Uthenga wa Ufumu Na. 35
Kodi Anthu Onse Adzakondanapo?
Chikondi cha Mnansi Chazirala
ANTHU miyandamiyanda akuona kuti alibe thandizo ndipo ngachisoni, osoŵa kopita. Mkazi wina yemwe kale anali wamalonda anati: ‘Madzulo ena mkazi wina wamasiye amene timakhala naye pansanjika imodzi anagogoda pachitseko panga ndi kundiuza kuti anasungulumwa. Ndinamuuza mwaulemu koma mosapita m’mbali kuti ndinali ndi zochita zina. Anapepesa pondivutitsa nachoka.’
Mwachisoni, usiku womwewo, mkazi wamasiyeyo anadzipha. Pambuyo pake, mkazi wamalondayo ananena kuti waphunzira “phunziro loŵaŵa.”
Kusakonda mnansi nthaŵi zambiri kwadzetsa tsoka. Pankhondo ya mafuko ku Bosnia ndi Herzegovina, omwe kale anali mbali ya Yugoslavia, anthu oposa miliyoni imodzi anathaŵa panyumba zawo ndipo zikwi makumi ambiri anaphedwa. Ndi yani? “Anansi athu,” analira motero mtsikana wina amene anathaŵa pamudzi pake. “Tinkawadziŵa.”
Ku Rwanda anthu zikwi mazana ambiri anaphedwa, ndi anansi awo makamaka. “Ahutu ndi Atutsi [ankakhala] pamodzi, kukwatirana, osasamala kapena osadziŵa nkudziŵa komwe kuti Mhutu ndani ndipo Mtutsi ndani,” inatero The New York Times. “Kenako zinthu zinangosintha,” ndipo “kuphana kunayamba.”
Momwemonso, Ayuda ndi Aluya ku Israel amakhala pamodzi, koma ambiri amadana. Ndi mmene zililinso ndi Akatolika ndi Aprotesitanti ku Ireland ndi anthu enanso omawonjezereka m’maiko ena. Dzikoli silinasoŵepo chikondi chonchi m’mbiri yonse.
Kodi Nchifukwa Ninji Chikondi cha Mnansi Chazirala?
Mlengi wathu akupereka yankho. Mawu ake, Baibulo, amatcha nthaŵi imene tikukhalamoyi kukhala “masiku otsiriza.” Inoyi ndiyo nthaŵi imene anthu adzakhala “opanda chikondi chachibadwidwe,” malinga ndi kunena kwa ulosi wa Baibulo. Ponena za “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino, zotchedwanso “mapeto a dongosolo la zinthu” m’Malemba, Yesu Kristu ananeneratu kuti “chikondano cha anthu aunyinji chidzazirala.”—2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:3, 12, New World Translation.
Chotero, kusoŵeka kwachikondi kwamakono ndiko mbali ya umboni wakuti tikukhala m’masiku otsiriza a dzikoli. Chokondweretsa nchakuti kumatanthauzanso kuti posachedwapa dzikoli la anthu osaopa Mulungu lidzachoka ndipo padzabwera dziko latsopano lolungama lolamuliridwa ndi chikondi.—Mateyu 24:3-14; 2 Petro 2:5; 3:7, 13.
Koma kodi tilidi nchifukwa chokhulupirira kuti kusintha kumeneku nkotheka—kuti anthu onse angaphunzire kukondana ndi kukhalira limodzi mwamtendere?
Chikondi cha Mnansi—Chidzakhalapodi
“MNANSI wanga ndani?” loya wina wa m’zaka za zana loyamba anafunsa Yesu motero. Ndithudi anayembekezera Yesu kunena kuti, ‘Ayuda anzako.’ Koma m’nthano ya Msamariya wachinansi, Yesu anasonyeza kuti anthu a mitundu ina alinso anansi athu.—Luka 10:29-37; Yohane 4:7-9.
Yesu anagogomezera kuti chachiŵiri chimene chiyenera kulamulira moyo wathu chotsatira chikondi cha pa Mulungu ndicho chikondi cha mnansi. (Mateyu 22:34-40) Koma kodi pali gulu lililonse la anthu amene anakondadi anansi awo? Akristu oyambirira anatero! Iwo ankadziŵika chifukwa cha chikondi chimene anali nacho pa ena.—Yohane 13:34, 35.
