Pamene Sikudzakhalanso Kupunduka
MAYI wina wakufa manja ndi miyendo yonse tsiku lina anati, anthu ambiri “amayenda ndi kugwira ntchito bwinobwino kwa kanthaŵi.” Zimenezo n’zoona kwambiri, chifukwa chakuti panthaŵi ina tidzapeza kuti tonsefe takhala ndi chilema china! N’chifukwa chake pali anthu ambiri ogula magalasi a maso, oikitsa mano, ogula zipangizo zothandizira kumva, ogula zipangizo zothandizira kugunda kwa mtima, ndi oikiridwa maondo ena. Monga mmene Aroma 8:22 amanenera kuti, “cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano.”
Choncho, tonsefe tingatonthozeke mtima pakumva zimene Mulungu walonjeza kuti adzapangitsa anthu kukhalanso ndi thanzi langwiro “m’dziko latsopano” lolungama. (2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4) Yesaya 35:5, 6 amati: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. . . . Wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba.”
Baibulo limaneneratu kuti “khamu lalikulu” lidzapulumuka pachiwonongeko cha dongosolo loipali. (Chivumbulutso 7:9, 14; Salmo 37:10, 11, 29) Sitikukayikira kuti pambuyo pa chiwonongekocho, anthu opunduka ndiponso amene ali ndi mavuto aakulu a thanzi adzachiritsidwa nthaŵi yomweyo! (Yesaya 33:24) Yesu adakali padziko lapansi anayamba wachiritsapo anthu mwa njira imeneyo, kuti asonyeze mmene zidzachitikira m’dziko latsopano la Mulungu. (Yerekezerani ndi Marko 5:25-29; 7:33-35.) Simungathe ngakhale pang’ono kusimba chimwemwe chimene anthu adzakhala nacho, ndi misozi yachisangalalo imene adzagwetsa, poona oduka ziŵalo akutaya ziŵalo zawo zopanga, kutaya ndodo, ndi njinga zawo zopalasa ndi manja! Poti tsopano thupi lawo lidzakhala lili bwino, adzakhoza kuchita ntchito imene Mulungu wawapatsa, yothandiza kusandutsa dzikoli kuti likhale mudzi wa paradaiso.—Luka 23:43.
Pakali pano, opunduka adakali kuvutikira kuchita zinthu. Nelson, munthu wopunduka wa ku Canada, anati: “Ndikangoyamba kudzimvera chisoni, ndimakumbukira mawu a Yesu a pa Mateyu 24:13, akuti: ‘Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.’” Anthu opunduka, ngakhale amalephera kuchita zinthu zina, ndi abwinobwino m’njira ina yofunika kwambiri—mwauzimu—mwa kupirira pachikhulupiriro chachikristu.—Yakobo 1:3, 4.
Mboni za Yehova zikuthandiza anthu mamiliyoni kukhala ndi chikhulupiriro chimenechi. Dell, munthu wina wopunduka amene mawu ake akupezeka m’nkhani yoyamba ija, anati: “Sindingasimbe mmene ndinamvera pamene ndinadziŵa kuti mavuto ngati angawa ndi akanthaŵi chabe.” Inde, chifukwa cholimbikitsidwa ndi chiyembekezo chimenecho Dell—limodzi ndi enanso onga iye—sangaonedwenso ngati opunduka ayi.
[Chithunzi patsamba 10]
Amene adzapulumuke pa chiwonongeko chikudzacho kupunduka kwawo kudzachiritsidwa modabwitsa