osakhala Akristu anali kuyamikira otsatira a Yesu kuti: ‘Taonani mmene amakonderana ndi mmene alili okonzekera kuferana.’

Mtumwi Yohane analemba kuti: “Tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale.” (1 Yohane 3:16) Yesu anaphunzitsanso otsatira ake kuti azikonda adani awo. (Mateyu 5:43-45) Kodi anthu akamakondadi anzawo monga mmene Yesu anaphunzitsira, chimachitika nchiyani?

Pali profesa wina wa zandale yemwe anaganizapo za funso limenelo. Choncho, malinga ndi kunena kwa magazini yotchedwa The Christian Century, profesayo anafunsa kuti: “Kodi pali aliyense amene angaganizire Yesu kukhala akuponya mabomba a m’manja kwa adani ake, akumagwiritsira ntchito mfuti yachiwaya, akumaponya pansi mabomba a nyukiliya ndi ndege kapena akumaponya chida cha ICBM chimene chingaphe anakubala ndi ana zikwi zambiri?”

Poyankha, profesayo anati: “Funso limenelo nlopanda tanthauzo moti silifunikira kuyankhidwa.” Ndiyeno anadzafunsa kuti: “Ngati kuchita zimenezo kunali kosagwirizana ndi umunthu wa Yesu, nanga ifeyo tingachite zimenezo bwanji koma nkukhalabe okhulupirika kwa iye?” Chotero, siziyenera kutidabwitsa poona kuti otsatira a Yesu oyambirira anali achete pankhani zankhondo, ndipo zonsezo zinalembedwa m’mabuku a mbiri yakale. Tangoganizani zitsanzo ziŵiri basi.

Buku lakuti Our World Through the Ages, lolembedwa ndi N. Platt ndi M. J. Drummond, limati: “Khalidwe la Akristu linali losiyana kwambiri ndi khalidwe la Aroma. . . . Popeza kuti Kristu ankalalikira za mtendere, iwo ankakana kukhala asilikali.” Edward Gibbon, m’buku lake lakuti The Decline and Fall of the Roman Empire, analemba kuti: “[Akristu a m’zaka za zana loyamba] anakana kutengamo phande lokangalika lililonse m’kulamulira kwa nkhondo kwa ufumuwo. . . . Kunali kosatheka kuti Akristu, popanda kukana ntchito yawo yopatulika koposa, apitirize nkukhala asilikali.”

Nanga Bwanji Lero?

Kodi alipo aliyense amene amasonyeza chikondi chonga cha Kristu? Encyclopedia Canadiana inati: “Ntchito ya Mboni za Yehova ndiyo kuyambitsidwanso ndi kukhazikitsidwanso kwa Chikristu chakale chochitidwa ndi Yesu ndi ophunzira ake mkati mwa zana loyamba ndi lachiŵiri la nyengo yathu . . . Onsewo ali abale.”

Kodi zimenezo zikutanthauzanji? Zikutanthauza kuti Mboni za Yehova sizimalola ufuko, kapena utundu—kuwadanitsa ndi anansi awo. Iwo samaphana, chifukwa mophiphiritsira anasula malupanga awo nkukhala zolimira, ndi nthungo zawo nkukhala anangwape, monga momwedi Baibulo linaneneratu kuti nzimene atumiki a Mulungu adzachita.—Yesaya 2:4.

Nchifukwa chake nkhani ina yamkonzi wa Sacramento Union ya ku California inati: “Tinganene motsimikiza kuti ngati dziko lonse linali kutsatira chiphunzitso cha Mboni za Yehova kukhetsa mwazi ndi udani zingathe, ndipo chikondi chingalamulire monga mfumu”!

Momwemonso, wolemba nkhani m’magazini yotchedwa Ring, ku Hungary, anati: “Ndikukhulupirira kuti ngati Mboni za Yehova zokha ndizo zinakhala padziko lapansi pamenepo nkhondo sizikanabuka kulikonse, ndipo ntchito yokha imene apolisi akanamachita ikanakhala yoongolera magalimoto pamsewu ndi kupatsa anthu mapasipoti.”

M’magazini yatchalitchi ya ku Italy, yotchedwa Andare alle genti, mvirigo wina wa Roma Katolika analemba mosirira Mboni kuti: “Iwo amakana kuchita chiŵaŵa chamtundu uliwonse ndipo samapanduka koma amapirira ziyeso zambiri zimene amakumana nazo chifukwa cha zikhulupiriro zawo . . . Dziko lingakhale losiyana chotani nanga ngati kuti mmaŵa wina tidzuka ndi kutsimikiza mtima zolimba kusanyamulanso zida, kaya zikhale zovuta motani kaya zikhale pazifukwa zotani, monga mmene zimachitira Mboni za Yehova!”