Nanga lero? Kodi alipo amene ali ndi chikondi chonga cha Kristu? Encyclopedia Canadiana imati: “Ntchito ya Mboni za Yehova ndiyo kudzukanso ndi kuyambikanso kwa Chikristu choyambirira chomwe Yesu ndi ophunzira ake ankachita . . . Onse ndi abale.”
Zikutanthauzanji zimenezo? Zikutanthauza kuti Mboni za Yehova sizimalola kalikonse—kaya fuko, kapena mtundu—kuwachititsa kuda anansi awo. Ndipo sizidzapha aliyense, chifukwa chakuti mophiphiritsira zasula malupanga awo kukhala zolimira ndi nthungo zawo kukhala anangwape. (Yesaya 2:4) Mboni, kwenikweni, zimadziŵika chifukwa chochitapo kanthu kuti zithandize anansi awo.—Agalatiya 6:10.
Ndiye chifukwa chake nkhani ina ya mkonzi mu Sacramento Union ya ku California inati: “Tinganene motsimikiza kuti ngati dziko lonse linali kutsatira chiphunzitso cha Mboni za Yehova kukhetsa mwazi ndi udani zingathe, ndipo chikondi chingalamulire monga mfumu.” Wolemba wina m’magazini ya Ring ya ku Hungary anati: “Ndaona kuti ngati Mboni za Yehova ndizo zokha zinali padziko lapansi, bwenzi kulibenso nkhondo, ndipo ntchito zokha za apolisi zikanakhala kuyang’anira kayendedwe ka magalimoto ndi kupereka mapasipoti.”
Koma ndithudi, padzafunikira kusintha kwakukulu padziko lonse kuti anthu onse azikondana. Kodi kusinthako kudzabwera motani? (Chonde onani patsamba lakumbuyo.)
Pamene Anthu Onse Adzakondana
PEMPHERO limene Yesu Kristu anaphunzitsa limasonyeza kuti kusintha kwakukulu kwatsala pang’ono kuchitika. Mu Ulaliki wake wa pa Phiri wotchukawo, Yesu anatiphunzitsa kupemphera kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:10.
Kodi Ufumu wa Mulungu nchiyani? Ndi boma lenileni, limene likulamulira lili kumwamba. Ndiye chifukwa chake ukutchedwa “ufumu wa Kumwamba.” Yesu, “Kalonga wa Mtendere,” waikidwa ndi Atate wake kukhala wolamulira wake.—Mateyu 10:7; Yesaya 9:6, 7; Salmo 72:1-8.
Ufumu wa Mulungu utadza, kodi nchiyani chidzachitikira dzikoli lodzala ndi udani? “Ulamuliro” umenewo, “udzaphwanya ndi kutha” maboma onse oipa a dzikoli. (Danieli 2:44) Baibulo limafotokoza kuti: “Dziko lapansi lipita, . . . koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.”—1 Yohane 2:17.
Ponena za dziko latsopano la Mulungu, Baibulo limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:9-11, 29; Miyambo 2:21, 22) Ndiyetu nthaŵi imeneyo idzakhala yaulemerero! “Sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.” (Chivumbulutso 21:4) Ngakhale akufa adzakhalanso ndi moyo, ndipo dziko lonse lidzasanduka paradaiso weniweni.—Yesaya 11:6-9; 35:1, 2; Luka 23:43; Machitidwe 24:15.
Kuti tikakhalemo m’dziko latsopano la Mulungu, tiyenera kukondana, monga momwe Mulungu amatiphunzitsira kukonda. (1 Atesalonika 4:9) Wophunzira Baibulo wina wa Kummaŵa anati: “Ndikuyembekeza nthaŵi pamene, monga momwe Baibulo limalonjezera, anthu onse adzakhala ataphunzira kukondana.” Ndipo ndife otsimikiza kuti Mulungu adzasunga malonjezo ake! “Ndanena,” akutero, “ndidzachichitanso.”—Yesaya 46:11.
Koma kuti mukasangalale ndi madalitso mu Ufumu wa Mulungu, muyenera kuloŵetsa chidziŵitso cha Baibulo, monga momwe anthu oona mtima mamiliyoni ambiri padziko lonse akuchitira. (Yohane 17:3) Brosha lamasamba 32 lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? lidzakuthandiza- ni. Pezani kope lake mwa kudzaza fomu yoperekedwa patsamba linalo ndi kuitumiza ku keyala yapafupi nanu.
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Wolasa anthu mfuti ndi maliro ku Bosnia: Reuters/Corbis-Bettmann