Mboni zimadziŵika mwa kuthandiza anansi awo. (Agalatiya 6:10) Mlativiani wina, m’buku lake lakuti Women in Soviet, anati anadwala kwambiri m’ndende ku Potma cha m’ma 1960. “Panthaŵi yonse imene ndinali kudwala, [Mboni] zinali kundisamala zedi. Zimene anandichitirazo zinali zopambana ndithu, ngakhale kuti munali m’ndende.” Anadzatinso: “Mboni za Yehova ngati ntchito yawo kuthandiza aliyense, samasamala kuti munthuyo ngwachipembedzo chanji kapena kuti ngwamtundu wanji.”

Olemba manyuzipepala ku Czech Republic anaonanso khalidwe limenelo la Mboni kumisasa yachibalo. Nyuzipepala ina yotchedwa Severocesky denik, pothirira ndemanga za filimu ina yotchedwa “The Lost Home,” yomwe inajambulidwa mumzinda wa Brno, inati: “Nzodabwitsa kuti [Ayuda achiczech ndi achislovak omwe anapulumuka] anawasirira ndi kuwayamikira andende amene anali Mboni za Yehova.” Ambirinso anathirira ndemanga kuti: “Iwo anali olimba mtima, ndipo nthaŵi zonse anali kutithandiza m’njira iliyonse imene akanatha, osasamala kuti anali kuika moyo wawo pachiswe. Ankatipempherera, ngati kuti tinali a m’banja mwawo; ankatilimbikitsa kuti tisaleme.”

Nanga bwanji tsopano zakukonda anthu amene kwenikweni amakudani? Zimenezo nzotheka?

Chikondi Chipambana Udani

Zimene Yesu anaphunzitsa za kukonda adani athu nzogwirizana ndi mwambo wa Baibulo wakuti: “Mdani wako akamva njala umdyetse, akamva ludzu ummwetse madzi.” (Miyambo 25:21; Mateyu 5:44) Ponena za mmene zinamkhudzira mtima posamalidwa mwachikondi ndi anthu amene kale anali kuwaona ngati adani, mkazi wina wachikuda yemwe anangokhala kumene wa Mboni za Yehova, analemba kuti: “Nthaŵi zina mtima wanga umakondwa kufikira pakugwetsa misozi chifukwa cha chikondi chenicheni chimene Mboni zachiyera zinandisonyeza, anthu amene ndinali nditatsala pang’ono kuwapha mosazengereza kuti ndale zisinthe.”

Mboni ina ya ku France inasimba kuti mnansi wawo wina anasumira amayi ake kwa a Gestapo pa Nkhondo Yadziko II. Mwana wamkaziyo anati: “Chifukwa cha zimenezo, amayi anga anakhala zaka ziŵiri kumisasa yachibalo ya Ajeremani, ndipo anangotsala pang’ono kufera konko. Nkhondoyo itatha, apolisi a France anafuna kuti Amayi asaine chipepala chomuimba mlandu mkazi uja chifukwa anali kugwirizana ndi Ajeremani. Koma amayi anga anakana.” Kenaka, mnansi uja anadwala kansa yakupha. Mwana wamkaziyo ndiye anati: “Amayi anatha maola ambiri akumayesetsa kumsamala pamiyezi yotsirizira ya moyo wake. Sindidzaiŵala mmene chikondicho chinapambanira udani.”

Mosakayikira, anthu angaphunzire kukondana. Omwe kale anali adani—Atutsi ndi Ahutu, Ayuda ndi Aarabu, Aarmenia ndi Ateki, Ajapani ndi Ameleka, Ajeremani ndi Arasha, Aprotesitanti ndi Akatolika—onse choonadi cha Baibulo chawagwirizanitsa!

Popeza kuti anthu mamiliyoni ambiri omwe kale anali odana tsopano akukondana, ndiye kuti zoonadi tsiku lina dziko lonse lingakondanenso. Komabe, pafunikira kuti zinthu zambiri zisinthe padziko lonse kuti anthu onse adzakondane. Kodi zinthuzo zidzasintha bwanji?

[Zithunzi patsamba 15]

Azungu ndi achikuda ku South Africa

Ayuda ndi Aarabu

Ahutu ndi Atutsi

Mophiphiritsira, Mboni zasula malupanga awo nkukhala zolimira

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena